NKHANI YOPHUNZIRA 31

Muziyamikira Mwayi Wanu wa Pemphero

Muziyamikira Mwayi Wanu wa Pemphero

“Pemphero langa likhale ngati zofukiza pamaso panu.”—SAL. 141:2.

NYIMBO NA. 47 Muzipemphera kwa Yehova Tsiku Lililonse

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi tiziona bwanji mwayi wopemphera kwa Yehova?

 TINAPATSIDWA mwayi wamtengo wapatali kwambiri wolankhulana m’pemphero ndi Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi. Tangoganizani, tingathe kumuuza Yehova zakukhosi kwathu nthawi ina iliyonse komanso m’chilankhulo chilichonse popanda kupempha kaye chilolezo. Tikhoza kupemphera kwa iye kaya tili m’chipatala kapena m’ndende n’kumakhulupirira kuti Atate wathu wachikondiyu atimvetsera. Sitimaona mopepuka mwayi umenewu.

2. Kodi Mfumu Davide inasonyeza bwanji kuti inkayamikira mwayi wa pemphero?

2 Mfumu Davide inkayamikira mwayi wa pemphero. Iye anaimbira Yehova kuti: “Pemphero langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza pamaso panu.” (Sal. 141:1, 2) M’nthawi ya Davide, zofukiza zopatulika zomwe ansembe ankagwiritsa ntchito polambira zinkakonzedwa mosamala kwambiri. (Eks. 30:34, 35) Potchula zofukiza, Davide ankatanthauza kuti ankaganizira bwino zomwe akufuna kulankhula m’pemphero kwa Atate wake wakumwamba. Zimenezi ndi zomwe ifenso timafuna, kuti mapemphero athu azikhala osangalatsa kwa Yehova.

3. Kodi tizikhala ndi maganizo otani tikamapemphera kwa Yehova, nanga n’chifukwa chiyani?

3 Tikamapemphera kwa Yehova tiyenera kuchita zinthu mwaulemu kwambiri. Taganizirani masomphenya ochititsa chidwi omwe Yesaya, Ezekieli, Danieli ndi Yohane anaonetsedwa. Ngakhale kuti masomphenyawo anali osiyana, panali chinthu china chofanana. Onsewa amasonyeza kuti Yehova ndi Mfumu yolemekezeka. Yesaya ‘anaona Yehova atakhala pampando wachifumu wolemekezeka umene unali pamalo okwezeka.’ (Yes. 6:1-3) Ezekieli anaona Yehova atakhala pagaleta lake lakumwamba “ndipo pamalo onse omuzungulira panali powala . . . ngati utawaleza.” (Ezek. 1:26-28) Danieli anaona “Wamasiku Ambiri” atavala zovala zoyera ndipo kumpando wake wachifumu kunkayaka moto. (Dan. 7:9, 10) Ndipo Yohane anaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu utazunguliridwa ndi utawaleza wooneka ngati mwala wa emarodi. (Chiv. 4:2-4) Tikamaganizira ulemerero waukulu womwe Yehova ali nawo, timakumbutsidwa za mwayi wamtengo wapatali wolankhula naye m’pemphero komanso kufunika kochita zimenezo mwaulemu. Koma kodi tizipemphera bwanji?

“KOMA INU MUZIPEMPHERA MOTERE”

4. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu oyamba a m’pemphero lachitsanzo la pa Mateyu 6:9, 10?

4 Werengani Mateyu 6:9, 10. Pa ulaliki wake wapaphiri, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake mmene angapempherere m’njira imene ingasangalatse Mulungu. Atanena kuti “koma inu muzipemphera motere,” choyamba Yesu anatchula nkhani zofunika zomwe zimagwirizana ndi cholinga cha Yehova. Anatchula za kuyeretsedwa kwa dzina lake, kubwera kwa Ufumu womwe udzawononge onse otsutsa Mulungu komanso madalitso a m’tsogolo okhudza anthu ndi dziko lapansili. Tikamatchula nkhani zimenezi m’mapemphero athu timasonyeza kuti timaona kuti chifuniro cha Mulungu n’chofunika.

5. Kodi n’zofunika kuti tizitchula m’mapemphero athu nkhani zokhudza ifeyo?

5 M’mbali yotsatira ya pempheroli, Yesu anasonyeza kuti n’zofunikanso kuti tizipempherera nkhani zokhudza ifeyo. Tingapemphe Yehova kuti atipatse chakudya cha tsikulo, atikhululukire machimo athu, atiteteze ku mayesero komanso atipulumutse kwa woipayo. (Mat. 6:11-13) Tikamamupempha zinthu zimenezi timasonyeza kuti tikumudalira komanso tikufunitsitsa kukhala naye pa ubwenzi.

Kodi mwamuna ndi mkazi wake angapempherere zinthu ziti? (Onani ndime 6) *

6. Kodi tiyenera kumangopempherera zinthu zokhazo zimene zinatchulidwa m’pemphero lachitsanzo? Fotokozani.

6 Yesu sankayembekezera kuti otsatira ake azitchula ndendende mawu a m’pemphero lachitsanzo. M’mapemphero ake ena anatchula nkhani zomwe zinali zofunika kwambiri kwa iye pa nthawiyo. (Mat. 26:39, 42; Yoh. 17:1-26) Mofanana ndi zimenezi, ifenso tingapempherere nkhani zomwe zikutidetsa nkhawa. Tikafuna kusankha zochita pa nkhani inayake tingapemphe Yehova kuti atipatse nzeru komanso atithandize kumvetsa zinthu. (Sal. 119:33, 34) Tikamayamba utumiki winawake wovuta, tingamupemphe kuti atithandize kukhala ozindikira. (Miy. 2:6) Makolo angapempherere ana awo ndipo ana angapempherere makolo awo, komanso tonsefe tizipempherera omwe timaphunzira nawo Baibulo ndiponso anthu omwe timawalalikira. Komabe mapemphero athu sayenera kukhala ongopempha zinazake.

Kodi tingatamande komanso kuyamikira Yehova pa zinthu ziti m’mapemphero athu? (Onani ndime 7-9) *

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kutamanda Yehova m’mapemphero athu?

7 Tizikumbukira kutamanda Yehova m’mapemphero athu. Palibe wina amene tiyenera kumutamanda kuposa Mulungu wathu. Iye ndi ‘wabwino ndipo ndi wokonzeka kukhululuka.’ Komanso ndi “wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndi wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.” (Sal. 86:5, 15) Poganizira mmene alili ndiponso zimene amachita, tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kumutamanda.

8. Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe zingatichititse kumuthokoza Yehova? (Salimo 104:12-15, 24)

8 Kuwonjezera pa kumutamanda m’mapemphero athu, tiyeneranso kumathokoza Yehova chifukwa cha zinthu zabwino zimene amatipatsa komanso chifukwa chokhala ndi anzathu ambiri abwino. Atate wathu wachikondi amatipatsa zimenezi ndi zinanso zambiri chifukwa amafuna tizisangalala. (Werengani Salimo 104:12-15, 24.) Koposa zonse, timathokoza Yehova chifukwa chotipatsa chakudya chauzimu chochuluka komanso chiyembekezo chosangalatsa cha m’tsogolo.

9. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikumbukira kuthokoza Yehova? (1 Atesalonika 5:17, 18)

9 Zingakhale zosavuta kuiwala kuthokoza Yehova pa zonse zimene amatichitira. Ndiye n’chiyani chingatithandize? Tingalembe zinthu zosiyanasiyana zomwe tamupempha n’kumaona nthawi ndi nthawi mmene wayankhira mapemphero athuwo. Kenako tizipemphera n’kumuthokoza chifukwa chotithandiza. (Werengani 1 Atesalonika 5:17, 18.) Taganizirani izi: Timasangalala komanso kumva kuti timakondedwa anthu ena akatiyamikira pa zimene tachita. Mofanana ndi zimenezi, tikamakumbukira kuthokoza Yehova chifukwa choyankha mapemphero athu, nayenso amasangalala. (Akol. 3:15) Koma kodi ndi chifukwa china chiti chachikulu chomwe chimatichititsa kuthokoza Mulungu wathu?

TIZITHOKOZA YEHOVA CHIFUKWA CHA MWANA WAKE

10. Mogwirizana ndi 1 Petulo 2:21, n’chifukwa chiyani tiyenera kuthokoza Yehova chifukwa chotumiza Yesu padzikoli?

10 Werengani 1 Petulo 2:21. Tiyenera kuthokoza Yehova chifukwa chotumiza Mwana wake kuti adzatiphunzitse. Kuphunzira za Yesu kumatithandiza kudziwa zambiri zokhudza Yehova komanso zimene tingachite kuti tizimusangalatsa. Ngati titamakhulupirira nsembe ya Khristu tikhoza kukhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova Mulungu komanso kukhala naye pamtendere.​—Aroma 5:1.

11. Kodi Yesu ali ndi udindo wotani pa mapemphero omwe timapereka kwa Yehova?

11 Timathokoza Yehova chifukwa tingathe kupemphera kwa iye kudzera mwa Mwana wake. Yehova amagwiritsa ntchito Yesu poyankha mapemphero athu. Iye amamvetsera komanso kuyankha tikapemphera kudzera m’dzina la Yesu. Yesu anafotokoza kuti: “Chilichonse chimene mudzapemphe m’dzina langa, ine ndidzachichita, kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana wake.”​—Yoh. 14:13, 14.

12. Kodi chifukwa chinanso n’chiti chotipangitsa kuthokoza Yehova potipatsa Mwana wake?

12 Yehova amatikhululukira machimo athu chifukwa cha nsembe ya Yesu. Malemba amafotokoza Yesu monga ‘mkulu wa ansembe amene wakhala pansi kumwamba, kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Wolemekezeka.’ (Aheb. 8:1) Iye ndi “mthandizi . . . amene ali ndi Atate.” (1 Yoh. 2:1) Timathokoza Yehova chifukwa chotipatsa Mkulu wa Ansembe yemwe amamvetsa zofooka zathu ndipo “amatilankhulira mochonderera” kwa Mulungu. (Aroma 8:34; Aheb. 4:15) Popeza si ife angwiro, sitikanatha kumalankhula ndi Yehova m’pemphero popanda nsembe ya Yesu. Kunena zoona, sitingathe kumuyamikira mokwanira chifukwa chotipatsa mphatso yamtengo wapatali yomwe ndi Mwana wake wokondedwa.

MUZIPEMPHERERA ABALE NDI ALONGO ANU

13. Pa usiku wake womaliza, kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakonda ophunzira ake?

13 Pa usiku wake womaliza, Yesu anapempherera ophunzira ake kwa nthawi yaitali, kupempha Atate wake kuti ‘awayang’anire kuopera woipayo.’ (Yoh. 17:15) Apatu Yesu anasonyeza chikondi chachikulu. Iye ankayembekezera kukumana ndi mayesero aakulu, komabe ankadera nkhawa za atumwi ake.

Kodi tingawapempherere chiyani abale ndi alongo athu? (Onani ndime 14-16) *

14. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda abale ndi alongo athu?

14 Potsanzira Yesu, ifenso sitimangoganizira zofuna zathu zokha. M’malomwake, nthawi zonse timapempherera abale ndi alongo athu. Tikamachita zimenezi timakhala tikumvera lamulo la Yesu lakuti tizikondana ndipo timamusonyeza Yehova kuti timakonda kwambiri Akhristu anzathu. (Yoh. 13:34) Kupempherera abale ndi alongo athu n’kothandiza kwambiri. Mawu a Mulungu amatiuza kuti “pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.”​—Yak. 5:16.

15. N’chifukwa chiyani tiyenera kupempherera Akhristu anzathu?

15 Timafunika kupempherera Akhristu anzathu chifukwa nawonso akukumana ndi mavuto ambiri. Tingapemphe Yehova kuti awathandize kupirira matenda, ngozi zam’chilengedwe, nkhondo, kuzunzidwa kapenanso mavuto ena. Tingapemphererenso abale ndi alongo amene amagwira ntchito mwakhama pothandiza omwe akumana ndi mavuto. Mwina mukudziwa ena amene akukumana ndi mavuto ngati amenewa. Bwanji osatchula mayina awo mukamapemphera panokha? Timasonyeza kuti timawakonda tikamapempha Yehova kuti awathandize kupirira.

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kumapempherera amene amatitsogolera?

16 Abale omwe amatsogolera mpingo amayamikira kwambiri tikamawapempherera ndipo mapempherowa amawathandiza. Ndi mmenenso zinalili ndi mtumwi Paulo. Iye analemba kuti: “[Muzipemphereranso] ineyo. Chitani zimenezi kuti ndikatsegula pakamwa panga kuti ndilankhule, ndizitha kulankhula mwaufulu kuti ndidziwitse ena chinsinsi chopatulika cha uthenga wabwino.” (Aef. 6:19) Masiku anonso pali abale ambiri omwe amagwira ntchito mwakhama potitsogolera. Timasonyeza kuti timawakonda tikamapempha Yehova kuti aziwathandiza pa ntchito yawo.

TIKAMAIMIRA ENA M’PEMPHERO

17-18. Kodi ndi pa nthawi ziti pamene tingapemphedwe kuimira ena m’pemphero, nanga tiyenera kukumbukira chiyani?

17 Nthawi zina tingapemphedwe kuti tipemphere m’malo mwa anthu ena. Mwachitsanzo, mlongo yemwe akuchititsa phunziro la Baibulo angapemphe mlongo wina yemwe wapita naye kuphunziroko kuti apemphere. Mlongo winayo angakhale kuti sakudziwa bwinobwino wophunzirayo. Choncho angakonde kupereka pemphero lomaliza. Zimenezi zingathandize kuti adziwe zomwe angatchule zokhudza wophunzirayo m’pempherolo.

18 M’bale angauzidwe kuti apemphere pamsonkhano wampingo kapena wokonzekera utumiki. Abale amene apatsidwa mwayi umenewu ayenera kukumbukira cholinga cha misonkhanoyi. Pemphero si njira yoperekera malangizo kapena zilengezo. Pamisonkhano yampingo yambiri pamaperekedwa 5 minitsi ya nyimbo ndi pemphero. Choncho m’bale amene akupemphera sayenera kunena “mawu ambirimbiri” makamaka m’pemphero la koyambirira kwa misonkhano.​—Mat. 6:7.

MUZIONA PEMPHERO KUKHALA LOFUNIKA KWAMBIRI PA MOYO WANU

19. Kodi n’chiyani chingatithandize kukonzekera tsiku la Yehova lachiweruzo?

19 Pamene tsiku lachiweruzo la Yehova likuyandikira, tiziona pemphero kukhala lofunika kwambiri pa moyo wathu. Pa nkhaniyi Yesu anati: “Chotero khalani maso ndipo muzipemphera mopembedzera nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kuchitika.” (Luka 21:36) Choncho kupemphera nthawi zonse kungatithandize kukhalabe maso mwauzimu kuti tsiku la Yehova lisadzatipeze modzidzimutsa tisanakonzekere.

20. Kodi tingatani kuti mapemphero athu azikhala ngati zofukiza zonunkhira bwino?

20 Kodi takambirana chiyani? Timaona kuti kupemphera ndi mwayi wamtengo wapatali. Nkhani zofunika kwambiri m’mapemphero athu ziyenera kukhala zogwirizana ndi cholinga cha Yehova. Timayamikiranso Mulungu chifukwa cha Mwana wake ndi Ufumu wake. Komanso timapempherera Akhristu anzathu. Tingathenso kupempherera zinthu zimene timafunikira pa moyo wathu komanso kuti Mulungu atithandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Tikamaganizira mosamala zimene tikufuna kutchula m’mapemphero athu, timasonyeza kuti timayamikira kwambiri mwayi wamtengo wapatali wa pemphero. Tikamachita zimenezi mapemphero athu adzakhala ngati zofukiza zonunkhira bwino kwa Yehova, zomwe ‘zimamusangalatsa.’​—Miy. 15:8.

NYIMBO NA. 45 Kusinkhasinkha kwa Mtima Wanga

^ Timayamikira kwambiri mwayi wopemphera kwa Yehova. Timafuna kuti mapemphero athu azikhala ngati zofukiza zonunkhira bwino, zomwe zingamusangalatse. Munkhaniyi, tikambirana zimene tingatchule m’mapemphero athu. Tikambirananso mfundo zina zimene tiyenera kukumbukira tikapemphedwa kuti tiimire anthu ena m’pemphero.

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mwamuna ndi mkazi wake akupempherera mwana wawo kuti akhale otetezeka kusukulu, kholo lawo lachikulire lomwe likudwala komanso wophunzira Baibulo wawo kuti apite patsogolo.

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Wachinyamata akuthokoza Yehova chifukwa cha nsembe ya Yesu, dziko lathu lokongolali komanso chakudya chopatsa thanzi.

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo akupempha Yehova kuti athandize Bungwe Lolamulira ndi mzimu wake komanso athandize omwe akuvutika chifukwa cha ngozi zam’chilengedwe ndiponso kuzunzidwa.