NKHANI YOPHUNZIRA 29

Tizithandiza Mtsogoleri Wathu Yesu

Tizithandiza Mtsogoleri Wathu Yesu

“Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.”​—MAT. 28:18.

NYIMBO NA. 13 Khristu Ndi Chitsanzo Chathu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi cholinga cha Yehova masiku ano n’chiyani?

 MASIKU ano, cholinga cha Mulungu ndi choti uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe padziko lonse. (Maliko 13:10; 1 Tim. 2:3, 4) Ntchitoyi ndi ya Yehova, choncho n’zosangalatsa kwambiri kuti wasankha Mwana wake wokondedwa kuti aziitsogolera. Tingakhale otsimikiza kuti popeza Yesu ndi amene akutsogolera ntchito yolalikirayi, tidzaimaliza monga mmene Yehova akufunira mapeto asanafike.​—Mat. 24:14.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Munkhaniyi, tiona mmene Yesu akugwiritsira ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” popereka malangizo a m’Mawu a Mulungu komanso kutsogolera otsatira ake pa ntchito yaikulu yolalikira yomwe ikuchitika. (Mat. 24:45) Tionanso zimene aliyense angachite pothandiza Yesu ndi kapolo wokhulupirika.

YESU AKUTSOGOLERA NTCHITO YOLALIKIRA

3. Kodi Yesu anapatsidwa udindo wotani?

3 Yesu ndi amene akutsogolera ntchito yolalikira. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Atangotsala pang’ono kupita kumwamba, Yesu anakumana ndi otsatira ake okhulupirika paphiri ku Galileya. Anawauza kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” Taonani zimene kenako ananena: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.” (Mat. 28:18, 19) Yesu anapatsidwanso udindo wotsogolera ntchito yolalikira.

4. N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti Yesu akupitiriza kutsogolera ntchito yolalikira?

4 Yesu ananena kuti ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa idzachitika ‘m’mitundu yonse’ ya anthu ndiponso kuti iye adzakhala ndi otsatira ake “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Mawu amenewa akusonyeza kuti Yesu akupitiriza kutsogolera ntchito yolalikira mpaka m’masiku athu ano.

5. Kodi timathandiza bwanji kukwaniritsa ulosi wa pa Salimo 110:3?

5 Yesu sankada nkhawa kuti kudzakhala anthu ochepa ogwira ntchito yolalikira munthawi ya mapeto. Iye ankadziwa kuti ulosi womwe wolemba masalimo ananena udzakwaniritsidwa, wakuti: “Anthu ako adzadzipereka mofunitsitsa pa tsiku limene udzatsogolera asilikali ako kunkhondo.” (Sal. 110:3) Ngati mukugwira nawo ntchito yolalikira, mukuthandiza Yesu ndi kapolo wokhulupirika komanso mukukwaniritsa nawo ulosiwu. Ntchitoyi ikupita patsogolo, komabe pali mavuto ena.

6. Kodi ndi vuto limodzi liti lomwe olalikira za Ufumu amakumana nalo masiku ano?

6 Vuto limodzi lomwe olalikira za Ufumu amakumana nalo ndi kutsutsidwa. Ampatuko, atsogoleri azipembedzo komanso andale achititsa anthu ambiri kuti aziona molakwika ntchito yathu. Ngati achibale athu, anthu odziwana nawo komanso amene timagwira nawo ntchito asokonezedwa ndi zimenezi, angatikakamize kuti tisiye kutumikira Yehova komanso kulalikira. Pofuna kutsutsa ntchito yathu, m’mayiko ena abale ndi alongo amaukiridwa, kuopsezedwa ngakhalenso kutsekeredwa m’ndende. Koma sitimadabwa nazo zimenezi. Yesu ananeneratu kuti: “Mitundu yonse idzadana nanu chifukwa cha dzina langa.” (Mat. 24:9) Zimene anthu amachita podana nafe ndi umboni wakuti Yehova akusangalala nafe. (Mat. 5:11, 12) Mdyerekezi ndi amene amachititsa kuti tizitsutsidwa. Koma iye alibe mphamvu poyerekeza ndi Yesu. Chifukwa choti Yesu akutithandiza, uthenga wabwino ukulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. Tiyeni tione umboni wake.

7. Kodi mukuona umboni wotani wosonyeza kuti lemba la Chivumbulutso 14:6, 7, likukwaniritsidwa?

7 Monga olalikira za Ufumu, vuto linanso lomwe timakumana nalo ndi lakuti timafunika kulalikira kwa anthu azilankhulo zosiyanasiyana. M’masomphenya amene anaonetsa mtumwi Yohane, Yesu anasonyeza kuti uthenga wabwino udzalalikidwabe ngakhale pali mavuto ambiri. (Werengani Chivumbulutso 14:6, 7.) Motani? Timayesetsa mmene tingathere kuuza anthu ambiri uthenga wa Ufumu. Masiku ano, anthu padziko lonse angathe kuwerenga mabuku ofotokoza Baibulo pawebusaiti yathu ya jw.org muzilankhulo zoposa 1,000. Bungwe Lolamulira linavomereza kuti buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, lomwe timagwiritsa ntchito pophunzira Baibulo ndi anthu, limasuliridwe m’zilankhulo zoposa 700. Malangizo a m’Baibulo akhala akuperekedwa kwa anthu amene ali ndi vuto losamva pogwiritsa ntchito mavidiyo komanso kwa anthu amene ali ndi vuto losaona pali mabuku othandiza anthu omwe ali ndi vutoli. Tikuona maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa. Anthu “ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu” akuphunzira kulankhula “chilankhulo choyera,” chomwe ndi mfundo za choonadi cha m’Baibulo. (Zek. 8:23; Zef. 3:9) Zonsezi zikutheka chifukwa chakuti Yesu Khristu ndi amene akutsogolera ntchitoyi.

8. Kodi ntchito yolalikira imakhala ndi zotsatirapo zotani?

8 Masiku ano, anthu oposa 8 miliyoni omwe ali m’mayiko 240, ali m’gulu la Yehova ndipo chaka chilichonse anthu ambiri amabatizidwa. N’zoona kuti anthuwo alipo ambiri, komabe chofunika kwambiri n’chakuti anthu amenewa asintha makhalidwe awo ndipo avala “umunthu watsopano.” (Akol. 3:8-10) Ambiri anasiya chiwerewere, chiwawa, tsankho komanso kukonda kwambiri dziko lawo. Ulosi wa pa Yesaya 2:4, ukukwaniritsidwa womwe umati, “sadzaphunziranso nkhondo.” Tikamayesetsa kuvala umunthu watsopano, timathandiza anthu kuti alowe m’gulu la Mulungu ndipo timasonyeza kuti tikutsatira mtsogoleri wathu Khristu Yesu. (Yoh. 13:35; 1 Pet. 2:12) Komatu zimenezi sikuti zimangochitika mwangozi. Yesu ndi amene amatithandiza.

YESU ANASANKHA KAPOLO

9. Mogwirizana ndi Mateyu 24:45-47, kodi Yesu ananeneratu chiyani zokhudza nthawi ya mapeto?

9 Werengani Mateyu 24:45-47. Yesu ananeneratu kuti munthawi yamapeto, adzasankha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azipereka malangizo a m’Mawu a Mulungu. Choncho tingayembekezere kuti kapoloyu azichita khama pa ntchito yake. Ndipo ndi zimene zikuchitikadi. Mtsogoleri wathu wakhala akugwiritsa ntchito kagulu ka amuna odzozedwa popereka ‘chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera’ kwa anthu ake komanso anthu omwe asonyeza chidwi. Amuna amenewa sadziona monga olamulira chikhulupiriro cha ena. (2 Akor. 1:24) M’malomwake iwo amazindikira kuti Yesu Khristu ndiye “mtsogoleri ndi wolamulira” wa anthu ake.​—Yes. 55:4.

10. Kodi ndi buku liti pachithunzipa lomwe linakuthandizani kuti muyambe kuyenda panjira yopita kumoyo wosatha?

10 Kungoyambira mu 1919, kapolo wokhulupirika wakhala akukonza mabuku osiyanasiyana omwe athandiza anthu achidwi kuphunzira mfundo za choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu. Mu 1921, kapoloyu anatulutsa buku lakuti Zeze wa Mulungu pofuna kuthandiza anthu omwe asonyeza chidwi kuphunzira mfundo zoyambirira za m’Baibulo. M’kupita kwa nthawi, mabuku enanso akhala akutulutsidwa. Ndi buku liti lomwe linakuthandizani inuyo kuti mudziwe komanso kuyamba kukonda Atate wathu wakumwamba? Kodi ndi la “Mulungu Akhale Woona,” Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, Zimene Baibulo Limaphunzitsa kapena ndi buku latsopano lakuti, Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale? Mabuku onsewa ankakonzedwa mogwirizana ndi mmene zinthu zinalili pa nthawi yomwe ankatulutsidwa.

11. N’chifukwa chiyani tonsefe timafunikira chakudya chauzimu?

11 Si anthu amene angoyamba kuphunzira Baibulo okha omwe amafunika kudziwa mfundo zozama zokhudza Yehova ndiponso Mawu ake. Tonsefe timafunikira mfundozi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chakudya chotafuna ndi cha anthu okhwima mwauzimu.” Iye anawonjezera kuti kugwiritsa ntchito mfundo zotere kungatithandize kuti ‘tizisiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’ (Aheb. 5:14) M’masiku ovuta ano, pomwe makhalidwe a anthu aipa kwambiri, si zophweka kutsatira mfundo za Yehova. Koma Yesu amaonetsetsa kuti tapeza mphamvu zomwe timafunikira potipatsa malangizo abwino omwe angalimbitse chikhulupiriro chathu. Malangizo amenewa amachokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Kapolo wokhulupirika amakonza komanso kugawa chakudya chauzimuchi motsogoleredwa ndi Yesu.

12. Mofanana ndi Yesu, kodi timasonyeza bwanji kuti timalemekeza dzina la Mulungu?

12 Mofanana ndi Yesu, dzina la Mulungu timalipatsa ulemu umene limafunikira. (Yoh. 17:6, 26) Mwachitsanzo, mu 1931 tinayamba kudziwika ndi dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova. Zimenezi zinasonyeza kuti timaona kuti dzina la Atate wathu wakumwambali ndi lofunika kwambiri kwa ife. (Yes. 43:10-12) Ndipo kuchokera mu October m’chaka chimenecho, dzinali lakhala likupezeka patsamba loyamba la magazini ya Nsanja ya Olonda. Kuwonjezera pamenepo, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika linabwezeretsa dzina la Mulungu m’malo ake oyenerera. Izitu n’zosiyana kwambiri ndi zomwe matchalitchi omwe amati ndi a Chikhristu achita pochotsa dzina la Yehova m’Mabaibulo awo.

YESU ANAKHAZIKITSA GULU LAKE

13. N’chiyani chimakutsimikizirani kuti Yesu akugwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” masiku ano? (Yohane 6:68)

13 Kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” Yesu anakhazikitsa gulu lochititsa chidwi padzikoli lomwe limalimbikitsa kulambira koyera. Kodi mumaliona bwanji gulu limeneli? Mwina mumamva ngati mmene mtumwi Petulo anamvera, yemwe anauza Yesu kuti: “Tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.” (Yoh. 6:68) Kodi bwenzi zinthu zili bwanji kwa aliyense wa ife zikanakhala kuti sitinalowe m’gulu la Yehova? Kudzera m’gululi, Khristu amaonetsetsa kuti tikudyetsedwa bwino mwauzimu. Amatiphunzitsanso mmene tingachitire utumiki wathu mwaluso. Kuwonjezera pamenepo, amatithandizanso kuvala “umunthu watsopano” n’cholinga choti tizisangalatsa Yehova.​—Aef. 4:24.

14. Kodi mwapindula bwanji pa nthawi ya mliri wa COVID-19, chifukwa chokhala m’gulu la Yehova?

14 Yesu amatipatsa malangizo anzeru pa nthawi yamavuto. Tinaona umboni wa zimenezi pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Pamene anthu ambiri m’dzikoli sankadziwa zoyenera kuchita, Yesu anaonetsetsa kuti tikulandira malangizo omveka bwino otithandiza kukhala otetezeka. Tinkalimbikitsidwa kuvala masiki tikakhala pagulu komanso kukhala motalikirana. Akulu analimbikitsidwa kuti ayenera kumalankhulana ndi abale ndi alongo a mumpingo mwawo kuti adziwe zimene akufunikira kuti akhale otetezeka, athanzi komanso kuti alimbitse ubwenzi wawo ndi Yehova. (Yes. 32:1, 2) Tinkalimbikitsidwa komanso kulandira malangizo owonjezereka kudzera m’malipoti a Bungwe Lolamulira.

15. Kodi ndi malangizo otani omwe anaperekedwa pa nthawi ya mliriwu okhudza misonkhano komanso kulalikira, ndipo panakhala zotsatirapo zotani?

15 Pa nthawi ya mliriyi tinalandiranso malangizo a mmene tingachitire misonkhano komanso kugwira ntchito yolalikira. Mofulumira kwambiri tinayamba kuchita misonkhano yampingo, yadera komanso yachigawo kudzera pavidiyokonferensi. Tinayambanso kulalikira pongogwiritsa ntchito foni komanso kulemba makalata. Yehova anadalitsa khama lathu. Malipoti a maofesi anthambi ambiri akusonyeza kuti chiwerengero cha ofalitsa chakwera. Ndipotu abale ndi alongo ambiri akumana ndi zosangalatsa pa nthawiyi.​—Onani bokosi lakuti, “ Yehova Amadalitsa Ntchito Yathu Yolalikira.”

16. Kodi tingakhale otsimikiza za chiyani?

16 Anthu ena akhoza kumaona ngati gulu linkakhwimitsa zinthu kwambiri pa nthawi ya mliriwu. Koma nthawi zonse zinkachita kuonekeratu kuti malangizo omwe tinkapatsidwa anali anzeru. (Mat. 11:19) Ndipo tikamaganizira mmene Yesu wakhala akutsogolera anthu ake mwachikondi, timakhala otsimikiza kuti kaya tikumana ndi zotani m’tsogolomu, Yehova ndi Mwana wake wokondedwa sadzatisiya.​—Werengani Aheberi 13:5, 6.

17. Kodi mumamva bwanji chifukwa chotsogoleredwa ndi Yesu?

17 Ndife osangalala kwambiri kuti timatsogoleredwa ndi Yesu. Tili m’gulu limene anthu ake ndi ogwirizana ngakhale kuti amasiyana zikhalidwe, mitundu komanso zilankhulo. Timapatsidwa malangizo ochuluka ochokera m’Mawu a Mulungu komanso timaphunzitsidwa mmene tingagwirire ntchito yolalikira. Aliyense payekha amathandizidwa kuvala umunthu watsopano ndipo timaphunzitsidwa kukondana. Tili ndi zifukwa zonse zokhalira onyadira chifukwa chokhala ndi Yesu monga mtsogoleri wathu.

NYIMBO NA. 16 Tamandani Yehova Chifukwa cha Mwana Wake Wodzozedwa

^ Amuna, akazi komanso ana ambirimbiri akulalikira mwakhama uthenga wabwino. Kodi inunso ndi m’modzi wa anthu amenewa? Ngati ndi choncho, dziwani kuti mukugwira nawo ntchito yomwe Ambuye wathu Yesu Khristu akutsogolera. Munkhaniyi, tiona umboni wosonyeza kuti Yesu akutsogolera ntchito yolalikirayi. Kuganizira zimenezi kutithandiza kuti tikhale otsimikiza kupitiriza kutumikira Yehova motsogoleredwa ndi Khristu.