NKHANI YOPHUNZIRA 28

Ufumu Ukulamulira

Ufumu Ukulamulira

“Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake.”​—CHIV. 11:15.

NYIMBO NA. 22 Ufumu Umene Ukulamulira Kumwamba Ubwere

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi sitiyenera kukayikira za chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

 MUKAGANIZIRA mmene zinthu zilili m’dzikoli, kodi mumakayikira kuti zinthu zidzakhala bwino? Anthu m’mabanja ambiri sakukondananso, ndipo anthu achiwawa, odzikonda komanso ankhanza ali pena paliponse. Ambirinso zimawavuta kukhulupirira anthu audindo. Komatu zochitika zimenezi zingakulimbikitseni. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa anthu akuchita ndendende zimene zinatchulidwa mu ulosi wochititsa chidwi wokhudza “masiku otsiriza.” (2 Tim. 3:1-5) Kukwaniritsidwa kwa ulosiwu, womwe anthu oona mtima sangatsutse kuti ukukwaniritsidwa, kumapereka umboni woti Khristu Yesu anayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Komatu palinso maulosi ena ambiri onena za Ufumuwu. Kuphunzira maulosi ena omwe akhala akukwaniritsidwa m’zaka zaposachedwapa, kungalimbitse kwambiri chikhulupiriro chathu.

Mofanana ndi zidutswa za chithunzi zomwe zikaikidwa pamodzi chithunzicho chimaoneka bwinobwino, maulosi a Baibulo a m’mabuku a Danieli ndi Chivumbulutso amatithandiza kuona pomwe tili munthawi ya Yehova ya zochitika zosiyanasiyana (Onani ndime 2)

2. Kodi munkhaniyi tikambirana chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani? (Fotokozani chithunzi chapachikuto.)

2 Munkhaniyi tikambirana (1) ulosi umene umatithandiza kudziwa nthawi imene Ufumu unakhazikitsidwa, (2) maulosi amene amatithandiza kudziwa kuti Yesu akulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, komanso (3) maulosi amene amatithandiza kudziwa mmene adani a Ufumu wa Mulungu adzawonongedwere. Tiona kuti maulosiwa ali ngati zidutswa za chithunzi zomwe zikaikidwa pamodzi chithunzicho chimaoneka bwinobwino. Maulosiwa atithandizanso kuona pomwe tili munthawi ya Yehova ya zochitika zosiyanasiyana.

MMENE TIMADZIWIRA NTHAWI IMENE UFUMU UNAKHAZIKITSIDWA

3. Kodi ulosi wa pa Danieli 7:13, 14 umatitsimikizira zotani zokhudza Mfumu ya Ufumu wa Mulungu?

3 Ulosi wa pa Danieli 7:13, 14 umatitsimikizira kuti Khristu Yesu adzakhala Mfumu yabwino kwambiri. Anthu a mitundu yonse ‘adzamutumikira’ ndipo sadzalowedwa m’malo ndi wina aliyense. Ulosi wina m’buku la Danieli unaneneratu kuti Yesu adzalandira Ufumu wake kumapeto kwa nthawi 7. Kodi n’zotheka kudziwa nthawi yeniyeni yomwe zinthu zosangalatsazi zinachitika?

4. Fotokozani mmene lemba la Danieli 4:10-17 limatithandizira kudziwa chaka chimene Khristu anakhala Mfumu. (Onaninso mawu a m’munsi.)

4 Werengani Danieli 4:10-17. “Nthawi zokwanira 7” zimaimira zaka 2,520. Zaka zimenezi zinayambira mu 607 B.C.E., pomwe Ababulo anachotsa mfumu yomaliza pampando wachifumu wa Yehova ku Yerusalemu. Nthawiyi inatha mu 1914 pomwe Yehova anaika Yesu, “amene ali woyenerera mwalamulo,” kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. *​—Ezek. 21:25-27.

5. Kodi ndi phindu limodzi liti lomwe timapeza chifukwa cha ulosi wonena za “nthawi zokwanira 7”?

5 Kodi ulosiwu umatithandiza bwanji? Kudziwa zokhudza “nthawi zokwanira 7” kumatitsimikizira kuti Yehova amakwaniritsa malonjezo ake pa nthawi yake. Mofanana ndi zimene anachita pokonzeratu nthawi yeniyeni yoti Ufumu wake udzakhazikitsidwe, adzaonetsetsanso kuti maulosi ena onse akwaniritsidwa pa nthawi yake yoyenera. Choncho ndife otsimikiza kuti tsiku la Yehova ‘silidzachedwa.’​—Hab. 2:3.

MMENE TIMADZIWIRA KUTI YESU AKULAMULIRA MONGA MFUMU YA UFUMU WA MULUNGU

6. (a) Kodi ndi umboni woonekeratu uti womwe umatitsimikizira kuti Khristu akulamulira kumwamba? (b) Kodi ulosi wa pa Chivumbulutso 6:2-8 umatsimikizira bwanji umboniwu?

6 Chakumapeto kwa utumiki wake padzikoli, Yesu ananeneratu zochitika zomwe zidzathandize otsatira ake kudziwa kuti iye wayamba kulamulira kumwamba. Mwa zina, iye anatchula nkhondo, njala komanso zivomerezi. Ananeneratunso kuti kudzakhala miliri kapena matenda “m’malo osiyanasiyana,” ndipo chitsanzo ndi mliri waposachedwawu wa COVID-19. Zochitika zimenezi ndi mbali ya zimene Baibulo limatchula kuti “chizindikiro” cha kukhalapo kwa Khristu. (Mat. 24:3, 7; Luka 21:7, 10, 11) Patapita zaka 60 kuchokera pamene anafa n’kuukitsidwa komanso kubwerera kumwamba, Yesu anatsimikizira mtumwi Yohane kuti zinthu zimenezi zidzachitikadi. (Werengani Chivumbulutso 6:2-8.) Ndipotu zonsezi zakhala zikuchitika kungochokera pamene Yesu anayamba kulamulira mu 1914.

7. N’chifukwa chiyani padzikoli panakhala mavuto Yesu atangoyamba kulamulira?

7 N’chifukwa chiyani zinthu zinayamba kuipa kwambiri padzikoli, Yesu atakhala Mfumu? Lemba la Chivumbulutso 6:2 limatchula mfundo ina yofunika. Chinthu choyamba chimene Yesu anachita atangokhala Mfumu ndi kumenya nkhondo. Iye anamenyana ndi Mdyerekezi ndi ziwanda zake. Mogwirizana ndi Chivumbulutso 12, Satana sanapambane nkhondoyi ndipo anaponyedwa padzikoli limodzi ndi ziwanda zake. Chifukwa cha mkwiyo, Satana anayamba kulimbana ndi anthu, zomwe zinachititsa ‘tsoka padziko lapansi.’​—Chiv. 12:7-12.

Sitisangalala ndi zoipa zomwe zikuchitika. Koma kuona kuti maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa, kumatithandiza kutsimikizira kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira (Onani ndime 8)

8. Kodi timapindula bwanji chifukwa choona mmene maulosi okhudza Ufumu akukwaniritsidwira?

8 Kodi maulosiwa amatithandiza bwanji? Zochitika padzikoli komanso kuona mmene anthu asinthira makhalidwe awo zimatithandiza kudziwa kuti Yesu anakhala Mfumu. Choncho m’malo mokhumudwa chifukwa choona kuti anthu ndi odzikonda komanso amadana ndi anzawo, tizikumbukira kuti zochita zawo zikukwaniritsa maulosi a m’Baibulo. Apa n’zoonekeratu kuti Ufumu ukulamulira. (Sal. 37:1) Ndipo tiziyembekezera kuti mavuto awonjezeka makamaka pamene Aramagedo ikuyandikira. (Maliko 13:8; 2 Tim. 3:13) Kodi simukuthokoza Atate wathu wakumwamba chifukwa chotithandiza kumvetsa chifukwa chake padzikoli pali mavuto ambiri?

MMENE ADANI A UFUMU WA MULUNGU ADZAWONONGEDWERE

9. Kodi ulosi wa pa Danieli 2:28, 31-35, umafotokoza bwanji ulamuliro wamphamvu padziko lonse womaliza, nanga unakhazikitsidwa liti?

9 Werengani Danieli 2:28, 31-35. Masiku ano timaona ulosiwu ukukwaniritsidwa. Maloto a Nebukadinezara anasonyeza zimene zidzachitike “m’masiku otsiriza” Khristu akadzayamba kulamulira. Adani a Yesu padzikoli akuphatikizapo ufumu wamphamvu padziko lonse womaliza womwe ukulamulira panopa, umene umaimiridwa ndi mapazi “achitsulo chosakanizika ndi dongo.” Ufumuwu unakhazikitsidwa pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse pomwe mayiko a Britain ndi America anachita mgwirizano wapadera. Maloto a Nebukadinezara anatchulanso zinthu ziwiri zokhudza ufumuwo zomwe zimauchititsa kukhala wosiyana ndi maufumu ena a m’mbuyo mwake.

10. (a) Kodi timaona zinthu ziti mu ulamuliro wa Britain ndi America zomwe ulosi wa Danieli unaneneratu? (b) Kodi tiyenera kusamala ndi chiyani? (Onani bokosi lakuti, “ Samalani ndi Dongo.”)

10 Choyamba, mosiyana ndi maulamuliro ena amphamvu padziko lonse otchulidwa m’masomphenyawa, ulamuliro wa Britain ndi America sukuimiridwa ndi zinthu zolimba ngati golide kapena siliva, koma chitsulo chosakanizika ndi dongo. Dongolo likuimira “ana a anthu” kapena kuti anthu wamba. (Dan. 2:43) Monga mmene timaonera masiku ano, zochita za anthu pa nkhani ya zisankho, ziwonetsero, kumenyera maufulu komanso kukhazikitsa mabungwe zimachititsa kuti ulamuliro womalizawu uzivutika kukwaniritsa zolinga zake.

11. Kodi kukhalapo kwa ulamuliro wa Britain ndi America kumatitsimikizira bwanji kuti tili munthawi ya mapeto?

11 Chachiwiri, popeza ulamuliro wa Britain ndi America umaimiridwa ndi mapazi a chifaniziro, ndi ulamuliro wapadziko lonse womaliza womwe Baibulo linaneneratu. Sudzalowedwa m’malo ndi ulamuliro wina wandale. M’malomwake, pa Aramagedo Ufumu wa Mulungu udzawononga mofulumira ulamulirowu pamodzi ndi maboma ena onse a anthu. *​—Chiv. 16:13, 14, 16; 19:19, 20.

12. Kodi ulosi wa Danieli umatipatsanso umboni uti wotilimbikitsa komanso kutipatsa chiyembekezo?

12 Kodi ulosiwu umatithandiza bwanji? Ulosi wa Danieli umatipatsa umboni wowonjezereka wosonyeza kuti tikukhala m’nthawi ya mapeto. Zaka pafupifupi 2,500 zapitazo, Danieli ananeneratu kuti pambuyo pa ulamuliro wa Babulo, padzabwera maulamuliro ena 4 omwe zochita zawo zidzakhudza kwambiri atumiki a Mulungu. Kuwonjezera pamenepo, iye anasonyeza kuti ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America udzakhala womaliza. Zimenezi zimatilimbikitsa komanso kutipatsa chiyembekezo choti posachedwapa, Ufumu wa Mulungu udzachotsa maboma onse a anthu n’kuyamba kulamulira dziko lonse.​—Dan. 2:44.

13. Kodi “mfumu ya 8” komanso “mafumu 10” otchulidwa pa Chivumbulutso 17:9-12 amaimira chiyani, nanga ulosi wa palembali unakwaniritsidwa bwanji?

13 Werengani Chivumbulutso 17:9-12. Nkhondo yoyamba ya padziko lonse, yomwe inawonongetsa zinthu zambiri, inachititsa kuti ulosi winanso wa m’Baibulo wokhudza masiku otsiriza ukwaniritsidwe. Olamulira a m’dzikoli ankafuna kuti padziko lonse pakhale mtendere. Choncho mu January 1920, iwo anakhazikitsa bungwe la League of Nations, lomwe linalowedwa m’malo ndi bungwe la United Nations mu October 1945. Bungweli limatchulidwa kuti “mfumu ya 8.” Koma si ulamuliro wamphamvu padziko lonse. M’malomwake, mphamvu zake zimachokera ku maboma apadzikoli omwe amalithandiza. Mophiphiritsa, Baibulo limanena kuti mabomawo ndi “mafumu 10.”

14-15. (a) Kodi lemba la Chivumbulutso 17:3-5 limatiuza zotani zokhudza “Babulo Wamkulu”? (b) Kodi n’chiyani chimene ambiri m’zipembedzo zonyenga akuchita?

14 Werengani Chivumbulutso 17:3-5. Mtumwi Yohane anaona masomphenya a hule lomwe ndi “Babulo Wamkulu” yemwe amaimira zipembedzo zonse zonyenga. Kodi masomphenyawa amasonyeza chiyani? Zipembedzo zonyenga zakhala zikuchita zinthu limodzi ndi maulamuliro amphamvu padziko lonse komanso kuwathandiza. Komabe posachedwapa Yehova adzaika zofuna zake m’mitima ya olamulirawa kuti achite “monga mwa maganizo ake.” Kodi zotsatirapo zake zidzakhala zotani? Olamulirawa, kapena kuti “mafumu 10” adzaukira zipembedzo zonyenga n’kuziwononga.​—Chiv. 17:1, 2, 16, 17.

15 Kodi timadziwa bwanji kuti mapeto a Babulo Wamkulu ayandikira? Kuti tiyankhe funsoli, tiyenera kukumbukira kuti mzinda wakale wa Babulo unkatetezedwa ndi madzi a mtsinje waukulu wa Firate. Buku la Chivumbulutso limayerekezera anthu mamiliyoni omwe ali mu Babulo Wamkulu ndi “madzi” otetezawa. (Chiv. 17:15) Koma limasonyezanso kuti madziwa ‘adzauma,’ zomwe zikutanthauza kuti anthu a m’zipembedzo zonyenga adzatulukamo. (Chiv. 16:12) Pokwaniritsa ulosiwu, anthu ambiri masiku ano ayamba kutuluka m’zipembedzo zonyenga n’kuyamba kufufuza kwina mmene angathetsere mavuto awo.

16. Kodi kumvetsa maulosi okhudza kukhazikitsidwa kwa United Nations ndi kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu kumatithandiza bwanji?

16 Kodi maulosiwa amatithandiza bwanji? Kukhazikitsidwa kwa United Nations komanso kuti anthu ambiri sakuthandizanso zipembedzo zonyenga zimatipatsanso umboni woti tikukhala m’masiku otsiriza. Ngakhale kuti madzi ophiphiritsa omwe amateteza Babulo akuuma, sikuti kumeneku ndiye kuwonongedwa kwa zipembedzo zonyenga. Monga tanenera kale, Yehova adzaika m’mitima ya “mafumu 10” kapena kuti maboma a padzikoli omwe amathandiza United Nations kuti achite “monga mwa maganizo ake.” Mabomawa adzawononga zipembedzo zonyenga modzidzimutsa zomwe zidzadabwitse anthu ambiri. * (Chiv. 18:8-10) Kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu kudzagwedeza dziko lonse ndipo mwina kudzachititsa kuti pakhale mavuto. Komabe anthu a Mulungu adzakhala ndi zifukwa ziwiri zosangalalira. Mdani wa Yehova ameneyu, yemwe wakhalako kwa nthawi yaitali sadzakhalakonso. Komanso tidzakhala titatsala pang’ono kuti tipulumutsidwe ku dziko loipali.​—Luka 21:28.

MUZIKHULUPIRIRA KUTI YEHOVA ADZAKUTETEZANI

17-18. (a) Kodi tingatani kuti tipitirize kulimbitsa chikhulupiriro chathu? (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

17 Danieli analosera kuti anthu “adzadziwa zinthu zambiri zoona.” Ndipo n’zimene zakhala zikuchitikadi. Panopa timamvetsa maulosi okhudza nthawi yathu ino. (Dan. 12:4, 9, 10) Timagoma kwambiri ndi Yehova komanso Mawu ake tikaona mmene maulosiwa akukwaniritsidwira. (Yes. 46:10; 55:11) Choncho pitirizani kulimbitsa chikhulupiriro chanu pophunzira Malemba mwakhama komanso pothandiza ena kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Iye adzateteza onse omwe amamudalira ndipo adzapitiriza kuwapatsa “mtendere wosatha.”​—Yes. 26:3.

18 Munkhani yotsatira, tidzakambirana maulosi okhudza mpingo wa Chikhristu munthawi ya mapeto ino. Monga mmene tidzaonere, kukwaniritsidwa kwa maulosiwa kumasonyezanso kuti tili m’masiku otsiriza. Tidzaonanso umboni wotsimikizira kuti Yesu yemwe ndi Mfumu yomwe ikulamulira akutsogolera otsatira ake okhulupirika.

NYIMBO NA. 61 Pitani Patsogolo Mboninu

^ Tikukhala munthawi yosangalatsa kwambiri chifukwa Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira, monga mmene maulosi a m’Baibulo ananenera. Nkhaniyi ifotokoza ena mwa maulosiwa n’cholinga chofuna kutithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova komanso kuti tizimudalira panopa ndiponso m’tsogolo.

^ Onani phunziro 32, mfundo 4 m’buku lakuti, Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale komanso onerani vidiyo ya pa jw.org yakuti, Ufumu wa Mulungu Unayamba Kulamulira mu 1914.

^ Kuti mudziwe zambiri zokhudza ulosi wa Danieli, onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 2012, tsamba 14-19.

^ Kuti mudziwe zambiri zomwe zichitike posachedwapa, onani mutu 21 m’buku lakuti, Ufumu wa Mulungu Ukulamulira.