NKHANI YOPHUNZIRA 30

Ulosi Wakalekale Umene Umakukhudzani

Ulosi Wakalekale Umene Umakukhudzani

“Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo.”​—GEN. 3:15.

NYIMBO NA. 15 Tamandani Mwana Woyamba Kubadwa wa Yehova

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yehova anatani Adamu ndi Hava atangochimwa? (Genesis 3:15)

 ADAMU ndi Hava atangochimwa, Yehova ananena ulosi wofunika womwe unapereka chiyembekezo kwa ana awo. Ulosiwu uli pa Genesis 3:15.​—Werengani.

2. N’chifukwa chiyani ulosiwu uli wapadera?

2 Ulosiwu umapezeka m’buku loyamba la Baibulo. Komabe mwa njira ina yake mabuku onse a m’Baibulo amagwirizana ndi ulosiwu. Mofanana ndi simenti yomwe imagwirizanitsa njerwa za khoma la nyumba, mawu a pa Genesis 3:15 amathandiza kuti uthenga wa m’mabuku onse a m’Baibulo ukhale wogwirizana. Uthenga wake ndi wakuti Mulungu adzatumiza Mpulumutsi yemwe adzawononge Mdyerekezi ndi oipa onse omwe amamutsatira. * Amenewatu ndi madalitso aakulu kwa omwe amakonda Yehova.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Munkhaniyi tipeza mayankho a mafunso otsatirawa okhudza ulosi wa pa Genesis 3:15: Kodi ndi ndani amene akutchulidwa mu ulosiwu? Kodi ulosiwu ukukwaniritsidwa bwanji? Nanga kodi ifeyo tikupindula bwanji ndi zimenezi?

KODI NDI NDANI AMENE AKUTCHULIDWA MU ULOSIWU?

4. Kodi “njoka” ndi ndani ndipo timadziwa bwanji zimenezi?

4 Omwe akutchulidwa pa Genesis 3:14, 15 akuphatikizapo “njoka,” “mbewu” ya njoka, “mkazi” komanso “mbewu” ya mkazi. Baibulo limatithandiza kudziwa bwino aliyense wa otchulidwawa. * Tiyeni tiyambe ndi njoka. Njoka yeniyeni sikanamva zomwe Yehova ananena m’munda wa Edeni. Choncho Yehova ankapereka chiweruzo chake kwa cholengedwa cha nzeru. Kodi cholengedwachi ndi ndani? Lemba la Chivumbulutso 12:9 limatifotokozera momveka bwino za nkhaniyi. Lembali limati ‘njoka yakaleyi’ ndi Satana Mdyerekezi. Nanga kodi mbewu ya njoka ndi ndani?

NJOKA

Satana Mdyerekezi, yemwe pa Chivumbulutso 12:9 amatchulidwa kuti “njoka yakale ija” (Onani ndime 4)

5. Kodi ndi ndani amene ali mbewu ya njoka?

5 Baibulo likamanena za mbewu, mophiphiritsa limanena za onse omwe amaganiza kapena kuchita zinthu ngati bambo wawo wophiphiritsayo. Choncho mbewu ya njoka ndi angelo osakhulupirika ndiponso anthu omwe mofanana ndi Satana, amakana Yehova Mulungu komanso kutsutsa anthu ake. Amenewa akuphatikizapo angelo omwe anasiya utumiki wawo kumwamba munthawi ya Nowa komanso anthu onse oipa omwe amachita zinthu ngati atate wawo Mdyerekezi.​—Gen. 6:1, 2; Yoh. 8:44; 1 Yoh. 5:19; Yuda 6.

MBEWU YA NJOKA

Angelo oipa komanso anthu omwe amakana Yehova Mulungu ndiponso kutsutsa anthu ake (Onani ndime 5)

6. N’chifukwa chiyani “mkazi” wotchulidwayo si Hava?

6 Tsopano tiyeni tidziwe za mkazi wotchulidwayo. N’zoonekeratu kuti sangakhale Hava. N’chifukwa chiyani tikutero? Tiyeni tione chifukwa chimodzi. Ulosiwu unanena kuti mbewu ya mkaziyo “idzaphwanya” mutu wa njoka. Monga taonera kale, njoka ndi Satana yemwe ndi cholengedwa chauzimu choncho sizikanatheka kuti mwana wa Hava yemwe si wangwiro athe kumuwononga. Ndiye kodi Satana akanawonongedwa bwanji?

7. Monga mmene lemba la Chivumbulutso 12:1, 2, 5, 10 likusonyezera, kodi mkazi wotchulidwa pa Genesis 3:15 ndi ndani?

7 Buku lomaliza la m’Baibulo limatiuza za mkazi wotchulidwa pa Genesis 3:15. (Werengani Chivumbulutso 12:1, 2, 5, 10.) Mkaziyu si wapadzikoli. Iye ali ndi mwezi kumapazi kwake ndipo kumutu kwake kuli chisoti chachifumu chokhala ndi nyenyezi 12. Mkaziyu anabereka mwana wapadera kwambiri yemwe ndi Ufumu wa Mulungu. Ufumuwu ndi wakumwamba choncho mkaziyu ayeneranso kuti ndi wakumwamba. Iye amaimira mbali yakumwamba ya gulu la Yehova lopangidwa ndi angelo okhulupirika.​—Agal. 4:26.

MKAZI

Mbali yakumwamba ya gulu la Yehova yopangidwa ndi angelo okhulupirika (Onani ndime 7)

8. Kodi mbali yoyamba ya mbewu ya mkazi ndi ndani, nanga ndi pa nthawi iti pamene anakhala mbewuyi? (Genesis 22:15-18)

8 Mawu a Mulungu amatithandizanso kudziwa mbali yoyamba ya mbewu ya mkazi. Mbewuyi inkayenera kukhala yochokera mu mzera wa Abulahamu. (Werengani Genesis 22:15-18.) Monga mmene ulosiwu unanenera, Yesu anachokeradi mu mzera wa kholo lokhulupirikali. (Luka 3:23, 34) Koma mbewuyi inkafunika kukhala yamphamvu kwambiri kuposa munthu chifukwa inkafunika kuwononga Satana Mdyerekezi. Choncho ali ndi zaka pafupifupi 30, Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera. Atadzozedwa anakhala mbali yoyamba ya mbewu ya mkazi. (Agal. 3:16) Yesu ataphedwa n’kuukitsidwa, Mulungu anamuveka “ulemerero ndi ulemu monga chisoti chachifumu” ndipo anamupatsa “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi,” kuphatikizapo mphamvu zoti “awononge ntchito za Mdyerekezi.”​—Aheb. 2:7; Mat. 28:18; 1 Yoh. 3:8.

MBEWU YA MKAZI

Yesu Khristu ndi olamulira anzake 144,000 (Onani ndime 8-9)

9-10. (a) Kodi ndi ndaninso omwe ali mbali ya mbewu ya mkazi, nanga ndi pa nthawi iti pamene amayamba kukhala mbewuyi? (b) Kodi tsopano tikambirana chiyani?

9 Palinso mbali yachiwiri ya mbewu ya mkazi. Mtumwi Paulo ananena za mbali ya mbewuyi pomwe anauza Akhristu odzozedwa a Chiyuda komanso mitundu ina kuti: “Ngati muli a Khristu, ndinudi mbewu ya Abulahamu, olandira cholowa mogwirizana ndi lonjezolo.” (Agal. 3:28, 29) Yehova akadzoza Mkhristu ndi mzimu wake woyera, munthuyo amakhala mbali ya mbewu ya mkazi. Choncho mbewu ya mkazi ndi Yesu Khristu ndi olamulira anzake okwana 144,000. (Chiv. 14:1) Onsewa amayesetsa kuti aziganiza ndi kuchita zinthu ngati Atate wawo Yehova Mulungu.

10 Popeza tsopano tadziwa onse otchulidwa pa Genesis 3:15, tiyeni tikambirane mwachidule mmene Yehova wakhala akukwaniritsira pang’onopang’ono ulosiwu komanso mmene timapindulira nawo.

KODI ULOSIWU WAKHALA UKUKWANIRITSIDWA BWANJI?

11. Kodi mbewu ya mkazi inavulazidwa bwanji “chidendene”?

11 Monga mmene ulosi wa pa Genesis 3:15 unanenera, njoka inkayenera kuvulaza “chidendene” cha mbewu ya mkazi. Zimenezi zinakwaniritsidwa pamene Satana anachititsa Ayuda ndi Aroma kuti aphe Mwana wa Mulungu. (Luka 23:13, 20-24) Mofanana ndi bala la chidendene lomwe lingachititse munthu kulephera kuyenda kwa kanthawi, imfa ya Yesu inachititsa kuti iye asiye kuchita zinthu kwa kanthawi pomwe anagona m’manda kwa masiku atatu.​—Mat. 16:21.

12. Kodi ndi liti pamene mutu wa njoka udzaphwanyidwe, nanga zimenezi zidzachitika bwanji?

12 Kuti ulosi wa pa Genesis 3:15 ukwaniritsidwe, Yesu sankafunika kukhalabe m’manda mpaka kalekale. Chifukwa chiyani? Chifukwa malinga ndi ulosi, mbewu ya mkazi inkafunika kudzaphwanya mutu wa njoka. Zimenezi zinkatanthauza kuti Yesu ankafunika kuukitsidwa zomwe zinali ngati kuchira bala la chidendene. Ndipotu iye anaukitsidwadi. Pa tsiku lachitatu Yesu anaukitsidwa ndi moyo womwe sungafe. Pa nthawi ya Mulungu, Yesu adzawononga Satana n’kumuchotseratu. (Aheb. 2:14) Anthu omwe adzalamulire ndi Khristu adzathandiza nawo kuchotsa adani a Mulungu onse padzikoli, omwe ndi mbewu ya njoka.​—Chiv. 17:14; 20:4, 10. *

KODI TIMAPINDULA BWANJI NDI ULOSIWU?

13. Kodi timapindula bwanji ndi kukwaniritsidwa kwa ulosiwu?

13 Ngati ndinu mtumiki wodzipereka wa Mulungu, mumapindula ndi kukwaniritsidwa kwa ulosiwu. Yesu anabwera padziko lapansi monga munthu. Iye anasonyeza bwino makhalidwe a Atate ake. (Yoh. 14:9) Choncho tikamaphunzira za Yesu timafika podziwa komanso kukonda Yehova Mulungu. Timapindulanso ndi zimene Yesu anaphunzitsa komanso malangizo amene amapereka akamatsogolera mpingo wa Chikhristu masiku ano. Watiphunzitsanso zimene tingachite kuti tizisangalatsa Mulungu. Tonsefe tingathe kupindula ndi imfa ya Yesu, yomwe ili ngati kuvulazidwa chidendene. Motani? Yesu ataukitsidwa anapereka mtengo wa magazi ake monga nsembe yangwiro yomwe ‘inatiyeretsa ku uchimo wonse.’​—Yoh. 1:7.

14. Kodi anthu ankayenera kuyembekezera kuti ulosi wa mu Edeni ukwaniritsidwa pa nthawi yomwe unanenedwayo? Fotokozani.

14 Mawu amene Yehova ananena mu Edeni amasonyeza kuti pankafunika kudutsa nthawi kuti ulosiwu ukwaniritsidwe wonse. Pankafunikanso nthawi kuti mbewu yolonjezedwa ya mkazi ionekere, Mdyerekezi asonkhanitse otsatira ake komanso kuti pakhale chidani pakati pa magulu awiriwa. Timapindula kudziwa zokhudza ulosiwu chifukwa umatichenjeza kuti dziko lolamulidwa ndi Satanali lidzadana ndi olambira Yehova. Patapita nthawi, Yesu anachenjezanso ophunzira ake za nkhani yomweyi. (Maliko 13:13; Yoh. 17:14) Taona kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu makamaka m’zaka 100 zapitazi. Motani?

15. N’chifukwa chiyani panopa dziko likudana kwambiri ndi anthu a Mulungu, koma n’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa Satana?

15 Atangoikidwa kukhala mfumu mu 1914, Yesu yemwe ndi Mesiya anachotsa Satana kumwamba. Satana anaponyedwa padzikoli ndipo akuyembekezera kuwonongedwa. (Chiv. 12:9, 12) Koma sikuti iye wangokhala podikira kuti adzawonongedwe. Posowa mtengo wogwira, panopa Satana ndi wokwiya kwambiri ndipo amasonyeza mkwiyo wakewo poukira anthu a Mulungu. (Chiv. 12:13, 17) Pa chifukwa chimenechi dzikoli likudana kwambiri ndi anthu a Mulungu. Komabe sitiyenera kuopa Satana ndi otsatira ake. Tingakhale otsimikiza ngati mtumwi Paulo amene analemba kuti: “Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?” (Aroma 8:31) Tikhoza kumakhulupirira kwambiri Yehova chifukwa monga mmene taonera, mbali yayikulu ya ulosi wa pa Genesis 3:15 yakwaniritsidwa kale.

16-18. Kodi kumvetsa ulosi wa pa Genesis 3:15, kwathandiza bwanji Curtis, Ursula ndi Jessica?

16 Lonjezo la Yehova la pa Genesis 3:15, lingatithandize kupirira mayesero aliwonse amene tingakumane nawo. Curtis yemwe ndi mmishonale ku Guam ananena kuti: “Nthawi zina ndinkalimbana ndi mayesero komanso zokhumudwitsa zomwe zikanachititsa kuti ndisakhale wokhulupirika kwa Yehova. Koma kuganizira ulosi wa pa Genesis 3:15, kwandithandiza kuti ndipitirize kukhulupirira Atate wanga wakumwamba.” Curtis akuyembekezera nthawi yomwe Yehova adzathetse mayesero onse omwe timakumana nawo.

17 Mlongo wina wa ku Bavaria dzina lake Ursula, anati kumvetsa lemba la Genesis 3:15 kunamuthandiza kuti azikhulupirira kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu. Anaona mmene maulosi ena onse amagwirizanirana ndi ulosiwu ndipo izi zinamuchititsa chidwi kwambiri. Iye ananenanso kuti: “Zinandikhudza nditadziwa kuti Yehova anachitapo kanthu mwamsanga kuti anthu akhale ndi chiyembekezo.”

18 Jessica wa ku Micronesia ananena kuti: “Ndimakumbukirabe mmene ndinamvera nditazindikira kwa nthawi yoyamba kuti ndapeza choonadi. Ndinadziwa kuti ulosi wa pa Genesis 3:15 ukukwaniritsidwa. Zimenezi zandithandiza kudziwa kuti mavuto amene timakumana nawo masiku ano, si zimene Yehova ankafuna. Ulosiwu wandithandizanso kukhulupirira kwambiri kuti kutumikira Yehova kungathandize munthu kuti azisangalala panopa komanso kuti adzapeze moyo wabwino m’tsogolo.”

19. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti mbali yomaliza ya ulosiwu idzakwaniritsidwa?

19 Monga mmene taonera, ulosi wa pa Genesis 3:15 ukukwaniritsidwa. Mbewu ya mkazi komanso njoka zadziwika bwino. Yesu yemwe ndi mbali yoyamba ya mbewu ya mkazi, anachira bala lake la pachidendene ndipo panopa ndi Mfumu ya ulemerero yomwe singafe. Kusankhidwa kwa omwe ndi mbali yachiwiri ya mbewu ya mkazi kwatsala pang’ono kufika kumapeto. Popeza kuti mbali yoyamba ya ulosiwu yakwaniritsidwa sitikukayikira ngakhale pang’ono kuti mbali yomaliza yomwe ndi kuphwanya mutu wa njoka ikwaniritsidwanso. Anthu okhulupirika adzasangalalatu kwambiri Satana akadzawonongedwa. Mpaka pa nthawiyo, sitiyenera kufooka. Mulungu wathu ndi wodalirika. Kudzera mwa mbewu ya mkazi, iye adzapereka madalitso ambiri ku “mitundu yonse ya padziko lapansi.”​—Gen. 22:18.

NYIMBO NA. 23 Yehova Wayamba Kulamulira

^ Sitingamvetse bwinobwino uthenga wa m’Baibulo ngati titapanda kumvetsa ulosi wa pa Genesis 3:15. Kuphunzira ulosiwu kungalimbitse chikhulupiriro chathu mwa Yehova komanso kuti tisamakaikire ngakhale pang’ono kuti adzakwaniritsa malonjezo ake onse.

^ Onani Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu pamutu wakuti, “Uthenga wa m’Baibulo.”

^ Onani bokosi lakuti “Amene Akutchulidwa pa Genesis 3:14, 15.”

^ Onani bokosi lakuti “Zochitika Zina Zikuluzikulu pa Kukwaniritsidwa kwa Ulosi wa pa Genesis 3:15.”