NKHANI YOPHUNZIRA 31
“Khalani Olimba, Osasunthika”
“Abale anga okondedwa, khalani olimba, osasunthika.”—1 AKOR. 15:58.
NYIMBO NA. 122 Khalani Olimba Komanso Osasunthika
ZIMENE TIPHUNZIRE a
1-2. Kodi Mkhristu amafanana bwanji ndi nyumba yaitali? (1 Akorinto 15:58)
CHA M’MA 1970, ku Tokyo m’dziko la Japan kunamangidwa nyumba ya nsanjika 60. Anthu amene ankaona nyumbayi ikumangidwa ankada nkhawa chifukwa mumzindawu munkakonda kuchitika zivomerezi. Kodi chinsinsi cha nyumbayi chinagona pati? Akatswiri amene anamanga nyumbayi anaimanga m’njira yakuti ikhale yolimba komanso kuti izitha kugwedezeka koma osawonongeka. Kodi Akhristu amafanana bwanji ndi nyumba imeneyi?
2 Mkhristu ayenera kukhala wosasunthika koma pa nthawi yofananayo ayeneranso kukhala wololera. Iye ayenera kukhala wolimba komanso wosasunthika pa nkhani yotsatira malamulo a Yehova ndi mfundo zake. (Werengani 1 Akorinto 15:58.) Amakhalanso ‘wokonzeka kumvera’ komanso amapitiriza kukhala wokhulupirika. Komabe amayenera kukhala ‘wololera’ ngati ndi zotheka kapenanso ngati pakufunika kutero. (Yak. 3:17) Mkhristu amene amaona zinthu moyenera pa nkhani zimenezi amapewa kukhwimitsa kwambiri kapena kulekerera zinthu. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tikhale osasunthika. Tikambirananso njira 5 zimene Satana amagwiritsa ntchito pofuna kutifooketsa komanso zimene tingachite polimbana naye.
KODI TINGATANI KUTI TIKHALE OSASUNTHIKA?
3. Kodi ndi Malamulo ati ochokera kwa Wotipatsa Malamulo Wamkulu omwe timawapeza pa Machitidwe 15:28, 29?
3 Monga Wotipatsa Malamulo Wamkulu, nthawi zonse Yehova wakhala akupereka malamulo omveka bwino kwa anthu ake. (Yes. 33:22) Mwachitsanzo, bungwe lolamulira la mu nthawi ya atumwi linafotokoza kuti Akhristu ayenera kukhala olimba m’njira zitatu izi: (1) kupewa kulambira mafano koma n’kumalambira Yehova yekha, (2) kulemekeza kupatulika kwa magazi komanso (3) kutsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza makhalidwe abwino. (Werengani Machitidwe 15:28, 29.) Kodi Akhristu masiku ano angapitirize bwanji kukhala osasunthika pa zinthu zitatu zimenezi?
4. Kodi timasonyeza bwanji kuti ndife odzipereka kwa Yehova yekha? (Chivumbulutso 4:11)
4 Timapewa kulambira mafano, n’kumalambira Yehova yekha. Iye analamula Aisiraeli kuti azidzipereka kwa iye yekha. (Deut. 5:6-10) Pamene ankayesedwa ndi Mdyerekezi, Yesu anafotokoza momveka bwino kuti tiyenera kumalambira Yehova yekha. (Mat. 4:8-10) Choncho sitimagwiritsa ntchito mafano polambira. Sitimalemekezanso kwambiri anthu mpaka kumakhala ngati tikuwalambira, kaya ndi atsogoleri a zipembedzo, andale kapenanso akatswiri a masewera ndi anthu ena otchuka. Timakhala kumbali ya Yehova komanso kulambira iye yekha chifukwa ndi amene ‘analenga zinthu zonse.’—Werengani Chivumbulutso 4:11.
5. N’chifukwa chiyani timamvera lamulo la Yehova lokhudza kupatulika kwa moyo ndi magazi?
5 Timamvera lamulo la Yehova lokhudza kupatulika kwa moyo ndi magazi. Chifukwa chiyani? Yehova amanena kuti magazi amaimira moyo, umene ndi mphatso yamtengo wapatali imene anatipatsa. (Lev. 17:14) Pa nthawi yoyamba imene Yehova analola kuti anthu azidya nyama, anawalamula kuti asamadye magazi. (Gen. 9:4) Iye anabwerezanso lamuloli pamene anapereka Chilamulo cha Mose kwa Aisiraeli. (Lev. 17:10) Ndipo anatsogoleranso bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi kuti lipereke lamulo lakuti Akhristu onse ‘apitirize kupewa . . . magazi.’ (Mac. 15:28, 29) Timakhala osasunthika pomvera lamulo limeneli tikamasankha thandizo lamankhwala loti tilandire. b
6. Kodi timafunika kuchita chiyani kuti tizitsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino?
6 Timatsatira ndi mtima wonse mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. (Aheb. 13:4) Pogwiritsa ntchito mawu a fanizo, mtumwi Paulo anatilangiza kuti ‘tichititse ziwalo za thupi lathu kukhala zakufa,’ kumene ndi kuchita zonse zomwe tingathe kuti tisamalakelake zinthu zoipa. Timapewa kuyang’ana kapena kuchita zinthu zomwe zingachititse kuti tichite chiwerewere. (Akol. 3:5; Yobu 31:1) Choncho tikakumana ndi mayesero, nthawi yomweyo timapewa kuganizira kapena kuchita zinthu zimene zingawononge ubwenzi wathu ndi Mulungu.
7. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
7 Yehova amayembekezera kuti ‘tizimumvera mochokera pansi pa mtima.’ (Aroma 6:17) Malangizo ake amathandiza ifeyo ndipo nthawi zonse timafunika kuwamvera. (Yes. 48:17, 18; 1 Akor. 6:9, 10) Timachita zonse zomwe tingathe kuti tizisangalatsa Yehova komanso kumakhala ndi maganizo amene wolemba masalimo anali nawo, yemwe anati: “Ndatsimikiza mtima kutsatira malangizo anu, mpaka kalekale, ndithu kwa moyo wanga wonse.” (Sal. 119:112) Komabe Satana amafuna kutifooketsa. Kodi amagwiritsa ntchito njira ziti pochita zimenezi?
KODI SATANA AMAGWIRITSA NTCHITO NJIRA ZITI POFUNA KUTIFOOKETSA?
8. Kodi Satana amagwiritsa ntchito bwanji kuzunzidwa pofuna kutifooketsa?
8 Kuzunzidwa. Mdyerekezi amatizunza pofuna kusokoneza cholinga chathu choti tikhale osasunthika. Cholinga chake ndi ‘kutimeza,’ kapena kuti kuwononga ubwenzi wathu ndi Yehova. (1 Pet. 5:8) Akhristu oyambirira ankaopsezedwa, kumenyedwa komanso kuphedwa chifukwa chakuti anali atatsimikiza mtima kukhalabe olimba. (Mac. 5:27, 28, 40; 7:54-60) Satana akupitirizabe kuchita zimenezi masiku ano. Timaona umboni wa zimenezi, tikaona mmene abale ndi alongo athu akuzunzidwira ku Russia ndi mayiko ena komanso kuukiridwa ndi anthu otsutsa.
9. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti tiyenera kukhala osamala ndi mayesero osaonekera.
9 Mayesero osaonekera. Kuwonjezera pa kuzunza mwachindunji atumiki a Yehova, Satana amagwiritsanso ntchito “zochita zachinyengo.” (Aef. 6:11) Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina dzina lake Bob, yemwe anagonekedwa m’chipatala poyembekezera kuti achitidwe opaleshoni. Iye anauza madokotala kuti mulimonse mmene zingakhalire sakuyenera kuikidwa magazi. Dokotala amene ankapanga opaleshoniyo, anavomera kuti adzachita zimene iye anasankha. Komabe, madzulo oti opaleshoniyo ichitika tsiku lotsatira, dokotala wina anapita kukakumana ndi Bob anthu a m’banja lake atapita kunyumba. Dokotalayo anauza Bob kuti, ngakhale kuti pa opaleshoniyo sadzamuika magazi, adzasunga magazi ena n’cholinga choti adzamupatse ngati patafunika kutero. Mwina dokotalayo ankaona kuti Bob akhoza kusintha maganizo ake poona kuti panalibe anthu a m’banja lake. Koma m’baleyu sanasinthe maganizo ndipo ananena kuti mulimonse mmene zidzakhalire, sadzalola kuikidwa magazi.
10. Kodi nzeru za anthu n’zoopsa bwanji? (1 Akorinto 3:19, 20)
10 Nzeru za anthu. Ngati timaona zinthu potengera nzeru za anthu, tingasiye kutsatira mfundo za Yehova. (Werengani1 Akorinto 3:19, 20.) Nthawi zambiri “nzeru za m’dzikoli” zimachititsa kuti anthu asamamvere Mulungu. Akhristu ena a ku Pegamo ndi Tiyatira anayamba kumaona nkhani yokhudza kulambira mafano komanso chiwerewere ngati mmene anthu ambiri m’mizindayo ankaonera. Yesu anadzudzula mwamphamvu mipingo imeneyi chifukwa cholekerera khalidwe la chiwerewere. (Chiv. 2:14, 20) Masiku anonso timakakamizidwa kuti tiziona zinthu molakwika. Achibale kapenanso anzathu angatikakamize kapena kutilimbikitsa kuti tichite zinthu zimene zingachititse kuti tisamvere Yehova. Mwachitsanzo, iwo angamatiuze kuti palibe vuto kuchita zomwe tikufuna komanso kuti mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino n’zachikale.
11. Kodi tiyenera kupewa chiyani pamene tikuyesetsa kukhala osasunthika?
11 Nthawi zina tingamaone kuti malangizo amene Yehova amatipatsa ndi osathandiza. Mwinanso mpaka tikhoza kuyesedwa kuti ‘tipitirire zinthu zolembedwa.’ (1 Akor. 4:6) Atsogoleri a chipembedzo a m’nthawi ya Yesu anali ndi vuto limeneli, ndipo pochita zimenezi iwo ankachimwa. Powonjezera malamulo awoawo m’Chilamulo, iwo ankasenzetsa anthu chimtolo. (Mat. 23:4) Yehova amatipatsa malangizo omveka bwino kudzera m’Mawu ake komanso m’gulu lake. Tilibe zifukwa zomveka zowonjezerera mfundo zathu pa malangizo amene amatipatsa. (Miy. 3:5-7) Choncho sitimapitirira zimene zinalembedwa m’Baibulo kapenanso kuikira malamulo Akhristu anzathu pa nkhani zimene aliyense ayenera kusankha yekha.
12. Kodi Satana amagwiritsa ntchito bwanji “chinyengo chopanda pake”?
12 Chinyengo. Satana amagwiritsa ntchito “chinyengo chopanda pake” ndi “mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli” pofuna kusocheretsa ndi kugawanitsa anthu. (Akol. 2:8) M’nthawi ya atumwi, zimenezi zinkaphatikizapo nzeru za anthu, miyambo ya Chiyuda yosemphana ndi malemba komanso chiphunzitso chakuti Akhristu azitsatira Chilamulo cha Mose. Izi zinali zachinyengo chifukwa zinkachititsa kuti anthu asamaganizire za Mwiniwake wa nzeru yemwe ndi Yehova. Satana amagwiritsa ntchito mawailesi, TV kapenanso malo ochezera a pa intaneti pofuna kufalitsa nkhani zabodza zomwe atsogoleri andale amalimbikitsa. Tinaona umboni wa zimenezi pa nthawi ya mliri wa COVID-19. c A Mboni za Yehova omwe ankamvera malangizo operekedwa ndi gulu lathu sankakhala ndi nkhawa ngati mmene zinalili ndi anthu omwe ankamvetsera mfundo zabodza.—Mat. 24:45.
13. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala ndi zosokoneza?
13 Zosokoneza. Tiyenera kupitiriza kuika maganizo athu pa “zinthu zofunika kwambiri.” (Afil. 1:9, 10) Zinthu zosokoneza zingatiwonongere nthawi komanso kutichititsa kuti tisamachite chidwi ndi zinthu zofunika kwambiri. Zinthu zomwe timachita nthawi zonse monga kudya, kumwa, zosangalatsa ndiponso ntchito zingatisokoneze ngati titayamba kuziika pamalo oyamba pa moyo wathu. (Luka 21:34, 35) Kuwonjezera pamenepo, tsiku lililonse timamva nkhani zokhudza mikangano ya anthu komanso zandale. Tisamalole kuti tizisokonezedwa ndi nkhani zimenezi. Ngati sitingatero, tikhoza kuyamba kulowerera mu zimenezi m’maganizo ndi mumtima mwathu. Satana amagwiritsa ntchito njira zonse zomwe tanenazi pofuna kusokoneza cholinga chathu choti tizichita zoyenera. Tiyeni tione zimene tingachite polimbana ndi mayesero akewa kuti tikhalebe olimba.
KODI TINGATANI KUTI TIKHALEBE OLIMBA?
14. Kodi ndi chinthu chimodzi chiti chimene chingatithandize kukhalabe kumbali ya Yehova?
14 Muziganizira chifukwa chake munadzipereka komanso kubatizidwa. Munachita zimenezi chifukwa chofuna kukhala ku mbali ya Yehova. Muzikumbukira chimene chinakutsimikizirani kuti munapeza choonadi. Munaphunzira mfundo zoona zokhudza Yehova ndipo munayamba kumukonda komanso kumulemekeza kwambiri monga Atate wanu wakumwamba. Munakhala ndi chikhulupiriro ndipo izi zinakuthandizani kuti mulape. Mtima wanu unakulimbikitsani kuti musiye makhalidwe oipa komanso kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Munamva bwino mutadziwa kuti Mulungu anakukhululukirani. (Sal. 32:1, 2) Munayamba kupezeka pamisonkhano komanso kuuza ena zinthu zochititsa chidwi zimene munkaphunzira. Monga Mkhristu wodzipereka komanso wobatizidwa, panopa mukuyenda pamsewu wopita kumoyo ndipo ndinu wotsimikiza kuti mupitiriza kuyenda pamsewu umenewu.—Mat. 7:13, 14.
15. Kodi kuphunzira komanso kuganizira mozama Mawu a Mulungu n’kothandiza bwanji?
15 Muziphunzira Mawu a Mulungu komanso kuwaganizira mozama. Mofanana ndi mtengo umene umakhala wolimba chifukwa chakuti uli ndi mizu yozama, ifenso tingakhale olimba ngati tili ndi chikhulupiriro chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu. Mtengo ukamakula, mizu yake imazama komanso kuchuluka. Mofanana ndi zimenezi, tikamaphunzira Mawu a Mulungu komanso kuwaganizira mozama, timakhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso otsimikiza kuti mfundo zake n’zabwino kwambiri. (Akol. 2:6, 7) Muziganizira mmene malangizo a Yehova anathandizira komanso kutetezera atumiki ake m’mbuyomu. Mwachitsanzo, Ezekieli ankachita chidwi pamene mngelo ankayeza kachisi amene mneneriyu anaona m’masomphenya. Masomphenyawa analimbikitsa Ezekieli ndipo timaphunziraponso mfundo zofunika zokhudza zimene tingachite kuti tizitsatira mfundo za Yehova zokhudza kulambira koona. d (Ezek. 40:1-4; 43:10-12) Ifenso timapindula kwambiri tikamapeza nthawi yophunzira komanso kuganizira zinthu zozama za m’Mawu a Mulungu.
16. Kodi kukhala ndi mtima wokhazikika kunathandiza bwanji Bob? (Salimo 112:7)
16 Muziyesetsa kukhala ndi mtima wokhazikika. Davide anasonyeza kuti sankafuna kusiya kukonda Yehova pomwe anaimba kuti: “Mtima wanga wakhazikika, inu Mulungu.” (Sal. 57:7) Ifenso tingakhale ndi mtima wokhazikika, kapena kuti wosasunthika, n’kumakhulupirira kwambiri Yehova. (Werengani Salimo 112:7.) Taganizirani mmene zimenezi zinathandizira Bob yemwe tamutchula kale uja. Atauzidwa kuti padzasungidwa magazi oti amuike ngati patafunika kutero, nthawi yomweyo anayankha kuti ngati madokotalawo akuona kuti angadzamuike magazi, iye achoka kuchipatalako. Pambuyo pake Bob anadzafotokoza kuti: “Ndinali wotsimikiza mtima ndipo sindinkadanso nkhawa.”
17. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Bob? (Onaninso chithunzi.)
17 Bob sanasunthike chifukwa anali atasankhiratu zimene angachite asanapite kuchipatalako. Choyamba, iye ankafuna kusangalatsa Yehova. Chachiwiri, anali ataphunzira mosamala zimene Baibulo ndi mabuku athu amanena pa nkhani yokhudza kupatulika kwa moyo ndi magazi. Ndipo chachitatu, iye sankakayikira kuti kutsatira malangizo a Yehova kukanachititsa kuti apeze madalitso osatha. Ifenso tingathe kukhala osasunthika kaya tikumane ndi mayesero otani.
18. Kodi chitsanzo cha Baraki chimatiphunzitsa chiyani pa nkhani yodalira Yehova? (Onani chithunzi chapachikuto.)
18 Muzidalira Yehova. Taganizirani mmene kudalira malangizo a Yehova kunathandizira Baraki. Ngakhale kuti m’dziko lawo munalibiretu zishango ndi mikondo, Yehova anamuuza kuti akamenye nkhondo ndi gulu la asilikali a ku Kanani, lotsogoleredwa ndi Sisera, lomwe linali ndi zida zonse zankhondo. (Ower. 5:8) Mneneri wamkazi Debora anauza Baraki kuti atsike m’phiri n’kupita kuchigwa kuti akakumane ndi Sisera, yemwe anali ndi magaleta 900. Baraki anamvera, ngakhale kuti zikanakhala zovuta kumenyana ndi asilikali a Sisera omwe magaleta awo sakanamavutika kuthamanga m’chigwamo . Pamene asilikaliwo ankayamba kutsika m’phiri la Tabori, Yehova anayamba kugwetsa mvula. Zimenezi zinachititsa kuti magaletawa azititimira m’matope, ndipo Yehova anachititsa kuti Baraki apambane pankhondoyi. (Ower. 4:1-7, 10, 13-16) Yehova adzachititsa kuti ifenso zinthu zitiyendere bwino ngati timamudalira komanso kumvera malangizo amene amatipatsa kudzera m’gulu lake.—Deut. 31:6.
KHALANI OTSIMIKIZA KUTI MUSAMASUNTHIKE
19. N’chifukwa chiyani mukufuna kukhalabe wosasunthika?
19 Nkhondo yathu yofuna kukhala osasunthika ipitirirabe pa nthawi yonse imene tikukhala m’dziko loipali. (1 Tim. 6:11, 12; 2 Pet. 3:17) Tiyeni tikhalebe otsimikiza kuti tisasokonezedwe ndi zinthu monga kuzunzidwa, mayesero osaonekera, nzeru za anthu, zochita zachinyengo komanso zosokoneza. (Aef. 4:14) M’malomwake, tiyeni tikhale olimba, osasunthika polambira Yehova ndipo tisamasiye kumvera malamulo ake. Komabe tikamachita zimenezi, tiyeneranso kukhala ololera. Munkhani yotsatira tidzakambirana chifukwa chake Yehova ndi Yesu ali zitsanzo zabwino pa nkhani yololera.
NYIMBO NA. 129 Tipitirizabe Kupirira
a Kungoyambira nthawi ya Adamu ndi Hava, Satana wakhala akulimbikitsa mfundo yakuti anthu azisankha okha chimene chili chabwino kapena choipa. Amafunanso kuti tiziwaona choncho malamulo a Yehova komanso malangizo amene gulu lake limatipatsa. Nkhaniyi itithandiza kuti tizipewa kukhala ndi maganizo odzidalira amene dziko lolamuliridwa ndi Satanali limalimbikitsa komanso kukhala otsimikiza kuti tizimvera Yehova.
b Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya zimene Mkhristu angachite kuti aziona magazi mmene Mulungu amawaonera, onani phunziro 39 m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.
c Onani pa jw.org nkhani yakuti “Dzitetezeni Kuti Musamapusitsidwe ndi Nkhani Zabodza.”
d Kuti mudziwe zambiri, onani chaputala 13 ndi 14 m’buku la Chingelezi lakuti Pure Worship of Jehovah—Restored At Last!
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA