Kodi zomwe ofukula zinthu za kale apeza kumene kunali Babulo, zokhudza njerwa komanso njira imene ankaziwotchera, zimasonyeza bwanji kuti Baibulo ndi lolondola?
OFUKULA zinthu zakale apeza njerwa zambiri pamalo amene panali mzinda wakale wa Babulo, zomwe zinagwiritsidwa ntchito pomanga mzindawu. Mogwirizana ndi zimene katswiri wina dzina lake Robert Koldewey ananena, njerwazo zinkawotchedwa mung’anjo “kunja kwa mzindawo komwe kunali dothi labwino komanso nkhuni . . . zambiri.”
Mbiri imasonyezanso kuti akuluakulu a ku Babulo ankagwiritsa ntchito ng’anjo zimenezi pochita zinthu zina zoipa kwambiri. Paul-Alain Beaulieu, yemwe ndi pulofesa wa mbiri ya Asuri pa Yunivesite ya Toronto, ananena kuti: “Zolemba zina za ku Babulo . . . zimasonyeza kuti mfumu inkalamula kuti anthu oukira komanso amene sankalemekeza zinthu zopatulika awotchedwe.” Zolemba zina za mu nthawi ya Mfumu Nebukadinezara zinali ndi mawu otsatirawa: “Awonongeni, awotcheni, apserezeni . . . m’ng’anjo ya wophika, . . . utsi wawo ukwere m’mwamba, muwaphe powaponya pamoto.”
Zimenezi zimakumbutsa anthu amene amawerenga Baibulo za nkhani yopezeka mu Danieli chaputala 3. Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, Mfumu Nebukadinezara inakonza fano lalikulu n’kukaliimika m’chigwa cha Dura, kunja kwa mzinda wa Babulo. Anyamata atatu a Chiheberi omwe ndi Sadirake, Mesake ndi Abedinego atakana kugwadira fanolo, Nebukadinezara anakwiya. Iye analamula kuti asonkhezere ng’anjo “kuwirikiza ka 7 kuposa mmene anali kuchitira nthawi zonse,” komanso kuti amuna atatuwo ‘aponyedwe m’ng’anjo yoyaka motoyo.’ Mngelo wamphamvu anawapulumutsa kuti asafe.—Dan. 3:1-6, 19-28.
Njerwa zimene zinapezeka ku Babulo zimatsimikiziranso kuti nkhani ya m’Baibuloyi ndi yolondola. Pa njerwa zina panadindidwa mawu otamanda mfumu. Ena mwa mawuwo ndi akuti: “Nebukadinezara, Mfumu ya Babulo . . . Nyumba yaikulu imene ine Mfumu Yaikulu ndamanga . . . Mbadwa zanga zidzakhale m’nyumba imeneyi n’kumalamulira mpaka kalekale.” Mawuwa akufanana ndi zomwe timawerenga pa Danieli 4:30, pomwe Nebukadinezara analankhula modzikweza kuti: “Kodi uyu si Babulo Wamkulu amene ine ndamanga ndi mphamvu zanga zazikulu ndiponso ndi ulemerero wanga waukulu ndi cholinga chakuti kukhale nyumba yachifumu?”