Mfundo Zothandiza Pophunzira YAMBANI Mfundo Zothandiza Pophunzira Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Muziyamba ndi Zinthu Zofunika Tonsefe timakhala ndi nthawi yochepa yoti tiziphunzira patokha. Ndiye kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu? Choyamba, muzikhala ndi nthawi yokwanira yoti muwerenge. Mukhoza kupindula kwambiri ngati mutamaphunzira mosamala zinthu zochepa kusiyana ndi kuphunzira zinthu zambiri mothamanga. Choncho muziona kuti zofunika kwambiri ndi ziti. (Aef. 5:15, 16) Taganizirani mfundo izi: Muziwerenga Baibulo tsiku lililonse. (Sal. 1:2) Ndandanda yowerengera Baibulo ya misonkhano ya mkati mwa mlungu ingakhale poyambira pabwino. Muzikonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda komanso misonkhano ya mkati mwa mlungu. Muzikhala okonzeka kukayankha.—Sal. 22:22. Ngati n’zotheka, muziyesetsa kupeza nthawi yowerenga zinthu zina zatsopano monga magazini yogawira komanso zinthu zomwe zaikidwa pa jw.org. Muzikonza zoti muphunzire nkhani inayake. Mukhoza kufufuza zokhudza vuto linalake lomwe mukukumana nalo, funso lomwe muli nalo kapena nkhani inayake ya m’Baibulo imene mumafuna mutaimvetsa. Kuti mupeze mfundo zina zoti muphunzire, pitani pa jw.org pa gawo lakuti “Zoti Muchite Pophunzira Baibulo.” Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Mfundo Zothandiza Pophunzira NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA Mfundo Zothandiza Pophunzira Chinenero Chamanja cha ku Malawi Mfundo Zothandiza Pophunzira https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/1add6d1d93/images/syn_placeholder_sqr.png w23 July