NKHANI YOPHUNZIRA 27

NYIMBO NA. 73 Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima

Muzikhala Olimba Mtima Ngati Zadoki

Muzikhala Olimba Mtima Ngati Zadoki

“Zadoki [anali] mnyamata wamphamvu ndi wolimba mtima.”1 MBIRI 12:28.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona mmene chitsanzo cha Zadoki chingatithandizire kuti tikhale olimba mtima.

1-2. Kodi Zadoki anali ndani? (1 Mbiri 12:​22, 26-28)

 YEREKEZERANI kuti mukuona gulu la anthu oposa 340,000 omwe asonkhana kuti amuike Davide kukhala mfumu ya Isiraeli. Kwa masiku atatu, m’dera la mapiri pafupi ndi ku Heburoni kukumveka phokoso la kulankhulana kwa anthu, kuseka komanso nyimbo zotamanda. (1 Mbiri 12:39) Pagulu la anthulo pali wachinyamata wina dzina lake Zadoki yemwe sanali wodziwika kwa anthu ambiri. Koma Yehova anafuna kuti tidziwe zoti iye anali pagululi. (Werengani 1 Mbiri 12:​22, 26-28.) Kodi Zadoki anali ndani?

2 Zadoki anali wansembe amene ankagwira ntchito ndi Abiyatara yemwe anali mkulu wa ansembe. Zadoki anali wamasomphenya yemwe ankatha kuzindikira zimene Mulungu akufuna ndipo anapatsidwa nzeru zapadera. (2 Sam. 15:27) Anthu akafuna malangizo anzeru ankapita kwa Zadoki. Iye analinso munthu wolimba mtima. Munkhaniyi, tikambirana kwambiri za khalidwe lake limeneli.

3. (a) N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova ayenera kukhala olimba mtima? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 M’masiku otsiriza ano, Satana akuukira kwambiri anthu a Mulungu. (1 Pet. 5:8) Tiyenera kukhala olimba mtima pamene tikuyembekezera kuti Yehova awononge Satana ndi dziko loipali. (Sal. 31:24) Tiyeni tikambirane njira zitatu zomwe tingatsanzirire kulimba mtima kwa Zadoki.

MUZIKHALA KUMBALI YA UFUMU WA MULUNGU

4. N’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu amafunika kulimba mtima kuti akhale kumbali ya Ufumu wa Mulungu? (Onaninso chithunzi.)

4 Anthu a Yehovafe timayesetsa kukhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu. Koma kuchita zimenezi kumafuna kuti tikhale olimba mtima. (Mat. 6:33) Mwachitsanzo, m’dziko loipali timafunika kukhala olimba mtima kuti tizitsatira mfundo za makhalidwe abwino za Yehova komanso kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (1 Ates. 2:2) Timafunikanso kulimba mtima kuti tisalowerere ndale m’dzikoli, limene anthu ake ndi osagwirizana. (Yoh. 18:36) Atumiki ambiri a Yehova akukumana ndi mavuto azachuma, amazunzidwa ndipo ena amaikidwa m’ndende chifukwa chokana kulowerera ndale kapena kulowa usilikali.

Kodi inuyo mudzatani anthu ena akamakambirana nkhani zandale? (Onani ndime 4)


5. N’chifukwa chiyani Zadoki ankafunika kukhala wolimba mtima kuti athandize Davide?

5 Zadoki sanapite ku Heburoni kukangosangalala kuti Davide waikidwa kukhala mfumu. Anapita kumeneko atanyamula zida zake komanso ali wokonzeka kumenya nkhondo. (1 Mbiri 12:38) Iye anali wofunitsitsa kuthandiza Davide pa nkhondo yolimbana ndi adani a Isiraeli. Ngakhale kuti mwina Zadoki analibe luso lomenyera nkhondo, koma anali wolimba mtima.

6. Kodi chitsanzo chabwino cha Davide chinathandiza bwanji Zadoki? (Salimo 138:3)

6 Kodi Zadoki, yemwe anali wansembe, anaphunzira kuti kukhala wolimba mtima? Iye ankakhala ndi anthu omwe anali amphamvu komanso olimba mtima. Ndipo zitsanzo zawo zinamuthandiza kwambiri. Mwachitsanzo, kulimba mtima kwa Davide pamene ‘ankatsogolera Aisiraeli kunkhondo,’ kunalimbikitsa Aisiraeli onse kuti akhale kumbali yake. (1 Mbiri 11:​1, 2) Nthawi zonse Davide ankadalira Yehova kuti amuthandize polimbana ndi adani ake. (Sal. 28:7; Werengani Salimo 138:3.) Panali amuna enanso amene anathandiza Zadoki kukhala wolimba mtima. Mwachitsanzo, panali Yehoyada ndi mwana wake Benaya yemwe anali msilikali wamphamvu, ndiponso atsogoleri 22 omwe anali kumbali ya Davide. (1 Mbiri 11:​22-25; 12:​26-28) Anthu onsewa anasankha kukhala kumbali ya Davide ndi ufumu wake.

7. (a) Kodi ndi zitsanzo zamasiku ano ziti zomwe zingatithandize kukhala olimba mtima? (b) Mogwirizana ndi vidiyo, kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha M’bale Nsilu?

7 Timalimbikitsidwa komanso kupeza mphamvu tikamaganizira zitsanzo za anthu omwe molimba mtima anatsimikiza kukhala kumbali ya ulamuliro wa Yehova. Mwachitsanzo, Mfumu yathu Khristu Yesu anakanitsitsa kulowerera ndale m’dziko la Satanali. (Mat. 4:​8-11; Yoh. 6:​14, 15) Nthawi zonse ankadalira Yehova kuti amupatse mphamvu. Palinso zitsanzo za masiku ano za achinyamata ambiri omwe anaikidwa m’ndende chifukwa cha zimene amakhulupirira komanso kukana kulowerera ndale. Mungachite bwino kuwerenga nkhani zawo pa jw.org. a

MUZITHANDIZA ABALE ANU

8. Kodi ndi pa nthawi iti pomwe akulu angafunike kulimba mtima kuti athandize abale awo?

8 Nthawi zonse anthu a Yehova amathandizana. (2 Akor. 8:4) Komabe iwo nthawi zina amafunika kulimba mtima kuti achite zimenezi. Mwachitsanzo kukakhala nkhondo, akulu amazindikira kuti abale ndi alongo awo amafunika kulimbikitsidwa, kupatsidwa zinthu zofunika pa moyo komanso chakudya chauzimu. Chifukwa chokonda nkhosa, iwo amalolera kuika moyo wawo pangozi kuti apereke thandizo lofunika kwa abale awo. (Yoh. 15:​12, 13) Akamachita zimenezi amakhala akutsanzira Zadoki pa nkhani ya kulimba mtima.

9. Mogwirizana ndi 2 Samueli 15:​27-29, kodi Davide anapempha Zadoki kuti achite chiyani? (Onaninso chithunzi.)

9 Moyo wa Davide unali pangozi. Mwana wake Abisalomu anali atatsimikiza kuti alande ufumu. (2 Sam. 15:​12, 13) Apa Davide ankafunika kuchoka ku Yerusalemu mwamsanga. Iye anauza atumiki ake kuti: “Konzekani msangamsanga! Tiyeni tithawe, chifukwa palibe amene angapulumuke m’manja mwa Abisalomu.” (2 Sam. 15:14) Pamene atumiki akewo ankachoka, Davide anazindikira kuti pankafunika kuti munthu wina atsale kuti azimuuza zimene Abisalomu angakonze. Choncho anatumiza Zadoki ndi ansembe ena mumzindawo kuti akagwire ntchito imeneyi. (Werengani 2 Samueli 15:​27-29.) Iwo ankafunika kuchita zinthu mosamala kwambiri chifukwa zimene Davide anawauza kukachitazi, zinali zoopsa komanso zoika moyo wawo pangozi. Abisalomu anali wankhanza, wodzikonda komanso anachitira chinyengo bambo ake enieni. Ndiye tangoganizani zimene akanachita akanadziwa kuti Zadoki ndi ansembe enawo anatsala n’cholinga choti akhale akazitape a Davide.

Davide anatuma Zadoki kuti agwire ntchito yomwe ikanaika moyo wake pangozi (Onani ndime 9)


10. Kodi Zadoki ndi anzake anateteza bwanji Davide?

10 Davide anapempha Zadoki komanso mnzake wina wokhulupirika dzina lake Husai kuti amuthandize pa nkhaniyi. (2 Sam. 15:​32-37) Potsatira malangizowo, Husai anachititsa kuti Abisalomu ayambe kumukhulupirira. Iye anapereka malangizo omenyera nkhondo omwe akanapereka mpata kwa Davide kuti akonzeke. Kenako Husai anauza Zadoki ndi Abiyatara zimene anakonzazo. (2 Sam. 17:​8-16) Choncho amuna awiriwa anatumiza uthenga kwa Davide. (2 Sam. 17:17) Yehova anathandiza Zadoki ndi ansembe enawo kuti ateteze Davide.—2 Sam. 17:​21, 22.

11. Kodi tingatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Zadoki tikamathandiza abale athu?

11 Ngati mutapemphedwa kuti muthandize abale anu pa nthawi yovuta, kodi mungasonyeze bwanji kulimba mtima ngati Zadoki? (1) Muzitsatira malangizo. Pa nthawi ngati imeneyi, mumafunika kuchita zinthu mogwirizana. Muyenera kutsatira malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi. (Aheb. 13:17) Nthawi ndi nthawi, akulu ayenera kumaonanso zimene anakonza pa nkhani yokonzekera ngozi komanso kutsatira malangizo a gulu pa nthawi ya ngoziyo. (1 Akor. 14:​33, 40) (2) Muzikhala olimba mtima koma muzichita zinthu mosamala. (Miy. 22:3) Muziganiza kaye musanachite zinazake. Muziyesetsa kuti mukhale otetezeka. (3) Muzidalira Yehova. Muzikumbukira kuti Yehova amakukondani inuyo komanso abale anuwo. Choncho angakuthandizeni kuti mupereke thandizo kwa abale anuwo muli otetezeka.

12-13. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Viktor ndi Vitalii? (Onaninso chithunzi.)

12 Taganizirani chitsanzo cha Viktor ndi Vitalii, abale awiri amene ankagwira ntchito yopereka chakudya ndi madzi kwa Akhristu anzawo ku Ukraine. Viktor anati: “Tinkasakasaka chakudya kwina kulikonse. Nthawi zambiri tinkamva anthu akuomberana chapafupi. M’bale wina ananena kuti tikatenge chakudya ku shopu yake. Chakudya chimenechi chinathandiza ofalitsa ambiri kwa kanthawi. Tikulongedza chakudyacho m’galimoto, bomba linagwera pamtunda wamamita pafupifupi 20 kuchokera pomwe tinali. Kwa tsiku lonse ndinkapemphera kwa Yehova kuti andithandize kukhala wolimba mtima kuti ndipitirize kuthandiza abale anga.”

13 Vitalii anati: “Tinkafunika kulimba mtima kwambiri. Ulendo wanga woyamba tinayenda kwa maola 12. Ndinakhala ndikupemphera kwa Yehova pa ulendo wonsewu.” Vitalii anali wolimba mtima komanso ankachita zinthu mosamala. Iye ananenanso kuti: “Ndinkapempha Yehova kuti andipatse nzeru komanso andithandize kukhala wodzichepetsa. Ndinkadutsa misewu yokhayo yomwe inali yovomerezedwa ndi boma. Chikhulupiriro changa chalimba kwambiri poona mmene abale ndi alongo amachitira zinthu mogwirizana. Iwo ankachotsa zinthu zimene zatchinga mumsewu, kuchotsa ndi kulongedza zakudya ndi zinthu m’galimoto komanso kutikonzera chakudya ndi malo ogona.”

Pa nthawi yovuta, muzithandiza abale anu molimba mtima koma muzichita zinthu mosamala (Onani ndime 12-13)


PITIRIZANI KUKHALA OKHULUPIRIKA KWA YEHOVA

14. Kodi zimatikhudza bwanji munthu amene timamukonda akasiya kutumikira Yehova?

14 Chimodzi mwa zinthu zimene zimayesa kwambiri chikhulupiriro chathu komanso kutifooketsa ndi pamene wachibale kapena mnzathu wasiya kutumikira Yehova. (Sal. 78:40; Miy. 24:10) Ngati timamukonda kwambiri munthuyo, zimakhalanso zovuta kwambiri kuti tivomereze zimene zachitikazo. Ngati inunso zimenezi zinakuchitikirani, kukhulupirika kwa Zadoki kungakulimbikitseni.

15. N’chifukwa chiyani Zadoki ankafunika kukhala olimba mtima kuti apitirize kukhala wokhulupirika kwa Yehova? (1 Mafumu 1:​5-8)

15 Zadoki anasankha kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova pamene mnzake Abiyatara anasankha kuchita zinthu mosakhulupirika. Izi zinachitika kumapeto kwa ulamuliro wa Davide. Davide atatsala pang’ono kufa, mwana wake Adoniya ankafuna kulanda ufumu wake ngakhale kuti Yehova anali atalonjeza kuti Solomo ndi amene adzakhale mfumu. (1 Mbiri 22:​9, 10) Abiyatara anasankha kukhala kumbali ya Adoniya. (Werengani 1 Mafumu 1:​5-8.) Pochita zimenezi, Abiyatara anakhala wosakhulupirika kwa Davide komanso Yehova. Kodi mukuganiza kuti Zadoki anamva bwanji ndi zimenezi? Kwa zaka zoposa 40, iye ndi Abiyatara anali atagwira ntchito limodzi monga ansembe. (2 Sam. 8:17) Pa nthawi ina iwo anathandizana kusamalira “likasa la Mulungu woona.” (2 Sam. 15:29) Poyamba onsewa anali kumbali ya Davide ndi ufumu wake ndipo anachita zambiri potumikira Yehova.—2 Sam. 19:​11-14.

16. Kodi n’chiyani chinathandiza Zadoki kuti akhalebe wokhulupirika?

16 Zadoki anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale kuti Abiyatara anachita zosakhulupirika. Davide sanasiye kumukhulupirira Zadoki. Chiwembu cha Adoniya chitadziwika, Davide anasankha Zadoki, Natani ndi Benaya kuti akadzoze Solomo kukhala mfumu. (1 Maf. 1:​32-34) Kukhala pakati pa atumiki a Yehova okhulupirika monga Natani ndi ena omwe anali kumbali ya Mfumu Davide, kuyenera kuti ndi kumene kunamulimbikitsa Zadoki. (1 Maf. 1:​38, 39) Solomo atakhala mfumu, anasankha “wansembe Zadoki kuti alowe m’malo mwa Abiyatara.”—1 Maf. 2:35.

17. Kodi mungatsanzire bwanji Zadoki ngati munthu yemwe mumamukonda wasiya kutumikira Yehova?

17 Kodi tingamutsanzire bwanji Zadoki? Ngati munthu amene mumamukonda wasiya kutumikira Yehova, inuyo muzisonyeza kuti mukufuna kukhalabe wokhulupirika. (Yos. 24:15) Yehova adzakupatsani mphamvu komanso kukulimbikitsani. Muzimudalira popemphera kwa iye komanso kupitiriza kukhala pa ubwenzi ndi Akhristu anzanu okhulupirika. Yehova amaona kukhulupirika kwanu ndipo adzakupatsani mphoto.—2 Sam. 22:26.

18. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Marco ndi Sidse?

18 Taganizirani zomwe zinachitikira Marco ndi mkazi wake Sidse, omwe ana awo awiri aakazi anasiya choonadi. Marco anati: “Makolo amakonda ana awo kungochokera pamene abadwa. Iwo amachita chilichonse chomwe angathe kuti awateteze. Choncho akasankha kusiya kutumikira Yehova zimakhala zopweteka kwambiri.” Iye ananenanso kuti: “Koma Yehova wakhala akutithandiza kuti tipirire. Iye wakhala akuonetsetsa kuti pamene ine ndafooka, mkazi wanga akhale ndi mphamvu, ndipo pamene iye wafooka, ine ndikhale ndi mphamvu.” Sidse anawonjezera kuti: “Sitikanakwanitsa kupirira zikanakhala kuti Yehova sanatipatse mphamvu zomwe tinkafunikira. Ndinkavutika ndi maganizo oona kuti ineyo ndi amene ndinachititsa zonsezo, choncho ndinkamuuza Yehova mmene ndinkamvera. Pasanapite nthawi yaitali, kunabwera mlongo wina yemwe panali patatenga zaka zambiri tisanaonane. Anandigwira m’mapewa n’kundiyang’ana ndipo anandiuza kuti, ‘Sidse kumbukira kuti vuto si iweyo.’ Mothandizidwa ndi Yehova, ndakwanitsa kupitiriza kumutumikira mosangalala.”

19. Kodi ndinu wofunitsitsa kuchita chiyani?

19 Yehova amafuna kuti atumiki ake onse azikhala olimba mtima ngati Zadoki. (2 Tim. 1:7) Komabe amafuna kuti tisamangodalira mphamvu zathu. Iye amafuna kuti tizimudalira. Choncho mukakumana ndi zinthu zina zofuna kuti musonyeze kulimba mtima, muzimupempha kuti akuthandizeni. Musamakayikire kuti iye adzakuthandizani kuti mukhale olimba mtima kwambiri ngati Zadoki.—1 Pet. 5:10.

NYIMBO NA. 126 Khalani Maso, Limbani M’chikhulupiriro, Khalani Amphamvu