Musamaiwale Nkhani Yofunika Kwambiri
“Kuti anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”—SAL. 83:18.
NYIMBO: 46, 136
1, 2. (a) Kodi nkhani yofunika kwambiri imene imakhudza anthu onse ndi iti? (b) Kodi kuganizira kwambiri nkhani imeneyi kungatithandize bwanji?
ANTHU ambiri masiku ano amaona kuti ndalama ndi zofunika kwambiri kuposa chinthu chilichonse. Iwo amangokhalira kufunafuna chuma kapena kuteteza chuma chimene ali nacho. Pomwe ena amaona kuti chofunika kwambiri ndi banja lawo, thanzi lawo kapena zinthu zimene akufuna kuchita pa moyo wawo.
2 Komabe chinthu chofunika kwambiri ndi nkhani ya ulamuliro wa Yehova yomwe imakhudza tonsefe. Tiyenera kusamala kuti tisamaiwale nkhani imeneyi. Koma kodi n’chiyani chingachititse kuti tiiwale nkhaniyi? Tikhoza kutanganidwa kwambiri ndi zinthu za tsiku ndi tsiku mpaka kuiwala zoti nkhani ya ulamuliro wa Mulungu ndi yofunika kwambiri. Apo ayi tingalole kuti mavuto amene tikukumana nawo atisokoneze maganizo n’kuiwala nkhani yaikulu kwambiriyi. Koma chimene tiyenera kudziwa n’chakuti tikamaganizira kwambiri nkhani yofunikayi m’pamene timakhala okonzeka kulimbana ndi vuto lililonse limene tingakumane nalo. Komanso kuganizira nkhani imeneyi kungatithandize kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.
N’CHIFUKWA CHIYANI TINGANENE KUTI NKHANI IMENEYI NDI YOFUNIKA?
3. Kodi maganizo a Satana ndi otani pa nkhani ya ulamuliro wa Mulungu?
3 Zimene Satana anachita zachititsa kuti ulamuliro wa Yehova uzikayikiridwa. Iye amanena kuti ulamuliro wa Mulungu si wachilungamo. Amanenanso kuti Mulungu amamana anthu ndiponso angelo zinthu zabwino. Maganizo a Mdyerekezi ndi oti anthu akhoza kukhala osangalala ngati atamadzilamulira okha. (Gen. 3:1-5) Iye ananenanso kuti munthu aliyense sangakhale wokhulupirika kwa Yehova ndi mtima wonse, moti atayesedwa kwambiri akhoza kukana ulamuliro wake. (Yobu 2:4, 5) Choncho Yehova walola kuti anthu azidzilamulira n’cholinga choti anthuwo aone okha mavuto amene angakhalepo ngati sakulamuliridwa ndi Yehova, yemwe ndi wachilungamo.
4. N’chifukwa chiyani nkhani yokhudza ulamuliro iyenera kuthetsedwa?
4 Popeza kuti Yehova amadziwa zoti zimene Satana amanenazi ndi zabodza, n’chifukwa chiyani walola kuti nkhaniyi itenge nthawi yaitali asanaithetse? Iye akudziwa kuti nkhaniyi ikukhudza anthu onse komanso angelo choncho m’pofunika kuti aliyense atsimikizire ngati zonena za Satanazo ndi zoona kapena ayi. (Werengani Salimo 83:18.) Tisaiwalenso kuti anthu awiri oyambirira anakana ulamuliro wa Yehova ndipo izi n’zimene anthu ambiri akhala akuchita. Zimenezi zingachititse anthu ena kuganiza kuti zonena za Satanazi ndi zoona. Ngati nkhani yokhudza ulamuliroyi singathetsedwe m’maganizo mwa anthu kapena angelo, pazikhalabe kusagwirizana kwa mayiko, mitundu, mafuko, mabanja komanso anthu. Koma Yehova akadzasonyeza zoti ndi woyenera kulamulira, aliyense azidzamvera ulamuliro wake wachilungamo ndipo padzakhala mtendere m’chilengedwe chonse.—Aef. 1:9, 10.
5. Kodi ifeyo tingathandize bwanji posonyeza kuti ulamuliro wa Yehova ndi woyenera?
5 Posachedwapa, Yehova adzasonyeza kuti ndi woyenera kulamulira ndipo ulamuliro wa Satana ndiponso wa anthu udzaonekeratu kuti ndi wolephera ndipo udzachotsedwa. Ufumu wa Mesiya udzasonyeza kuti ulamuliro wa Mulungu ndi wabwino ndipo anthu amene adzakhalebe okhulupirika adzasonyeza kuti n’zotheka kukhalabe kumbali ya ulamuliro wa Mulungu. (Yes. 45:23, 24) Kodi inuyo mukufuna kukhala m’gulu la anthu osonyeza kuti ulamuliro wa Yehova ndi wabwino? Mosakayikira mwayankha kale kuti inde. Koma kuti tikhalebe okhulupirika tiyenera kumaona kuti nkhani ya ulamuliroyi ndi yofunika kwambiri.
NKHANIYI NDI YOFUNIKA KUPOSA KUPULUMUKA KWATHU
6. Kodi nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova ndi yofunika bwanji?
6 Monga tanenera kale, nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova iyenera kukhala yofunika kwambiri kwa munthu aliyense. Ndipotu nkhaniyi ndi yofunika kuposa kusangalala kapena kupulumuka kwa anthu. Kodi mfundoyi ikusonyeza kuti kupulumuka si kofunika komanso kuti Yehova satiganizira? Ayi. N’chifukwa chiyani tikutero?
7, 8. Kodi tikudziwa bwanji kuti Mulungu akadzasonyeza kuti ndi woyenera kulamulira adzakwaniritsanso malonjezo ake?
7 Yehova amakonda anthu kwambiri ndipo amaona kuti ndi amtengo wapatali. N’chifukwa chake analolera kupereka moyo wa Mwana wake kuti tidzapeze moyo wosatha. (Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:9) Yehova atapanda kukwaniritsa malonjezo ake, Mdyerekezi angakhale ndi chifukwa chonenera kuti Mulungu ndi wabodza, amatimana zinthu zabwino komanso salamulira mwachilungamo. Nawonso anthu otsutsa Mulungu akhoza kuoneka ngati amanena zoona. Paja amanena kuti: “Kukhalapo kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti? Taonani, kuchokera tsiku limene makolo athu anamwalira, zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi ngati mmene zakhalira kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe.” (2 Pet. 3:3, 4) Yehova akadzasonyeza kuti ndi woyenera kulamulira adzapulumutsanso anthu omvera. (Werengani Yesaya 55:10, 11.) Mfundo ina yofunika kuikumbukira ndi yakuti ulamuliro wa Yehova ndi wachikondi. Choncho sitiyenera kukayikira kuti nthawi zonse Yehova amakonda anthu ake okhulupirika, amawayamikira ndiponso amawaona kuti ndi ofunika.—Eks. 34:6.
8 Ponena kuti nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova ndi yofunika kwambiri sitikutanthauza kuti ifeyo komanso kupulumuka kwathu si zofunika kwa iye. Tikungosonyeza kuti tikayerekezera nkhani ziwirizi, yofunika kwambiri ndi imeneyo. Kukumbukira mfundo imeneyi kungatithandize kuti tisaiwale nkhani yofunika kwambiriyi komanso kuti tikhale kumbali ya ulamuliro wa Yehova.
ZIMENE TINGAPHUNZIRE PA NKHANI YA YOBU
9. Fotokozani zimene Satana ananena zokhudza Yobu. (Onani chithunzi choyambirira.)
9 Buku la Yobu, lomwe linalembedwa kalekale, likhoza kutithandiza kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ulamuliroyi. M’bukuli timamva kuti Satana ananena kuti Yobu akhoza kukana ulamuliro wa Mulungu ngati atayesedwa kwambiri. Iye anauza Mulungu kuti azunze Yobu. Koma Yehova sanachite zimenezi. M’malomwake analola kuti Satana ayese Yobu. Anamuuza kuti: “Chilichonse chimene ali nacho chikhale m’manja mwako.” (Werengani Yobu 1:7-12.) Pasanapite nthawi yaitali, ziweto zina za Yobu zinabedwa ndipo zina zinaphedwa. Antchito ake komanso ana ake anaphedwanso. Satana anachita zonsezi m’njira yoti zizioneka kuti Mulungu ndi amene wachititsa mavutowo. (Yobu 1:13-19) Kenako Satana anachititsa kuti Yobu adwale matenda onyansa komanso opweteka. (Yobu 2:7) Mavuto ake anawonjezereka pamene mkazi wake komanso anzake atatu anamulankhula mawu opweteka.—Yobu 2:9; 3:11; 16:2.
10. (a) Kodi Yobu anasonyeza bwanji kuti anali wokhulupirika kwa Yehova? (b) Kodi iye anali ndi maganizo olakwika ati?
10 Kodi nkhani ya Yobu inatha bwanji? Zimene Satana ananena zinaonekeratu kuti ndi zabodza. Yobu sanalole kuti asiye kutumikira Yehova. (Yobu 27:5) Komabe, pa nthawi ina Yobu anali ndi maganizo olakwika. Iye ankafuna kusonyeza kuti ndi wolungama komanso ankaona kuti Mulungu ayenera kumufotokozera chifukwa chomveka chomwe chachititsa kuti akumane ndi mavutowo. (Yobu 7:20; 13:24) Mwina tikhoza kuganiza kuti maganizo a Yobuwa anali omveka. Koma Yehova anaona kuti ndi bwino kumuthandiza kuti asinthe maganizo akewo. Kodi Yehova anamuthandiza bwanji?
11, 12. Kodi Yehova anathandiza Yobu kuzindikira chiyani, nanga Yobu anatani atalandira malangizowo?
11 Zimene Yehova anayankha timazipeza m’buku la Yobu chaputala 38 mpaka 41. Koma palibe paliponse pamene anamufotokozera chimene chinachititsa kuti avutike choncho. Cholinga chake pomuyankha sichinali kumufotokozera chifukwa chake anakumana ndi mavutowo ngati kuti Mulungu ankafunika kuyankha mlandu kwa Yobu. Koma ankafuna kumuthandiza kuzindikira kuti Yehovayo ndi wamkulu kwambiri poyerekezera ndi Yobuyo. Yehova anathandizanso Yobu kuzindikira kuti panali nkhani zina zimene zinali zofunika kwambiri kuposa mavuto akewo. (Werengani Yobu 38:18-21.) Mawu a Yehovawa anathandiza Yobu kuti ayambe kuona zinthu moyenera.
12 Popeza Yobu anali atavutika kwambiri, kodi zimene Yehova ananenazo zinali zankhanza komanso zopanda chifundo? Ayi, ndipo nayenso Yobu sanaganize choncho. Ngakhale kuti anali atakumana ndi mavutowo, Yobu anayamikira zimene Yehova anamuuza. Iye anafika ponena kuti: “Ndikulapa m’fumbi ndi m’phulusa.” Izi zikusonyeza kuti malangizo olimbikitsa koma osapita m’mbali a Mulungu anamuthandiza. (Yobu 42:1-6) Yobu anali atalandiranso malangizo ochokera kwa Elihu yemwe anali wamng’ono kwa iye. (Yobu 32:5-10) Yobu atalandira malangizo a Mulungu n’kusintha maganizo ake, Mulunguyo analankhula kwa anthu ena mawu osonyeza kuti akusangalala ndi Yobu chifukwa cha kukhulupirika kwake.—Yobu 42:7, 8.
13. Kodi malangizo a Yehova akanathandiza bwanji Yobu pambuyo pa mavuto ake?
13 Malangizo a Yehovawa ayenera kuti anathandizanso Yobu pambuyo pa mavuto akewo. N’chifukwa chiyani tikutero? N’zoona kuti “Yehova anadalitsa kwambiri mapeto a Yobu kuposa chiyambi chake.” Ndipo Yobu “anakhalanso ndi ana aamuna 7 ndi ana aakazi atatu.” (Yobu 42:12-14) Koma payenera kuti panatenga nthawi yaitali kuti zonsezi zichitike. N’zosachita kufunsa kuti Yobu ankawasowa ana ake amene anaphedwa ndi Satana aja. Ndipo kwa nthawi ndithu, ayenera kuti ankavutika akakumbukira mavuto amene anakumana nawo. Ngakhale atakhala kuti anamvetsa zimene zinachititsa mavuto akewo, ayenera kuti nthawi zina ankadzifunsa kuti, ‘Kodi zinalidi zofunika kuti mavuto ake afike poipa kwambiri choncho?’ Kaya ankaganiza zotani, kuganizira malangizo amene Mulungu anamupatsa kukanamuthandiza. Ndipo izi zikanachititsa kuti akhale ndi maganizo oyenera komanso kuti alimbikitsidwe.—Sal. 94:19.
14. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Yobu?
14 Nkhani ya Yobu ikhozanso kutilimbikitsa komanso kutithandiza kuti tikhale ndi maganizo oyenera. Ndipo Yehova analola kuti nkhaniyi isungidwe m’Mawu ake ‘kuti itilangize. Malembawa amatipatsa chiyembekezo chifukwa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.’ (Aroma 15:4) Ndiye kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Yobuyi? Phunziro lalikulu ndi lakuti tisalole kuti zimene zikuchitika pa moyo wathu zitiiwalitse mfundo yakuti nkhani yofunika kwambiri ndi ya ulamuliro wa Yehova. Tizikumbukiranso kuti tikamatsanzira Yobu, n’kumakhala okhulupirika ngakhale pa nthawi imene tikuvutika kwambiri, tidzasonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wa Mulungu.
15. Kodi chimachitika n’chiyani tikakhalabe okhulupirika pa nthawi imene tikukumana ndi mavuto?
15 Kodi kuganizira ubwino wokhalabe okhulupirika kungatilimbikitse bwanji? Kungatithandize kuzindikira kuti mavuto athu amatipatsa mwayi wosonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wa Yehova ndipo si umboni woti iye sakusangalala nafe. (Miy. 27:11) Paja Baibulo limanena kuti kupirira kumachititsa kuti “tikhale ovomerezeka kwa Mulungu” ndipo kumatithandiza kuti tikhale ndi chiyembekezo champhamvu. (Werengani Aroma 5:3-5.) Nkhani ya Yobu imasonyezanso kuti “Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.” (Yak. 5:11) Choncho tisamakayikire kuti iye adzatidalitsa komanso adzadalitsa anthu onse amene ali kumbali ya ulamuliro wake. Kudziwa zimenezi kungatithandize “kupirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.”—Akol. 1:11.
KODI TINGATANI KUTI TISAMAIWALE NKHANI YOFUNIKA KWAMBIRI?
16. N’chifukwa chiyani tiyenera kumadzikumbutsa za nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova?
16 N’zoona kuti kukumbukira nthawi zonse nkhani yofunika yokhudza ulamuliro wa Yehova si kophweka. Zili choncho chifukwa nthawi zina timapanikizika ndi mavuto. Komanso ngakhale mavuto aang’ono akhoza kutivutitsa maganizo tikamawaganizira kwambiri. Choncho tikamakumana ndi mavuto ndi bwino kumadzikumbutsa nthawi ndi nthawi za kufunika kosonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wa Yehova.
17. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kugwira ntchito yolalikira kungatithandize kuti tisamaiwale nkhani yofunika.
17 Kugwirabe ntchito yolalikira mwakhama kungatithandize kuti tisamaiwale nkhani yofunikayi. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Renee. Iye ankadwala khansa, anachita sitiroko ndipo thupi lake linkaphwanya nthawi zonse. Akapita kuchipatala, ankakonda kulalikira ogwira ntchito kuchipatalako, odwala ena komanso anthu odzaona odwala. Kuchipatala china, analalikira kwa maola 80 pa milungu iwiri ndi hafu yokha. Ngakhale atatsala pang’ono kumwalira, mlongoyu sanaiwale nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova. Izi zinamuthandiza kuti asamavutike kwambiri maganizo.
18. Kodi chitsanzo cha mlongo wina chikusonyeza bwanji ubwino woganizira nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova?
18 Timafunikanso kukumbukira nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova tikamakumana ndi mavuto a tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, Jennifer anakhala pabwalo la ndege masiku atatu akudikira kuti papezeke ndege yopita kwawo. Izi zinachitika chifukwa ndege zimene ankafuna kukwera zinkaletsedwa kunyamuka pa zifukwa zina. Iye anatopa kwambiri komanso anali yekhayekha ndipo zikanakhala zosavuta kuti ayambe kudandaula. Koma m’malomwake anapempha Mulungu kuti amuthandize kulimbikitsa anthu ena amene ankadikiranso ndege. Kodi zimenezi zinamuthandiza bwanji? Iye anatha kulalikira anthu ambiri komanso kuwapatsa mabuku ambiri. Mlongoyu anati: “Ndikuona kuti Yehova anandidalitsa pa nthawi yovutayi ndipo anandipatsa mphamvu yoti ndizichita zinthu zothandiza kuti dzina lake lilemekezeke.” Iye sanasiye kuganizira cholinga cha Yehova.
19. Kodi maganizo a anthu a Yehova ndi otani pa nkhani ya Ulamuliro wa Mulungu?
19 Anthu a m’chipembedzo choona amasiyana ndi a m’chipembedzo chonyenga chifukwa amazindikira kufunika kwa nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova. Kuyambira kale, anthu a Mulungu akhala akusonyeza kuti ali kumbali ya ulamuliro wake. Popeza kuti tili m’gulu la Yehova, aliyense wa ife ayenera kuyesetsa kuchita zimenezi.
20. Kodi Yehova amamva bwanji akaona mukuyesetsa kukhala kumbali ya ulamuliro wake?
20 Dziwani kuti Yehova amasangalala kwambiri mukamayesetsa kukhala kumbali yake pomutumikira mokhulupirika komanso popirira mavuto. (Sal. 18:25) Munkhani yotsatira tidzapitiriza kuona chifukwa chake tiyenera kukhala kumbali ya ulamuliro wa Yehova komanso mmene tingachitire zimenezi ndi mtima wonse.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA