Muzikhala Kumbali ya Ulamuliro wa Yehova

Muzikhala Kumbali ya Ulamuliro wa Yehova

“Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse.”​—CHIV. 4:11.

NYIMBO: 112, 133

1, 2. Kodi munthu aliyense ayenera kutsimikizira chiyani? (Onani chithunzi choyambirira.)

MUNKHANI yapita ija, taona kuti Mdyerekezi amanena kuti Yehova salamulira bwino ndipo zinthu zingayende bwino ngati anthu atamadzilamulira okha. Koma kodi zimenezi ndi zoona? Tiyerekeze kuti anthu ofuna kudzilamulira akhoza kukhala ndi moyo wosatha. Kodi angathe kuchitadi zinthu bwino popanda ulamuliro wa Mulungu? Kodi inuyo panokha mungasangalale kukhala ndi moyo wosatha mukudzilamulira nokha?

2 Munthu aliyense ayenera kupeza yekha mayankho a mafunso amenewa, osati kuyankhiridwa. Ngati titaiganizira bwino nkhaniyi, titha kuoneratu kuti ulamuliro wa Mulungu ndi woyenera komanso wabwino kwambiri. Tonsefe tiyenera kukhala kumbali ya ulamuliro umenewu. Baibulo limapereka zifukwa zomveka zochitira zimenezi. Mwachitsanzo, tiyeni tikambirane zimene Malemba amanena pa nkhani yoti Yehova ndi woyenera kulamulira.

YEHOVA NDI WOYENERA KULAMULIRA

3. N’chifukwa chiyani Yehova yekha ndi amene ali woyenera kulamulira?

3 Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse chifukwa ndi amene analenga zinthu zonse komanso ndi Mulungu wamphamvuyonse. (1 Mbiri 29:11; Mac. 4:24) Pa Chivumbulutso 4:11, Yohane anaona masomphenya a anthu 144,000 amene adzalamulire ndi Khristu akunena kuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” Popeza Yehova ndi amene analenga zinthu zonse, iye ndi woyenera kulamulira anthu komanso angelo.

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti munthu akakana ulamuliro wa Mulungu ndiye kuti sanagwiritse ntchito moyenera ufulu wake wosankha?

4 Satana sanalenge chinthu ngakhale chimodzi. Chifukwa cha zimenezi si woyenera kulamulira. Iye limodzi ndi Adamu ndi Hava anachita zinthu modzikuza kwambiri pogalukira ulamuliro wa Yehova. (Yer. 10:23) N’zoona kuti anali ndi ufulu wosankha zochita. Koma kodi anagwiritsa ntchito ufuluwu moyenera? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti anthu ali ndi ufulu wosankha zochita za tsiku ndi tsiku koma alibe ufulu wogalukira Mulungu amene anawalenga. Choncho anthufe tiyenera kugonjera ulamuliro wa Yehova womwe ndi wachilungamo.

5. N’chiyani chikutitsimikizira kuti zimene Mulungu amasankha kuchita ndi zachilungamo?

5 Chinthu china chimene chimachititsa kuti Yehova akhale woyenera kulamulira n’chakuti amalamulira mwachilungamo kwambiri. Iye anati: “Ine ndine Yehova, amene ndimasonyeza kukoma mtima kosatha, ndimapereka ziweruzo ndi kuchita chilungamo padziko lapansi. Pakuti zinthu zimenezi zimandisangalatsa.” (Yer. 9:24) Kuti achite zinthu mwachilungamo, Yehova sadalira malamulo amene anthu omwe si angwiro analemba. Iye ndi wachilungamo kale moti amadziwa yekha zoyenera kuchita ndipo ndi amene anapereka malamulo kwa anthu. Paja Baibulo limati: “Chilungamo ndi chiweruzo ndizo maziko a mpando [wake] wachifumu.” (Sal. 89:14; 119:128) Choncho sitiyenera kukayikira kuti malamulo ake, mfundo zake komanso zonse zimene amasankha ndi zachilungamo. Koma Satana, yemwe amanena kuti Yehova salamulira bwino, walephera kuthandiza kuti zinthu ziziyenda mwachilungamo m’dzikoli.

6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi woyenera kulamulira dzikoli?

6 Yehova ndi woyeneranso kulamulira chifukwa choti amadziwa chilichonse ndipo ali ndi nzeru zomuthandiza kusamalira chilengedwe chonse. Mwachitsanzo, iye anathandiza Mwana wake kuti achiritse matenda amene madokotala sakanachiza. (Mat. 4:23, 24; Maliko 5:25-29) Kwa Yehova zimenezi si zodabwitsa ayi. Iye amadziwa bwino matupi athu ndiponso zimene angachite kuti akonze chilichonse chimene chawonongeka. Akhozanso kuukitsa akufa kapena kuchititsa kuti ngozi zadzidzidzi zisamachitike padzikoli.

7. Kodi nzeru za Yehova zimaposa bwanji za anthu a m’dziko la Satanali?

7 Anthu a m’dziko la Satanali akukanika kuthetsa mikangano ya pakati pa mitundu ya anthu ndi mayiko. Koma Yehova yekha ndi amene ali ndi nzeru zothandiza kuti padziko lonse pakhale mtendere. (Yes. 2:3, 4; 54:13) Tikaphunzira bwinobwino nzeru za Yehova, timamva mmene anamvera mtumwi Paulo yemwe analemba kuti: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukire njira zake?”​—Aroma 11:33.

ULAMULIRO WA YEHOVA NDI WABWINO KWAMBIRI

8. Kodi inuyo chimakusangalatsani n’chiyani mukaganizira za ulamuliro wa Yehova?

8 Baibulo limasonyezanso kuti ulamuliro wa Yehova ndi wabwino kuposa wa munthu wina aliyense. Chifukwa choyamba n’chakuti iye amalamulira mwachikondi. Timasangalala kwambiri tikaganizira zimene amachita polamulira. Iye ndi “wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.” (Eks. 34:6) Iye amalemekeza kwambiri atumiki ake apadzikoli. Amatisamaliranso kuposa mmene tingadzisamalire tokha. Mosiyana ndi zimene Satana ananena, Yehova satimana chilichonse chabwino. Paja anapereka Mwana wake wamtengo wapatali kuti tikhale ndi mwayi wodzapeza moyo wosatha.​—Werengani Salimo 84:11; Aroma 8:32.

9. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amaganizira munthu aliyense payekha?

9 Sikuti Yehova amangosamalira anthu ake monga gulu koma amaganiziranso munthu aliyense payekha. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene Yehova anachita kwa zaka 300 pamene ankagwiritsa ntchito oweruza populumutsa Aisiraeli kwa adani awo. Pa nthawi yovutayi, iye ankaganiziranso munthu aliyense payekha. Anaona zimene munthu wina dzina lake Rute anachita. Iye anasiya anthu a mtundu wake n’kuyamba kulambira Yehova limodzi ndi Aisiraeli. Yehova anadalitsa Rute pomupatsa mwamuna wabwino komanso mwana wamwamuna. Komatu si zokhazi. Rute akadzaukitsidwa adzamva kuti mwana wake anali mumzere wa makolo a Mesiya. Adzasangalalanso kuzindikira kuti nkhani yake inalembedwa m’buku la m’Baibulo lodziwika ndi dzina lake.​—Rute 4:13; Mat. 1:5, 16.

10. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova salamulira mopondereza?

10 Yehova salamulira mopondereza ndipo si womva zake zokha. Iye anapereka ufulu kwa anthu ndipo izi zimathandiza kuti anthu azisangalala. (2 Akor. 3:17) Pa nkhani imeneyi, Davide analemba kuti: “Ulemu ndi ulemerero zili pamaso pake [pa Mulungu], pokhala pake pali mphamvu ndi chimwemwe.” (1 Mbiri 16:7, 27) Nayenso Etani, amene analemba masalimo ena, anati: “Odala ndi anthu amene amafuula mosangalala. Iwo amayendabe m’kuwala kwa nkhope yanu, inu Yehova. Iwo amakondwera ndi dzina lanu tsiku lonse. Chilungamo chanu chimawakweza.”​—Sal. 89:15, 16.

11. N’chiyani chingatithandize kutsimikizira kuti ulamuliro wa Yehova ndi wabwino kwambiri?

11 Tikamaganizira zinthu zabwino zimene Yehova amachita timatsimikizira kuti ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. Timakhala ndi maganizo a wamasalimo amene ananena kuti: “Kukhala tsiku limodzi m’mabwalo anu n’kwabwino kuposa kukhala masiku 1,000 kwina.” (Sal. 84:10) Maganizo amenewa ndi omveka chifukwa Yehova ndi amene anatilenga komanso amadziwa zimene zingatisangalatse ndipo amatipatsa zinthuzo mowolowa manja. Chilichonse chimene amatiuza kuti tichite chimakhala chotithandiza ndipo tikamvera timasangalala. Izi zimachitika ngakhale pamene tiyenera kudzimana zinthu zina kuti timumvere.​—Werengani Yesaya 48:17.

12. Tchulani chifukwa chachikulu chimene chimatichititsa kukhala kumbali ya ulamuliro wa Yehova.

12 Baibulo limasonyeza kuti pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu anthu ena adzagalukira ulamuliro wa Yehova. (Chiv. 20:7, 8) Koma n’chifukwa chiyani adzachite zimenezi? Satana akadzamasulidwa adzayesetsa kusocheretsa anthu pogwiritsa ntchito njira yake yomwe ija yowachititsa kukhala odzikonda. Mwina adzachititsa anthu kuganiza kuti n’zotheka kukhala ndi moyo wosatha popanda kumvera Yehova. Koma limeneli lidzakhala bodza lankunkhuniza. Tingachite bwino kudzifunsa kuti: Kodi ineyo ndidzakopeka ndi bodza lakelo? Ngati timakonda Yehova n’kumamutumikira chifukwa chodziwa kuti ndi wabwino komanso woyenera kulamulira, bodza limeneli lidzatinyansa kwambiri. Sitidzayerekeza n’komwe kuganiza kuti zinthu zingatiyendere bwino popanda kulamuliridwa ndi Yehova yemwe ndi wachikondi.

ZIMENE TINGACHITE POSONYEZA KUTI TILI KUMBALI YA ULAMULIRO WA YEHOVA

13. Kodi tingachitenso zinthu ziti posonyeza kuti tili kumbali ya Yehova?

13 Yehova ndi woyenera kumumvera ndi mtima wathu wonse. Monga taonera, iye ndi woyenera kulamulira ndipo ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. Tingasonyeze kuti tili kumbali ya ulamuliro wake tikamamumvera komanso kumutumikira mokhulupirika. Koma kodi tingachitenso zinthu zina ziti posonyeza kuti tili kumbali yake? Tiyenera kuyesetsa kuchita zinthu ngati mmene Yehova angazichitire. Tikatero timasonyeza kuti timakonda ulamuliro wake ndipo tili kumbali yake.​—Werengani Aefeso 5:1, 2.

14. Kodi amuna ndi akulu angatsanzire bwanji Yehova?

14 Baibulo latithandiza kudziwa kuti Yehova amalamulira mwachikondi. Choncho amuna komanso akulu amene amakonda ulamuliro wa Yehova sayenera kudziona ngati mafumu n’kumapondereza anthu a m’banja lawo kapena mumpingo. M’malomwake amatsanzira Yehova. Paulo ankayesetsa kutsanzira Mulungu komanso Yesu. (1 Akor. 11:1) Iye sankachititsa anthu ena manyazi kapena kuwakakamiza kuchita zinthu. Koma ankachita kuwapempha mwachikondi kapena kuwadandaulira. (Aroma 12:1; Aef. 4:1; Filim. 8-10) Umu ndi mmene Yehova amachitira zinthu ndipo aliyense amene amakonda komanso kugonjera ulamuliro wake ayenera kuchitanso zimenezi.

15. Kodi kugonjera anthu amene Yehova akuwagwiritsa ntchito kumasonyeza bwanji kuti timakonda ulamuliro wake?

15 Kodi ifeyo timachita bwanji pa nkhani yogonjera anthu amene Yehova wawapatsa udindo? Tikamawalemekeza komanso kuwagonjera timasonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wa Yehova. Tiyenera kugonjera anthu amene Yehova akuwagwiritsa ntchito ngakhale pamene sitikumvetsa zimene asankha kapena sitikugwirizana nazo. Munthu akamachita zimenezi amasonyeza kuti amamvera ulamuliro wa Yehova ndipo amasiyana kwambiri ndi anthu a m’dzikoli. (Aef. 5:22, 23; 6:1-3; Aheb. 13:17) Ndipo zotsatira zake n’zakuti zinthu zimamuyendera bwino chifukwa chilichonse chimene Yehova amatiuza chimakhala chothandiza.

16. Kodi anthu amene ali kumbali ya ulamuliro wa Yehova amasankha bwanji zochita?

16 Zimene timasankha kuchita zingasonyezenso ngati tili kumbali ya ulamuliro wa Yehova kapena ayi. Pa zinthu zina, palibe lamulo lachindunji limene Yehova anapereka. Iye amangotithandiza kudziwa mmene amaganizira. Mwachitsanzo, Yehova sanapereke malamulo oti Akhristu azivala zovala zakutizakuti. M’malomwake amatithandiza kudziwa zimene amafuna. Iye amafuna kuti tizivala mwaulemu komanso kusankha zovala zoyenera anthu amene amati amalemekeza Mulungu. (1 Tim. 2:9, 10) Yehova amafunanso kuti tizipewa kusankha zinthu zomwe zingadabwitse kapena kukhumudwitsa anthu ena. (1 Akor. 10:31-33) Choncho tikamasankha zinthu motsatira maganizo a Yehova osati mtima wathu, timasonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wake.

Muzisonyeza kuti muli kumbali ya ulamuliro wa Yehova posankha zochita komanso pochita zinthu m’banja (Onani ndime 16-18)

17, 18. Kodi anthu amene ali pa banja angasonyeze bwanji kuti ali kumbali ya ulamuliro wa Yehova?

17 Kodi anthu amene ali pa banja angasonyeze bwanji kuti ali kumbali ya ulamuliro wa Mulungu? Tiyerekeze kuti banja lanu silikuyenda bwino mmene munkaganizira. Mwina zafika poti silikukusangalatsani ngakhale pang’ono. Zimene zingakuthandizeni ndi kuganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli. Iye ankadziyerekezera kuti ndi mwamuna wa Aisiraeliwo. (Yes. 54:5; 62:4) Aisiraeli, omwe anali ngati mkazi wa Mulungu, anali ovuta kwambiri. Koma Yehova sanafulumire kuwasiya. Mobwerezabwereza ankawachitira chifundo ndipo ankakumbukira pangano limene anapangana nawo. (Werengani Salimo 106:43-45.) Izi zikusonyeza kuti Yehova ndi wachikondi komanso wokhulupirika.

18 Mabanja amene amakonda Mulungu amayesetsa kumutsanzira. Choncho ngati banja lawo silikuyenda bwino, sangalithetse pa zifukwa zosagwirizana ndi Malemba. Iwo amadziwa kuti Yehova amafuna kuti asasiyane. Malemba amasonyeza kuti munthu angathetse banja n’kukhala ndi ufulu wokwatira kapena kukwatiwanso ngati mwamuna kapena mkazi wake wachita chigololo. (Mat. 19:5, 6, 9) Munthu akamachita zonse zimene angathe kuti banja lake liziyenda bwino amasonyeza kuti ali kumbali ya ulamuliro wa Yehova.

19. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati talakwitsa zinazake?

19 Popeza si ife angwiro, nthawi zina tikhoza kuchita zinthu zosasangalatsa Yehova. Iye amadziwa zimenezi ndipo anapereka dipo la Khristu kuti litithandize. Choncho tikalakwitsa zinazake tiyenera kupempha Yehova kuti atikhululukire. (1 Yoh. 2:1, 2) Ndipo m’malo mongokhalira kudziimba mlandu, tiyenera kungophunzirapo kanthu. Ngati timakonda kwambiri Yehova, iye adzatikhululukira komanso kutithandiza kuti tisiye kudziimba mlandu. Angatithandizenso kuti tipitirize kumutumikira mokhulupirika.​—Sal. 103:3.

20. N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza kuti tili kumbali ya Yehova panopa?

20 M’dziko latsopano, anthu onse azidzagonjera ulamuliro wa Yehova ndipo adzaphunzira njira zake zachilungamo. (Yes. 11:9) Koma Yehova wayambiratu panopa kutiphunzitsa. Ndipo nkhani yotsimikizira kuti iye ndi woyenera kulamulira ili mkati. Choncho inoyo ndi nthawi yoti tisonyeze kuti tili kumbali ya Yehova. Tingachite zimenezi pokhalabe okhulupirika, kuchita utumiki wathu ndi mtima wonse komanso kuyesetsa kumutsanzira pa zonse zimene timachita.