Yehova Amatitonthoza M’masautso Athu Onse

Yehova Amatitonthoza M’masautso Athu Onse

‘Mulungu amatitonthoza m’masautso athu onse.’—2 AKOR. 1:3, 4.

NYIMBO: 38, 56

1, 2. Kodi Yehova amatitonthoza bwanji, nanga Malemba amatitsimikizira chiyani pa nkhaniyi?

MNYAMATA wina amene tangomupatsa dzina loti Eduardo ankacheza ndi wachikulire wina dzina lake Stephen. Mnyamatayu ankaganizira mfundo ya pa 1 Akorinto 7:28 yakuti: ‘Olowa m’banja adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.’ Ndiyeno anamufunsa kuti: “Kodi masautso amene akutchulidwa palembali ndi ati, nanga ndingadzathane nawo bwanji ndikadzalowa m’banja?” Koma asanayankhe funsoli, Stephen anauza Eduardo kuti aganizire kaye mfundo ina imene mtumwi Paulo analemba. Mfundo yake ndi yakuti Yehova ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.”​—2 Akor. 1:3, 4.

2 Yehova ndi Atate wachikondi ndipo amatilimbikitsa tikakumana ndi mavuto. Muyenera kuti mwaonapo Mulungu akukuthandizani komanso kukutsogolerani ndipo nthawi zambiri mwina anachita zimenezi pogwiritsa ntchito Mawu ake. Iye amatifunira zabwino ngati mmene ankachitira ndi atumiki ake akale.​—Werengani Yeremiya 29:11, 12.

3. Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Mavuto ambiri tikhoza kuwapirira ngati titadziwa zimene zayambitsa mavutowo. N’chimodzimodzinso ndi mavuto a m’banja. Ndiye kodi ndi zinthu ziti zimene zingayambitse mavuto amene Paulo anawatchula kuti “nsautso m’thupi”? Nanga ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo komanso za masiku ano zimene zingatilimbikitse? Mayankho a mafunsowa angatithandize kupirira mavuto amene tingakumane nawo m’banja.

MAVUTO AMENE TINGAKUMANE NAWO M’BANJA

4, 5. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingayambitse “nsautso m’thupi”?

4 Mulungu atalenga Hava, anapita naye kwa Adamu kuti akhale mkazi wake ndipo ananena kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” (Gen. 2:24) Koma popeza kuti si ife anthu angwiro, kutsatira malangizowa kungakhale kovuta. (Aroma 3:23) Anthu akalowa m’banja, mwamuna ndi amene amatsogolera zinthu osati makolo awo. Zili choncho chifukwa chakuti Mulungu ananena kuti mwamuna ndi mutu wa mkazi wake. (1 Akor. 11:3) Amuna ndi akazi ena amene angolowa kumene m’banja amavutika kuzolowera zimenezi. Koma mogwirizana ndi Baibulo, mkazi ayenera kulola kuti mwamuna wake azimutsogolera osati makolo ake. Nthawi zina zimenezi zingachititse kuti banjalo lisamagwirizane ndi makolowo, mwinanso n’kubweretsa mavuto ena m’banja.

5 Banja likhozanso kukumana ndi mavuto ena mkazi akakhala woyembekezera. N’zoona kuti banja limasangalala likadziwa kuti lidzakhala ndi mwana. Komabe likhoza kuda nkhawa poganiza kuti, ‘Kodi mayiyo adzabereka bwinobwino, nanga mwanayo adzabadwa wathanzi?’ Banjalo limaderanso nkhawa mavuto azachuma amene angakumane nawo akakhala ndi mwana. Ndipotu mwanayo akabadwa mavuto enanso akhoza kuyamba. Zili choncho chifukwa chakuti nthawi imene mayi amakhala akusamalira mwana imakhala yambiri ndipo izi zingachititse kuti mwamuna aziona ngati akunyalanyazidwa. Komanso udindo wa mwamunayo umawonjezereka chifukwa amafunika kusamaliranso mwanayo ndiponso kumupezera zofunika pa moyo.

6-8. Kodi chimachitika n’chiyani ngati munthu akufuna kukhala ndi mwana koma sizikutheka?

6 Koma mabanja ena amakhala ndi vuto lina. Iwo amafunitsitsa kukhala ndi mwana koma sizitheka. Mkazi akhoza kudandaula kwambiri chifukwa choti sakubereka. N’zoona kuti munthu akakhala ndi mwana sikuti sadzakhalanso ndi mavuto ena. Komabe ngati munthu akufuna kwambiri mwana koma osakhala naye tinganene kuti ali ndi “nsautso m’thupi.” (Miy. 13:12) Kale, munthu amene analibe mwana ankanyozeka kwambiri. Mwachitsanzo, Rakele, yemwe anali mkazi wa Yakobo, anadandaula kwambiri kuti mchemwali wake anali ndi ana koma iye analibe. (Gen. 30:1, 2) Nthawi zambiri amishonale amene amatumikira kumayiko amene anthu ambiri amakhala ndi mabanja aakulu amafunsidwa chifukwa chake alibe ana. Ngakhale kuti amayesetsa kufotokoza bwinobwino, anthuwo amanena mawu ngati akuti, “Ii pepani, tikupemphererani.”

7 Pali mlongo wina wa ku England amene ankafunitsitsa atakhala ndi mwana koma sizinatheke. Kenako anafika msinkhu woti sangaberekenso. Iye ananena kuti anadandaula kwambiri atazindikira kuti sadzaberekanso mwana m’dziko lakaleli. Choncho iye ndi mwamuna wake anasankha kuti angopeza mwana woti azimulera ngati wawo. Komabe mlongoyo anati: “Zinkandiwawabe chifukwa ndinkadziwa kuti kulera mwana wa wina si kofanana ndi kulera mwana wakowako.”

8 Baibulo limanena kuti akazi achikhristu ‘amatetezeka akabereka mwana.’ (1 Tim. 2:15) Izi sizikutanthauza kuti akabereka mwana amakhala ndi mwayi wopeza moyo wosatha. Zikungotanthauza kuti akamasamalira mwanayo komanso kugwira ntchito zina zapakhomo, sakhala ndi nthawi yolowerera nkhani za eni kapena kuchita miseche. (1 Tim. 5:13) Ngakhale zili choncho, akhoza kukumanabe ndi mavuto ena a m’banja.

Kodi n’chiyani chingathandize munthu amene mwamuna kapena mkazi wake wamwalira? (Onani ndime 9 ndi 12)

9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti imfa ya mwamuna kapena mkazi wako ndi yowawa kwambiri?

9 Koma pali vuto linanso lokhudza banja limene anthu saliganizira kwambiri. Vuto lake ndi la imfa ya mwamuna kapena mkazi. Pali anthu ambiri amene mwamuna kapena mkazi wawo anamwalira. Ambiri mwa anthuwa sankaganiza kuti zimenezi zingawachitikire. Akhristu amakhulupirira ndi mtima wonse zimene Yesu analonjeza zoti akufa adzauka. (Yoh. 5:28, 29) Zimene Yesu analonjezazi zimalimbikitsa kwambiri munthu amene waferedwa. Imeneyi ndi njira inanso imene Atate wathu wachikondi amalimbikitsira anthu kudzera m’Mawu ake. Tiyeni tsopano tikambirane mmene Yehova wakhala akulimbikitsira atumiki ake komanso mmene atumiki akewo anamvera.

AMATILIMBIKITSA TIKAKUMANA NDI MAVUTO

10. N’chiyani chinathandiza Hana kuti asakhalenso ndi nkhawa? (Onani chithunzi choyambirira.)

10 Hana anali mkazi wa Elikana ndipo anali ndi vuto lalikulu. Iye analibe mwana, pomwe mkazi mnzake dzina lake Penina anali ndi ana. (Werengani 1 Samueli 1:4-7.) “Chaka ndi chaka,” Penina ankanyoza Hana. Izi zinachititsa kuti Hana azidandaula kwambiri. Choncho anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize ndipo Baibulo limanena kuti anapemphera “kwa nthawi yaitali.” Ayenera kuti ankakhulupirira kwambiri kuti Yehova ayankha pemphero lakeli chifukwa “sanakhalenso ndi nkhawa.” (1 Sam. 1:12, 17, 18) Iye ankaona kuti Yehova adzamuthandiza kuti akhale ndi mwana kapena kumulimbikitsa m’njira inayake.

11. Kodi pemphero lingatithandize bwanji tikakumana ndi mavuto?

11 Popeza si ife angwiro komanso tili m’dziko la Satanali, tizikumanabe ndi mavuto. (1 Yoh. 5:19) Koma chosangalatsa n’chakuti tikhoza kupemphera kwa Yehova, yemwe ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” Paja Hana atavutika anapemphera kwa Yehova kuchokera mumtima. Nafenso tikakumana ndi mavuto, tisamangotchula mmene tikumvera chifukwa cha mavutowo. Koma tizipemphera kuchokera mumtima n’kumachonderera Yehova kuti atithandize.​—Afil. 4:6, 7.

12. N’chiyani chinathandiza Anna kuti azisangalala?

12 Kaya vuto lanu ndi lakuti mulibe mwana, kaya ndi loti mwamuna kapena mkazi wanu anamwalira, Yehova akhoza kukulimbikitsani. Nthawi ya Yesu panali mneneri wina wamkazi dzina lake Anna yemwe mwamuna wake anamwalira atangokhala m’banja zaka 7 zokha. Baibulo silisonyeza kuti iye anali ndi ana. Koma pa Luka 2:37 timawerenga kuti Anna ali ndi zaka 84 “sanali kusowa pakachisi. Anali kuchita utumiki wopatulika usana ndi usiku, anali kusala kudya ndi kupereka mapembedzero.” Anna ankalimbikitsidwa kwambiri komanso ankasangalala akamatumikira Yehova.

13. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti anzathu apamtima angatilimbikitse pa nthawi imene achibale sakutilimbikitsa.

13 Tikamasonkhana komanso kucheza ndi abale ndi alongo, timapeza anzathu apamtima. (Miy. 18:24) Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Paula ananena kuti mayi ake anasiya kutumikira Yehova iye ali ndi zaka 5 zokha. Iye anadandaula kwambiri ndipo zinali zovuta kuti apirire. Koma analimbikitsidwa kwambiri ataona kuti mlongo wina dzina lake Ann, yemwe anali mpainiya, anayamba kumuthandiza kuti azitumikira bwinobwino Yehova. Paula anati: “Ann sanali wachibale wanga koma ankandisonyeza chikondi ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndisafooke.” Paula akutumikirabe Yehova ndipo akusangalala kwambiri kuti mayi ake anabwereranso m’gulu la Yehova. Nayenso Ann amasangalala kwambiri chifukwa anathandiza Paula ngati mwana wake weniweni.

14. Kodi anthu amene amalimbikitsa anzawo amadalitsidwa bwanji?

14 Chochititsa chidwi n’chakuti tikamathandiza ena timaiwala mavuto athu komanso timasiya kudandaula. Alongo onse, kaya ali pa banja kapena ayi, akhoza kukhala osangalala akakhala antchito anzake a Mulungu n’kumalalikira uthenga wabwino. Cholinga chawo chimakhala kulemekeza Mulungu n’kumachita zimene amafuna. Ena amafika poona kuti kulalikira kuli ngati mankhwala awo. Tonsefe tingathandize kuti mpingo ukhale wogwirizana ngati timaganizira abale ndi alongo athu komanso anthu a m’gawo lathu. (Afil. 2:4) Mtumwi Paulo ndi chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye ankasamalira Akhristu a ku Tesalonika ngati mmene “mayi woyamwitsa” amachitira posamalira mwana wake. Iye analinso ngati bambo wawo.​—Werengani 1 Atesalonika 2:7, 11, 12.

KULIMBIKITSA MABANJA

15. Kodi Malemba amati udindo wophunzitsa ana Baibulo ndi wa ndani?

15 Mabanja ambiri amafunika kulimbikitsidwa komanso kuthandizidwa. Mwachitsanzo, anthu amene angolowa kumene m’gulu la Yehova angapemphe Akhristu ena kuti aziphunzitsa ana awo Baibulo. Malemba amanena kuti udindo wophunzitsa ana ndi wa makolo. (Miy. 23:22; Aef. 6:1-4) Koma makolo ena amafunika kuthandizidwa pa nkhani imeneyi. Ngakhale zili choncho, udindo wophunzitsawo umakhalabe wa makolowo. Choncho makolo angachite bwino kumalankhulana ndi ana awo komanso kuwathandiza.

16. Kodi tiyenera kukumbukira mfundo ziti pophunzitsa ana a anthu ena?

16 Munthu akapemphedwa ndi makolo ena kuti aziphunzira ndi ana awo, sayenera kuchita zinthu ngati watenga udindo wa makolowo. Nthawi zina, Mkhristu angapemphedwe kuti aziphunzira ndi ana amene makolo awo si Mboni. Akhristu oterewa ayenera kukumbukira kuti udindo wawo ndi wophunzitsa Baibulo osati kukhala makolo a anawo. Ndipo ndi nzeru kuphunzira ndi anawo kunyumba kwawo pali makolo awo kapena Mkhristu wina wodalirika, apo ayi angaphunzire nawo pamalo ena oonekera. Zimenezi zingathandize kuti anthu ena asamawakayikire. Komabe zingakhale bwino ngati patapita nthawi, makolo angayambe kukwaniritsa okha udindo wawo wophunzitsa ana.

17. Kodi ana angalimbikitse bwanji mabanja?

17 Ana akaphunzitsidwa bwino n’kuyamba kukonda Yehova komanso kutsatira malangizo ake, amalimbikitsa anthu a m’banja lawo. Iwo amalemekeza makolo awo komanso kuwathandiza m’njira zina. Amawathandizanso pa nkhani zokhudza kulambira. Mwachitsanzo, Chigumula chisanafike, Lameki ankalambira Yehova ndipo anafotokoza za Nowa, yemwe anali mwana wake, kuti: “Uyu ndi amene adzatibweretsere mpumulo ku ntchito yathu yopweteketsa manja, chifukwa cholima nthaka imene Yehova anaitemberera.” Ulosi umenewu unakwaniritsidwa pamene Mulungu anachotsa temberero limeneli. (Gen. 5:29; 8:21) Masiku anonso, ana amene amalambira Yehova amalimbikitsa mabanja awo ndipo amawathandiza kuti apirire mavuto. Amawathandizanso kuti adzapulumuke pa chisautso chachikulu chimene chidzakhale choposa Chigumula.

18. N’chiyani chingatithandize kukhala olimba mtima komanso kupirira vuto lililonse limene tingakumane nalo?

18 Panopa, anthu ambiri akutha kupirira mavuto awo chifukwa choti amakonda kupemphera, kuganizira zitsanzo za m’Baibulo komanso kugwirizana ndi abale ndi alongo. (Werengani Salimo 145:18, 19.) Kudziwa kuti Yehova amatitonthoza m’masautso athu onse kungatithandize kuti tipirire vuto lililonse limene tingakumane nalo panopa kapena m’tsogolo.