Tizitumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu

Tizitumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu

“Yehova, chonde kumbukirani kuti ndinayenda pamaso panu mokhulupirika ndiponso ndi mtima wathunthu.”​—2 MAF. 20:3.

NYIMBO: 52, 65

1-3. Kodi kutumikira Yehova ndi “mtima wathunthu” kumatanthauza chiyani? Perekani chitsanzo.

 POPEZA anthufe si ife angwiro, timalakwitsa zambiri. Koma tikuthokoza Yehova chifukwa anatipatsa dipo ndipo ndi wokonzeka kutikhululukira. Choncho tikadzichepetsa n’kulapa, tingathe kumupempha kuti atikhululukire. Timayamikira kuti iye ‘satichitira mogwirizana ndi machimo athu.’ (Sal. 103:10) Komabe, mogwirizana ndi zimene Davide anauza Solomo, tiyenera kutumikira Yehova “ndi mtima wathunthu.” (1 Mbiri 28:9) Zimenezi n’zofunika kuti Yehova azisangalala ndi zimene timachita pomulambira. Koma kodi anthu ochimwafe tingachite bwanji zimenezi?

2 Kuti tiyankhe funsoli tiyeni tiyerekezere zimene mafumu awiri a Yuda anachita. Mafumu ake ndi Asa ndi Amaziya. Mafumu awiri onsewa anachita zoyenera pamaso pa Yehova koma Asa anali ndi mtima wathunthu. (2 Mbiri 15:16, 17; 25:1, 2; Miy. 17:3) Mafumu onsewa anali ochimwa ndipo ankalakwitsa zinthu zina. Komabe Asa anali wodzipereka kwa Mulungu “ndi mtima wathunthu” ndipo sanasiye kutsatira malamulo ake. (1 Mbiri 28:9) Koma Amaziya sankatumikira Yehova ndi mtima wonse. Iye atagonjetsa adani a Mulungu anatenga milungu yawo n’kuyamba kuilambira.​—2 Mbiri 25:11-16.

3 Munthu amene amatumikira Yehova ndi “mtima wathunthu” amakonda kwambiri Yehova ndipo amafuna kumulambira mpaka kalekale. M’Baibulo mawu akuti “mtima” nthawi zambiri amanena za munthu wamkati. Amanena za mmene munthu amaganizira, zimene amakonda, zimene amafuna kuchita pa moyo wake komanso zolinga zake pochita zinthu. Munthu amene ali ndi mtima wathunthu satumikira Mulungu mwachinyengo kapena mwamwambo chabe. Choncho ngakhale kuti si ife angwiro, ngati tili odzipereka kwambiri komanso timapewa chinyengo, tingathe kumatumikira Mulungu ndi mtima wathunthu.​—2 Mbiri 19:9.

4. Kodi tsopano tikambirana chiyani?

4 Kuti timvetse bwino zimene kutumikira Mulungu ndi mtima wathunthu kumatanthauza, tiyeni tikambirane bwinobwino za​ Mfumu Asa, Yehosafati, Hezekiya ndi Yosiya. Mafumu 4 onsewa anatumikira Mulungu modzipereka kwambiri. Onsewa analakwitsapo zinthu zina komabe Yehova ankasangalala nawo. N’chifukwa chiyani Mulungu ankawaona kuti anamutumikira ndi mtima wathunthu? Nanga tingawatsanzire bwanji?

“ASA ANATUMIKIRA YEHOVA NDI MTIMA WATHUNTHU”

5. Kodi Asa anachita zinthu ziti?

5 Asa anali mfumu yachitatu kulamulira ku Yuda pambuyo poti mafuko 10 apanga ufumu wawo. Iye anachotsa mafano komanso mahule aamuna a pakachisi. Anachotsanso agogo ake aakazi pa udindo wawo wokhala “mayi wa mfumu, chifukwa anapanga fano lonyansa kwambiri.” (1 Maf. 15:11-13) Komanso Asa analimbikitsa anthu ake kuti “afunefune Yehova . . . ndi kutsatira chilamulo.” Zonsezi zikusonyeza kuti iye anayesetsa kuthandiza anthu kuti azilambira Yehova.​—2 Mbiri 14:4.

6. Kodi Asa anatani Aitiyopiya ataukira Yuda?

6 Yehova anadalitsa Yuda ndipo kwa zaka 10 zoyambirira za ulamuliro wa Asa, m’dzikolo munali mtendere. Kenako Zera wa ku Itiyopiya anabwera ndi gulu lake la asilikali okwana 1 miliyoni ndi magaleta 300 kuti adzamenyane ndi Yuda. (2 Mbiri 14:1, 6, 9, 10) Ndiye kodi Asa anatani? Iye anadalira kwambiri Yehova. (Werengani 2 Mbiri 14:11.) Mulungu anayankha pemphero la Asa lochokera pansi pa mtima, ndipo anamuthandiza kuti apambane pa nkhondo yomenyana ndi asilikali a ku Itiyopiya. (2 Mbiri 14:12, 13) Nthawi zina Yehova ankathandizanso mafumu osakhulupirika kuti apambane polimbana ndi adani awo ndipo ankachita izi chifukwa cha dzina lake. (1 Maf. 20:13, 26-30) Popeza Asa anadalira Yehova, iye anayankha pemphero lake. N’zoona kuti pa nthawi ina Asa anachita zinthu mopanda nzeru. Iye anadalira mfumu ya Siriya m’malo modalira Yehova. (1 Maf. 15:16-22) Komabe Mulungu anaona kuti Asa ankamutumikira ndi “mtima wathunthu masiku ake onse.” Ndiye kodi tingatengere bwanji chitsanzo cha Asa?​—1 Maf. 15:14.

7, 8. Kodi mungatsanzire bwanji Asa?

7 Tonsefe tiyenera kufufuza mtima wathu kuti tione ngati timatumikira Mulungu modzipereka kwambiri. Tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndimafunitsitsa kusangalatsa Yehova, kuteteza mpingo kuti ukhalebe woyera komanso kuteteza anthu a Mulungu ku zinthu zoipa?’ Asa anafunikatu kukhala wolimba mtima kuti achotse a Maaka pa udindo wokhala “mayi wa mfumu.” Nthawi zina inunso mungafunike kukhala olimba mtima ngati Asa. Mwachitsanzo, kodi mumatani ngati wachibale kapena mnzanu wapamtima wachita tchimo koma sanalape ndipo wachotsedwa mumpingo? Kodi mungalimbe mtima n’kusiya kuchita naye zinthu? Kodi mtima wanu umakulimbikitsani kutsatira malangizo a Mulungu?

8 Mofanana ndi Asa tingasonyezenso kuti timatumikira Mulungu ndi mtima wathunthu ngati timamudalira anthu ena akamatitsutsa. Mwina anzanu akusukulu angamakunyozeni chifukwa choti ndinu wa Mboni za Yehova. Kapena anzanu akuntchito angamaone kuti simuganiza bwino mukamapempha tchuthi kuti mukakhale nawo pamsonkhano kapena mukamakana kugwira ovataimu. Zikatere, muzipemphera kwa Mulungu ngati mmene Asa anachitira, muzimudalira komanso muziyesetsa kuchita zomwe mukudziwa kuti n’zoyenera. Muzikumbukira kuti Mulungu anathandiza Asa ndipo angakuthandizeninso inuyo.

9. Kodi Yehova amasangalala tikamachita chiyani?

9 Koma sikuti atumiki a Mulungu amangoganizira za iwowo. Paja Asa analimbikitsa anthu kuti azilambira Yehova. Ifenso tingathandize ena kuti “afunefune Yehova.” Yehova amasangalala tikamauza ena za iye chifukwa chomukonda komanso chifukwa chofuna kuti enawo adzapeze moyo wosatha.

YEHOSAFATI ANAFUNAFUNA YEHOVA

10, 11. Kodi tingatsanzire bwanji Yehosafati?

10 Yehosafati “anapitiriza kuyenda m’njira za Asa bambo ake.” (2 Mbiri 20:31, 32) Kodi anachita bwanji zimenezi? Iye analimbikitsa anthu kuti afunefune Yehova. Anayambitsa ntchito yapadera yophunzitsa anthu “pogwiritsira ntchito buku la chilamulo cha Yehova.” (2 Mbiri 17:7-10) Yehosafati anafika mpaka kudera la Efuraimu lomwe linali mu ufumu wa kumpoto wa Isiraeli ndipo anathandiza anthu kuti abwerere kwa Yehova. (2 Mbiri 19:4) Baibulo limati Mfumu Yehosafati “anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.”—2 Mbiri 22:9.

11 Ifenso tikhoza kuthandiza kwambiri pa ntchito yophunzitsa anthu imene Yehova akufuna kuti izigwiridwa masiku ano. Kodi inuyo mumafunitsitsa kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu mwezi uliwonse n’cholinga choti ayambe kutumikira Yehova? Ngati titachita khama, Yehova angatithandize kuti tiyambe kuphunzira Baibulo ndi munthu. Kodi mumapempha Yehova kuti akuthandizeni pa nkhaniyi? Nanga mumayesetsa kuphunzira ndi anthu ngakhale pa nthawi imene mukanafuna kupuma? Paja Yehosafati anakathandiza anthu a ku Efuraimu kuti abwerere kwa Yehova. Nafenso tingachite bwino kuthandiza anthu amene anafooka kuti ayambirenso kutumikira Mulungu. Nawonso akulu ayenera kuyendera anthu a m’gawo la mpingo wawo amene anachotsedwa, koma asintha.

12, 13. (a) Kodi Yehosafati anatani pa nthawi imene adani oopsa anabwera? (b) Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yehosafati?

12 Mofanana ndi bambo ake, Yehosafati anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu pa nthawi imene adani oopsa anabwera. (Werengani 2 Mbiri 20:2-4.) N’zoona kuti Yehosafati anachita mantha. Koma “anatsimikiza mumtima mwake kuti afunefune Yehova.” Iye anapemphera modzichepetsa n’kunena kuti anthu ake alibe “mphamvu zotha kulimbana ndi khamu lalikulu.” Ananenanso kuti iye ndi anthu akewo sankadziwa zochita. Posonyeza kuti ankadalira Yehova, Yehosafati anati: “Maso athu ali pa inu.”​—2 Mbiri 20:12.

13 Nthawi zina ifenso tikhoza kuchita mantha mpaka kufika posowa zochita. (2 Akor. 4:8, 9) Koma mfundo yoyenera kuikumbukira ndi yoti Yehosafati anapemphera pagulu n’kufotokoza mmene zinthu zinalili. (2 Mbiri 20:5) Amunanso ayenera kutsanzira Yehosafati n’kumapempha Yehova kuti awapatse nzeru komanso mphamvu zowathandiza pa vuto limene akumana nalo. Mukamapemphera ndi banja lanu musamachite manyazi kutchula mavuto amene akukudetsani nkhawa. Mukamatero iwo amadziwa kuti mumadalira Yehova. Kumbukirani kuti Yehova anathandiza Yehosafati choncho akhoza kukuthandizaninso inuyo.

HEZEKIYA ANAPITIRIZA KUCHITA ZOYENERA

14, 15. Kodi Hezekiya anasonyeza bwanji kuti ankadalira Yehova?

14 Mfumu ina yokhulupirika inali Hezekiya. Iye “anapitiriza kumamatira Yehova.” Hezekiya anachita zimenezi ngakhale kuti bambo ake ankalambira mafano. Koma Hezekiya “anachotsa malo okwezeka, kugwetsa zipilala zopatulika, ndi kudula mzati wopatulika. Iye anaphwanyaphwanya njoka yamkuwa imene Mose anapanga” chifukwa pa nthawiyo anthu ankaigwiritsa ntchito polambira mafano. Hezekiya anali wodzipereka kwambiri ndipo “anapitiriza kusunga malamulo amene Yehova analamula Mose.”​—2 Maf. 18:1-6.

15 Komanso pamene Asuri, omwe anali ulamuliro wamphamvu pa nthawiyo anaukira Yerusalemu, Hezekiya anadalira Yehova ndi mtima wonse. Mfumu ya Asuri dzina lake Senakeribu inanyoza Yehova komanso inauza Hezekiya kuti angonena kuti wagonja. Koma Hezekiya anapemphera kwa Yehova ndipo sankakayikira kuti iye ali ndi mphamvu zowapulumutsa. (Werengani Yesaya 37:15-20.) Mulungu anayankha pemphero la Hezekiya ndipo anatumiza mngelo amene anapha Asuri okwana 185,000.​—Yes. 37:36, 37.

16, 17. Kodi tingatsanzire bwanji Hezekiya?

16 Kenako Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa. Iye anachonderera Yehova kuti akumbukire zoti anali munthu wokhulupirika. (Werengani 2 Mafumu 20:1-3.) Tikudziwa kuti panopa sitingayembekezere Yehova kutichiritsa mozizwitsa kapena kutalikitsa moyo wathu. Komabe mofanana ndi Hezekiya tingathe kupemphera kwa Yehova kuti: “Kumbukirani kuti ndinayenda pamaso panu mokhulupirika ndiponso ndi mtima wathunthu.” Kodi inuyo mumakhulupirira kuti Yehova angathe kukuthandizani pamene mukudwala?​—Sal. 41:3.

17 Mukaganizira chitsanzo cha Hezekiya, kodi mukuona kuti pali chilichonse chimene chikusokoneza ubwenzi wanu ndi Mulungu? Nanga pali zimene zikukulepheretsani kuti muzimulambira mokhulupirika? Mwachitsanzo, ambiri m’dzikoli amachita zinthu ngati amalambira anthu. Amagomera anthu otchuka komanso ena amene sawadziwa n’komwe. Ena amatha nthawi yambiri pamalo ochezera pa intaneti n’kumawerenga za anthu amenewo, kuona zithunzi zawo komanso kulemberana nawo mameseji. N’zoona kuti tingagwiritse ntchito intaneti polumikizana ndi achibale komanso anzathu. Koma kupanda kusamala tikhoza kumawononga nthawi yambiri pa zinthu ngati zimenezi. Vuto linanso ndi loti tingayambe kunyada ngati anthu ambiri asonyeza kuti akukonda zithunzi kapena zinthu zina zimene taika. Apo ayi tikaona kuti sakulembanso zosonyeza kuti aona zimene taika, tingakhumudwe. Akhristufe tiyenera kutsanzira mtumwi Paulo komanso Akula ndi Purisikila. Kodi mukuganiza kuti iwo ankatha nthawi yawo yambiri akufufuza zimene anthu ena akuchita mwinanso, za anthu oti sanali Akhristu n’komwe? Baibulo limati Paulo ‘ankatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira mawu a Mulungu.’ Ndipo Akula ndi Purisikila ankatha nthawi yambiri akulalikira komanso kufotokozera ena “njira ya Mulungu molondola.” (Mac. 18:4, 5, 26) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimapewa kulambira anthu? Nanga ndimapewa kuwononga nthawi yambiri pa zinthu zosafunika kwenikweni?’​—Werengani Aefeso 5:15, 16.

YOSIYA ANKAMVERA MALAMULO A YEHOVA

18, 19. Kodi mukufuna kutsanzira Yosiya pa zinthu ziti?

18 Yosiya anali mwana wa mdzukulu wake wa Hezekiya ndipo anatsimikiza kuti azimvera malamulo a Mulungu “ndi mtima wake wonse.” (2 Mbiri 34:31) Yosiya “anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide” asanakwanitse n’komwe zaka 20. Ndipo pamene anali ndi zaka 20 anayamba ntchito yochotsa mafano onse mu Yuda. (Werengani 2 Mbiri 34:1-3.) Yosiya ankadzipereka kwambiri pa zinthu zosangalatsa Mulungu kuposa mafumu ambiri a Yuda. Pa nthawi ina mkulu wa ansembe anapeza buku la Chilamulo cha Mose m’kachisi ndipo mlembi anawerengera Yosiya zimene zinali m’Chilamulocho. Yosiya anazindikira kuti panali zinthu zambiri zomwe ankafunika kuchita. Analimbikitsanso anthu ake kuti achite chimodzimodzi. Zotsatira zake zinali zakuti pa nthawi yonse ya ulamuliro wa Yosiya, anthu “sanasiye kutsatira Yehova.”​—2 Mbiri 34:27, 33.

19 Achinyamata angatsanzire Yosiya n’kuyamba kutumikira Yehova adakali aang’ono. N’kutheka kuti Mfumu Manase italapa inaphunzitsa Yosiya za chifundo cha Yehova. Achinyamatanu, muzigwirizana ndi anthu achikulire a m’banja lanu kapena mumpingo ndipo mungaphunzire zambiri pa zimene Yehova wawachitira. Musaiwalenso kuti Yosiya anakhudzidwa mtima kwambiri atamva mawu a m’Chilamulo ndipo anachitapo kanthu. Inunso mukamawerenga Mawu a Mulungu mungakhale osangalala komanso mungalimbitse ubwenzi wanu ndi iye. Zingakulimbikitseninso kuthandiza ena kuti nawonso ayambe kutumikira Yehova. (Werengani 2 Mbiri 34:18, 19.) Kuphunzira Baibulo panokha kungakuthandizeni kuti muone ngati pali zinthu zina zofunika kusintha kuti muzitumikira bwino Mulungu. Ndipo mukaona kuti zilipodi, muyenera kusintha ngati mmene anachitira Yosiya.

TIZITUMIKIRA YEHOVA NDI MTIMA WATHUNTHU

20, 21. (a) Kodi mafumu 4 amene takambirana m’nkhaniyi ankafanana pa zinthu ziti? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

20 Kodi taphunzira chiyani kuchokera kwa mafumu 4 a Yuda omwe anatumikira Yehova ndi mtima wathunthu? Mafumu onsewa ankafunitsitsa kusangalatsa Yehova komanso kumulambira kwa moyo wawo onse. Iwo anadalira Yehova pamene adani amphamvu anabwera kudzalimbana nawo. Koma chofunika kwambiri n’chakuti ankatumikira Yehova chifukwa chomukonda.

21 Monga tidzaonere m’nkhani yotsatira, mafumu 4 onsewa analakwitsapo zinthu zina. Koma popeza Mulungu amafufuza mitima, anaona kuti anthuwa ankamutumikira ndi mtima wathunthu. Ifenso timalakwitsa zinthu zina. Ndiye kodi Yehova akamafufuza mtima wathu amaona kuti timamutumikira ndi mtima wathunthu? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.