NKHANI YOPHUNZIRA 11

Kodi Ndinu Okonzeka Kubatizidwa?

Kodi Ndinu Okonzeka Kubatizidwa?

“Chofanana ndi chingalawacho chikupulumutsanso inuyo tsopano. Chimenechi ndicho ubatizo.”​1 PET. 3:21.

NYIMBO NA. 28 Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi munthu amafunika kuchita chiyani asanayambe kumanga nyumba?

TIYEREKEZE kuti munthu wina akufuna kumanga nyumba. Akudziwa mtundu wa nyumba imene akufuna kumanga. Kodi angachite bwino kungopita kukagula zipangizo n’kuyamba kumanga? Ayi. Asanayambe angafunike kuwerengera mtengo wake. Zimenezi zingamuthandize kudziwa ngati ali ndi ndalama zokwanira kuimaliza nyumbayo. Ngati atawerengetsa bwino zingakhale zosavuta kuti aimalize.

2. Malinga ndi Luka 14:27-30, kodi munthu ayenera kuganizira chiyani asanabatizidwe?

2 Mwina panopa mukuganiza zobatizidwa chifukwa choti mumakonda kwambiri Yehova komanso kuyamikira zimene wakuchitirani. Ngati ndi choncho, ndiye kuti muli ngati munthu amene akufuna kumanga nyumba. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani mawu a Yesu a pa Luka 14:27-30. (Werengani.) Yesu ananena zimenezi pofotokoza zimene wophunzira wake ayenera kuchita. Iye anati munthu amene akufuna kumutsatira ayenera kuwerengera mtengo wake kapena kuti kudziwa mavuto amene angakumane nawo komanso zinthu zimene ayenera kulolera kuzisiya. (Luka 9:23-26; 12:51-53) Choncho musanabatizidwe muyenera kumvetsa zonse zimene zimafunika. Mukatero mudzakhala okonzeka kuti mupitirize kutumikira Yehova pambuyo poti mwabatizidwa.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 N’chifukwa chiyani tinganene kuti kubatizidwa n’kukhala wophunzira wa Khristu n’kofunika kwambiri ngakhale kuti munthu amakumana ndi mavuto? Munthu akabatizidwa amakhala ngati watsegula khomo loti alandire madalitso panopa komanso m’tsogolo. Tiyeni tsopano tikambirane mafunso ena ofunika okhudza ubatizo. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kudziwa ngati mwakonzekeradi kubatizidwa.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA PA NKHANI YA KUDZIPEREKA KWA YEHOVA NDI UBATIZO

4. (a) Kodi kudzipereka n’kutani? (b) Kodi mawu akuti ‘kudzikana’ opezeka pa Mateyu 16:24 amatanthauza chiyani?

4 Kodi kudzipereka n’kutani? Munthu asanabatizidwe amafunika kudzipereka. Pochita zimenezi, munthu amapemphera kwa Yehova kuchokera mumtima n’kumuuza kuti akupereka moyo wake kuti azimutumikira mpaka kalekale. Munthu akadzipereka kwa Mulungu zimatanthauza kuti ‘wadzikana yekha.’ (Werengani Mateyu 16:24.) Izi zikutanthauza kuti munthuyo tsopano ndi wa Yehova ndipo umenewu ndi mwayi waukulu kwambiri. (Aroma 14:8) Munthu amauza Yehova kuti chofunika kwambiri pa moyo wake chidzakhala kumutumikira osati kudzisangalatsa. Choncho tingati kudzipereka ndi lumbiro lofunika kwambiri limene timalonjeza kwa Mulungu. Yehova satikakamiza kuti tilonjeze zimenezi. Koma tikalonjeza amafuna kuti tikwaniritse zimene tanenazo.​—Sal. 116:12, 14.

5. Kodi kudzipereka kumasiyana bwanji ndi kubatizidwa?

5 Kodi kudzipereka kumasiyana bwanji ndi kubatizidwa? Kudzipereka kumachitika munthu ali kwayekha ndipo ndi nkhani ya pakati pa munthuyo ndi Yehova. Koma kubatizidwa kumachitika pamaso pa anthu ambiri, makamaka pamsonkhano wadera kapena wachigawo. Munthu akamabatizidwa amasonyeza anthu ena kuti anadzipereka kale kwa Yehova. * Choncho ubatizo umasonyeza kuti munthu amakonda Yehova ndi mtima wake wonse, moyo wake wonse, maganizo ake onse ndi mphamvu zake zonse ndipo akufuna kumutumikira mpaka kalekale.​—Maliko 12:30.

6-7. Malinga ndi 1 Petulo 3:18-22, kodi ubatizo ndi wofunika pa zifukwa ziwiri ziti?

6 Kodi kubatizidwa n’kofunikadi? Taganizirani mawu a pa 1 Petulo 3:18-22. (Werengani.) Chingalawa chinkasonyeza kuti Nowa amakhulupirira Mulungu. Nawonso ubatizo umasonyeza kuti munadzipereka kwa Mulungu. Koma kodi kubatizidwa n’kofunikadi? Inde. Petulo anafotokoza chifukwa chake. Choyamba, ananena kuti: “Chofanana ndi chingalawacho chikupulumutsanso inuyo.” Ubatizo umatipulumutsa ngati tasonyeza kuti timakhulupirira Yesu, komanso zoti anatifera kenako n’kuukitsidwa kupita kumwamba ndipo panopa ali “kudzanja lamanja la Mulungu.”

7 Chachiwiri, ubatizo umatithandiza kuti tikhale ndi “chikumbumtima chabwino.” Tikadzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa, timakhala naye pa ubwenzi wapadera. Ndipo tikalapa machimo athu ndiponso kukhulupirira nsembe ya Yesu, Mulungu amatikhululukira. Izi zimathandiza kuti tikhale ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu.

8. Kodi chifukwa chachikulu chokuchititsani kuti mubatizidwe chiyenera kukhala chiyani?

8 Kodi chifukwa chachikulu chokuchititsani kubatizidwa n’chiyani? Pophunzira Baibulo mwadziwa zinthu zambiri zokhudza Yehova, makhalidwe ake komanso mmene amachitira zinthu. Zimene mwaphunzira zimakusangalatsani ndipo zachititsa kuti muzimukonda kwambiri. Choncho kukonda Yehova kuyenera kukhala chifukwa chachikulu chokuchititsani kuti mubatizidwe.

9. Malinga ndi Mateyu 28:19, 20, kodi kubatizidwa m’dzina la Atate, la Mwana ndi la mzimu woyera kumatanthauza chiyani?

9 Chifukwa china chokuchititsani kuti mubatizidwe ndi mfundo za m’Baibulo zimene mwaphunzira ndipo mumazikhulupirira. Kumbukirani zimene Yesu ananena polamula anthu kuti azigwira ntchito yophunzitsa anthu. (Werengani Mateyu 28:19, 20.) Yesu ananena kuti munthu ayenera kubatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.” Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani? Munthu ayenera kukhulupirira ndi mtima wonse mfundo za m’Baibulo zokhudza Yehova, Yesu komanso mzimu woyera. Mfundo zimenezi ndi zamphamvu kwambiri moti zikhoza kukufikani pamtima. (Aheb. 4:12) Tiyeni tsopano tikambirane zina mwa mfundo zimenezi.

10-11. Kodi ndi mfundo ziti zokhudza Atate zimene mwaphunzira komanso kuzikhulupirira?

10 Mutayamba kuphunzira munadziwa zambiri zokhudza Atate wathu. Mwachitsanzo, munadziwa kuti ‘dzina lake ndi Yehova,’ ‘ndi Wam’mwambamwamba’ komanso iye yekha ndi “Mulungu woona.” (Sal. 83:18; Yes. 37:16) Iye ndi amene anatilenga ndipo “chipulumutso chimachokera kwa Yehova.” (Sal. 3:8; 36:9) Yehova wakonza njira yothandiza kuti tipulumutsidwe ku uchimo ndi imfa ndipo watipatsa chiyembekezo cha moyo wosatha. (Yoh. 17:3) Mukabatizidwa mudzayamba kudziwika kuti ndinu wa Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12) Mudzakhala m’gulu la anthu amene amalambira Mulungu woona, amasangalala kudziwika ndi dzina lake ndipo amauza ena za dzinalo.​—Sal. 86:12.

11 Ndi mwayi waukulu kudziwa zimene Baibulo limanena zokhudza Atate wathu. Munthu akakhulupirira mfundo zimenezi amafunitsitsa kudzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa.

12-13. Kodi ndi mfundo ziti zokhudza Mwana zimene munaphunzira komanso kuzikhulupirira?

12 Kodi munamva bwanji mutaphunzira mfundo zotsatirazi zokhudza Mwana? Yesu ndi wachiwiri kwa Wolamulira wa chilengedwe chonsechi. Iye anapereka moyo wake kuti ukhale dipo lotiwombola ndipo anachita zimenezi ndi mtima wonse. Kukhulupirira dipo kungathandize kuti machimo athu akhululukidwe, tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu komanso tidzapeze moyo wosatha. (Yoh. 3:16) Yesu ndi Mkulu wa Ansembe wathu. Iye amafuna kutithandiza kuti tipeze madalitso chifukwa cha dipo komanso tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. (Aheb. 4:15; 7:24, 25) Iye ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo Yehova adzamugwiritsa ntchito kuti ayeretse dzina lake, athetse zoipa zonse komanso abweretse madalitso osatha padzikoli. (Mat. 6:9, 10; Chiv. 11:15) Yesu ndi chitsanzo chathunso. (1 Pet. 2:21) Iye anapereka chitsanzo chabwino podzipereka ndi mtima wonse kuti achite chifuniro cha Mulungu.​—Yoh. 4:34.

13 Munthu akakhulupirira zimene Baibulo limanena zokhudza Mwana wa Mulungu amayamba kumukonda kwambiri. Ndiye chikondi chimenechi n’chimene chingakulimbikitseni kuti muzichita chifuniro cha Mulungu pa moyo wanu ngati mmene Yesu anachitira. Izi zingakulimbikitseni kuti mudzipereke kwa Yehova ndiponso kubatizidwa.

14-15. Kodi ndi mfundo ziti zokhudza mzimu woyera zimene munaphunzira komanso kuzikhulupirira?

14 Kodi munamva bwanji mutaphunzira mfundo zotsatirazi zokhudza mzimu woyera? Mzimuwu si munthu koma mphamvu ya Mulungu. Yehova anagwiritsa ntchito mzimuwu pothandiza anthu amene analemba Baibulo ndipo mzimu womwewo ndi umene umatithandiza kuti tizimvetsa mfundo za m’Baibulozo n’kumazitsatira. (Yoh. 14:26; 2 Pet. 1:21) Yehova amagwiritsanso ntchito mzimu woyera kuti atipatse “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akor. 4:7) Mzimuwu umatipatsa mphamvu kuti tizilalikira uthenga wabwino, tisagonje poyesedwa, tizipirira tikakhumudwitsidwa komanso tizipirira mavuto. Umatithandizanso kuti tizikhala ndi makhalidwe abwino amene ‘mzimu woyerawo umatulutsa.’ (Agal. 5:22) Mulungu amapereka mzimu woyera kwa anthu amene amamukhulupirira komanso kupempha mzimuwo kuchokera mumtima.​—Luka 11:13.

15 N’zosangalatsa kuona kuti atumiki a Yehova amadalira mzimu wake kuti uziwathandiza kumutumikira bwinobwino. Munthu akaphunzira zoona zake pa nkhani ya mzimu woyera amafunitsitsa kudzipereka kwa Mulungu n’kubatizidwa.

16. Kodi pofika pano takambirana chiyani munkhaniyi?

16 Pofika pano, takambirana kuti kudzipereka kwa Mulungu komanso kubatizidwa ndi zinthu zofunika kwambiri. Takambirananso kuti munthu asanachite zimenezi ayenera kuganizira mavuto amene angakumane nawo komanso zinthu zimene ayenera kudzimana. Koma madalitso amene munthu amapeza amakhala ambiri kuposa zinthu zimene amalolera kuti asakhale nazo. Ubatizo ukhoza kukupulumutsani komanso kukuthandizani kuti mukhale ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu. Munthu ayenera kubatizidwa chifukwa chokonda Yehova. Muyeneranso kukhulupirira mfundo zoona zimene mwaphunzira zokhudza Atate, Mwana ndi mzimu woyera. Ndiye malinga ndi zimene takambirana pofika pano munkhaniyi, kodi inuyo ndinu wokonzeka kubatizidwa?

ZIMENE MUYENERA KUCHITA MUSANABATIZIDWE

17. Kodi munthu amafunika kuchita zinthu ziti asanabatizidwe?

17 Ngati mukufuna kubatizidwa, ndiye kuti mwachita kale zinthu zingapo zokuthandizani kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. * Mwachitsanzo, mwakhala mukuphunzira Baibulo ndipo mukudziwa zambiri zokhudza Yehova ndi Yesu. Panopa muli ndi chikhulupiriro. (Aheb. 11:6) Mumakhulupirira ndi mtima wonse malonjezo a Yehova amene ali m’Baibulo ndipo simukayikira kuti mukamakhulupirira nsembe ya Yesu mukhoza kupulumutsidwa ku uchimo ndi imfa. Munalapa machimo anu ndipo mumamva chisoni ndi zimene munkalakwitsa moti munapempha Yehova kuti akukhululukireni. Panopa munatembenuka, kutanthauza kuti munasiya zoipa zonse n’kuyamba moyo wosangalatsa Mulungu. (Mac. 3:19) Mumafunitsitsa kuuza anthu ena zimene mumakhulupirira. Munayenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa ndipo munayamba kulalikira limodzi ndi mpingo. (Mat. 24:14) Yehova amayamikira kwambiri kuona mutachita zonsezi ndipo dziwani kuti zimene mwachitazi zimakondweretsa mtima wake.​—Miy. 27:11.

18. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene muyenera kuchita musanabatizidwe?

18 Koma pali zinthu zinanso zimene muyenera kuchita musanabatizidwe. Paja takambirana kuti muyenera kudzipereka kwa Mulungu. Mungachite zimenezi popemphera kwa iye panokha n’kumulonjeza kuti muzimutumikira kwa moyo wanu wonse. (1 Pet. 4:2) Kenako muyenera kudziwitsa wogwirizanitsa ntchito za akulu kuti mukufuna kubatizidwa. Iye adzauza akulu ena kuti akambirane nanu. Simuyenera kuchita mantha kukambirana ndi akuluwo chifukwa amakudziwani bwino komanso amakukondani. Iwo adzakambirana nanu mfundo za m’Baibulo zoyambirira zimene mwaphunzira. Cholinga chawo ndi kutsimikizira kuti mukumvetsa mfundozo komanso mukudziwa kufunika kwa kudzipereka ndiponso kubatizidwa. Iwo akatsimikizira kuti ndinu okonzeka kubatizidwa, adzakudziwitsani kuti mudzabatizidwa pamsonkhano wadera kapena wachigawo wotsatira.

ZIMENE MUYENERA KUCHITA PAMBUYO POBATIZIDWA

19-20. Kodi ndi zinthu ziti zimene muyenera kuchita pambuyo pobatizidwa, nanga mungazichite bwanji?

19 Kodi ndi zinthu ziti zimene muyenera kuchita pambuyo pobatizidwa? * Muyenera kukumbukira kuti pamene munkadzipereka, munalumbira kwa Yehova ndipo iye amafuna kuti mukwaniritse zimene munalonjeza. Choncho mukabatizidwa muyenera kuchita zimene munalonjeza. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

20 Muyenera kugwirizana kwambiri ndi anthu mumpingo. Munthu akabatizidwa amakhala kuti walowa ‘m’gulu la abale.’ (1 Pet. 2:17) Choncho abale ndi alongo mumpingo ali ngati anthu a m’banja lanu. Mukamasonkhana nawo nthawi zonse, ubwenzi wanu umakhala wolimba. Muyenera kuwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse. (Sal. 1:1, 2) Mukamaliza kuwerenga, muzipeza nthawi yoganizira mozama zimene mwawerengazo. Mukatero, mfundo zake zikhoza kukufikani pamtima. Muyeneranso ‘kupemphera kosalekeza.’ (Mat. 26:41) Munthu akamapemphera kuchokera pansi pa mtima, ubwenzi wake ndi Yehova umalimba kwambiri. Komanso “pitirizani kufunafuna ufumu choyamba.” (Mat. 6:33) Mungachite zimenezi ngati mumaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri pa moyo wanu. Mukamalalikira nthawi zonse, chikhulupiriro chanu chimalimba ndipo mukhoza kuthandiza anthu ena kuti ayambe kuyenda panjira ya ku moyo wosatha.​—1 Tim. 4:16.

21. Kodi ndi madalitso ati amene mungapeze mukabatizidwa?

21 Kudzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu kuposa chilichonse. N’zoona kuti pali mavuto ena amene mungakumane nawo koma madalitso amene mungapeze ndi osaneneka. Mavuto amene mungakumane nawo m’dzikoli “ndi akanthawi ndipo ndi opepuka.” (2 Akor. 4:17) Koma mukabatizidwa mudzapeza madalitso panopa komanso “moyo weniweniwo” m’tsogolo. (1 Tim. 6:19) Choncho muyenera kupemphera komanso kuganizira mozama funso lakuti, ‘Kodi ndine wokonzeka kubatizidwa?’

NYIMBO NA. 50 Pemphero Langa Losonyeza Kudzipereka

^ ndime 5 Kodi inuyo mukufuna kubatizidwa? Ngati ndi choncho, nkhaniyi yakonzedwa kuti ikuthandizeni. Tikambirana mafunso ofunika kwambiri pa nkhani imeneyi. Zimene mungayankhe pa mafunsowo zingakuthandizeni kudziwa ngati mwakonzekadi kuti mubatizidwe.

^ ndime 19 Ngati simunamalize kuphunzira buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa ndiponso lakuti Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani? muyenera kupitiriza mpaka mumalize mabuku awiriwa.