NKHANI YOPHUNZIRA 10

Munthu Amabatizidwa Chifukwa Chokonda Yehova Komanso Kumuyamikira

Munthu Amabatizidwa Chifukwa Chokonda Yehova Komanso Kumuyamikira

“Chikundiletsa kubatizidwa n’chiyani?”​—MAC. 8:36.

NYIMBO NA. 37 Kutumikira Yehova ndi Moyo Wonse

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Malinga ndi Machitidwe 8:27-31, 35-38, kodi n’chiyani chinalimbikitsa nduna ya ku Itiyopiya kuti ibatizidwe?

KODI inuyo mukufuna kubatizidwa n’kukhala wophunzira wa Khristu? Anthu ambiri anachita zimenezi chifukwa choti amakonda kwambiri Yehova komanso kuyamikira zimene amawachitira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi munthu wina amene anali nduna ya mfumukazi ya ku Itiyopiya.

2 Munthuyu atangophunzira mfundo za m’Malemba anabatizidwa nthawi yomweyo. (Werengani Machitidwe 8:27-31, 35-38.) Kodi n’chifukwa chiyani anachita zimenezi? N’zosakayikitsa kuti ankakonda kwambiri Mawu a Mulungu chifukwa ankawerenga buku la Yesaya ali m’galeta lake. Ndipo atakambirana ndi Filipo, anayamikira kwambiri zimene Yesu anamuchitira. Koma kodi n’chifukwa chiyani munthu wa ku Itiyopiyayu anapita ku Yerusalemu? N’chifukwa chakuti anali atayamba kale kukonda Yehova. Tikutero chifukwa chakuti anapita ku Yerusalemuko kukalambira Yehova. Ayenera kuti anasiya chipembedzo chake n’kuyamba kugwirizana ndi mtundu umene unadzipereka kwa Mulungu woona. Kukonda Yehova n’kumene kunamuthandizanso kuti abatizidwe n’kukhala wophunzira wa Khristu.​—Mat. 28:19.

3. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingalepheretse munthu kubatizidwa? (Onani bokosi lakuti “ Kodi Mtima Wanu Ndi Wotani?”)

3 Kukonda Yehova kungakulimbikitseninso inuyo kuti mubatizidwe. Koma kukonda anthu ena kapena zinthu zina kukhoza kukulepheretsani kuti mubatizidwe. Mwachitsanzo, ngati mumakonda kwambiri achibale kapena anzanu mukhoza kulephera kubatizidwa poopa kuti iwo akhumudwa. (Mat. 10:37) Apo ayi, mukhoza kulephera chifukwa choti mumakonda zinthu zina zimene Mulungu amadana nazo ndipo simukufuna kuzisiya. (Sal. 97:10) Mwinanso munakulira m’banja limene munkachita miyambo yokhudza zipembedzo zonyenga. Ndipo mumakonda kwambiri zimene zimachitika pa miyamboyo. Choncho ngakhale kuti Yehova amadana nazo, zingakuvuteni kusiya miyamboyo. (1 Akor. 10:20, 21) Chofunika ndi kungosankha kuti, “Kodi ineyo ndikufuna kuti ndizikonda kwambiri ndani?”

KODI TIYENERA KUKONDA KWAMBIRI NDANI?

4. Kodi n’chiyani chingakulimbikitseni kuti mubatizidwe?

4 Pali zinthu zambiri zimene mumazikonda komanso kuziyamikira. Mwachitsanzo, mwina musanayambe kuphunzira ndi a Mboni za Yehova munkalemekeza kwambiri Baibulo. Ndipo mwina munkakonda Yesu. Popeza tsopano mwadziwana ndi a Mboni za Yehova, muyeneranso kuti mumaona kuti ndi anthu abwino kukhala nawo. Koma kukonda zinthu zimenezi sikungakulimbikitseni kuti mudzipereke kwa Yehova n’kubatizidwa. Kukonda Yehova n’kumene kungakulimbikitseni kuti mubatizidwe. Ngati mumakonda Yehova kuposa aliyense kapena chilichonse, palibe chimene chingakulepheretseni kumutumikira. Choncho kukonda Yehova n’kumene kungakulimbikitseni kuti mubatizidwe komanso musasiye kumutumikira mokhulupirika.

5. Kodi tikambirana mafunso ati?

5 Yesu ananena kuti tiyenera kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, maganizo athu onse komanso mphamvu zathu zonse. (Maliko 12:30) Kodi munthu angayambe bwanji kukonda kwambiri Yehova komanso kumuyamikira? Kuganizira mmene Yehova amatikondera n’kumene kungatilimbikitse kuti nafenso tizimukonda. (1 Yoh. 4:19) Kodi chimachitika n’chiyani munthu akayamba kukonda kwambiri Yehova? *

6. Malinga ndi Aroma 1:20, kodi njira imodzi imene tingadziwire za Yehova ndi iti?

6 Kuphunzira za Yehova poona chilengedwe. (Werengani Aroma 1:20; Chiv. 4:11) Mukhoza kuona nzeru za Yehova mukaganizira mmene anapangira zomera ndi nyama. Muziganizira njira yodabwitsa imene anapangira thupi lanu. (Sal. 139:14) Muziganiziranso mphamvu zimene Yehova anaika m’dzuwa lomwe ndi imodzi mwa nyenyezi mabiliyoni ambiri. * (Yes. 40:26) Mukatero mudzayamba kulemekeza kwambiri Yehova. Koma kungodziwa kuti Yehova ndi wanzeru komanso wamphamvu ndi chiyambi chabe choti akhale mnzanu. Muyenera kudziwa zambiri zokhudza iyeyo kuti mukhale naye pa ubwenzi wolimba.

7. Kodi muyenera kutsimikizira chiyani kuti muyambe kukonda kwambiri Yehova?

7 Muyenera kutsimikizira kuti Yehova amakukondani inuyo panokha. Kodi inuyo zimakuvutani kukhulupirira kuti amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi amakudziwani komanso kukukondani? Ngati ndi choncho, kumbukirani kuti Yehova “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Mac. 17:26-28) Iye amasanthula mitima yonse ndipo amalonjeza kuti ‘tikamufunafuna adzalola kuti timupeze.’ (1 Mbiri 28:9) Ndipo ngati panopa mukuphunzira Baibulo, umenewu ndi umboni wakuti Yehova wakukokani kuti mumuyandikire. (Yer. 31:3) Munthu akazindikira zinthu zambiri zimene Yehova wamuchitira m’pamene amayamba kumukonda kwambiri.

8. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira chikondi cha Yehova?

8 Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timayamikira chikondi cha Yehova ndi kupemphera kwa iye. Mumayamba kukonda kwambiri Mulungu ngati mumamuuza zinthu zonse zimene zikukudetsani nkhawa komanso kumuyamikira pa zonse zimene wakuchitirani. Ndipo ubwenzi wanu ndi iye udzalimba mukamaona akuyankha mapemphero anu. (Sal. 116:1) Mudzafika potsimikizira ndi mtima wonse kuti amakumvetsani. Koma kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ulimbe kwambiri muyenera kuzindikira zimene amakonda ndi zimene amadana nazo. Muyeneranso kudziwa zimene amafuna kuti muzichita. Ndipo kuti mudziwe zonsezi muyenera kuphunzira Baibulo.

Kuphunzira Baibulo n’kumene kungatithandize kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kudziwa zimene amafuna kuti tizichita (Onani ndime 9) *

9. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakonda Mawu a Mulungu?

9 Muzikonda kwambiri Mawu a Mulungu. Baibulo lokha ndi limene limanena zoona zokhudza Yehova komanso cholinga chake potilenga. Mungasonyeze kuti mumakonda Mawu a Mulungu mukamawawerenga tsiku lililonse, kukonzekera phunziro lanu la Baibulo komanso kutsatira zimene mukuphunzira. (Sal. 119:97, 99; Yoh. 17:17) Kodi inuyo muli ndi ndandanda yowerengera Baibulo? Kodi mumaitsatira n’kumawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku?

10. Kodi chinthu china chosangalatsa m’Baibulo n’chiyani?

10 Chinthu china chosangalatsa m’Baibulo n’chakuti muli nkhani za Yesu zofotokozedwa ndi anthu amene anamuona. Choncho m’Baibulo muli nkhani zofotokoza bwino zimene Yesu anakuchitirani. Mukamaphunzira zimene Yesu analankhula komanso kuchita, mtima wofuna kukhala naye pa ubwenzi udzakula kwambiri.

11. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzikonda kwambiri Yehova?

11 Mukamakonda Yesu mudzayambanso kukonda kwambiri Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yesu amatsanzira Atate wake ndendende. (Yoh. 14:9) Choncho mukadziwa bwino za Yesu mumadziwanso bwino Yehova n’kumamukonda kwambiri. Taganizirani mmene Yesu ankakondera anthu onyozeka monga osauka, odwala komanso amene ankaponderezedwa. Ndiye taganiziraninso malangizo othandiza amene anapereka komanso mmene amatithandizira tikamawatsatira.​—Mat. 5:1-11; 7:24-27.

12. Kodi chingachitike n’chiyani mukazindikira zinthu zambiri zokhudza Yesu?

12 Kuganizira nsembe imene Yesu anapereka kuti machimo athu akhululukidwe kungatithandize kuti tizimukonda kwambiri. (Mat. 20:28) Mukazindikira kuti Yesu anadzipereka kuti akufereni, mumafunitsitsa kulapa n’kupempha Yehova kuti akukhululukireni. (Mac. 3:19, 20; 1 Yoh. 1:9) Ndipo mukamakonda Yesu ndi Yehova mumayambanso kukonda anthu ena amene ali nawo pa ubwenzi.

13. Kodi Yehova wakupatsani chiyani?

13 Muzikonda anthu amene ali m’banja la Yehova. Anzanu komanso achibale anu omwe si Mboni sangamvetse akaona kuti mukufuna kudzipereka kwa Yehova. Ndipo mwina akhoza kukutsutsani. Koma Yehova angakuthandizeni pokupatsani abale ndi alongo mumpingo. Mukamagwirizana nawo akhoza kumakukondani komanso kukuthandizani. (Maliko 10:29, 30; Aheb. 10:24, 25) Ndipo mwina m’tsogolomu achibale anu akhoza kudzayambanso kutumikira Yehova komanso kutsatira mfundo zake.​—1 Pet. 2:12.

14. Malinga ndi 1 Yohane 5:3, kodi inuyo mwazindikira kuti mfundo za Yehova n’zotani?

14 Muzikonda mfundo za Yehova komanso kuzitsatira. Mwina musanaphunzire za Yehova munali ndi mfundo zimene munkayendera, koma panopa mumaona kuti mfundo za Yehova ndi zabwino kwambiri. (Sal. 1:1-3; werengani 1 Yohane 5:3.) Taganizirani malangizo amene Baibulo limapereka kwa amuna, akazi, makolo ndi ana. (Aef. 5:22–6:4) Kodi inuyo munaona kuti zinthu zikuyenda bwino m’banja lanu chifukwa chotsatira malangizowa? Kodi makhalidwe anu asinthanso chifukwa chotsatira malangizo a Yehova oti tizisankha bwino anthu ocheza nawo? Kodi panopa ndinu munthu wosangalala? (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33) N’zosachita kufunsa kuti mwayankha kuti inde pa mafunso amenewa.

15. Kodi mungatani ngati mukuvutika kudziwa zimene mungachite kuti mutsatire mfundo za m’Baibulo?

15 Nthawi zina mukhoza kuvutika kuti mudziwe zimene mungachite kuti mutsatire mfundo za m’Baibulo zimene mwaphunzira. N’chifukwa chake Yehova amagwiritsa ntchito gulu lake kuti lizitipatsa zinthu monga mabuku zotithandiza kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera. (Aheb. 5:13, 14) Mukamaphunzira zinthu zimenezi mumaona kuti n’zothandiza ndipo mumadziwa zoyenera kuchita. Izi zingakuthandizeni kuti muzikonda kwambiri gulu la Yehova.

16. Kodi Yehova wakonza zotani pofuna kuthandiza anthu ake?

16 Muzikonda komanso kuthandiza gulu la Yehova. Yehova wakonza zoti anthu ake azikhala m’mipingo ndipo wasankha Mwana wake, Yesu, kuti aziyang’anira mipingoyo. (Aef. 1:22; 5:23) Yesu wasankha kagulu kochepa ka amuna odzozedwa kuti azitsogolera pa ntchito imene akufuna kuti tizigwira masiku ano. Yesu anatchula kaguluka kuti ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) Kapoloyu amachita khama kwambiri potidyetsa komanso kutiteteza mwauzimu. Njira ina imene kapoloyu amagwiritsa ntchito pofuna kutithandiza ndi yoika akulu oyenerera kuti azitisamalira. (Yes. 32:1, 2; Aheb. 13:17; 1 Pet. 5:2, 3) Akulu amachita zonse zimene angathe kuti azitilimbikitsa komanso kutithandiza kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ukhale wolimba. Koma chinthu chofunika kwambiri chimene amachita ndi kutithandiza kuti tiziphunzitsa anthu za Yehova.​—Aef. 4:11-13.

17. Malinga ndi Aroma 10:10, 13, 14, n’chifukwa chiyani timakonda kuuza ena za Yehova?

17 Muzithandiza ena kuti azikonda Yehova. Yesu anauza otsatira ake kuti aziphunzitsa anthu za Yehova. (Mat. 28:19, 20) N’zotheka kumangotsatira lamuloli mwamwambo. Koma mukayamba kukonda kwambiri Yehova mumakhala ndi maganizo amene Petulo ndi Yohane anali nawo pamene ananena kuti: “Ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:20) Munthu amasangalala kwambiri akathandiza wina kuti ayambe kukonda Yehova. Kodi mukuganiza kuti Filipo anamva bwanji atathandiza nduna ya ku Itiyopiya ija kumvetsa choonadi n’kubatizidwa? Mukamatsanzira Filipo pomvera lamulo la Yesu lakuti tizilalikira, mumasonyeza kuti mukufunadi kukhala wa Mboni za Yehova. (Werengani Aroma 10:10, 13, 14.) Ndipo mudzafika pofunsa funso limene nduna ija inafunsa lakuti: “Chikundiletsa kubatizidwa n’chiyani?”​—Mac. 8:36.

18. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

18 Kubatizidwa ndi nkhani yaikulu komanso yofunika kwambiri. Choncho muyenera kuiganizira mofatsa. Kodi inuyo muyenera kudziwa zinthu zotani pa nkhani ya ubatizo? Kodi ndi zinthu ziti zimene muyenera kuchita musanabatizidwe komanso pambuyo pobatizidwa? Tidzakambirana mayankho a mafunso amenewa munkhani yotsatira.

NYIMBO NA. 2 Dzina Lanu Ndinu Yehova

^ ndime 5 Anthu ena amakonda Yehova koma amakayikira zoti abatizidwe n’kukhala a Mboni. Ngati inunso mumamva choncho, nkhaniyi ikuthandizani kudziwa zinthu zimene mungachite kuti mubatizidwe.

^ ndime 5 Popeza anthufe timasiyanasiyana pa mfundo zimene zili munkhaniyi, zimene wina angayambe kuchita kuti azikonda Yehova zikhoza kukhala zosiyana ndi zimene wina angayambe.

^ ndime 6 Kuti mudziwe zambiri, onani kabuku kakuti Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa? ndiponso kakuti Mmene Moyo Unayambira​—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI Tsamba 5: Mlongo akupereka kapepala kwa mtsikana amene wakumana naye kumsika.