NKHANI YOPHUNZIRA 13

Muzikondana Kwambiri

Muzikondana Kwambiri

‘Muzikondana kwambiri kuchokera mumtima.’​—1 PET. 1:22.

NYIMBO NA. 109 Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima

ZIMENE TIPHUNZIRE *

Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anatsindika mfundo ya chikondi kwa ophunzira ake (Onani ndime 1-2)

1. Kodi Yesu anapatsa ophunzira ake lamulo liti? (Onani chithunzi chapachikuto.)

USIKU woti aphedwa mawa lake, Yesu anapatsa ophunzira ake lamulo lakuti: “Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana.” Kenako anawonjezera kuti: “Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”​—Yoh. 13:34, 35.

2. N’chifukwa chiyani kusonyezana chikondi kuli kofunika?

2 Yesu ananena kuti anthu angazindikire ophunzira ake ngati akukondana mmene iye ankawakondera. Zimene Yesu ananenazi zinali zoona mu nthawi ya atumwi ndipo ndi zoonanso masiku ano. N’chifukwa chake kukondana kwambiri n’kofunika ngakhale pamene zavuta.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Popeza si ife angwiro, zimativuta kuti tizikondana kwambiri. Komabe tiyenera kuyesetsa kutsanzira Khristu. Munkhaniyi, tiphunzira mmene chikondi chingatithandizire kuti tizikhala mwamtendere ndi anzathu, tikhale opanda tsankho komanso ochereza. Tikamaphunzira nkhaniyi, muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndingaphunzire chiyani kwa abale ndi alongo omwe apitiriza kusonyezana chikondi ngakhale pali mavuto?’

MUZIKHALA MWAMTENDERE NDI ENA

4. Malinga ndi Mateyu 5:23, 24, n’chifukwa chiyani tiyenera kukhazikitsa mtendere ndi m’bale amene ali nafe chifukwa?

4 Yesu anatiphunzitsa kufunika kokhazikitsa mtendere ndi anthu amene ali nafe chifukwa. (Werengani Mateyu 5:23, 24.) Iye ananena kuti tiyenera kukhala mwamtendere ndi anthu kuti tizisangalatsa Mulungu. Yehova amasangalala tikamayesetsa kuti tizikhala mwamtendere ndi abale athu. Iye sangasangalale ndi kulambira kwathu ngati timasungira ena zifukwa komanso kukana kukhazikitsa mtendere.​—1 Yoh. 4:20.

5. Kodi n’chiyani chinachititsa m’bale wina kuti avutike kukhazikitsa mtendere?

5 Nthawi zina zingativute kukhazikitsa mtendere. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira Mark. * Iye anakhumudwa kwambiri m’bale wina atamuuza kuti sachita bwino zinthu zina n’kuyamba kuuza anthu mumpingo zinthu zoipa zokhudza iyeyo. Kodi Mark anatani? Iye ananena kuti: “Zinandinyansa kwambiri moti ndinamulalatira.” Kenako Mark anadzimvera chisoni ndipo anayesetsa kupepesa kwa m’baleyo kuti akhalenso pa mtendere. Koma m’baleyo anakana kukhululuka. Poyamba, Mark anaganiza kuti, ‘Ine ndikuyesetsa kumupepesa koma iye akukana, ndiye basi ndingomusiya.’ Komabe woyang’anira dera analimbikitsa Mark kuti asagwe ulesi. Ndiye kodi Mark anatani?

6. (a) Kodi Mark anachita chiyani pofuna kukhazikitsa mtendere? (b) Kodi Mark anagwiritsa ntchito bwanji mfundo za pa Akolose 3:13, 14?

6 Mark ataganiza mofatsa, anazindikira kuti iyeyo sanali wodzichepetsa ndipo ankadziona ngati wolungama. Iye anazindikira kuti ayenera kusintha. (Akol. 3:8, 9, 12) Kenako anafikira m’bale uja modzichepetsa ndipo anamupepesanso kachiwiri. Mark analemberanso m’baleyo makalata omupepesa komanso kupempha kuti ayambirenso kugwirizana. Iye anapatsa m’baleyo timphatso tomwe ankaganiza kuti timusangalatsa. N’zomvetsa chisoni kuti m’baleyo anakanabe kukhululuka ndipo anasunga chakukhosi. Koma Mark anapitiriza kumvera lamulo la Yesu loti tizikonda abale athu komanso kuwakhululukira. (Werengani Akolose 3:13, 14.) Tikamakonda anthu ngati mmene Yesu ankachitira, tidzayesetsabe kukhazikitsa mtendere ndi abale athu n’kumapemphera kuti tigwirizanenso nawo.​—Mat. 18:21, 22; Agal. 6:9.

Tingafunike kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana pokhazikitsa mtendere ndi munthu wina (Onani ndime 7-8) *

7. (a) Kodi Yesu anatipatsa malangizo otani? (b) Kodi mlongo wina anakumana ndi vuto lotani?

7 Yesu anatilangiza kuti tizichitira anthu zinthu zimene tingafune kuti iwowo atichitire. Ananenanso kuti tisamangokonda anthu amene amatikonda. (Luka 6:31-33) Ngakhale kuti sizichitika kawirikawiri, koma tiyerekeze kuti m’bale kapena mlongo wina wamumpingo mwanu safuna kulankhula nanu kapena kukupatsani moni. Kodi mungatani? Zoterezi zinachitikira mlongo wina dzina lake Lara. Iye anafotokoza kuti: “Mlongo wina anasiya kundilankhula ndipo sindinkadziwa chifukwa chake. Ndinkadandaula kwambiri ndipo sindinkasangalala kupita kumisonkhano.” Poyamba, Lara ankadziuza kuti, ‘Ine sindinamulakwire chilichonse. Ndipo anthu ena amumpingo amaonanso kuti mlongoyu ndi wovuta.’

8. Kodi Lara anachita chiyani kuti akhazikitse mtendere, nanga tikuphunzirapo chiyani?

8 Lara anayesetsa kukhazikitsa mtendere. Iye anapemphera kenako anaganiza zoti alankhule ndi mlongoyo. Atakambirana za vutoli anahagana n’kuyambiranso kukhala mwamtendere. Zinkaoneka ngati nkhani yatha. Koma Lara ananena kuti: “Patapita nthawi, mlongo uja anayambiranso kundikwiyira ndipo ndinadandaula kwambiri.” Poyamba, Lara ankaona kuti angamasangalale pokhapokha ngati mlongoyo wasiya kumukwiyira. Koma anazindikira kuti chinthu chanzeru chimene angachite ndi kungopitiriza kusonyeza mlongoyo chikondi komanso ‘kumukhululukira ndi mtima wonse.’ (Aef. 4:32–5:2) Lara anakumbukira kuti chikondi “sichisunga zifukwa, chimakwirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse, [komanso] chimapirira zinthu zonse.” (1 Akor. 13:5, 7) Kenako Lara anasiya kudandaula za nkhaniyi ndipo patapita nthawi mlongo uja anayambanso kumulankhula. Mukamayesetsa kukhala mwamtendere ndi Akhristu anzanu n’kumapitiriza kuwakonda, “Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.”​—2 Akor. 13:11.

MUZIPEWA TSANKHO

9. Malinga ndi Machitidwe 10:34, 35, n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala opanda tsankho?

9 Yehova alibe tsankho. (Werengani Machitidwe 10:34, 35.) Ifenso tikakhala opanda tsankho timasonyeza kuti ndife ana ake. Timamveranso lamulo lakuti tizikonda anzathu ngati mmene timadzikondera tokha, ndipo timathandiza kuti m’banja lathu lauzimu mupitirize kukhala mtendere.​—Aroma 12:9, 10; Yak. 2:8, 9.

10-11. Kodi mlongo wina anathana bwanji ndi maganizo ake olakwika?

10 Ena zimawavuta kukhala opanda tsankho. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Ruth. Ali mwana, munthu wina wochokera kudziko lina sanamuchitire zinthu zabwino. Kodi zimenezi zinamukhudza bwanji? Ruth ananena kuti: “Ndinkadana ndi chilichonse chokhudza dzikolo. Ndinkaganiza kuti anthu onse am’dzikolo ndi achoncho, ngakhale abale ndi alongo.” Kodi Ruth anathana bwanji ndi maganizo olakwikawa?

11 Ruth anazindikira kuti ayenera kuchita khama kuti asinthe maganizo olakwikawa. Iye anawerenga malipoti komanso nkhani za mu Buku Lapachaka zokhudza dzikolo. Ruth ananena kuti: “Ndinachita khama kuti ndiziona moyenera anthu am’dzikolo. Ndinayamba kuzindikira kuti abale ndi alongowo ndi akhama potumikira Yehova. Ndinaona kuti nawonso ali m’banja lathu lapadziko lonse.” Pang’ono ndi pang’ono, Ruth anazindikira kuti anafunika kusonyeza kwambiri chikondi. Iye anati: “Ndikakumana ndi abale ndi alongo ochokera m’dzikolo, ndinkayesetsa kuwamasukira. Ndinkalankhula nawo komanso kuyesetsa kuti ndidziwane nawo bwino.” Ndiye kodi zotsatira zake zinali zotani? Ruth anati: “Patapita nthawi, maganizo anga olakwika aja anatheratu.”

Ngati timakonda “gulu lonse la abale,” tidzapewa kukhala ndi tsankho (Onani ndime 12-13) *

12. Kodi Sarah anali ndi vuto lotani?

12 Ena sazindikira n’komwe kuti ali ndi mtima watsankho. Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Sarah ankaganiza kuti alibe tsankho chifukwa sankaweruza anthu potengera mtundu wawo, ndalama zawo kapena udindo womwe ali nawo m’gululi. Koma iye anati: “Ndinazindikira kuti munthune ndinali ndi tsankho.” Kodi tsankho lake linali lotani? Sarah anakulira m’banja la anthu ophunzira kwambiri ndiye ankakonda kucheza ndi anthu ophunziranso. Pa nthawi ina anauza mnzake kuti: “Ndimakonda kucheza ndi abale ndi alongo omwe ndi ophunzira. Enawa si kwenikweni.” Apa zikuonekeratu kuti Sarah ankafunika kusintha maganizo ake. Ndiye kodi anachita bwanji zimenezi?

13. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitika kuti Sarah asinthe maganizo ake olakwika?

13 Woyang’anira dera anathandiza Sarah kuti azindikire vuto lake. Sarah anati: “Woyang’anira derayo anandiyamikira chifukwa ndimatumikira Yehova mokhulupirika, ndimapereka ndemanga zabwino komanso ndimadziwa Malemba. Kenako anafotokoza kuti tikamadziwa zinthu zambiri timafunikanso kukhala ndi makhalidwe abwino monga kudzichepetsa komanso chifundo.” Sarah anatsatira zimene woyang’anira derayo anamuuza. Iye anati: “Ndinazindikira kuti chofunika kwambiri ndi kukhala munthu wachifundo komanso wachikondi.” Izi zinachititsa kuti asiye kuona abale ndi alongo molakwika. Iye anati: “Ndinayamba kuganizira makhalidwe awo abwino, omwe amachititsa kuti Yehova aziwaona kuti ndi amtengo wapatali.” Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tisamadzione kuti ndife apamwamba kuposa ena chifukwa cha maphunziro athu. Ngati ‘timakonda gulu lonse la abale,’ tidzapewa tsankho.​—1 Pet. 2:17.

KHALANI OCHEREZA

14. Mogwirizana ndi Aheberi 13:16, kodi Yehova amamva bwanji tikamachereza ena?

14 Yehova amasangalala tikamacherezana. (Werengani Aheberi 13:16.) Iye amaona kuti kuchereza komanso kuthandiza anthu ovutika ndi mbali ya kulambira kwathu. (Yak. 1:27; 2:14-17) N’chifukwa chake Malemba amatilimbikitsa kuti ‘tikhale ochereza.’ (Aroma 12:13) Tikamachereza ena timasonyeza kuti timawakondadi komanso timafuna kuti akhale anzathu. Kaya taitanira ena kachakudya kopepuka, zakumwa zoziziritsa kukhosi kapena tangopeza nthawi yocheza nawo, Yehova amasangalala kwambiri. (1 Pet. 4:8-10) Koma pali zinthu zina zimene zingatilepheretse kukhala ochereza.

“Poyamba, sindinkakonda kuchereza alendo koma ndasintha ndipo ndine wosangalala kwambiri” (Onani ndime 16) *

15-16. (a) N’chifukwa chiyani ena amaona kuti sangakwanitse kuchereza? (b) N’chiyani chinathandiza mlongo wina kuti akhale ndi mtima wochereza?

15 Nthawi zina tingamaope kuchereza ena chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Chitsanzo ndi mlongo wina dzina lake Edit yemwe mwamuna wake anamwalira. Asanakhale wa Mboni, sankakonda kucheza ndi anthu. Iye ankaona kuti sangakwanitse kuitana alendo ngati mmene anthu ena amachitira.

16 Edit anasintha maganizo ake atakhala wa Mboni. Anayetsetsa kukhala wochereza. Iye anati: “Pamene Nyumba ya Ufumu yathu yatsopano inkamangidwa, mkulu wina anandifunsa ngati banja lina lomwe linkabwera kudzagwira nawo ntchitoyo lingadzakhale kunyumba kwathu kwa masabata awiri. Ndinakumbukira mmene Yehova anadalitsira mayi wamasiye wa ku Zarefati.” (1 Maf. 17:12-16) Edit anavomera kuti banjalo lidzakhale kunyumba kwawo. Ndiye kodi anadalitsidwa bwanji? Iye anati: “M’malo moti angokhala kwa masabata awiri, anakhala nane kwa miyezi iwiri. Kukhala nawo nthawi imeneyi kunathandiza kuti akhale anzanga apamtima.” Edit anapezanso anzake apamtima mumpingo. Panopa iye ndi mpainiya, ndipo amakonda kuitanira abale ndi alongo omwe amayenda nawo mu utumiki kunyumba kwake kuti adzadye nawo chakudya chopepuka. Iye anati: “Kupatsa kumandichititsa kukhala wosangalala. Ndipo kunena zoona, ndimalandira madalitso ochuluka.”​—Aheb. 13:1, 2.

17. Kodi Luke ndi mkazi wake anazindikira chiyani?

17 N’kutheka kuti tili ndi mtima wochereza, koma kodi pali zina zomwe tiyenera kusintha pa nkhaniyi? Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Luke ndi mkazi wake ndi anthu ochereza. Nthawi zambiri amaitanira kunyumba kwawo makolo awo, achibale, anzawo komanso woyang’anira dera ndi mkazi wake. Koma Luke ananena kuti: “Tinazindikira kuti tinkangoitana anthu omwe timadziwana nawo bwino.” Kodi iwo atazindikira zimenezi anatani?

18. Kodi Luke ndi mkazi wake anachita chiyani powonjezera mtima wawo wochereza?

18 Luke ndi mkazi wake anamvetsa tanthauzo lenileni la kuchereza ataganizira mawu a Yesu akuti: “Mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, kodi mudzalandira mphoto yotani?” (Mat. 5:45-47) Iwo anazindikira kuti akufunika kutsanzira Yehova, yemwe amapereka zinthu zabwino kwa anthu onse. Choncho anaganiza zoti aziitana abale ndi alongo amene anali asanawaitanepo. Luke anati: “Tonse timasangalala kwambiri tikamacheza limodzi. Timalimbikitsana komanso kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova.”

19. Kodi timasonyeza bwanji kuti ndife ophunzira a Yesu, nanga mwatsimikiza kuchita chiyani?

19 Munkhaniyi taona kuti kukonda kwambiri anthu ena kungatithandize kukhala amtendere, opanda tsankho komanso ochereza. Tiyenera kuthetsa maganizo alionse olakwika omwe tingakhale nawo n’kumakonda kwambiri abale ndi alongo athu. Tikatero tidzakhala osangalala komanso tidzasonyeza kuti ndifedi ophunzira a Yesu.​—Yoh. 13:17, 35.

NYIMBO NA. 88 Ndidziwitseni Njira Zanu

^ ndime 5 Yesu ananena kuti chikondi ndi chizindikiro cha Akhristu oona. Kukonda abale ndi alongo athu kumatithandiza kuti tizikhazikitsa mtendere, tikhale opanda tsankho komanso tizicherezana. Koma nthawi zina zimenezi zimakhala zovuta. Munkhaniyi tikambirana mfundo zimene zingatithandize kuti tipitirize kukondana kwambiri kuchokera mumtima.

^ ndime 5 Mayina ena munkhaniyi asinthidwa.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo akuyesetsa kukhazikitsa mtendere. Poyamba, sizinatheke koma akupitirizabe kuti agwirizanenso ndi mlongo mnzake. Chifukwa choyesetsa kusonyeza chikondi, wakwanitsa kukhazikitsa mtendere.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wachikulire akuona kuti abale ena akumusala.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo amene poyamba ankaopa kuchereza wasintha maganizo ake, ndipo akusangalala chifukwa chochereza anthu.