NKHANI YOPHUNZIRA 12

Kodi Mumadziwa Nthawi Yoyenera Kulankhula?

Kodi Mumadziwa Nthawi Yoyenera Kulankhula?

“Chilichonse chili ndi nthawi yake, . . . nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula.”​—MLAL. 3:1, 7

NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi tikuphunzira chiyani pa lemba la Mlaliki 3:1, 7?

PALI anthu ena amene amakonda kulankhula pomwe ena amakonda kungokhala phee. Lemba limene lili kumayambiriro kwa nkhaniyi likunena kuti pali nthawi yolankhula ndi nthawi yokhala chete. (Werengani Mlaliki 3:1, 7.) Pali anthu ena amene timalakalaka atamalankhula kwambiri, pomwe ena timafuna atamachepetsa zolankhula zawo.

2. Kodi ndi ndani ayenera kutiuza nthawi yoyenera kulankhula komanso mmene tingalankhulire?

2 Kulankhula ndi mphatso yochokera kwa Yehova. (Eks. 4:10, 11; Chiv. 4:11) Ndipo Mawu ake amatithandiza kuti zolankhula zathu zizikhala zabwino. Munkhaniyi tikambirana zitsanzo za m’Baibulo zosonyeza nthawi yoyenera kulankhula ndi nthawi yoyenera kukhala chete. Tikambirananso mmene zolankhula zathu zimakhudzira Yehova. Tiyeni tsopano tiyambe n’kukambirana nthawi imene tiyenera kulankhula.

KODI TIYENERA KULANKHULA PA NTHAWI ITI?

3. Malinga ndi Aroma 10:14, kodi tiyenera kulankhula bwanji?

3 Nthawi zonse tiyenera kukhala okonzeka kulankhula za Yehova ndi Ufumu wake. (Mat. 24:14; werengani Aroma 10:14.) Tikamatero ndiye kuti tikutsanzira Yesu. Chifukwa chimodzi chimene Yesu anabwerera padzikoli chinali kudzauza anthu zoona zenizeni zokhudza Atate wake. (Yoh. 18:37) Koma tiyenera kuganiziranso mmene timalankhulira. Tikamauza anthu ena za Yehova tiyenera kulankhula “ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.” (1 Pet. 3:15) Tiziganizira zimene munthu amakhulupirira komanso mmene akumvera mumtima mwake. Tikamatero tikhoza kuwaphunzitsa bwino ndipo mawu athu akhoza kuwafika pamtima.

4. Malinga ndi Miyambo 9:9, kodi zolankhula zathu zingathandize bwanji anthu ena?

4 Akulu ayeneranso kulankhula akaona kuti m’bale kapena mlongo akufunika kulangizidwa. Koma ayenera kusankha nthawi yabwino kuti asamuchititse manyazi. Mwina angadikire mpaka atapeza mpata woti alankhulane ali paokha osati pagulu. Akulu ayenera kulangiza munthu m’njira yaulemu. Koma sayenera kulephera kutchula mwachindunji mfundo za m’Baibulo zimene zingathandize munthu kuchita zinthu mwanzeru. (Werengani Miyambo 9:9.) N’chifukwa chiyani tiyenera kulimba mtima n’kulankhula pa nthawi yoyenera? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane zitsanzo ziwiri. Choyamba ndi cha mwamuna amene anafunika kulangiza ana ake ndipo chachiwiri ndi cha mkazi amene anafunika kukalankhula ndi munthu amene ankayembekezera kukhala mfumu.

5. Kodi Eli analephera kulankhula pa nthawi iti?

5 Eli, yemwe anali mkulu wa ansembe, anali ndi ana aamuna awiri amene ankawakonda kwambiri. Koma anawo sankaopa Yehova. Iwo anali ndi maudindo akuluakulu chifukwa anali ansembe otumikira pachihema. Koma sankagwiritsa ntchito bwino udindo wawowo, sankalemekeza nsembe zoperekedwa kwa Yehova ndipo ankachita chiwerewere mopanda manyazi. (1 Sam. 2:12-17, 22) Malinga ndi Chilamulo cha Mose, ana a Eli anafunika kuphedwa. Koma Eli anangowadzudzula pang’ono basi n’kuwasiya kuti azitumikirabe pachihema. (Deut. 21:18-21) Kodi Yehova anamva bwanji ndi zimene Eli anachitazi? Iye anafunsa Eli kuti: ‘N’chifukwa chiyani ukumalemekezabe ana ako kuposa ine?’ Yehova anaganiza zopha anthu awiri oipawa.​—1 Sam. 2:29, 34.

6. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Eli?

6 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Eli? Tikazindikira kuti mnzathu kapena wachibale wathu waphwanya lamulo la Yehova tiyenera kulankhulapo n’kumukumbutsa mfundo za Yehova. Kenako tiyenera kuonetsetsa kuti walandira thandizo loyenerera kwa akulu, omwe amaimira Yehova. (Yak. 5:14) Sitiyenera kukhala ngati Eli n’kumalemekeza kwambiri mnzathu kapena wachibale kuposa Yehova. Pamafunika kulimba mtima kuti tilankhule pa nthawi ngati imeneyi koma zotsatira zake zimakhala zabwino kwambiri. Ndiye tiyeni tione kusiyana pakati pa zimene Eli anachita ndi zimene mkazi wina wa Chiisiraeli dzina lake Abigayeli anachita.

Abigayeli anapereka chitsanzo chabwino polankhula pa nthawi yoyenera (Onani ndime 7-8) *

7. N’chifukwa chiyani Abigayeli anapita kukalankhula ndi Davide?

7 Abigayeli anali mkazi wa munthu wina wachuma dzina lake Nabala. Pamene Davide ndi anthu ake ankathawa Sauli, anafika kudera limene kunali abusa a ziweto za Nabala ndipo anawathandiza kuti ziweto zawo zisabedwe. Koma Nabala sanayamikire zimenezi. Davide atatuma anthu kukapempha chakudya ndi madzi, iye anakwiya n’kuwakalipira. (1 Sam. 25:5-8, 10-12, 14) Zitatero, Davide anaganiza zokapha amuna onse a m’nyumba ya Nabala. (1 Sam. 25:13, 22) Kodi nkhondo imeneyi ikanapewedwa bwanji? Abigayeli anaona kuti imeneyi inali nthawi yoyenera kulankhula. Choncho anapita kukakumana ndi Davide yemwe anali ndi anthu okwana 400 omwe anali anjala, okwiya komanso onyamula zida.

8. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Abigayeli?

8 Abigayeli atakumana ndi Davide analankhula molimba mtima, mwaulemu komanso momufika pamtima. Iye anapepesa Davide ngakhale kuti wolakwa sanali iyeyo. Abigayeli sankakayikira kuti Yehova amuthandiza ndipo ananena kuti ankadziwa kuti Davide ali ndi makhalidwe abwino. (1 Sam. 25:24, 26, 28, 33, 34) Nafenso tiyenera kulimba mtima n’kulankhula ngati taona kuti zimene munthu wina akufuna kuchita zingamubweretsere mavuto. (Sal. 141:5) Tiyenera kulankhula mwaulemu koma molimba mtima. Tikamapereka malangizo oyenera kwa munthu timasonyeza kuti ndife mnzake weniweni.​—Miy. 27:17.

9-10. Kodi akulu ayenera kukumbukira chiyani akamalangiza anthu ena?

9 Makamaka akulu ayenera kulimba mtima n’kulankhula ndi anthu amene ayamba kuyenda panjira yolakwika. (Agal. 6:1) Akuluwo amakumbukira kuti nawonso si angwiro ndipo nthawi zina angafunike kulangizidwa. Koma zimenezi sizingawalepheretse kuthandiza anthu amene akufunika kulangizidwa. (2 Tim. 4:2; Tito 1:9) Iwo amayesetsa kuti apereke malangizowo mwaluso komanso moleza mtima. Amachita zonsezi chifukwa chokonda m’bale wawoyo. (Miy. 13:24) Koma chofunika kwambiri kwa iwo ndi kulemekeza Yehova polimbikitsa anthu kutsatira mfundo zake komanso kuteteza mpingo kuti usasokonezedwe.​—Mac. 20:28.

10 Pofika pano, takambirana za nthawi yoyenera kulankhula. Koma palinso nthawi yoyenera kukhala chete. Kodi ndi mavuto ati amene tingakumane nawo pa nthawi imeneyo?

KODI TIYENERA KUKHALA CHETE PA NTHAWI ITI?

11. Kodi Yakobo anagwiritsa ntchito fanizo liti, nanga n’chifukwa chiyani lili loyenera?

11 Nthawi zina anthufe timalephera kudziletsa pa nkhani yolankhula. Yakobo anafotokoza bwino vuto limeneli m’Baibulo. Iye analemba kuti: “Ngati wina sapunthwa pa mawu, ameneyo ndi munthu wangwiro, ndipo akhoza kulamuliranso thupi lake lonse.” (Yak. 3:2, 3) Anthu amatha kumangirira zingwe pakamwa pa hatchi kuti ziziwathandiza poilamulira kuti iyende kapena iime. Koma ngati zingwezo zagwa m’manja mwa munthu wokwera hatchi, hatchiyo ikhoza kumangothamangira kulikonse n’kuvulala kapenanso kuvulaza munthuyo. N’chimodzimodzinso ndi lilime lathu, ngati sitililamulira pakhoza kukhala mavuto aakulu. Kodi ndi pa nthawi iti pamene tiyenera kudzilamulira kuti tisalankhule kanthu?

12. Kodi ndi pa nthawi ina iti pamene tiyenera kudzigwira kuti tisalankhule?

12 Kodi inuyo mumatani ngati pali nkhani inayake yachinsinsi yokhudza m’bale kapena mlongo? Mwachitsanzo, ngati mwakumana ndi m’bale amene amatumikira m’dziko limene muli bani, kodi mumafuna kumufunsa mmene ntchito yathu ikuyendera m’dzikolo? N’kutheka kuti mungakhale ndi zolinga zabwino. Paja anthufe timakondana ndipo timafuna kudziwa mmene zikuyendera pa moyo wa anzathu. Timafunanso tizitchula zinthu zenizeni popempherera abale athu. Koma nthawi imeneyi ndi yofunika kulamulira lilime lathu kuti tikhale chete. Tikamakakamiza m’bale wathu kuti anene zinthu zachinsinsi timasonyeza kuti sitikumuganizira iyeyo komanso abale ndi alongo ena amene akumudalira kuti sangaulule zinthu ngati zimenezo. Ndipo palibe amene angafune kuchita zinthu zimene zingawonjezere mavuto a abale athu m’mayiko amene muli bani.

13. Malinga ndi Miyambo 11:13, kodi akulu ayenera kuchita chiyani? Perekani chifukwa.

13 Akulu ayenera kuyesetsa kwambiri kutsatira mfundo ya pa Miyambo 11:13 pa nkhani yosunga chinsinsi. (Werengani.) Zimenezi zimakhala zovuta ngati mkuluyo ndi wokwatira. Banja limalimba ngati anthu amalankhulana momasuka n’kumauzana zimene zili mumtima, zimene akuganiza komanso zimene zikuwadetsa nkhawa. Koma mkulu ayenera kupewa kuulula zinsinsi za abale ndi alongo mumpingo. Kupanda kutero anthu sangamukhulupirire ndipo mbiri yake ikhoza kuipa kwambiri. Paja anthu amene apatsidwa udindo mumpingo ayenera kukhala “osanena pawiri” kapena achinyengo. (1 Tim. 3:8) Apa zikutanthauza kuti ayenera kupewa kupusitsa anzawo kapena kunena miseche. Ngati mkulu amakonda mkazi wake, sangamuuze nkhani zimene safunika kuzidziwa.

14. Kodi mkazi angathandize bwanji mwamuna wake kuti akhalebe ndi mbiri yabwino?

14 Akazi a akulu ayenera kupewa kukakamiza amuna awo kuti awauze nkhani zachinsinsi. Mkazi akamapewa zimenezi amathandiza mwamuna wake komanso amasonyeza kuti amalemekeza anthu amene akukhudzidwa ndi nkhani zachinsinsizo. Koma chofunika kwambiri n’chakuti amasangalatsa Yehova chifukwa cholimbikitsa mtendere ndi mgwirizano mumpingo.​—Aroma 14:19.

ZIMENE TIMALANKHULA ZIMAKHUDZA YEHOVA

15. Kodi Yehova anamva bwanji ndi zimene anzake atatu a Yobu anachita? Perekani chifukwa.

15 Nkhani ya Yobu ikhoza kutithandiza kudziwa nthawi yolankhula komanso mmene tingalankhulire. Yobu atakumana ndi mavuto motsatizana, anthu 4 anabwera kuti adzamulimbikitse komanso kumupatsa malangizo. Anthuwo atafika anakhala nthawi yaitali osalankhula kalikonse. Koma zimene Elifazi, Bilidadi ndi Zofari analankhula pambuyo pake zimasonyeza kuti nthawi imene anakhala cheteyo sankaganizira mmene angathandizire Yobu. M’malomwake ankaganizira mmene angasonyezere kuti Yobu walakwitsa zinazake. Mfundo zina zimene ananena zinali zolondola koma zinthu zambiri zimene ananena zokhudza Yobu komanso Yehova zinali zopweteka komanso zabodza. Iwo ankasonyeza kuti Yobu anali munthu woipa. (Yobu 32:1-3) Kodi Yehova anatani? Iye anakwiya kwambiri ndi anthu atatuwo. Ananena kuti anthuwo ndi opusa ndipo ayenera kupempha Yobu kuti awapempherere.​—Yobu 42:7-9.

16. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Elifazi, Bilidadi ndi Zofari analakwitsa?

16 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Elifazi, Bilidadi ndi Zofari anachita? Choyamba, si bwino kuweruza abale athu. (Mat. 7:1-5) Ndi bwino kuwamvetsera mosamala tisanayambe kulankhula. Tikatero tikhoza kumvetsa bwino mavuto amene akukumana nawo. (1 Pet. 3:8) Chachiwiri, ngati tikulankhula tizitsimikizira kuti tikulankhula mokoma mtima ndipo mfundo zathu ndi zoona. (Aef. 4:25) Chachitatu, zimene timalankhula kwa anzathu zimakhudza Yehova.

17. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Elihu?

17 Munthu wina amene anapita kukaona Yobu anali Elihu, yemwe anali pachibale ndi Abulahamu. Iye ankamvetsera pamene Yobu ndi anthu atatuwo ankalankhula. N’zosachita kufunsa kuti ankamvetsera bwinobwino zonse zimene zinkanenedwa. Tikutero chifukwa chakuti anapereka malangizo mokoma mtima omwe anathandiza Yobu kuti asinthe maganizo ake olakwika. (Yobu 33:1, 6, 17) Chofunika kwambiri kwa Elihu chinali kulemekeza Yehova osati kudzitama kapena kutamanda anthu ena. (Yobu 32:21, 22; 37:23, 24) Zimene Elihu anachita zikusonyeza kuti pali nthawi yoyenera kukhala chete n’kumangomvetsera. (Yak. 1:19) Tikuphunziranso kuti tikamapereka malangizo kwa munthu, cholinga chathu chizikhala choti ulemerero upite kwa Yehova osati kwa ifeyo.

18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mphatso ya kulankhula?

18 Timasonyeza kuti timayamikira mphatso ya kulankhula tikamatsatira malangizo a m’Baibulo n’kumadziwa nthawi yoyenera kulankhula ndi kukhala chete. Mfumu Solomo anauziridwa kulemba kuti: “Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.” (Miy. 25:11) Tikamamvetsera zimene anzathu akulankhula komanso kuganiza kaye tisanalankhule, mawu athu adzakhala ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva. Mawuwo amakhala abwino komanso othandiza kwambiri. Ndipo kaya timalankhula pang’ono kapena kwambiri, mawu athu adzakhala olimbikitsa ndipo Yehova adzasangalala nafe. (Miy. 23:15; Aef. 4:29) Tikatero tidzasonyeza kuti timayamikira kwambiri mphatso imene Mulungu anatipatsa.

NYIMBO NA. 82 “Onetsani Kuwala Kwanu”

^ ndime 5 M’Mawu a Mulungu muli mfundo zotithandiza kudziwa nthawi yoyenera kulankhula ndi yoyenera kukhala chete. Tikadziwa zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi n’kumazitsatira, zolankhula zathu zidzakhala zosangalatsa Yehova.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo akupereka malangizo othandiza kwa mnzake.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akupereka malangizo pa nkhani ya ukhondo.

^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Abigayeli anakalankhula ndi Davide pa nthawi yoyenera ndipo zotsatira zake zinali zabwino.

^ ndime 68 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Banja likukana kunena zokhudza ntchito yathu m’dziko limene muli bani.

^ ndime 70 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mkulu akusamala kuti ena asamve nkhani zachinsinsi zakumpingo.