NKHANI YOPHUNZIRA 10

Aliyense Mumpingo Angathandize Ophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe

Aliyense Mumpingo Angathandize Ophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe

“Thupi lonselo limakula . . . malinga ndi ntchito yoyenera ya chiwalo chilichonse.”​AEF. 4:16.

NYIMBO NA. 85 Landiranani

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi ndi ndani angathandize wophunzira Baibulo kuti afike pobatizidwa?

MLONGO wina yemwe amakhala ku Fiji, dzina lake Amy, ananena kuti: “Ndinkakonda kwambiri zimene ndinkaphunzira m’Baibulo. Ndinkadziwa kuti ndi choonadi. Koma nditayamba kucheza kwambiri ndi abale ndi alongo ndi pamene ndinayamba kusintha zinthu pa moyo wanga n’kufika pobatizidwa.” Zimene Amy anafotokozazi zikutsimikizira mfundo yofunika yakuti: Wophunzira Baibulo angathe kupita patsogolo mpaka kubatizidwa akamathandizidwa ndi ena mumpingo.

2 Wofalitsa aliyense angathandize kuti mpingo ukule. (Aef. 4:16) Mpainiya wina yemwe amakhala ku Vanuatu, dzina lake Leilani, ananena kuti: “Pali mawu akuti udindo wolera mwana ndi wa mudzi wonse. Ndikuona kuti zimenezi n’zofanana ndi ntchito yothandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Anthu onse mumpingo amathandiza nawo kuti munthu afike podziwa choonadi.” Kuti mwana akule bwino, makolo ake, anzawo a makolowo, achibale komanso aphunzitsi ake amathandizana. Iwo amachita zimenezi pomulimbikitsa komanso kumuphunzitsa zinthu zofunika. Mofanana ndi zimenezi, ofalitsa mumpingo angapereke chitsanzo chabwino, malangizo komanso kulimbikitsa ophunzira Baibulo zomwe zingawathandize kuti afike pobatizidwa.​—Miy. 15:22.

3. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Ana, Daniel ndi Leilani ananena?

3 N’chifukwa chiyani wofalitsa amene akuchititsa phunziro la Baibulo ayenera kulola kuti ofalitsa ena azithandiza wophunzirayo? Taonani zimene mpainiya wina wapadera dzina lake Ana, yemwe amakhala ku Moldova ananena, iye anati: “Zimakhala zovuta kuti munthu mmodzi akwaniritse zonse zimene zimafunikira pothandiza wophunzira Baibulo kuti apite patsogolo.” Mpainiya wapadera winanso yemwe akutumikira m’dziko lomwelo, dzina lake Daniel, * anati: “Nthawi zambiri ofalitsa ena amalankhula zinthu zimene zimam’fika pamtima wophunzirayo, zomwe ineyo sindikanaziganizira n’komwe.” Leilani, yemwe tamutchula kale uja anafotokozanso chifukwa china, anati: “Chikondi chimene abale ndi alongo amamusonyeza, chimamuthandiza wophunzira Baibulo kudziwa kuti ndifedi atumiki a Yehova.”​—Yoh. 13:35.

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Komabe mwina mungadzifunse kuti, ‘kodi ndingathandize bwanji wophunzira Baibulo kupita patsogolo pamene si ine amene ndimamuphunzitsa?’ Tiyeni tikambirane zimene tingachite wina akatipempha kuti tipite naye kuphunziro lake la Baibulo komanso wophunzira Baibuloyo akayamba kufika kumisonkhano. Tionanso mmene akulu angathandizire kuti ophunzira Baibulo afike pobatizidwa.

ENA AKAKUITANIRANI KUPHUNZIRO LAWO

Mukapemphedwa kuti mukakhale nawo paphunziro la Baibulo, muzikonzekera bwino (Onani ndime 5-7)

5. Kodi udindo wanu umakhala wotani mukapita ndi munthu wina kuphunziro lake la Baibulo?

5 Paphunziro la Baibulo, mwiniwake wa phunzirolo ndi amene amakhala ndi udindo wothandiza wophunzirayo kumvetsa mfundo za m’Mawu a Mulungu. Choncho wina akakupemphani kuti mumuperekeze kuphunziro lake, muziona kuti wakutengani kuti mukamuthandize. (Mlal. 4:9, 10) Ndiye kodi mungatani kuti mukathandize kuti phunzirolo likakhale lopindulitsa?

6. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo ya pa Miyambo 20:18, mukapita ndi munthu wina kuphunziro lake?

6 Muzikonzekera. Choyamba, muzifunsa mphunzitsiyo kuti akuuzeni zina ndi zina zokhudza wophunzirayo. (Werengani Miyambo 20:18.) Mungamufunse kuti: “Kodi mbiri ya wophunzirayo ndi yotani? Kodi mukaphunzira naye mutu uti? Kodi ndi mfundo zazikulu ziti zimene mukufuna mukamuphunzitse? Kodi pali zinazake zimene mukufuna kuti ndikanene kapena ndisakanene pamene tikuphunzira naye? Kodi ndingakalimbikitse bwanji wophunzirayo kuti apite patsogolo?” Si kuti mphunzitsiyo angakufotokozereni nkhani zachinsinsi zokhudza wophunzirayo komabe zimene angakufotokozerenizo zingakuthandizeni kwambiri. Mmishonale wina dzina lake Joy, amakambirana mfundo ngati zimenezi ndi aliyense amene akupita naye kuphunziro lake. Iye anati: “Kuchita zimenezi kumathandiza amene ndayenda nayeyo kuti azisonyeza chidwi kwa wophunzirayo komanso kudziwiratu zomwe angalankhule paphunzirolo.”

7. N’chifukwa chiyani muyenera kukonzekera bwino mukamapita kuphunziro la munthu wina?

7 Ngati wina wakupemphani kuti mupite naye kuphunziro lake, mungachite bwino kukonzekera phunzirolo. (Ezara 7:10) M’bale Daniel, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Ndimasangalala ngati munthu amene ndapita naye kuphunziro wakonzekera bwino chifukwa ndi pamene amatha kufotokoza mfundo zothandiza.” Wophunzira amatha kuzindikira kuti nonse mwakonzekera bwino ndipo zimenezi zimamupatsa chitsanzo chabwino. Ngati simungakwanitse kukonzekera phunziro lonse, mungachite bwino kupeza nthawi kuti muone mfundo zazikulu m’phunzirolo.

8. Kodi mungatani kuti muzitchula mfundo zofunika mukapemphedwa kuti mupemphere paphunziro la Baibulo?

8 Pemphero ndi lofunika kwambiri paphunziro la Baibulo. Choncho muyenera kuganizira pasadakhale zimene munganene ngati mutapemphedwa kuti mupemphere. Zimenezi zingathandize kuti mutchule mfundo zofunika m’pempherolo. (Sal. 141:2) Hanae, yemwe amakhala ku Japan, amakumbukirabe mapemphero a mlongo wina amene ankabwera ndi mphunzitsi wake. Iye anati: “Ndinkaona kuti mlongoyo anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo ndinkafunitsitsa kukhala ngati iyeyo. Ndinkaonanso kuti amandikonda akamatchula dzina langa m’mapempherowo.”

9. Mogwirizana ndi Yakobo 1:19, kodi mungatani kuti muzithandiza munthu amene mwapita naye kuphunziro lake?

9 Muzithandiza mphunzitsi. Mpainiya wina wapadera wa ku Nigeria, dzina lake Omamuyovbi, anati: “Mnzako wabwino amamvetsera ukamaphunzitsa. Iye amafotokoza mfundo zothandiza koma salankhula kwambiri chifukwa amazindikira kuti si iye amene akuchititsa phunzirolo.” Ndiyeno, kodi mungadziwe bwanji nthawi yoti mulankhulepo komanso zimene muyenera kulankhula? (Miy. 25:11) Muzimvetsera mwatcheru mphunzitsiyo akamakambirana ndi wophunzirayo. (Werengani Yakobo 1:19.) Zimenezi zingakuthandizeni kudziwa nthawi yoyenera kulankhula. Komabe muyenera kuganizira kaye musanayambe kulankhula. Mwachitsanzo, simuyenera kulankhula kwambiri, kumudula mawu mphunzitsiyo kapena kuyambitsa nkhani ina. Koma mukhoza kumveketsa mfundo imene akukambiranayo popereka ndemanga yachidule, fanizo kapena funso. Nthawi zina mungaone kuti palibe zambiri zomwe mungalankhulepo. Koma ngati mungamuyamikire wophunzirayo komanso kumusonyeza kuti mukuchita naye chidwi, mungamuthandize kwambiri kuti apite patsogolo.

10. Kodi zimene zinakuchitikirani zingathandize bwanji wophunzira Baibulo?

10 Muzifotokoza zimene zinakuchitikirani. Ngati zingakhale zothandiza kwa wophunzirayo, mungamufotokozere mwachidule mmene munaphunzirira choonadi, zimene zinakuthandizani mutakumana ndi mavuto enaake kapenanso mmene Yehova wakuthandizirani pa moyo wanu. (Sal. 78:4, 7) N’kutheka kuti zimene mungafotokoze zingamuthandize kwambiri wophunzirayo. Zingalimbitse chikhulupiriro chake kapena kumulimbikitsa kuti apitirize kuphunzira mpaka kufika pobatizidwa. Ndiponso mwina zingamuthandize kuti apirire mayesero omwe akukumana nawo. (1 Pet. 5:9) Gabriel, yemwe amakhala ku Brazil ndipo panopa ndi mpainiya, amakumbukira zimene zinamuthandiza pamene ankaphunzira Baibulo. Iye anati: “Abale akamafotokoza zimene zinawachitikira, zinkandithandiza kudziwa kuti Yehova amaona mavuto amene timakumana nawo. Ndipo ndinkaona kuti ngati iwo anakwanitsa kupirira, ndiye kuti inenso ndingapirire.”

WOPHUNZIRA BAIBULO AKAFIKA KUMISONKHANO

Tonsefe tingalimbikitse wophunzira kuti apitirize kufika kumisonkhano (Onani ndime 11)

11-12. N’chifukwa chiyani tiyenera kulandira ndi manja awiri wophunzira Baibulo amene wabwera kumisonkhano?

11 Kuti wophunzira Baibulo afike pobatizidwa, ayenera kumapezeka pamisonkhano nthawi zonse. (Aheb. 10:24, 25) Mosakayikira, mphunzitsi wake angamuitanire kumisonkhano. Akabwera, tonsefe tingamulimbikitse kuti apitirize kumabwera ku Nyumba ya Ufumu. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

12 Tizimulandira ndi manja awiri. (Aroma 15:7) Wophunzira akaona kuti walandiridwa bwino, zingakhale zosavuta kuti apitirize kumabwera ku Nyumba ya Ufumu. Popanda kumuchititsa manyazi, muzimupatsa moni mosangalala komanso muzimudziwikitsa kwa anthu ena. N’kutheka kuti mphunzitsi wake angachedwe kubwera kapena angatanganidwe ndi zinthu zina pa Nyumba ya Ufumupo choncho musamaganize kuti pali winawake amene akumusamalira. Muzimvetsera mwatcheru wophunzirayo akamalankhula ndipo muzichita naye chidwi. Kodi zimenezi zingamuthandize bwanji? Taonani zimene zinachitikira Dmitrii, yemwe anabatizidwa zaka zingapo zapitazo ndipo panopa ndi mtumiki wothandiza. Pokumbukira zimene zinamuchitikira atabwera kumisonkhano koyamba, iye anati: “M’bale wina atandiona ndikudikira panja pa Nyumba ya Ufumu, ananditenga n’kukalowa nane mkati. Anthu ambiri anabwera kudzandipatsa moni. Zimenezi zinandidabwitsa kwambiri komanso zinandisangalatsa moti ndinkangofuna misonkhano itamachitika tsiku lililonse. Ndinali ndisanaonepo zinthu ngati zimenezi.”

13. Kodi zochita zanu zingathandize bwanji wophunzira Baibulo?

13 Tizipereka chitsanzo chabwino. Zochita zanu zingathandize wophunzira Baibulo kutsimikizira kuti wapeza choonadi. (Mat. 5:16) Vitalii, yemwe ndi mpainiya ku Moldova, anati: “Ndinkaona mmene ena mumpingo ankakhalira, ankaganizira komanso mmene ankachitira zinthu. Izi zinandithandiza kutsimikizira kuti a Mboni za Yehova alidi m’chipembedzo choona.”

14. Kodi chitsanzo chanu chabwino chingathandize bwanji wophunzira Baibulo?

14 Kuti wophunzira afike pobatizidwa, ayenera kutsatira zimene akuphunzira. Kuchita zimenezitu si kophweka. Koma wophunzirayo akaona mmene kutsatira mfundo za m’Baibulo kwakuthandizirani, angafunitsitse kukutsanzirani. (1 Akor. 11:1) Taganizirani zimene zinachitikira Hanae, yemwe tamutchula kale uja. Iye anati: “Abale ndi alongo ankachitanso zimene ndinkaphunzitsidwa. Ndinkaona zimene ndingachite kuti ndizitha kukhululuka, kulimbikitsa ena komanso kusonyeza chikondi. Nthawi zonse iwo ankalankhula zabwino zokhudza anthu ena. Choncho ndinkafunitsitsa kutengera chitsanzo chawo.”

15. Kodi lemba la Miyambo 27:17, likutithandiza bwanji pa nkhani yopanga wophunzira Baibulo kukhala mnzathu?

15 Tiziwapanga kukhala anzathu. Wophunzira akamabwera kumisonkhano, muzipitiriza kumusonyeza chidwi. (Afil. 2:4) Muzicheza naye kuti mumudziwe bwino. Popanda kulowerera pa nkhani zake zaumwini, mungamuyamikire pa zimene wakwanitsa kusintha, mungamufunse mmene phunziro la Baibulo likuyendera, zokhudza banja lake komanso ntchito yake. Izi zingathandize kuti mukhale mabwenzi apamtima komanso kuti wophunzirayo apite patsogolo n’kufika pobatizidwa. (Werengani Miyambo 27:17.) Hanae panopa ndi mpainiya wokhazikika. Pokumbukira zimene zinachitika atafika pamisonkhano kwa nthawi yoyamba, anati: “Nditayamba kukhala ndi anzanga ambiri mumpingo, ndinkafunitsitsa kuti ndizipezeka pamisonkhano. Ndipo ndinkayesetsa kupezekapo ngakhale pamene ndinkamva kuti ndatopa kwambiri. Ndinkasangalala kucheza ndi anzanga atsopanowa ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndisiye kucheza ndi anzanga akale omwe sankalambira Yehova. Ndinkafuna kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso abale ndi alongo. Choncho, ndinaganiza zobatizidwa.”

16. Kodi mungachitenso chiyani pothandiza wophunzira Baibulo kuti aziona kuti amawerengeredwa mumpingo?

16 Wophunzira Baibulo akayamba kupita patsogolo komanso kusintha zinthu pa moyo wake, muzimuthandiza kuona kuti amawerengeredwa mumpingo. Mungachite zimenezi pomuitanira kunyumba kuti mudzacheze naye. (Aheb. 13:2) Denis, yemwe amakhala ku Moldova, amakumbukira zimene zinkachitika pamene ankaphunzira Baibulo. Iye anati: “Nthawi zambiri abale ndi alongo ankandiitana limodzi ndi mkazi wanga kuti tikacheze nawo. Iwo ankatifotokozera mmene Yehova wakhala akuwathandizira ndipo zinkatilimbikitsa kwambiri. Zochitika zimenezi zinatithandiza kuti tikhale ofunitsitsa kutumikira Yehova komanso kuti tiziyembekezera moyo wabwino m’tsogolo.” Wophunzira Baibulo akavomerezedwa kukhala wofalitsa, mungamamutenge popita mu utumiki. Wofalitsa wina wa ku Brazil, dzina lake Diego, ananena kuti: “Abale ambiri ankanditenga akamapita mu utumiki. Izi zinandithandiza kuti ndiwadziwe bwino. Ndikamayenda nawo ndinkaphunzira zambiri ndipo ndinkaona kuti ndili pa ubwenzi ndi Yehova komanso Yesu.”

MMENE AKULU ANGATHANDIZIRE

Akulu mukamachita chidwi ndi ophunzira Baibulo, mungawathandize kuti apite patsogolo (Onani ndime 17)

17. Kodi akulu angathandize bwanji ophunzira Baibulo?

17 Muziyesetsa kuwadziwa ophunzira Baibulo. Akulu, mukamakonda komanso kusonyeza chidwi anthu amene akuphunzira Baibulo, mungawathandize kuti apite patsogolo mpaka kubatizidwa. Muzilankhula nawo nthawi zonse akafika pamisonkhano. Iwo angaone kuti mumachita nawo chidwi mukamakumbukira mayina awo, makamaka akayamba kuyankha pamisonkhano. Kodi mungakonzenso ndandanda yanu kuti muzipeza nthawi yopita ndi ofalitsa kumaphunziro awo a Baibulo? Dziwani kuti mungathandize kwambiri wophunzira Baibulo kuposa mmene mumaganizira. Mpainiya wina yemwe amakhala ku Nigeria, dzina lake Jackie ananena kuti: “Ophunzira ambiri amadabwa akamva kuti m’bale amene ndinapita naye kuphunzirolo ndi mkulu. Moti munthu wina amene ndimaphunzira naye ananena kuti: ‘Abusa anga sangachite zimenezi. Iwo amayendera olemera okhaokha ndipo amachita zimenezi anthuwo akawalipira.’” Panopa wophunzirayu amapezeka pamisonkhano.

18. Kodi akulu angagwiritse ntchito bwanji mfundo ya pa Machitidwe 20:28, pokwaniritsa udindo wawo?

18 Muziphunzitsa komanso kulimbikitsa ofalitsa. Akulu muli ndi udindo waukulu wothandiza ofalitsa kuti azikhala aluso mu utumiki komanso pochititsa maphunziro a Baibulo. (Werengani Machitidwe 20:28.) Ngati wofalitsa akuchita manyazi kuchititsa phunziro lake muli pompo, mungadzipereke kuchititsa phunzirolo. Jackie, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Nthawi zambiri akulu amandifunsa za anthu amene ndimaphunzira nawo Baibulo. Ndikamakumana ndi mavuto pochititsa phunziro la Baibulo, iwo amandipatsa malangizo othandiza.” Akulu angachite zambiri pothandiza komanso kulimbikitsa ofalitsa amene ali ndi maphunziro a Baibulo. (1 Ates. 5:11) Jackie ananenanso kuti: “Ndimasangalala akulu akamandilimbikitsa n’kumandiuza kuti amayamikira khama limene ndimachita pochititsa maphunziro a Baibulo. Mawu ngati amenewa amanditsitsimula ngati ndamwa madzi ozizira patsiku limene kunja kwatentha kwambiri. Zimandithandizanso kuti ndizisangalala komanso ndiziona kuti ndikugwira ntchito yofunika kwambiri.”​—Miy. 25:25.

19. Kodi tonsefe tingasangalale chifukwa chochita chiyani?

19 Ngakhale zitakhala kuti panopa tilibe phunziro la Baibulo, tingathandize winawake kupita patsogolo mpaka kubatizidwa. Tikakhala nawo paphunziro la Baibulo la munthu wina, tisamalankhule kwambiri. Ndipo ngati takonzekera bwino, ndemanga zathu zingathandize mwiniwake wa phunzirolo kufotokoza bwino mfundo za m’phunzirolo. Tingathenso kupanga ophunzirawo kukhala anzathu akabwera ku Nyumba ya Ufumu komanso tiziwapatsa chitsanzo chabwino. Akulu angalimbikitsenso ophunzira popeza nthawi yocheza nawo. Angalimbikitsenso ofalitsa amene ali ndi maphunziro a Baibulo powaphunzitsa komanso kumawayamikira. Kunena zoona, timakhalatu osangalala kwambiri tikachita zinazake pothandiza munthu wina kuti ayambe kukonda komanso kutumikira Atate wathu, Yehova.

NYIMBO NA. 79 Athandizeni Kukhala Olimba

^ ndime 5 Si tonse amene panopa tili ndi mwayi wochititsa phunziro la Baibulo. Komabe, aliyense mumpingo angathandize kuti winawake abatizidwe. Munkhaniyi tiona zimene tingachite kuti tizithandiza ophunzira Baibulo kuti afike pobatizidwa.

^ ndime 3 Mayina ena asinthidwa.