NKHANI YOPHUNZIRA 9

Kodi Achinyamata Mungatani Kuti Anthu Ena Azikudalirani?

Kodi Achinyamata Mungatani Kuti Anthu Ena Azikudalirani?

“Gulu la achinyamata amene ali ngati mame . . . lili pamodzi ndi iwe.”​SAL. 110:3.

NYIMBO NA. 39 Tipange Dzina Labwino Ndi Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi tiziwaona bwanji abale achinyamata?

PALI zambiri zimene abale achinyamatanu mungachite. Ambiri a inu muli ndi mphamvu komanso thanzi labwino. (Miy. 20:29) Mumachita zambiri pothandiza abale ndi alongo anu mumpingo. Ndipo n’kutheka kuti mumafuna mutakhala mtumiki wothandiza koma mwina mungaganize kuti ena azikuonani kuti ndinu wamng’ono komanso simunafike popatsidwa ntchito zofunika kwambiri. Ngakhale kuti ndinu wachinyamata, pali zambiri zimene mungachite panopa zomwe zingathandize kuti anthu ena mumpingo azikudalirani komanso kukulemekezani.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Munkhaniyi, tikambirana za Mfumu Davide. Tikambirananso mwachidule zimene zinachitikira mafumu awiri a Yuda, omwe ndi Asa komanso Yehosafati. Tionanso mavuto omwe anthu atatuwa anakumana nawo, zimene anachita atakumana ndi mavutowo komanso zomwe abale achinyamata angaphunzire pa zitsanzo zawo.

ZIMENE MUNGAPHUNZIRE KWA MFUMU DAVIDE

3. Kodi ndi njira ina iti imene achinyamata angathandizire achikulire mumpingo?

3 Davide ali wachinyamata anaphunzira maluso omwe anali othandiza kwa anthu ena. N’zoonekeratu kuti Davide anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Iye anali ndi luso loimba ndipo anagwiritsa ntchito luso limeneli pothandiza Sauli, yemwe anali mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. (1 Sam. 16:16, 23) Kodi abale achinyamatanu, muli ndi luso linalake lomwe lingathandize ena mumpingo? Ambiri a inu muli ndi maluso osiyanasiyana. Mwachitsanzo, mwina mumaona kuti achikulire amayamikira akasonyezedwa mmene angagwiritsire ntchito zipangizo zawo zamakono pophunzira Baibulo pawokha komanso pamisonkhano. Ndiye mungathandize achikulirewa chifukwa mumadziwa zambiri zokhudza zipangizo zamakono.

Davide anali wodalirika ndipo ankaona kuti ndi udindo wake kusamalira nkhosa za bambo ake. Nthawi ina anateteza nkhosazo pamene chimbalangondo chinkafuna kuzigwira (Onani ndime 4)

4. Mofanana ndi Davide, kodi ndi makhalidwe ati amene abale achinyamata ayenera kukhala nawo? (Onani chithunzi chapachikuto.)

4 Pa moyo wake, Davide anasonyeza kuti anali munthu wodalirika. Mwachitsanzo, ali wachinyamata iye ankachita khama posamalira nkhosa za bambo ake. Nthawi zina ntchito imeneyi inkakhala yoopsa. Davide anauza Mfumu Sauli kuti: “Ine mtumiki wanu ndinakhala m’busa wa nkhosa za bambo anga. Ndiyeno kunabwera mkango komanso chimbalangondo moti chilichonse mwa zilombo zimenezi chinagwira nkhosa ya m’gululo. Pamenepo ine ndinatsatira chilombocho n’kuchipha, ndipo ndinapulumutsa nkhosa mkamwa mwake.” (1 Sam. 17:34, 35) Davide ankaona kuti ndi udindo wake kusamalira nkhosa ndipo molimba mtima ankachita zonse zomwe angathe kuti aziteteze. Abale achinyamata angatsanzire Davide ngati amachita khama pogwira ntchito iliyonse imene apatsidwa.

5. Mogwirizana ndi Salimo 25:14, kodi chinthu chofunika kwambiri chimene abale achinyamata angachite ndi chiyani?

5 Davide ali wachinyamata anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ubwenzi umenewu unali wofunika kwambiri kuposa kulimba mtima kwa Davide kapenanso luso limene anali nalo loimba zeze. Si kuti Davide ankangoona Yehova monga Mulungu wake koma ankamuonanso monga mnzake weniweni. (Werengani Salimo 25:14.) Choncho abale achinyamatanu, chinthu chofunika kwambiri chimene muyenera kuchita ndi kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Atate wanu wakumwamba ndipo zimenezi zingathandize kuti mupatsidwe maudindo mumpingo.

6. Kodi anthu ena ankamuona bwanji Davide?

6 Vuto lina limene Davide anakumana nalo linali lokhudza mmene anthu ena ankamuonera. Mwachitsanzo, pamene Davide anadzipereka kuti akamenyane ndi Goliati, Mfumu Sauli inayesa kumugwetsa ulesi pomuuza kuti: “Ndiwe mwana.” (1 Sam. 17:31-33) Sauli asananene zimenezi, m’bale wake wina wa Davide anali atamunena kuti anali wachibwana. (1 Sam. 17:26-30) Komabe, Yehova sankaona Davide ngati wamng’ono kapenanso kuti anali wachibwana. Iye ankamudziwa bwino Davide. Ndipo chifukwa chodalira Yehova yemwe anali mnzake wapamtima kuti amupatse mphamvu, Davide anapha Goliati.​—1 Sam. 17:45, 48-51.

7. Kodi mungaphunzire chiyani pa nkhani ya Davide?

7 Kodi mungaphunzire chiyani pa zimene zinachitikira Davide? Muyenera kukhala woleza mtima. Dziwani kuti pangatenge nthawi kuti anthu amene anakudziwani muli mwana avomereze kuti tsopano mukukula. Komabe mungakhale wotsimikiza kuti Yehova amaona zambiri osati chabe mmene mukuonekera. Iye amakudziwani bwino kwambiri ndipo amadziwa zimene mungakwanitse kuchita. (1 Sam. 16:7) Choncho muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu. Davide anachita zimenezi poyang’anitsitsa zimene Yehova analenga komanso kuganizira zimene akuphunzirapo zokhudza Mlengi. (Sal. 8:3, 4; 139:14; Aroma 1:20) Chinthu china chimene mungachite ndi kupempha Yehova kuti azikupatsani mphamvu. Mwachitsanzo, kodi anzanu akusukulu amakusekani kapena kukuvutitsani chifukwa choti ndinu wa Mboni za Yehova? Ngati ndi choncho, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kupirira vutolo. Muzigwiritsa ntchito malangizo othandiza opezeka m’Mawu ake komanso mabuku ndi mavidiyo othandiza pophunzira Baibulo. Mungamakhulupirire kwambiri Yehova mukaona nthawi iliyonse imene wakuthandizani kulimbana ndi mavuto anu. Kuwonjezera apo, anthu ena akaona kuti mumadalira Yehova akhoza kuyamba kukudalirani.

Abale achinyamata angathandize ena modzichepetsa m’njira zambiri (Onani ndime 8-9)

8-9. Kodi n’chiyani chinathandiza Davide kuyembekezera moleza mtima asanayambe kulamulira, nanga abale achinyamata angaphunzire chiyani pa chitsanzo chake?

8 Taganizirani vuto linanso limene Davide anakumana nalo. Atadzozedwa kuti akhale mfumu, iye anafunika kuyembekezera kwa zaka zambiri asanayambe kulamulira. (1 Sam. 16:13; 2 Sam. 2:3, 4) Ndiye pa nthawiyi kodi chinamuthandiza n’chiyani kudikira moleza mtima? M’malo moti zimenezi zimufooketse, Davide ankagwiritsa ntchito nthawi yake pochita zimene akanakwanitsa. Mwachitsanzo, pamene iye anathawira m’dziko la Afilisiti, anagwiritsa ntchito nthawi imeneyi pomenyana ndi adani a Aisiraeli. Pochita zimenezi iye anathandiza kuteteza malire a ufumu wa Yuda.​—1 Sam. 27:1-12.

9 Kodi abale achinyamata angaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Davide? Muzigwiritsa ntchito mwayi uliwonse umene mungapeze potumikira abale anu. Taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina dzina lake Ricardo. * Kuyambira ali wamng’ono iye ankafuna atakhala mpainiya wokhazikika. Koma akulu anamuuza kuti adikire kaye. M’malo motaya mtima kapena kukhumudwa, Ricardo anaonjezera nthawi imene ankathera mu utumiki. Iye anati: “Ndikaganizira nthawi imeneyo, ndimaona kuti zimenezo zinandithandiza kudziwa zimene ndinkafunika kukonza. Ndinkaonetsetsa kuti ndikumabwerera kwa anthu amene asonyeza chidwi komanso ndinkakonzekera bwino ulendo uliwonse wobwereza. Ndinafika mpaka pokhala ndi phunziro langa la Baibulo. Pamene ndinkalowa mu utumiki kawirikawiri ndinayamba kusiya kuchita mantha.” Panopa Ricardo ndi mpainiya wokhazikika waluso komanso mtumiki wothandiza.

10. Kodi pa nthawi ina Davide anachita chiyani asanasankhe zochita pa nkhani yofunika kwambiri?

10 Tiyeni tionenso zinthu zina zimene zinachitika pa moyo wa Davide. Pa nthawi ina pomwe iye ndi amuna omwe anali nawo ankakhala m’dera la Afilisiti pothawa Sauli, anasiya mabanja awo n’kupita kukamenya nkhondo. Kenako kunabwera adani kudzaukira mabanja awo, ndipo anawatenga n’kupita nawo monga akapolo. Davide akanatha kuganiza kuti popeza anali msilikali wodziwa kumenya nkhondo, ndiye kuti akanathanso kupeza njira yabwino yoti akapulumutse anthu omwe anatengedwawo. Koma iye anapempha Yehova kuti amuthandize kudziwa zoyenera kuchita. Kudzera mwa wansembe dzina lake Abiyatara, Davide anafunsira kwa Yehova kuti: “Kodi ndithamangitse gulu la achifwambali?” Yehova anavomereza kuti Davide achite zimenezo ndipo anamutsimikizira kuti akapambana. (1 Sam. 30:7-10) Kodi mungaphunzirepo chiyani pa nkhaniyi?

Abale achinyamata ayenera kupempha malangizo kwa akulu (Onani ndime 11)

11. Kodi muyenera kuchita chiyani musanasankhe zochita?

11 Muzifufuza kaye malangizo musanasankhe zochita. Muzipempha makolo anu kuti akuthandizeni. Mukhozanso kupeza malangizo abwino kwa akulu amene akhala akutumikira kwa nthawi yaitali. Yehova amawadalira akuluwa ndipo inunso mukhoza kumawadalira. Ndipotu iye amaona akulu monga “mphatso” mumpingo. (Aef. 4:8) Mukhoza kumasankha zinthu moyenera mukamatsanzira chikhulupiriro chawo komanso mukamamvera malangizo anzeru amene angakupatseni. Tsopano tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa Mfumu Asa.

ZIMENE MUNGAPHUNZIRE KWA MFUMU ASA

12. Kodi Mfumu Asa anali ndi makhalidwe ati pamene ankayamba kulamulira?

12 Mfumu Asa ali wachinyamata anali wodzichepetsa komanso wolimba mtima. Mwachitsanzo, bambo ake Abiya atamwalira, Asa anayamba kulamulira ndipo anayamba kuchotsa mafano onse m’dzikolo. Komanso “anauza Ayuda kuti afunefune Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kutsatira Chilamulo.” (2 Mbiri 14:1-7) Ndiponso Zera Mwitiyopiya atabwera kudzamenyana nawo ndi asilikali ake 1 miliyoni, Asa anachita zinthu mwanzeru popempha Yehova kuti awathandize. Iye anati: “Inu Yehova mukafuna kuthandiza, zilibe kanthu kuti anthuwo ndi ambiri kapena ndi opanda mphamvu. Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu.” Mawu amenewa akusonyeza kuti Asa ankakhulupirira kwambiri kuti Yehova awapulumutsa. Choncho Asa ankadalira kwambiri Atate wake wakumwamba ndipo “Yehova anagonjetsa Aitiyopiyawo.”​—2 Mbiri 14:8-12.

13. Kodi n’chiyani chinachitikira Asa, nanga n’chifukwa chiyani?

13 Mungavomereze kuti zinali zoopsa kwambiri kwa Asa kuti amenyane ndi gulu la asilikali 1 miliyoni. Koma chifukwa chakuti iye anadalira Yehova anapambana. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti iye atakumana ndi vuto lina lomwe linali laling’ono, sanadalire Yehova. Ataopsezedwa ndi mfumu yoipa ya Isiraeli dzina lake Basa, iye anapempha thandizo kwa mfumu ya Siriya. Zimenezi zinam’bweretsera mavuto aakulu. Kudzera mwa mneneri wake Haneni, Yehova anauza Asa kuti: “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Siriya, osadalira Yehova Mulungu wanu, gulu lankhondo la mfumu ya Siriya lathawa m’manja mwanu.” Ndipotu kuchokera nthawi imeneyo, Asa ankangokhalira kumenya nkhondo. (2 Mbiri 16:7, 9; 1 Maf. 15:32) Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani?

14. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumadalira Yehova, ndipo mogwirizana ndi 1 Timoteyo 4:12, kodi chingachitike n’chiyani mukamachita zimenezi?

14 Pitirizani kukhala odzichepetsa ndipo muzidalira Yehova nthawi zonse. Pamene munabatizidwa, munasonyeza kuti mumadalira komanso kumukhulupirira kwambiri. Ndipo Yehova anasangalala n’kukupatsani mwayi wokhala m’banja lake. Panopa chimene muyenera kuchita ndi kupitirizabe kumudalira. Zingakhale zosavuta kudalira Yehova mukamafuna kusankha zochita pa nkhani zofunika kwambiri pa moyo wanu, koma nanga bwanji pa nkhani zing’onozing’ono? N’zofunika kwambiri kuti muzidalira Yehova mukamasankha zochita pa nkhani zosiyanasiyana kuphatikizapo zosangalatsa, ntchito komanso zolinga zimene muli nazo pa moyo wanu. Musamadalire nzeru zanu. M’malomwake muzifufuza mfundo za m’Baibulo zokhudza zimene mukufuna kusankha ndipo muzichita zinthu mogwirizana ndi malangizowo. (Miy. 3:5, 6) Mukamachita zimenezi mudzasangalatsa mtima wa Yehova ndipo anthu ena mumpingo adzayamba kukulemekezani.​—Werengani 1 Timoteyo 4:12.

ZIMENE MUNGAPHUNZIRE KWA MFUMU YEHOSAFATI

15. Mogwirizana ndi zimene zili pa 2 Mbiri 18:1-3; 19:2, kodi ndi zinthu ziti zimene Mfumu Yehosafati analakwitsa?

15 N’zoona kuti inunso achinyamata mofanana ndi aliyense, si inu angwiro ndipo mumalakwitsa zinthu zina. Komabe zimenezi siziyenera kukulepheretsani kuchita zonse zimene mungathe potumikira Yehova. Taganizirani chitsanzo cha Mfumu Yehosafati. Iye anali ndi makhalidwe abwino ambiri. Ali wachinyamata, “Iye anafunafuna Mulungu wa bambo ake ndipo anayenda motsatira chilamulo chake.” Kuwonjezera pamenepo, iye anatumiza akalonga m’mizinda yonse ya Yuda kuti aziphunzitsa anthu za Yehova. (2 Mbiri 17:4, 7) Ngakhale kuti ankayesetsa kuchita zabwino, Yehosafati nthawi zina ankasankha zinthu molakwika. Pa nthawi ina atasankha zinthu molakwika, iye anapatsidwa uphungu ndi mtumiki wa Yehova. (Werengani 2 Mbiri 18:1-3; 19:2.) Kodi mungaphunzire chiyani pa nkhaniyi?

Abale ndi alongo amalemekeza achinyamata amene ndi akhama komanso odalirika (Onani ndime 16)

16. Kodi mungaphunzire chiyani pa zimene zinachitikira Rajeev?

16 Muzitsatira komanso kugwiritsa ntchito malangizo amene mungapatsidwe. N’kutheka kuti mofanana ndi achinyamata ambiri, inunso zimakuvutani kuti muziona kutumikira Yehova kukhala chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanu. Ngati zili choncho musataye mtima. Taganizirani chitsanzo cha Rajeev. Iye anafotokoza zimene zinamuchitikira ali wachinyamata ndipo anati: “Nthawi zina sindinkadziwa zoyenera kuchita pa moyo wanga. Mofanana ndi achinyamata ena ambiri, ndinkakonda masewera komanso zinthu zina zosangalatsa m’malo mopita kumisonkhano kapena kukalalikira.” Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza? Mkulu wina wachikondi anamupatsa malangizo. Rajeev anafotokoza kuti: “Mkuluyu anandithandiza kuganizira mfundo yopezeka pa 1 Timoteyo 4:8.” Modzichepetsa iye anatsatira malangizowo ndipo anayamba kuganizira zinthu zimene ayenera kuziona kukhala zofunika kwambiri pa moyo wake. Iye anati: “Ndinaganiza zoika kutumikira Yehova pamalo oyamba pa moyo wanga.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? Rajeev anati: “Patangopita zaka zochepa kuchokera pamene ndinalandira malangizo aja, ndinavomerezedwa kukhala mtumiki wothandiza.”

MUZICHITA ZIMENE ZINGASANGALATSE ATATE WANU WAKUMWAMBA

17. Kodi achikulire amamva bwanji akaona achinyamata amene akutumikira Yehova?

17 Achikulire amasangalala achinyamatanu mukamatumikira nawo limodzi Yehova “mogwirizana.” (Zef. 3:9) Iwo amayamikira kwambiri khama lanu komanso kudzipereka kwanu pogwira ntchito iliyonse imene mwapatsidwa. Ndipotu iwo amakukondani kwambiri.​—1 Yoh. 2:14.

18. Mogwirizana ndi Miyambo 27:11, kodi Yehova amamva bwanji akaona achinyamata amene amamutumikira?

18 Achinyamatanu, muzikumbukira kuti Yehova amakukondani ndipo amakudalirani. Iye ananeneratu kuti m’masiku otsiriza padzakhala achinyamata ambiri amene azadzipereke mofunitsitsa kuti amutumikire. (Sal. 110:1-3) Yehova akudziwa kuti mumamukonda ndipo mumayesetsa kuchita zonse zomwe mungathe pomutumikira. Choncho muzichita zinthu moleza mtima mukamachita zinthu ndi anthu ena komanso panokha. Mukalakwitsa zinazake, muzivomereza ena akakupatsani uphungu kapena malangizo ndipo muziona kuti akuchokera kwa Yehova. (Aheb. 12:6) Muzichita khama kugwira ntchito iliyonse imene mwapatsidwa. Ndipo koposa zonse, pa chilichonse chimene mukuchita, muziyesetsa kusangalatsa Atate wanu wakumwamba.​—Werengani Miyambo 27:11.

NYIMBO NA. 135 Yehova Akutipempha Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzeru”

^ ndime 5 Abale achinyamata akayamba kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova amafuna kuchita zambiri pomutumikira. Ndipo kuti ayenerere kukhala atumiki othandiza, amafunika kumachita zinthu zimene zingachititse kuti anthu ena mumpingo aziwalemekeza. Ndiye kodi angatani kuti ena aziwalemekeza?

^ ndime 9 Mayina ena asinthidwa.