NKHANI YOPHUNZIRA 13

Kodi Yehova Amatiteteza Bwanji?

Kodi Yehova Amatiteteza Bwanji?

“Ambuye ndi wokhulupirika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipitsitsayo.”​2 ATES. 3:3.

NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani Yesu anapempha Yehova kuti ayang’anire ophunzira ake?

PA USIKU wake womaliza kukhala ndi moyo monga munthu, Yesu ankaganizira mavuto omwe ophunzira ake adzakumane nawo. Chifukwa choti ankawakonda kwambiri anzakewa, iye anapempha Yehova kuti ‘awayang’anire kuopera woipayo.’ (Yoh. 17:14, 15) Yesu ankadziwa kuti akangobwerera kumwamba, Satana Mdyerekezi apitiriza kumenya nkhondo ndi onse amene akufuna kutumikira Yehova. Apa n’zoonekeratu kuti anthu a Yehova ankafunika kutetezedwa.

2. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova adzayankha mapemphero athu?

2 Yehova anayankha pemphero la Yesu chifukwa amamukonda Mwana wakeyu. Ifenso tikamayesetsa kusangalatsa Yehova, iye angamatikonde ndipo akhoza kumayankha mapemphero athu omupempha kuti atithandize komanso kutiteteza. Popeza iye ndi Atate wachikondi, adzapitiriza kutisamalira monga ana ake. Ndipotu atapanda kutero, dzina lake kapena kuti mbiri yake ikhoza kudetsedwa.

3. Kodi n’chifukwa chiyani masiku ano timafunika kuti Yehova azititeteza?

3 Panopa tikufunika kutetezedwa kwambiri ndi Yehova kuposa kale. Satana anachotsedwa kumwamba ndipo “ali ndi mkwiyo waukulu.” (Chiv. 12:12) Iye wachititsa anthu amene amatizunza kuti aziona ngati “akuchita utumiki kwa Mulungu.” (Yoh. 16:2) Ndipo ena omwe sakhulupirira Mulungu amatizunza chifukwa timachita zosiyana ndi anthu a m’dzikoli. Koma kaya amatizunza pa zifukwa zotani, sitimachita mantha. Chifukwa chiyani? Chifukwa Mawu a Mulungu amati: “Ambuye ndi wokhulupirika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipitsitsayo.” (2 Ates. 3:3) Kodi Yehova amatiteteza bwanji? Tiyeni tikambirane njira ziwiri.

YEHOVA WATIPATSA ZIDA ZANKHONDO

4. Mogwirizana ndi Aefeso 6:13-17, kodi Yehova watipatsa chiyani pofuna kutiteteza?

4 Yehova watipatsa zida zankhondo zomwe zingatiteteze Satana akamatiukira. (Werengani Aefeso 6:13-17.) Zidazi ndi zamphamvu komanso zodalirika. Koma kuti titetezeke, nthawi zonse tiyenera kuvala komanso kugwiritsa ntchito chida chilichonse. Kodi chida chilichonse chimaimira chiyani? Tiyeni tione.

5. Kodi lamba wachoonadi n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuvala lambayu?

5 Lamba wachoonadi amaimira choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. N’chifukwa chiyani tiyenera kuvala lamba ameneyu? Chifukwa Satana ndi “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44) Iye wakhala akunama kwa zaka zambiri ndipo wasocheretsa “dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chiv. 12:9) Koma choonadi cha m’Baibulo chimatiteteza kuti tisanamizidwe. Kodi timavala bwanji lamba wophiphiritsirayu? Timavala lambayu pophunzira choonadi chonena za Yehova, kumulambira “motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi” komanso poyesetsa kuchita zinthu moona mtima.​—Yoh. 4:24; Aef. 4:25; Aheb. 13:18.

Lamba: Choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu

6. Kodi chodzitetezera pachifuwa chachilungamo n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuvala chida chimenechi?

6 Chodzitetezera pachifuwa chachilungamo chimaimira mfundo zolungama za Yehova. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuvala chodzitetezera pachifuwachi? Mofanana ndi chodzitetezera pachifuwa chenicheni chomwe chimateteza mtima wa msilikali, chodzitetezera pachifuwa chachilungamo chimateteza mtima wathu wophiphiritsira kapena kuti umunthu wathu wamkati, kuti tisasokonezedwe ndi zinthu zoipa za m’dzikoli. (Miy. 4:23) Yehova amafuna kuti tizimukonda komanso kumutumikira ndi mtima wathu wonse. (Mat. 22:36, 37) Choncho Satana amayesa kutichititsa kuti tisiye kutumikira Yehova ndi mtima wonse potipangitsa kuti tizikonda zinthu zam’dzikoli, zomwe Yehova amadana nazo. (Yak. 4:4; 1 Yoh. 2:15, 16) Ndipo akaona kuti zimenezi sizikutheka, amayamba kutizunza n’cholinga choti tichite zimene Yehova sasangalala nazo.

Chodzitetezera pachifuwa: Mfundo zolungama za Yehova

7. Kodi timavala bwanji chodzitetezera pachifuwa chachilungamo?

7 Timavala chodzitetezera pachifuwa chachilungamo tikamatsatira mfundo za Yehova zokhudza zoyenera ndi zosayenera komanso tikamazigwiritsa ntchito pa moyo wathu. (Sal. 97:10) Ena angamaone kuti mfundo za Yehova ndi zopanikiza. Koma ngati tingasiye kutsatira mfundo za m’Baibulo, tingakhale ngati msilikali yemwe wavula chodzitetezera pachifuwa chifukwa choona kuti chikulemera kwambiri. Kuchita zimenezitu kungakhale kupusa. Kwa amene amakonda Yehova, ‘malamulo ake ndi osalemetsa’ koma ndi opulumutsa moyo.​—1 Yoh. 5:3.

8. Kodi kuvala nsapato zokonzekera uthenga wabwino wamtendere kumatanthauza chiyani?

8 Paulo akutilimbikitsanso kuti tiyenera kuveka mapazi athu nsapato zokonzekera uthenga wabwino wamtendere. Zimenezi zikutanthauza kuti nthawi zonse tizikhala okonzeka kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Tikamauza ena uthenga wa m’Baibulo, timakhala tikulimbitsanso chikhulupiriro chathu. N’zolimbikitsa kwambiri kuona kuti anthu a Yehova padziko lonse amayesetsa kupeza mipata yolalikira uthenga wabwino kaya ndi kuntchito, kusukulu kapena kumalo a malonda. Amalalikiranso kunyumba ndi nyumba, akamakagula zinthu, akamakaona achibale kapenanso akamalankhula ndi anthu amene amawadziwa komanso omwe amabwera kunyumba kwawo. Ngati tingamachite mantha n’kusiya kulalikira, tikhoza kufanana ndi msilikali yemwe wavula nsapato zake pa nthawi ya nkhondo. Msilikali ameneyu, mapazi ake akhoza kuvulala mosavuta. Zimenezi zingachititse kuti alephere kudziteteza ndipo sangathenso kutsatira malangizo a mtsogoleri wake.

Nsapato: Kukhala okonzeka kulalikira uthenga wabwino

9. N’chifukwa chiyani tiyenera kunyamula chishango chachikulu chachikhulupiriro?

9 Chishango chachikulu chachikhulupiriro chimaimira chikhulupiriro chathu mwa Yehova. Timakhulupirira kuti iye adzakwaniritsa zonse zomwe analonjeza. Chikhulupiriro chimenechi chimatithandiza ‘kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’ N’chifukwa chiyani tiyenera kunyamula chishango chachikuluchi? Chifukwa chimatiteteza kuti tisatengeke ndi zimene a mpatuko amaphunzitsa komanso tisamakhumudwe anthu ena akamanyoza zimene timakhulupirira. Popanda chikhulupiriro, sitingakhale ndi mphamvu zoti tikane ena akamatikakamiza kuti tisatsatire mfundo za Yehova. Koma nthawi iliyonse yomwe takana kuchita zomwe Yehova amadana nazo, kaya tili kuntchito kapena kusukulu, timakhala kuti tanyamula chishango chathu. (1 Pet. 3:15) Nthawi iliyonse imene takana kulembedwa ntchito yamalipiro ambiri, yomwe ikanamatilepheretsa kuchita zinthu zokhudza kulambira, timakhalanso titanyamula chishango chathu. (Aheb. 13:5, 6) Ndiponso nthawi iliyonse imene tikutumikira Yehova ngakhale ena azititsutsa, chishango chathu chimakhala chikutiteteza.​—1 Ates. 2:2.

Chishango: Kukhulupirira Yehova ndi malonjezo ake

10. Kodi chisoti chachipulumutso n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuvala chisotichi?

10 Chisoti chachipulumutso chikuimira chiyembekezo chimene Yehova watipatsa choti adzatipulumutsa ku imfa komanso adzapereka mphoto kwa onse amene amachita chifuniro chake. (1 Ates. 5:8; 1 Tim. 4:10; Tito 1:1, 2) Mofanana ndi mmene chisoti chenicheni chimatetezera mutu wa msilikali, chiyembekezo chathu chachipulumutso chimateteza maganizo athu. Tikutero chifukwa chiyembekezochi chimatithandiza kuti tiziganizira zomwe Mulungu walonjeza komanso kuti tiziona moyenera mavuto omwe timakumana nawo. Ndiye kodi timavala bwanji chisoti chimenechi? Timachita zimenezi tikamaganiza mogwirizana ndi zomwe Mulungu amafuna. Mwachitsanzo, sitimadalira chuma chosadalirika koma timadalira Mulungu.​—Sal. 26:2; 104:34; 1 Tim. 6:17.

Chisoti: Chiyembekezo cha moyo wosatha

11. Kodi lupanga la mzimu n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuligwiritsa ntchito?

11 Lupanga la mzimu ndi Mawu a Mulungu, Baibulo. Lupangali lili ndi mphamvu yothetsa chinyengo chamtundu uliwonse komanso kumasula anthu ku ziphunzitso zabodza ndi makhalidwe oipa. (2 Akor. 10:4, 5; 2 Tim. 3:16, 17; Aheb. 4:12) Timaphunzira mmene tingagwiritsire ntchito lupangali moyenera tikamaphunzira patokha komanso kudzera m’maphunziro amene gulu la Mulungu limatipatsa. (2 Tim. 2:15) Kuwonjezera pa zida zankhondo, Yehova watipatsanso chinthu china champhamvu kwambiri chomwe chingatiteteze. Kodi chinthu chimenechi n’chiyani?

Lupanga: Mawu a Mulungu, Baibulo

SITIYENERA KUMENYA TOKHA NKHONDOYI

12. Kodi n’chiyaninso chomwe timafunikira pankhondo yolimbana ndi Satana, nanga n’chifukwa chiyani?

12 Msilikali wodziwa kumenya nkhondo, amadziwa kuti payekha sangalimbane ndi gulu lalikulu la asilikali n’kupambana, koma amafunika kuthandizidwa ndi anzake. Mofanana ndi zimenezi, ifenso patokha sitingapambane pankhondo yolimbana ndi Satana ndi otsatira ake, timafunika kuti abale ndi alongo athu atithandize. Yehova watipatsa “gulu la abale” la padziko lonse, lomwe lingatithandize.​—1 Pet. 2:17.

13. Mogwirizana ndi Aheberi 10:24, 25, kodi timapindula bwanji tikamapezeka pamisonkhano?

13 Njira ina imene timalandirira thandizo ndi kupezeka pamisonkhano yathu. (Werengani Aheberi 10:24, 25.) Tonsefe timafooka nthawi zina koma misonkhano imatithandiza kuti tipezenso mphamvu. Timalimbikitsidwa ndi ndemanga zochokera pansi pa mtima zimene abale ndi alongo athu amapereka. Nkhani za m’Baibulo komanso zitsanzo zimene amakamba pamisonkhano zimatilimbikitsa kuti tipitirize kutumikira Yehova. Timalimbikitsidwanso ndi macheza amene timakhala nawo misonkhano isanayambe komanso ikatha. (1 Ates. 5:14) Kuwonjezera pamenepo, misonkhano yathu imatipatsa mwayi wopeza chimwemwe chimene chimabwera chifukwa chothandiza anthu ena. (Mac. 20:35; Aroma 1:11, 12) Misonkhano imatithandizanso m’njira zina. Imatithandiza kuti tizilalikira komanso kuphunzitsa mwaluso. Mwachitsanzo, timaphunzitsidwa mmene tingagwiritsire ntchito bwino Zinthu Zophunzitsira. Choncho, tizikonzekera bwino misonkhano. Tikakhala pamisonkhano, tizimvetsera mwatcheru. Misonkhano ikatha, tizigwiritsa ntchito maphunziro amene talandira. Tikamachita zimenezi, tidzakhala “msilikali wabwino wa Khristu Yesu.”​—2 Tim. 2:3.

14. Kodi Yehova amagwiritsanso ntchito ndani potiteteza?

14 Tilinso ndi angelo amphamvu mamiliyoni amene amatithandiza. Taganizirani zimene mngelo mmodzi yekha angakwanitse kuchita. (Yes. 37:36) Ndiye taganizirani zimene gulu la angelo amphamvu lingachite. Palibe munthu kapena chiwanda chimene chingalimbane ndi asilikali amphamvu a Yehova amenewa. Popeza Yehova ndi wamphamvu zonse, akakhala nafe timakhala amphamvu kuposa adani athu ngakhale atakhala ochuluka bwanji. (Ower. 6:16) Ndipo sitimakayikira zimenezi ngakhale pang’ono. Choncho, muzikumbukira mfundo zimenezi ngati anzanu a kuntchito, kusukulu kapena achibale anu omwe si Mboni alankhula kapena kuchita zinthu zomwe zakukhumudwitsani. Kumbukirani kuti simuli nokha pankhondoyi koma Yehova ndi amene akukutsogolerani.

YEHOVA APITIRIZA KUTITETEZA

15. Mogwirizana ndi Yesaya 54:15, 17, n’chifukwa chiyani palibe amene angalepheretse anthu a Mulungu kugwira ntchito yolalikira?

15 Anthu a m’dziko lolamulidwa ndi Satanali ali ndi zifukwa zambiri zomwe zimawachititsa kuti azidana nafe. Sitimachita nawo zandale kapena kumenya nkhondo. M’malomwake, timalalikira za dzina la Mulungu, kuthandiza anthu kudziwa kuti ndi Ufumu wake wokha umene udzabweretse mtendere komanso kumvera mfundo zake zolungama. Timathandizanso anthu kudziwa kuti wolamulira wadzikoli ndi wabodza ndiponso wopha anthu. (Yoh. 8:44) Komanso timalengeza kuti dziko la Satanali liwonongedwa posachedwapa. Ndipotu, Satana ndi otsatira ake sangatiletse kugwira ntchito yolalikira. Choncho, tipitiriza kutamanda Yehova muli monse mmene tingathere. Ngakhale kuti Satana ali ndi mphamvu, iye walephera kuletsa ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu kuti usafike kwa anthu padziko lonse. Komatu zimenezi zatheka chifukwa choti Yehova amatiteteza.​—Werengani Yesaya 54:15, 17.

16. Kodi Yehova adzapulumutsa bwanji anthu ake pa nthawi ya chisautso chachikulu?

16 Kodi tikuyembekezera chiyani kutsogoloku? Pa nthawi ya chisautso chachikulu, Yehova adzatipulumutsa modabwitsa pazochitika ziwiri. Choyamba, iye adzapulumutsa atumiki ake okhulupirika pa nthawi imene adzachititse mafumu a dzikoli kuwononga Babulo Wamkulu, yemwe ndi ufumu wa zipembedzo zonse zonyenga. (Chiv. 17:16-18; 18:2, 4) Chachiwiri, iye adzapulumutsa anthu ake pamene azidzawononga anthu onse omwe ali kumbali ya Satana pankhondo ya Aramagedo.​—Chiv. 7:9, 10; 16:14, 16.

17. Kodi timapindula bwanji tikakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

17 Tikakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, Satana sangatichite chilichonse chomwe chingativulaze mpaka kalekale. Ndipotu ndi iyeyo amene adzawonongedwe kuti asadzakhaleponso mpaka kalekale. (Aroma 16:20) Choncho, valani zida zonse zankhondo ndipo musazivule. Musamayese kumenya nkhondo yolimbana ndi Satana ndi dziko lakeli panokha. Muzithandiza abale ndi alongo anu komanso muzitsatira malangizo a Yehova. Mukamachita zimenezi, mudzakhala otsimikiza kuti Atate wanu wakumwamba, yemwe ndi wachikondi adzakupatsani mphamvu komanso kukutetezani.​—Yes. 41:10.

NYIMBO NA. 149 Tiimbire Yehova Chifukwa Wapambana

^ ndime 5 M’Baibulo, Yehova amatilonjeza kuti adzatipatsa mphamvu komanso kutiteteza ku zinthu zimene zingawononge ubwenzi wathu ndi iye komanso zomwe zingativulaze. Munkhaniyi, tikambirana mayankho a mafunso awa: Kodi n’chifukwa chiyani timafunika kutetezedwa? Kodi Yehova amatiteteza bwanji? Komanso, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova azitithandiza?