NKHANI YOPHUNZIRA 11

Malemba Angatithandize Kuti Tizipirira

Malemba Angatithandize Kuti Tizipirira

“Mulungu . . . amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira.”AROMA 15:5.

NYIMBO NA. 94 Timayamikira Mulungu Potipatsa Mawu Ake

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi atumiki a Yehova amakumana ndi mayesero otani?

KODI mukukumana ndi mayesero aakulu? N’kutheka kuti mwina munthu wina mumpingo wakukhumudwitsani. (Yak. 3:2) Mwinanso anzanu a kuntchito kapena kusukulu amakunyozani chifukwa chotumikira Yehova. (1 Pet. 4:3, 4) Kapenanso anthu a m’banja lanu amakuletsani kuti musamapite kumisonkhano komanso musamauze ena zimene mumakhulupirira. (Mat. 10:35, 36) Mayesero amene mukukumana nawo akakhala aakulu, mungayambe kuganiza kuti mwina ndi bwino kusiya kutumikira Yehova. Komabe muyenera kukhala otsimikiza kuti ngakhale mutakumana ndi mayesero otani, Yehova adzakupatsani nzeru komanso mphamvu zoti mupirire.

2. Mogwirizana ndi Aroma 15:4, kodi kuwerenga Mawu a Mulungu kungatithandize bwanji?

2 M’Mawu ake Yehova anaikamo nkhani za anthu amene si angwiro ndiponso zimene anachita kuti athe kulimbana ndi mayesero amene ankakumana nawo. Iye anachita zimenezi n’cholinga choti tiziphunzirapo kanthu. Zimenezi ndi zomwe anauzira mtumwi Paulo kuti alembe. (Werengani Aroma 15:4) Tikamawerenga nkhanizi zimatilimbikitsa ndiponso zimatipatsa chiyembekezo. Koma kuti tipindule, pali zambiri zimene tiyenera kuchita osati kungowerenga Baibulo. Tizilola Malemba kuti azisintha mmene timaganizira komanso azitifika pamtima. Mwachitsanzo, kodi tingatani ngati tikufuna malangizo pa vuto limene takumana nalo? Tiyenera kugwiritsa ntchito mfundo 4 zotsatirazi: (1Kupemphera, (2Kuyerekezera, (3Kuganizira mozama komanso (4Kugwiritsa ntchito. Tiyeni tikambirane mfundo iliyonse payokha. * Kenako tigwiritsa ntchito njira imeneyi yophunzirira, pokambirana zimene zinachitika pa moyo wa Mfumu Davide komanso mtumwi Paulo.

1. KUPEMPHERA

Musanayambe kuwerenga Baibulo, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kupindula ndi zimene mukufuna kuwerengazo (Onani ndime 3)

3. Kodi musanayambe kuwerenga Baibulo muyenera kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

3 (1Kupemphera. Musanayambe kuwerenga Baibulo, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kupindula ndi zimene mukufuna kuwerengazo. Mwachitsanzo, ngati mukufufuza malangizo amene angakuthandizeni pa vuto linalake, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kupeza mfundo za m’Mawu ake zimene zingakuthandizeni kudziwa zoyenera.​—Afil. 4:6, 7; Yak. 1:5.

2. KUYEREKEZERA

Muzidziyerekezera muli munthu amene akutchulidwa munkhani ya m’Baibulo imene mukuwerenga (Onani ndime 4)

4. N’chiyani chingakuthandizeni kuti muziona nkhani za m’Baibulo kuti ndi zenizeni?

4 (2Kuyerekezera. Yehova anatipatsa luso lodabwitsa lotha kuyerekezera. Kuti muziona nkhani imene mukuwerenga m’Baibulo kuti ndi yeniyeni, muziyesa kuyerekezera zimene zikuchitika ndipo muzidziyerekezera kuti ndinu munthu amene akutchulidwa munkhaniyo. Muziyesa kuona zimene munthuyo anaona komanso m’mene ankamvera.

3. KUGANIZIRA MOZAMA

Muziganizira mozama zimene mukuwerenga komanso kuona mmene mungagwiritsire ntchito mfundo zake pa moyo wanu (Onani ndime 5)

5. Kodi tiyenera kuganizira mozama zinthu ziti, nanga tingachite bwanji zimenezo?

5 (3Kuganizira mozama. Tiyenera kumaganizira mozama zimene tikuwerenga komanso kuona mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zake pa moyo wathu. Kuchita zimenezi kungatithandize kumvetsa bwino nkhaniyo. Kuwerenga Baibulo popanda kuganizira mozama kuli ngati kumangoona zidutswa za chithunzi zomwe zamwazikana. Pamene kuganizira mozama kuli ngati kulumikiza zidutswazo kuti tione mmene chithunzi chonsecho chimaonekera. Kuti muzitha kuganizira mozama, muzidzifunsa komanso kuyesa kupeza mayankho a mafunso ngati awa: ‘Kodi munthu wotchulidwa munkhaniyi anatani kuti alimbane ndi vuto lake? Kodi Yehova anamuthandiza bwanji? Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji zimene ndaphunzira munkhaniyi kuti zindithandize kupirira mayesero?’

4. KUGWIRITSA NTCHITO

Muzigwiritsa ntchito zimene mumaphunzira kuti muzisankha zinthu mwanzeru, muzikhala ndi mtendere wamumtima komanso kuti mukhale ndi chikhulupiriro cholimba (Onani ndime 6)

6. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito zimene timaphunzira?

6 (4Kugwiritsa ntchito. Yesu ananena kuti ngati sitigwiritsa ntchito zimene timaphunzira, tingafanane ndi munthu amene wamanga nyumba yake pamchenga. Iye amagwira ntchito mwakhama, koma nthawi yake imangopita pachabe. Tikutero chifukwa ngati kutabwera mphepo kapena mvula yamphamvu, nyumbayo imagwa. (Mat. 7:24-27) Mofanana ndi zimenezi, ngati timapemphera, kuyerekezera komanso kuganizira mozama koma osagwiritsa ntchito zimene tikuphunzira, tikhoza kungowononga nthawi yathu pachabe. Choncho tikamayesedwa kapena kuzunzidwa, chikhulupiriro chathu sichingakhale cholimba. Koma tikamaphunzira komanso kugwiritsa ntchito zimene taphunzirazo, timasankha zinthu mwanzeru, timakhala ndi mtendere wamumtima komanso chikhulupiriro chathu chimalimba. (Yes. 48:17, 18) Pogwiritsa ntchito mfundo 4 tangokambiranazi, tiyeni tione zimene tingaphunzire pa zomwe zinachitika pa moyo wa Mfumu Davide.

ZIMENE TINGAPHUNZIRE KWA MFUMU DAVIDE

7. Kodi tikambirana nkhani ya m’Baibulo iti?

7 Kodi mnzanu kapena wachibale wanu anakukhumudwitsani chifukwa cholephera kukhala wokhulupirika kwa inu? Ngati ndi choncho mungapindule mukamawerenga nkhani ya Mfumu Davide ndi mwana wake Abisalomu, yemwe anakhala wosakhulupirika kwa bambo ake ndipo ankafuna kulanda ufumu wawo.​—2 Sam. 15:5-14, 31; 18:6-14.

8. Kodi muyenera kuchita chiyani kuti Yehova akuthandizeni?

8 (1Kupemphera. Muzimuuza Yehova mmene mukumvera chifukwa cha zoipa zimene ena akuchitirani. (Sal. 6:6-9) Muzitchula zinthu zenizeni zimene zikukudetsani nkhawa. Ndipo kenako muzimupempha kuti akuthandizeni kupeza mfundo zimene zingakutsogolereni polimbana ndi vuto limene mwakumana nalo.

9. Kodi mungafotokoze bwanji mwachidule zimene zinachitika pakati pa Davide ndi Abisalomu?

9 (2Kuyerekezera. Ganizirani zochitika za munkhaniyi ndipo yesani kuona mmene Davide anamvera pa nthawiyo. Kwa zaka zambiri Abisalomu akuyesetsa kuchititsa anthu kuti azimukonda. (2 Sam. 15:7) Kenako pamene akuona kuti nthawi yoyenera yakwana, iye akutumiza akazitape m’dziko lonse la Isiraeli n’cholinga chofuna kukonzekeretsa anthu kuti amuvomereze kukhala mfumu yawo. Iye akuyesanso kunyengerera Ahitofeli yemwe ndi mlangizi komanso mnzake wa Davide, kuti akhale ku mbali yake. Abisalomu akudziika yekha kukhala mfumu ndipo kenako akufuna kugwira komanso kupha Davide yemwe ayenera kuti anali akudwala kwambiri pa nthawiyo. (Sal. 41:1-9) Davide akuzindikira za chiwembucho ndipo akuthawira ku Yerusalemu. Pasanapite nthawi, asilikali a Abisalomu akuyamba kumenyana ndi asilikali omwe anali okhulupirika kwa Davide. Asilikali oukirawo akugonja pa nkhondoyo ndipo Abisalomu mwana wa Davide akuphedwa.

10. Kodi Mfumu Davide akanatha kuchita chiyani?

10 Tsopano ganizirani mmene Davide ankamvera pamene zonsezi zinkamuchitikira. Iye ankakonda kwambiri Abisalomu ndipo ankakhulupirira Ahitofeli. Komatu awiri onsewa, analephera kukhala okhulupirika kwa iye. Iwo anamukhumudwitsa kwambiri ndipo anafika mpaka pofuna kumupha. Davide akanatha kusiya kukhulupirira anzake ena onse n’kumakayikira kuti mwina nawonso ali kumbali ya Abisalomu. Akanatha kumangoganizira zake zokha mwinanso kuganiza zongothawa yekha m’dzikolo. Davide akanathanso kumangodziona ngati wolephera. Koma iye sanachite zonsezi. M’malomwake anapirira mavuto onsewa. Kodi n’chiyani chinamuthandiza?

11. Kodi Davide anatani chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo?

11 (3Kuganizira mozama. Kodi ndi mfundo ziti zimene mungaphunzire munkhaniyi? Dzifunseni kuti, ‘Kodi Davide anatani kuti athe kulimbana ndi vuto limene anakumana nalo?’ Davide sanapupulume kapena kusankha zinthu mopanda nzeru. Iye sanachite mantha kwambiri mpaka kufika polephera kusankha zochita. M’malomwake anapemphera kwa Yehova. Anapemphanso anzake kuti amuthandize. Komanso anachita mwamsanga zimene anasankha. Ngakhale kuti anali atakhumudwa kwambiri, Davide sanasiye kukhulupirira anthu ena kapena kumangokhala okwiya. Iye anapitiriza kukhulupirira Yehova komanso anzake.

12. Kodi Yehova anamuthandiza bwanji Davide?

12 Kodi Yehova anathandiza bwanji Davide? Ngati mutafufuza mukhoza kupeza kuti Yehova anapatsa Davide mphamvu zoti athe kupirira mayesero amene ankakumana nawo. (Sal. 3:1-8; timawu tapamwamba) Yehova anadalitsa zimene Davide anasankha. Komanso anathandiza anzake okhulupirika a Davide pamene ankamenya nkhondo kuti amuteteze monga mfumu yawo.

13. Kodi tingatsanzire bwanji Davide ngati munthu wina watikhumudwitsa kwambiri? (Mateyu 18:15-17)

13 (4Kugwiritsa ntchito. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndingatsanzire bwanji Davide?’ Muyenera kuchita zinthu mwamsanga mukamayesetsa kuthana ndi vuto limene mwakumana nalo. Mogwirizana ndi mmene zinthu zilili, mungagwiritse ntchito mwachindunji malangizo a Yesu opezeka pa Mateyu chaputala 18 kapena mukhoza kungogwiritsa ntchito mfundo yake. (Werengani Mateyu 18:15-17.) Koma simuyenera kusankha zochita mopupuluma makamaka ngati mwakwiya. Muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukhazikitsa mtima pansi komanso kuti akupatseni nzeru zimene zingakuthandizeni polimbana ndi vutolo. Musamasiye kukhulupirira anzanu. M’malomwake muzivomereza akamakuthandizani. (Miy. 17:17) Koma chofunika kwambiri ndikutsatira malangizo a Yehova omwe amakupatsani kudzera m’Mawu ake.​—Miy. 3:5, 6.

ZIMENE MUNGAPHUNZIRE KWA PAULO

14. Kodi lemba la 2 Timoteyo 1:12-16; 4:6-11, 17-22, lingakulimbikitseni pa zochitika ngati ziti?

14 Kodi anthu a m’banja lanu amakutsutsani chifukwa choti mukutumikira Yehova? Kapena kodi mukukhala m’dziko limene ntchito ya Mboni za Yehova ndi yoletsedwa? Ngati ndi choncho mungalimbikitsidwe mutawerenga lemba la 2 Timoteyo 1:12-16 ndi 4:6-11, 17-22. * Paulo analemba mavesi a m’Baibulo amenewa ali m’ndende.

15. Kodi muyenera kum’pempha chiyani Yehova?

15 (1Kupemphera. Musanawerenge nkhaniyo muuzeni Yehova vuto limene mwakumana nalo komanso muzimufotokozera mmene mukumvera. Kenako muzimupempha kuti akuthandizeni kupeza mfundo zimene zingakuthandizeni polimbana ndi vuto lanu mukamawerenga nkhani yofotokoza mayesero amene Paulo anakumana nawo.

16. Kodi mungafotokoze bwanji mwachidule zimene zinachitikira Paulo?

16 (2Kuyerekezera. Yerekezerani kuti zimene zinachitikira Paulo zikuchitikira inuyo. Iye wamangidwa ndi unyolo ndipo ali m’ndende ku Roma. Paulo anamangidwaponso m’mbuyomu, koma ulendo uno sakukayikira kuti aphedwa. Anzake ena amusiya ndipo wafookeratu.​—2 Tim. 1:15.

17. Kodi Paulo akanatha kuchita chiyani?

17 Paulo akanatha kuyamba kuganizira zam’mbuyo n’kumaona kuti akanapanda kukhala Mkhristu wodzipereka, sakanamangidwa. Iye akanatha kukwiyira abale a ku Asia omwe anamusiya yekha ndipo mwina zimenezi zikanamuchititsa kuti asiye kukhulupirira anzake ena. Koma Paulo sanachite zimenezi. N’chifukwa chiyani iye sankakayikira kuti anzakewa apitirizabe kukhala okhulupirika kwa iye komanso kuti Yehova adzamupatsa mphoto?

18. Kodi Paulo anatani chifukwa cha mayesero amene anakumana nawo?

18 (3Kuganizira mozama. Pezani yankho la funso lakuti, “Kodi Paulo anatani kuti athe kulimbana ndi vuto limene anakumana nalo?” Ngakhale kuti iye ankadziwa kuti anali atatsala pang’ono kufa, sanasiye kuona kuti chinthu chofunika kwambiri ndi kulemekezedwa kwa Yehova. Komanso anapitiriza kuganizira mmene angalimbikitsire ena. Paulo ankadalira kwambiri Yehova ndipo ankapemphera kwa iye nthawi zonse. (2 Tim. 1:3) M’malo momangoganizira za abale omwe anali atamusiya, iye ananena kuti ankayamikira kwambiri anzake okhulupirika omwe ankamuthandiza m’njira zosiyanasiyana. Kuwonjezera pamenepo, Paulo anapitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu. (2 Tim. 3:16, 17; 4:13) Koma chofunika kwambiri n’chakuti iye sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova ndi Yesu amamukonda. Iwo sanamusiye, ndipo Paulo anali wotsimikiza kuti adzamupatsa mphoto chifukwa chotumikirabe mokhulupirika.

19. Kodi Yehova anamuthandiza bwanji Paulo?

19 Yehova anali atamuchenjezeratu Paulo kuti adzazunzidwa chifukwa chokhala Mkhristu. (Mac. 21:11-13) Koma kodi Yehova anamuthandiza bwanji? Anayankha mapemphero ake ndipo anamupatsa mphamvu. (2 Tim. 4:17) Paulo anauzidwa kuti adzapatsidwa mphoto imene anaigwirira ntchito mwakhama kuti aipeze. Kuwonjezera pamenepo, Yehova anachititsa anzake okhulupirika kuti amuthandize.

20. Poganizira mfundo ya pa Aroma 8:38, 39, kodi tingatsanzire bwanji Paulo?

20 (4Kugwiritsa ntchito. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndingatsanzire bwanji Paulo?’ Mofanana ndi Paulo ifenso tiziyembekezera kuti tidzazunzidwa chifukwa cha zimene timakhulupirira. (Maliko 10:29, 30) Kuti tipitirizebe kukhala okhulupirika tikamakumana ndi mayesero, tiyenera kudalira Yehova n’kumapemphera nthawi zonse komanso kumaphunzira Mawu ake. Ndipo tizikumbukira kuti chofunika kwambiri ndi kuchita zimene zingapangitse kuti Yehova alemekezedwe. Ndife otsimikiza kuti Yehova sadzatisiya ngakhale pang’ono ndipo palibe chimene wina aliyense angachite kuti amulepheretse kutikonda.​—Werengani Aroma 8:38, 39; Aheb. 13:5, 6.

ZIMENE TINGAPHUNZIRE KWA ANTHU ENA OTCHULIDWA M’BAIBULO

21. Kodi n’chiyani chinathandiza Aya ndi Hector kuti athe kulimbana ndi mavuto omwe anakumana nawo?

21 Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tikhoza kulimbitsa chikhulupiriro chathu pophunzira nkhani za anthu a m’Baibulo. Mwachitsanzo, mpainiya wina wa ku Japan, dzina lake Aya, ananena kuti nkhani ya Yona inamuthandiza kuti asamachite mantha akamalalikira m’malo opezeka anthu ambiri. Wachinyamata wina wa ku Indonesia, dzina lake Hector, yemwe makolo ake satumikira Yehova, ananena kuti nkhani ya Rute yamuthandiza kuti aphunzire za Yehova komanso kuyamba kumutumikira.

22. Kodi mungapindule bwanji ndi masewero a m’Baibulo komanso nkhani zakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo”?

22 Kodi mungapeze kuti nkhani za m’Baibulo zimene zingakulimbikitseni? Mavidiyo, masewero ongomvetsera komanso nkhani zakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” zimathandiza kuti muziona kuti nkhani za m’Baibulo ndi zenizeni. * Musanayambe kuonera, kumvetsera kapena kuwerenga nkhanizi zomwe zinafufuzidwa bwino, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kupeza mfundo zimene muyenera kutsatira. Muzidziyerekezera kuti ndinu munthu wotchulidwa munkhaniyo. Muziganizira mozama zimene atumiki okhulupirika a Yehovawo anachita komanso mmene Yehova anawathandizira kuti athe kulimbana ndi mavuto. Kenako muzigwiritsa ntchito mfundo zimene mwaphunzirazo pa zimene zikukuchitikirani. Muzithokoza Yehova pa zimene akukuchitirani. Ndipo mungasonyeze kuti mukuyamikira mukamalimbikitsa komanso kuthandiza anthu ena.

23. Mogwirizana ndi Yesaya 41:10, 13, kodi Yehova akutilonjeza kuti adzachita chiyani?

23 Moyo m’dziko la Satanali ukhoza kukhala wovuta kwambiri mpaka kulephera kudziwa zoyenera kuchita. (2 Tim. 3:1) Koma sitiyenera kuda nkhawa mpaka kuchita mantha. Yehova amadziwa zimene tikukumana nazo. Tikagwa iye amatilonjeza kuti adzatigwira ndi dzanja lake lamanja lamphamvu. (Werengani Yesaya 41:10, 13.) Ndife otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza ndipo kudzera m’Malemba tingapeze mphamvu zotithandiza kupirira mavuto ena alionse.

NYIMBO NA. 96 Buku la Mulungu Ndi Chuma

^ ndime 5 Nkhani zambiri za m’Baibulo zimasonyeza kuti Yehova amakonda atumiki ake ndipo adzapitiriza kuwathandiza akamakumana ndi mayesero. Nkhaniyi itithandiza kuona zimene tingachite kuti tikamaphunzira nkhani za m’Baibulo patokha tizipindula kwambiri.

^ ndime 2 Imene tafotokozayi ndi imodzi mwa njira zimene mungagwiritse ntchito pophunzira. Njira zina zophunzirira Baibulo mungazipeze mu Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani, pa mutu wakuti “Baibulo” pansi pa kamutu kakuti “Kuwerenga ndi Kumvetsa Bwino Baibulo.”

^ ndime 14 Musawerenge malembawa pa nthawi ya Phunziro la Nsanja ya Olonda.

^ ndime 22 Onani nkhani zakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo​—Amuna ndi Akazi Otchulidwa M’Baibulo” pa jw.org. (Pitani pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUKHULUPIRIRA MULUNGU.)