NKHANI YOPHUNZIRA 11

Mmene Mungakonzekerere Kubatizidwa

Mmene Mungakonzekerere Kubatizidwa

“Chikundiletsa kubatizidwa n’chiyani?”​—MAC. 8:36.

NYIMBO NA. 50 Pemphero Langa Losonyeza Kudzipereka

ZIMENE TIPHUNZIRE a

Padziko lonse, achinyamata ndi achikulire omwe akupita patsogolo komanso kubatizidwa (Onani ndime 1-2)

1-2. Ngati panopa simunakonzeke kubatizidwa, n’chifukwa chiyani simuyenera kutaya mtima? (Onani chithunzi chapachikuto.)

 NGATI mukufuna kubatizidwa, dziwani kuti muli ndi cholinga chabwino kwambiri. Koma kodi ndinu wokonzeka kubatizidwa panopa? Ngati mukuona kuti mwakonzeka komanso akulu avomereza, musadzalephere kuchita zimenezo pamsonkhano wotsatira. Mukachita zimenezi mudzasangalala kwambiri kutumikira Yehova.

2 Kapena kodi mwauzidwa kuti mukufunika kukonza zina ndi zina musanabatizidwe? Kapenanso mwazindikira zimenezi panokha? Ngati ndi choncho, musataye mtima. Mungathe kupita patsogolo mpaka kukwaniritsa cholinga chanucho, kaya ndinu wamng’ono kapena wamkulu.

“CHIKUNDILETSA KUBATIZIDWA N’CHIYANI?”

3. Kodi ndi funso liti limene nduna ya ku Itiyopiya inafunsa Filipo, nanga zimenezi zikudzutsa funso liti? (Machitidwe 8:36, 38)

3 Werengani Machitidwe 8:36, 38. Nduna ya ku Itiyopiya inafunsa mlaliki wina dzina lake Filipo kuti: “Chikundiletsa kubatizidwa n’chiyani?” Munthu wa ku Itiyopiyayu ankafunitsitsa kubatizidwa. Koma kodi anali wokonzeka kuchita chinthu chofunikachi?

Nduna ya ku Itiyopiya inali yofunitsitsa kupitiriza kuphunzira za Yehova (Onani ndime 4)

4. Kodi munthu wa ku Itiyopiya anasonyeza bwanji kuti ankafunitsitsa kupitiriza kuphunzira?

4 Munthu wa ku Itiyopiyayu “anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu.” (Mac. 8:27) Choncho iye ayenera kuti anali wotembenukira ku Chiyuda. Mosakayikira, iye anaphunzira zokhudza Yehova kuchokera m’Malemba opatulika a Chiheberi. Komabe anali wofunitsitsa kuphunzira zambiri. Ndipo kodi pamene Filipo anakumana naye panjira, anamupeza akuchita chiyani? Anali akuwerenga mpukutu wa mneneri Yesaya. (Mac. 8:28) Zimenezotu zinali mfundo zozama za choonadi. Ndunayi sinangokhutira ndi mfundo zoyambirira zimene inaphunzira, koma inkafuna kupitiriza kuphunzira.

5. Kodi munthu wa ku Itiyopiya anachita chiyani pa zimene anaphunzira?

5 Munthuyo anali ndi udindo waukulu mu ulamuliro wa Kandake, Mfumukazi ya Itiyopiya. Ndipo “anali woyang’anira chuma chonse cha mfumukaziyo.” (Mac. 8:27) Choncho iye ayenera kuti ankatanganidwa ndi zochita zambiri. Komabe ankapeza nthawi yolambira Yehova. Sikuti ankangokhutira ndi kuphunzira choonadi, koma ankachita zomwe ankaphunzirazo. Choncho anayenda mtunda wautali kuchoka ku Itiyopiya kuti akalambire Yehova kukachisi ku Yerusalemu. Ulendowu uyenera kuti unatenga nthawi yaitali komanso ndalama zambiri. Koma munthuyu ankafunitsitsa kukalambira Yehova posatengera kuti awononga zotani.

6-7. Kodi munthu wa ku Itiyopiya anatani kuti apitirize kukonda kwambiri Yehova?

6 Munthu wa ku Itiyopiyayu anaphunzira mfundo za choonadi zatsopano kuchokera kwa Filipo, kuphatikizapo zoti Yesu ndi Mesiya. (Mac. 8:34, 35) N’zosachita kufunsa kuti munthu waudindoyu anasangalala kwambiri ataphunzira zimene Yesu anamuchitira. Ndiye kodi iye akanachita chiyani? Akanatha kungokhala mmene analili, monga munthu wotembenukira ku Chiyuda yemwe ankalemekezedwa. M’malomwake, iye anayamba kukonda kwambiri Yehova ndi Mwana wake. Chikondichi chinamuchititsa kusankha chinthu chofunika kwambiri pa moyo chomwe ndi kubatizidwa n’kukhala wotsatira wa Yesu Khristu. Filipo ataona kuti munthuyu anali wokonzeka, anamubatiza.

7 Ngati mutatengera chitsanzo cha munthu wa ku Itiyopiyayu, inunso mungakhale wokonzeka kubatizidwa. Munganenenso motsimikiza kuti, “Chikundiletsa kubatizidwa n’chiyani?” Tsopano tiyeni tikambirane zimene inunso mungachite kuti mufike pobatizidwa ngati mmene iye anachitira. Iye anapitiriza kuphunzira, ankachita zomwe ankaphunzirazo komanso anapitiriza kukonda kwambiri Mulungu.

PITIRIZANI KUPHUNZIRA

8. Kodi lemba la Yohane 17:3 limanena kuti muyenera kuchita chiyani?

8 Werengani Yohane 17:3. Kodi mawu a Yesuwa anakuthandizani kuti muyambe kuphunzira Baibulo? Ndi mmene zilili ndi ambirife. Koma kodi mawuwa amatiuzanso kuti tipitirize kuphunzira? Inde. Tidzapitirizabe “kudziwa . . . Mulungu yekhayo amene ali woona.” (Mlal. 3:11) Tidzapitiriza kuphunzira mpaka kalekale. Ndipotu tikamaphunzira kwambiri za Yehova m’pamenenso timayamba kumukonda kwambiri.​—Sal. 73:28.

9. Kodi muyenera kuchita chiyani pambuyo pophunzira ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo?

9 N’zomveka kuti kuphunzira zokhudza Yehova kumayamba ndi kuphunzira ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. M’kalata imene analembera Aheberi, mtumwi Paulo anatchula ziphunzitsozi monga “mfundo zoyambirira” za m’Mawu a Mulungu. Iye sankasonyeza kuti ‘ziphunzitso zoyambirirazi’ n’zosafunika, koma ankaziyerekezera ndi mkaka womwe umathandiza kuti mwana akhale wathanzi. (Aheb. 5:12; 6:1) Komabe iye analimbikitsa Akhristu onse kuti asamangokhutira ndi ziphunzitso zoyambirirazi ndipo azipitiriza kuphunzira mfundo zozama za m’Mawu a Mulungu. Kodi mumafunitsitsa kuphunzira mfundo zozama za m’Baibulo? Nanga mukufunitsitsa kupitiriza kuphunzira zokhudza Yehova ndi zolinga zake?

10. N’chifukwa chiyani ena amaona kuti kuphunzira n’kovuta?

10 Kwa ambirife kuphunzira si kophweka. Nanga bwanji inuyo? Muli kusukulu, kodi kuwerenga ndi kuphunzira sikunkakuvutani? Kodi munkaona kuti kuphunzira n’kosangalatsa komanso kopindulitsa? Kapena munkangoona kuti inuyo simungakwanitse kuphunzira pogwiritsa ntchito mabuku? Ngati ndi choncho, dziwani kuti si muli nokha. Yehova angakuthandizeni. Iye ndi wangwiro komanso Mphunzitsi wabwino kwambiri.

11. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi ‘Mlangizi wathu Wamkulu’?

11 Yehova amadzitchula kuti ndi ‘Mlangizi wathu Wamkulu.’ (Yes. 30:20, 21) Iye ndi Mphunzitsi woleza mtima, wokoma mtima komanso womvetsetsa. Amaona zabwino mwa ophunzira ake. (Sal. 130:3) Sayembekezera kuti tichita zimene sitingakwanitse. Kumbukirani kuti iye ndi amene anapanga ubongo wanu womwe ndi mphatso yodabwitsa. (Sal. 139:14) Mwachibadwa, anthufe timafuna kuphunzira. Mlengi wathu amafuna kuti tipitirize kuphunzira mpaka kalekale komanso tizisangalala nako. Choncho ndi nzeru kuti ‘tizilakalaka’ kuphunzira choonadi cha m’Baibulo panopa. (1 Pet. 2:2) Muzidziikira cholinga chomwe mungachikwaniritse ndipo nthawi zonse muzitsatira ndandanda yanu yowerengera ndi kuphunzirira Baibulo. (Yos. 1:8) Mothandizidwa ndi Yehova, mudzayamba kusangalala kwambiri ndi kuwerenga komanso kuphunzira za iye.

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kumaganizira za moyo wa Yesu tikamaphunzira patokha?

12 Nthawi ndi nthawi muziganizira za moyo ndi utumiki wa Yesu ali padzikoli. N’zofunika kwambiri kumatsatira mosamala mapazi a Yesu ngati tikufuna kutumikira Yehova, makamaka masiku ovuta ano. (1 Pet. 2:21) Mosapita m’mbali, Yesu anatchula mavuto omwe otsatira ake adzakumane nawo. (Luka 14:27, 28) Koma sankakayikira kuti otsatira ake enieni adzapambana ngati mmene iyeyo anachitira. (Yoh. 16:33) Phunzirani mwatsatanetsatane zokhudza moyo wa Yesu ndipo dziikireni zolinga zomwe zingakuthandizeni kuti muzimutsanzira tsiku lililonse.

13. Kodi muyenera kupitiriza kupempha chiyani kwa Yehova, nanga n’chifukwa chiyani?

13 Kungodziwa zinthu pakokha si kokwanira. Cholinga chachikulu ndi kukuthandizani kuphunzira zambiri zokhudza Yehova, komanso kukhala ndi makhalidwe monga kukonda Mulungu ndi kumukhulupirira. (1 Akor. 8:1-3) Pamene mukupitiriza kuphunzira, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuwonjezera chikhulupiriro chanu. (Luka 17:5) Iye amayankha mofunitsitsa mapemphero ngati amenewo. Chikhulupiriro chenicheni, chomwe chimabwera chifukwa chodziwa zolondola zokhudza Mulungu wathu, chidzakuthandizani kuti mupite patsogolo.​—Yak. 2:26.

PITIRIZANI KUCHITA ZIMENE MUMAPHUNZIRA

Chigumula chisanachitike, Nowa ndi banja lake ankachita mokhulupirika zimene ankaphunzira (Onani ndime 14)

14. Kodi mtumwi Petulo anatsindika bwanji kufunika kochita zimene timaphunzira? (Onaninso chithunzi.)

14 Mtumwi Petulo anatsindika kufunika koti otsatira a Khristu azipitiriza kuchita zimene amaphunzira. Iye anatchula za nkhani ya m’Baibulo yokhudza Nowa. Yehova anauza Nowa kuti adzabweretsa Chigumula chomwe chidzawononge anthu oipa a mu nthawi yake. Kungodziwa kuti kukubwera Chigumula si kunali kokwanira kuti Nowa ndi banja lake apulumuke. Onani kuti Petulo ananena za nthawi imene Chigumula chinali chisanayambe “pamene chingalawa chinali kupangidwa.” (1 Pet. 3:20) Nowa ndi banja lake ankachita zimene Mulungu ankawaphunzitsa ndipo anamanga chingalawa, chomwe chinali boti lalikulu. (Aheb. 11:7) Kenako Petulo anayerekezera zimene Nowa anachita ndi ubatizo, pomwe analemba kuti: “Chofanana ndi chingalawacho chikupulumutsanso inuyo tsopano. Chimenechi ndicho ubatizo.” (1 Pet. 3:21) Choncho tingayerekezere ntchito imene mukuchita pokonzekera kubatizidwa ndi ntchito imene Nowa ndi banja lake anagwira kwa zaka zambiri pokonza chingalawa. Kodi ndi ntchito yotani yomwe mumagwira pokonzekera kuti mubatizidwe?

15. Kodi kulapa kwenikweni kumaphatikizapo chiyani?

15 Chimodzi mwa zinthu zoyambirira zomwe tiyenera kuchita ndi kulapa machimo athu mochokera pansi pa mtima. (Mac. 2:37, 38) Kulapa kwenikweni kumatithandiza kuti tisinthe. Kodi munasiya makhalidwe amene Yehova amadana nawo monga chiwerewere, kusuta fodya, kulankhula mawu oipa kapena kutukwana? (1 Akor. 6:9, 10; 2 Akor. 7:1; Aef. 4:29) Ngati simunasiyebe zinthu zimenezi, pitirizani kuyesetsa kuti musinthe. Mungapemphe amene amakuphunzitsani Baibulo kapena akulu kuti akuthandizeni komanso kukupatsani malangizo. Ngati ndinu wamng’ono ndipo mumakhala ndi makolo anu, pitirizani kuwapempha kuti akuthandizeni kusiya makhalidwe oipa omwe angakulepheretseni kubatizidwa.

16. Kodi kuchita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse kumaphatikizapo chiyani?

16 N’zofunikanso kuti nthawi zonse muzichita zinthu zokhudza kulambira. Zimenezi zikuphatikizapo kupezeka pamisonkhano, kukamba nkhani komanso kupereka ndemanga. (Aheb. 10:24, 25) Ndipo akakuvomerezani kuti muyambe kulalikira, muzichitanso zimenezo nthawi zonse. Mukamaigwira kwambiri ntchito yopulumutsa anthuyi, m’pamenenso mumasangalala nayo kwambiri. (2 Tim. 4:5) Ngati ndinu wamng’ono ndipo mumakhala ndi makolo anu dzifunseni kuti: ‘Kodi makolo anga amachita kufunika kundikumbutsa kuti ndikasonkhane kapena ndikalalikire? Kapena kodi ndimachita zimenezi pandekha?’ Mukamachita zimenezi panokha mumasonyeza chikhulupiriro chanu komanso kuti mumakonda ndi kuyamikira Yehova Mulungu. Zimenezi ndi “ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu,” kapena kuti mphatso zimene mumapatsa Yehova. (2 Pet. 3:11; Aheb. 13:15) Mulungu wathu amasangalala ndi mphatso zimene timapereka mofunitsitsa, osati mokakamizidwa ndi winawake. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 9:7.) Timasangalala kuchita zimenezi chifukwa timafuna kum’patsa Yehova zinthu zabwino kwambiri.

PITIRIZANI KUKONDA KWAMBIRI YEHOVA

17-18. Kodi ndi khalidwe lofunika liti lomwe lingakuthandizeni kuti mupite patsogolo mpaka kubatizidwa, nanga lingakuthandizeni bwanji? (Miyambo 3:3-6)

17 Pamene mukupitiriza kupita patsogolo kuti mubatizidwe muzikumana ndi mavuto. Anthu ena angamakunyozeni chifukwa cha zimene mwayamba kukhulupirira, kukutsutsani kapena kukuzunzani. (2 Tim. 3:12) N’kutheka kuti mukuyesetsa kuti musiye khalidwe linalake loipa koma nthawi zina mumapezeka kuti mwalichitanso. Kapena mwina mungayambe kutaya mtima komanso kukhumudwa chifukwa choti cholinga chanu sichikukwaniritsidwa msanga. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mupirire? Ndi khalidwe lofunika kwambiri lomwe ndi kukonda Yehova.

18 Kukonda Yehova ndi khalidwe lofunika kwambiri lomwe muyenera kukhala nalo. (Werengani Miyambo 3:3-6.) Kukonda kwambiri Mulungu kungatithandize kuti tizipirira mavuto amene timakumana nawo. Nthawi zambiri Baibulo limafotokoza mmene Yehova amasonyezera chikondi chokhulupirika kwa atumiki ake. Chikondichi ndi champhamvu kwambiri moti sichitha zivute zitani. (Sal. 100:5) Inuyo munalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. (Gen. 1:26) Ndiye kodi mungasonyeze bwanji chikondi ngati chimenechi?

Tsiku lililonse mungasonyeze kuti mumayamikira Yehova (Onani ndime 19) b

19. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira kwambiri zonse zimene Yehova wakuchitirani? (Agalatiya 2:20)

19 Muziyamikira. (1 Ates. 5:18) Tsiku lililonse muzidzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amandikonda?’ Kenako muzionetsetsa kuti mukumuthokoza m’mapemphero anu ndipo muzitchula zenizeni zimene wakuchitirani. Muziona kuti chikondicho akusonyeza inuyo panokha, mofanana ndi mmenenso mtumwi Paulo ankaonera. (Werengani Agalatiya 2:20.) Dzifunseni kuti, ‘Kodi inenso ndikufuna kumusonyeza chikondi?’ Kukonda Yehova kudzakuthandizani kuti mupitirize kulimbana ndi mayesero komanso mavuto omwe mukukumana nawo. Chikondichi chidzakulimbikitsaninso kuti mupitirize kumachita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse, n’kumasonyeza kuti mumakonda Atate wanu tsiku ndi tsiku.

20. Kodi muyenera kuchita chiyani kuti mudzipereke kwa Yehova, nanga n’chifukwa chiyani kusankha kuchita zimenezi kuli kofunika?

20 M’kupita kwa nthawi, kukonda kwanu Yehova kudzakulimbitsani kuti mupereke pemphero lapadera losonyeza kuti mukudzipereka kwa iye. Kumbukirani kuti pamene mwadzipereka kwa Yehova mumakhala ndi chiyembekezo choti mudzakhala ake mpaka kalekale. Mumamulonjeza kuti mudzamutumikira pa nthawi zabwino ndi zovuta. Dziwani kuti mukalonjeza kamodzi simubwerezanso lonjezoli. N’zoona kuti kudzipereka ndi nkhani yaikulu, komabe taganizirani izi: Mudzafunika kusankha zochita pa zinthu zambiri, zina zabwino, koma simudzasankha chinthu chabwino kwambiri kuposa kudzipereka kwa Yehova. (Sal. 50:14) Satana adzayesetsa kukuchititsani kuti musiye kukonda Atate wanu poganiza kuti mudzasiya kukhala okhulupirika kwa iye. Koma musalole kuti iye apambane. (Yobu 27:5) Kukonda kwambiri Yehova kudzakuthandizani kuti mukwaniritse lonjezo lanu, lakuti mudzamutumikira mpaka kalekale komanso kukhala naye pa ubwenzi wolimba.

21. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ubatizo n’chiyambi chabe osati mapeto a zonse?

21 Pambuyo podzipereka kwa Yehova mungalankhule ndi akulu a mumpingo mwanu, kuwafotokozera za cholinga chanu chofuna kubatizidwa. Komabe nthawi zonse muzikumbukira kuti kubatizidwa ndi chiyambi chabe osati mapeto a zonse. Chimenechi ndi chiyambi chotumikira Yehova kwa moyo wanu wonse. Choncho panopa muyenera kumakonda kwambiri Atate wanu. Muzidziikira zolinga zomwe zingakuthandizeni kuwonjezera chikondichi tsiku ndi tsiku. Kuchita zimenezi kungakulimbikitseni kuti mubatizidwe. Tsiku limene mudzabatizidwe lidzakhalatu lapadera kwambiri. Koma ichi chidzangokhala chiyambi chabe. Choncho pitirizani kukonda kwambiri Yehova ndi Mwana wake mpaka kalekale.

NYIMBO NA. 135 Yehova Akutipempha Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzeru”

a Kuti tipite patsogolo mpaka kufika pobatizidwa, tiyenera kukhala ndi cholinga choyenera, komanso kumachita zinthu zoyenera. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha nduna ya ku Itiyopiya, tikambirana zimene ophunzira Baibulo angachite kuti akhale oyenera kubatizidwa.

b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo wachitsikana akuuza Yehova m’pemphero mmene amayamikirira zimene wamuchitira.