NKHANI YOPHUNZIRA 12

Muziphunzira Zambiri Zokhudza Yehova Poona Chilengedwe Chake

Muziphunzira Zambiri Zokhudza Yehova Poona Chilengedwe Chake

“Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino . . . m’zinthu zimene anapanga.”​—AROMA 1:20.

NYIMBO NA. 6 Kumwamba Kumalengeza Ulemelero wa Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi ndi njira imodzi iti yomwe inathandiza Yobu kumudziwa bwino Yehova?

 PA MAKAMBIRANO onse omwe Yobu anakhala nawo pa moyo wake, makambirano apadera kwambiri anali amene anakhala nawo ndi Yehova Mulungu. Pofuna kumuthandiza Yobu kuti azikhulupirira kwambiri nzeru za Mulungu komanso kuti amasamalira atumiki ake, Yehova anatchula zinthu zina zodabwitsa zam’chilengedwe. Mwachitsanzo, Mulungu anakumbutsa Yobu kuti iye amasamalira nyama, choncho akanatha kumusamaliranso iyeyo. (Yobu 38:39-41; 39:1, 5, 13-16) Poganizira zinthu zam’chilengedwe, Yobu anaphunzira makhalidwe ambiri a Mulungu wake.

2. N’chifukwa chiyani nthawi zina zingakhale zovuta kumachita chidwi ndi zinthu zomwe Yehova analenga?

2 Ifenso tingaphunzire zokhudza Mulungu wathu tikamachita chidwi ndi zinthu zimene analenga. Komabe si nthawi zonse pamene kuchita zimenezi kumakhala kophweka. Ngati timakhala m’mizinda ikuluikulu, sitingamaone zinthu zambiri zimene Mulungu analenga. Mwina ngakhale pamene tikukhala m’dera limene kuli zachilengedwe zambiri, tingamaone kuti tilibe nthawi yokwanira yoziphunzira. Choncho tiyeni tikambirane chifukwa chake zili zofunika kuti tizipeza nthawi komanso kumachita khama kuphunzira zinthu zachilengedwe. Tiona mmene Yehova ndi Yesu anagwiritsira ntchito chilengedwe pophunzitsa komanso zimene tingachite kuti tiziphunzira zambiri pa zinthu zam’chilengedwe.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUMACHITA CHIDWI NDI CHILENGEDWE?

Yehova ankafuna kuti Adamu azisangalala ndi zinthu zimene analenga komanso kupereka mayina kwa nyama (Onani ndime 3)

3. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova ankafuna kuti Adamu azisangalala ndi chilengedwe?

3 Yehova ankafuna kuti munthu woyambirira azisangalala ndi zinthu zimene iye analenga. Mulungu atalenga Adamu anamuika m’malo abwino kwambiri oti azikhalamo n’kumaphunzira zinthu zimene zinali mmenemo. Anamupatsanso ntchito yoti azisamalira komanso kuwonjezera munda wokongolawo. (Gen. 2:8, 9, 15) Tangoganizani mmene Adamu ankasangalalira akamaona mbewu zikumera komanso zomera zina zikuchita maluwa. Iye analitu ndi mwayi waukulu wosamalira munda wa Edeni. Yehova anapemphanso Adamu kuti apereke mayina kwa nyama zosiyanasiyana. (Gen. 2:19, 20) Yehova akanatha kuchita yekha zimenezi, koma anapereka ntchitoyi kwa Adamu. Mosakayikira, asanapereke mayina kwa nyamazo, Adamu ankaziyang’anitsitsa n’kumaona zimene zikuchita komanso makhalidwe awo. Iye ayenera kuti anasangalala kwambiri kugwira ntchitoyi. N’zoonekeratu kuti izi zinamuthandiza kumvetsa kuti Atate wake ndi wanzeru komanso kuti zinthu zimene analenga ndi zokongola ndi zosangalatsa.

4. (a) Kodi ndi chifukwa chimodzi chiti chomwe chiyenera kutichititsa kuti tizichita chidwi ndi chilengedwe? (b) Kodi ndi zinthu ziti zomwe zimakuchititsani chidwi m’chilengedwechi?

4 Chifukwa chimodzi chotichititsa kuti tizichita chidwi ndi chilengedwe n’chakuti Yehova amafuna kuti tizitero. Iye amatipempha kuti, “Kwezani maso anu kumwamba muone.” Kenako amatifunsa kuti, “Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo?” Yankho ndi lodziwikiratu. (Yes. 40:26) Yehova anadzaza kumwamba, dziko lapansi komanso nyanja ndi zinthu zambiri zomwe zingatiphunzitse zokhudza iye. (Sal. 104:24, 25) Ndipo tangoganizani mmene Mulungu anatilengera anthufe. Anatilenga m’njira yoti tizitha kusangalala ndi zinthu zokongola. Anatilenganso m’njira yoti tizitha kusangalala ndi zinthu zosiyanasiyana poona, kumva, kulawa, kununkhiza komanso kukhudza.

5. Mogwirizana ndi Aroma 1:20, kodi timapindula bwanji chifukwa chophunzira chilengedwe cha Yehova?

5 Baibulo limatiuza chifukwa china chotichititsa kuti tizichita chidwi ndi chilengedwe. Chilengedwe chimatiphunzitsa zokhudza makhalidwe a Yehova. (Werengani Aroma 1:20.) Mwachitsanzo, taganizira zinthu zochititsa chidwi zomwe timaona m’chilengedwe. Kodi sizimatithandiza kudziwa kuti Mulungu ndi wanzeru? Taganiziraninso zakudya zosiyanasiyana zomwe timasangalala nazo. Umenewu ndi umboni woonekeratu woti Yehova amakonda anthu. Tikamamvetsa makhalidwe ake kudzera m’zinthu zimene anapanga timafika pomudziwa bwino kwambiri komanso timakhala naye pa ubwenzi wolimba. Tsopano tiyeni tione njira zina zimene Yehova anagwiritsira ntchito chilengedwe pophunzitsa anthu mfundo zofunika.

MULUNGU AMAGWIRITSA NTCHITO CHILENGEDWE POFUNA KUTIPHUNZITSA ZOKHUDZA IYE

6. Kodi tingaphunzire chiyani kwa mbalame zomwe nthawi zina zimasamuka?

6 Yehova ali ndi nthawi yochitira zinthu. Chaka chilichonse, kuyambira kumapeto kwa February mpaka mkatikati mwa May, Aisiraeli ankaona adokowe akuuluka kulowera chakumpoto. Mulungu anauza Aisiraeli kuti, “Dokowe, mbalame youluka m’mlengalenga, imadziwa bwino nthawi yake yoikidwiratu.” (Yer. 8:7) Mofanana ndi mmene Yehova anachitira poikira nthawi mbalamezi, anaikanso nthawi imene adzapereke ziweruzo zake. Masiku ano tikamaona mbalame zikusamuka kupita dera lina, timakumbutsidwa kuti sitiyenera kukayikira kuti Yehova ali ndi “nthawi yake yoikidwiratu” yoti adzawononge dziko loipali.​—Hab. 2:3.

7. Kodi tingaphunzire chiyani poona mmene mbalame zimaulukira? (Yesaya 40:31)

7 Yehova amapatsa mphamvu atumiki ake. Kudzera mwa Yesaya, iye analonjeza kuti adzapatsa anthu ake mphamvu, ndipo “iwo adzaulukira m’mwamba ngati ali ndi mapiko a chiwombankhanga” pa nthawi imene afooka kapena kukhumudwa. (Werengani Yesaya 40:31.) Sizinali zachilendo kwa Aisiraeli kuona ziwombankhanga zikuulukira m’mwamba kwambiri mosavutikira mothandizidwa ndi mpweya. Zimenezi zimatikumbutsa kuti monga mmene Yehova amaperekera mphamvu kwa mbalamezi, angaperekenso mphamvu kwa atumiki ake. Mukaona mbalame yaikulu ikuulukira m’mwamba kwambiri itangotambasula mapiko ake, muzikumbukira kuti Yehova angakupatseni mphamvu zotha kulimbana ndi mavuto amene mukukumana nawo.

8. Kodi Yobu anaphunzira chiyani pa zinthu zochititsa chidwi zimene Mulungu analenga, nanga ifeyo tingaphunzirepo chiyani?

8 Yehova ndi woyenera kuti tizimudalira. Iye anathandiza Yobu kuti azimukhulupirira kwambiri. (Yobu 32:2; 40:6-8) Pamene ankakambirana ndi Yobu, Mulungu anatchula zinthu zambiri zimene zili m’chilengedwe chake monga nyenyezi, mitambo komanso mphezi. Anatchulanso za nyama monga ng’ombe yamphongo yam’tchire komanso hatchi. (Yobu 38:32-35; 39:9, 19, 20) Zinthu zonsezi zinapereka umboni wosonyeza kuti Mulungu ali ndi mphamvu zodabwitsa, wachikondi komanso ndi wanzeru kwambiri. Chifukwa chokambirana zinthu zimenezi ndi Yehova, Yobu anayamba kumukhulupirira kwambiri kuposa kale. (Yobu 42:1-6) Mofanana ndi zimenezi, tikamaphunzira zinthu zam’chilengedwe timakumbutsidwa kuti Yehova ndi wanzeru kwambiri komanso ali ndi mphamvu kuposa ifeyo. Iye angathenso kuthetsa mayesero amene timakumana nawo ndipo ndi zimene adzachite. Mfundo imeneyi ingatithandize kuti tizimukhulupirira kwambiri.

YESU ANAGWIRITSA NTCHITO CHILENGEDWE POPHUNZITSA ZOKHUDZA ATATE WAKE

9-10. Kodi dzuwa ndi mvula zimatiuza chiyani zokhudza Yehova?

9 Yesu ankadziwa zambiri zokhudza chilengedwe. Monga “mmisiri waluso,” iye anali ndi mwayi wogwira ntchito ndi Atate wake polenga zinthu zam’chilengedwe. (Miy. 8:30) Kenako ali padzikoli, Yesu anagwiritsa ntchito chilengedwe pophunzitsa ophunzira ake zokhudza Atate wake. Taganizirani mfundo zingapo zomwe anaphunzitsa.

10 Yehova amakonda aliyense. Mu ulaliki wake wapaphiri, Yesu anafotokozera ophunzira ake zokhudza dzuwa ndi mvula, zinthu zimene anthu ambiri saziganizira kwenikweni. Zinthu ziwirizi ndi zofunika kwambiri kuti padzikoli pakhale zamoyo. Yehova akanatha kusankha kuti asamapereke zinthuzi kwa anthu omwe samutumikira. M’malomwake, mwachikondi, iye amapereka dzuwa komanso mvula kwa anthu onse. (Mat. 5:43-45) Yesu anagwiritsa ntchito mfundo imeneyi pophunzitsa ophunzira ake kuti Yehova amafuna kuti tizikonda anthu onse. Nthawi zonse tikaona kuwala kwa dzuwa kosangalatsa komanso kamvula kotsitsimula tizikumbukira kuti Yehova amakonda anthu onse. Chitsanzo chake chizitilimbikitsa kuti ifenso tizisonyeza chikondi ngati chimenechi polalikira kwa anthu onse.

11. Kodi tingalimbikitsidwe bwanji tikamachita chidwi ndi mbalame?

11 Yehova amatipatsa zinthu zofunika pa moyo. Pa ulaliki wapaphiri womwewu Yesu ananenanso kuti: “Onetsetsani mbalame zam’mlengalenga, pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola, kapenanso kusunga chakudya m’nkhokwe. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa.” N’kutheka kuti anthu omwe ankamumvetsera Yesu ankaona mbalame zikuuluka m’mwamba pomwe iye anafunsa kuti: “Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?” (Mat. 6:26) M’njira yachikondi imeneyi, Yesu anatitsimikizira kuti Yehova adzatisamalira. (Mat. 6:31, 32) Mfundo imeneyi yomwe timaphunzira m’chilengedwe, ikupitirizabe kulimbikitsa atumiki okhulupirika a Yehova masiku ano. Mpainiya wina wachitsikana ku Spain anakhumudwa chifukwa sankapeza malo abwino okhala. Koma ataona mbalame zikudya mbewu komanso zipatso za m’mitengo analimbikitsidwa kwambiri. Iye anati: “Mbalamezi zinandikumbutsa kuti Yehova amazisamalira ndipo inenso adzandisamalira.” Pasanapite nthawi, mlongoyu anapeza malo okhala.

12. Mogwirizana ndi Mateyu 10:29-31, kodi mpheta zimatithandiza kudziwa zotani zokhudza Yehova?

12 Yehova amationa kuti aliyense payekha ndi wamtengo wapatali. Asanatume atumwi ake kuti akalalikire, Yesu anawathandiza kuti asamaope anthu otsutsa. (Werengani Mateyu 10:29-31.) Iye anawauza za mpheta, zomwe zinali mbalame zodziwika kwambiri ku Isiraeli. Mbalame zimenezi zinali zotsika mtengo m’nthawi ya Yesu. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa.” Kenako anawonjezera kuti: “Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.” Apa Yesu anatsimikizira ophunzira akewo kuti Yehova amaona kuti aliyense payekha ndi wofunika kwambiri, choncho sankafunika kuopa kuzunzidwa. N’zosakayikitsa kuti ophunzirawo ankakumbukira mawu a Yesuwa akaona mpheta pamene ankagwira ntchito yolalikira m’matauni ndi m’midzi. Nthawi iliyonse yomwe mwaona mbalame yaing’ono, muzikumbukira kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali panokha chifukwa inunso “ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.” Mothandizidwa ndi iye, simungamaope anthu ena akamakutsutsani.​—Sal. 118:6.

KODI TINGATANI KUTI TIZIPHUNZIRA ZAMBIRI ZOKHUDZA MULUNGU POONA CHILENGEDWE?

13. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziphunzirapo kanthu pa zinthu zachilengedwe?

13 Tikhoza kuphunzira zambiri zokhudza Yehova m’chilengedwechi. Motani? Choyamba, tifunika kumapeza nthawi yochita chidwi ndi chilengedwe. Kenako tiyenera kumaganizira zimene zinthuzo zikutiphunzitsa zokhudza Yehova. Komatu nthawi zina zingamativute kuchita zimenezi. Mlongo wina wa ku Cameroon dzina lake Géraldine ananena kuti, “Ndinakulira m’tauni, choncho ndimazindikira kuti pamafunika kuyesetsa kuti ndizichita chidwi ndi zachilengedwe.” Mkulu wina dzina lake Alfonso anafotokoza kuti, “Ndaphunzira kuti ndimafunika kukonza nthawi yoti ndikhale pandekha n’kumachita chidwi ndi zimene Yehova analenga komanso kuganizira zimene zinthuzo zikundiphunzitsa zokhudza iye.”

Pochita chidwi ndi zinthu zam’chilengedwe, Davide ankaganizira zomwe zinthuzo zinkamuphunzitsa zokhudza Yehova (Onani ndime 14)

14. Kodi Davide anaphunzira chiyani chifukwa choganizira zimene Mulungu analenga?

14 Davide ankaganizira mozama zimene Mulungu analenga. Iye anauza Yehova kuti: “Ndikayang’ana kumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga, ndimaganiza kuti: Munthu ndani kuti muzimuganizira?” (Sal. 8:3, 4) Davide ankati akayang’ana kumwamba usiku, sikuti ankangogoma ndi kukula kwa chilengedwechi koma ankaganiziranso zimene nyenyezi zinkamuphunzitsa zokhudza Mulungu. Iye anaphunzira kuti Yehova ndi wamkulu kwambiri. Nthawi zinanso ankaganizira mmene thupi lake linayambira m’mimba mwa mayi ake. Akamaganizira mfundo zochititsa chidwizi ankamvetsa kwambiri kuti Yehova ndi wanzeru.​—Sal. 139:14-17.

15. Perekani zitsanzo zosonyeza mmene timaonera makhalidwe a Yehova m’zinthu zimene analenga. (Salimo 148:7-10)

15 Mofanana ndi Davide, sitimachita kufunika kupita kutali kuti tione zinthu zam’chilengedwe zoti tiziganizire. Kulikonse komwe tili tingathe kuona makhalidwe ambiri a Yehova. Mwachitsanzo, tikamamva kutentha kwa dzuwa timazindikira kuti Yehova ndi wamphamvu. (Yer. 31:35) Timachita chidwi ndi nzeru za Mulungu tikamaona mbalame ikumanga chisa. Timadziwanso kuti Yehova ndi wanthabwala tikamaona kagalu kakuthamangitsa mchira wake womwe. Nthawi iliyonse yomwe taona mayi akusewera ndi mwana wake timathokoza Yehova chifukwa cha chikondi chake. Pali zinthu zambiri zomwe zingatithandize kuphunzira zokhudza Yehova chifukwa kaya zinthuzo n’zazikulu kapena zazing’ono, zili kutali kapena pafupi, zimamutamanda.​—Werengani Salimo 148:7-10.

16. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

16 Mulungu wathu ndi wanzeru kwambiri, wachikondi, waluso komanso wamphamvu. Makhalidwe amenewa komanso ena ambiri tingathe kuwaona mosavuta m’zinthu zimene analenga ngati timachita nazo chidwi. Tiyeni tonse tiziyesetsa kupeza nthawi yosangalala ndi zinthu zachilengedwe komanso kumaganizira zimene zinthuzo zikutiphunzitsa zokhudza Yehova. Tikamachita zimenezi tidzakhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Mlengi wathu. (Yak. 4:8) Munkhani yotsatira tidzaona mmene makolo angagwiritsire ntchito chilengedwe pothandiza ana awo kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova.

NYIMBO NA. 5 Ntchito Zodabwitsa za Mulungu

a Chilengedwe cha Yehova n’chodabwitsa. Timachita chidwi ndi zinthu zimene anapanga monga mphamvu yodabwitsa ya dzuwa komanso tinthu tosalimba ngati maluwa. Chilengedwe chingatithandizenso kuzindikira makhalidwe a Yehova. Munkhaniyi, tikambirana chifukwa chake tiyenera kumapeza nthawi yophunzira zinthu zam’chilengedwe komanso mmene kuchita zimenezi kungatithandizire kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu wathu.