NKHANI YOPHUNZIRA 10

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kubatizidwa?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kubatizidwa?

“Aliyense wa inu abatizidwe.”​—MAC. 2:38.

NYIMBO NA. 34 Kuyenda ndi Mtima Wosagawanika

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1-2. Kodi n’chiyani chimene chimachitika nthawi zambiri munthu akamabatizidwa, nanga muyenera kuganizira za chiyani?

 KODI munayamba mwaonapo gulu la anthu amene akukabatizidwa? Muyenera kuti munamva akuyankha motsimikiza mafunso awiri omwe anafunsidwa asanabatizidwe. Munaonanso achibale ndi anzawo akusangalala. Pamene ankatuluka m’madzi, munaona nkhope zawo zili zachimwemwe komanso munamva anthu akuomba m’manja. Tingati pafupifupi mlungu uliwonse anthu masauzande amadzipereka n’kubatizidwa kukhala Mboni za Yehova Mulungu.

2 Kodi zinthu zili bwanji ndi inuyo? Ngati mukufuna kubatizidwa dziwani kuti ndinu munthu wapadera kwambiri m’dziko loipali chifukwa ‘mukufunafuna Yehova.’ (Sal. 14:1, 2) Nkhaniyi yalembedwera inuyo kaya ndinu wamkulu kapena wamng’ono. Komabe ifenso amene tinabatizidwa kale timafunanso kutsimikiza mtima kuti tipitirizabe kutumikira Yehova mpaka kalekale. Choncho tiyeni tikambirane zitatu mwa zifukwa zambiri zimene zimatichititsa kutumikira Yehova.

MUMAKONDA CHOONADI NDI CHILUNGAMO

Satana wakhala akudetsa dzina labwino la Yehova kwa zaka zambiri ndipo akupitirizabe kuchita zimenezi (Onani ndime 3-4)

3. N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova amakonda choonadi ndi chilungamo? (Salimo 119:128, 163)

3 Yehova analamula anthu ake kuti ‘azikonda choonadi.’ (Zek. 8:19) Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti azifunafuna chilungamo. (Mat. 5:6) Zimenezi zikusonyeza kuti munthu ayenera kukhala wofunitsitsa kuchita zoyenera, zabwino komanso zoyera pamaso pa Mulungu. Kodi inuyo mumakonda choonadi ndi chilungamo? Sitikukayikira kuti mumatero. Mumadana ndi mabodza komanso zinthu zonse zoipa. (Werengani Salimo 119:128, 163.) Mabodza amasonyeza makhalidwe a Satana yemwe ndi wolamulira wa dzikoli. (Yoh. 8:44; 12:31) Chimodzi mwa zolinga za Satana ndi kudetsa dzina loyera la Yehova Mulungu. Iye wakhala akufalitsa mabodza okhudza Mulungu wathu kungochokera pamene anachimwitsa Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni. Satana anachititsa kuti anthu aziona ngati Yehova ndi Wolamulira wodzikonda komanso wachinyengo yemwe amamana anthu zinthu zabwino. (Gen. 3:1, 4, 5) Mabodza akewa akhala akuchititsa ambiri kuti azimuona molakwika Yehova. Anthu akasankha kuti ‘asamakonde choonadi,’ Satana angawachititse kuti azichita zosalungama zilizonse komanso makhalidwe oipa.​—Aroma 1:25-31.

4. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti ndi “Mulungu wachoonadi”? (Onaninso chithunzi.)

4 Yehova ndi “Mulungu wachoonadi,” ndipo mofunitsitsa amaphunzitsa choonadicho kwa anthu amene amamukonda. (Sal. 31:5) Amawathandiza kuti asapusitsidwenso ndi mabodza a Satana. Yehova amaphunzitsanso atumiki ake kuti azikhala oona mtima komanso achilungamo. Zimenezi zimathandiza kuti ena aziwalemekeza ndiponso azikhala ndi mtendere wamumtima. (Miy. 13:5, 6) Kodi inuyo mwaona akukuchitirani zimenezi pamene mumaphunzira Baibulo? Mwaphunzira kuti njira za Yehova ndi zabwino kwambiri kwa anthu onse kuphatikizaponso inuyo. (Sal. 77:13) Choncho mumafuna kuchita zimene Mulungu amaona kuti n’zachilungamo. (Mat. 6:33) Mumafuna kukhala kumbali ya choonadi komanso kutsimikizira kuti zimene Satana ananena zokhudza Mulungu wathu Yehova ndi zabodza. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

5. Kodi mungasankhe bwanji kukhala kumbali ya choonadi ndi chilungamo?

5 Zimene mumasankha pa moyo wanu zingakhale ngati mukunena kuti: “Ndimakana mabodza a Satana ndipo ndimakonda choonadi. Ndikufuna kuti Yehova akhale Wolamulira wanga ndipo ndikufuna kuti ndizichita zimene iye amanena kuti n’zoyenera.” Kodi mungachite bwanji zimenezi? Mungachite zimenezi podzipereka kwa Yehova m’pemphero kenako n’kusonyeza poyera kudzipereka kwanuko pobatizidwa. Kukonda choonadi ndi chilungamo ndi chifukwa chachikulu chimene chingakuchititseni kuti musankhe kubatizidwa.

KUKONDA YESU KHRISTU

6. Kodi pa Salimo 45:4, pali zifukwa ziti zokuchititsani kukonda Yesu Khristu?

6 N’chifukwa chiyani mumakonda Yesu Khristu? Taonani zifukwa zina zabwino pa Salimo 45:4. (Werengani.) Iye amakonda choonadi, kudzichepetsa komanso chilungamo. Ngati mumakonda choonadi ndi chilungamo n’zomveka kuti mumakondanso Yesu Khristu. Taganizirani mmene iye anachitira zinthu molimba mtima pokhala kumbali ya choonadi ndi chilungamo. (Yoh. 18:37) Koma kodi Yesu amasonyeza bwanji kuti amalimbikitsa khalidwe la kudzichepetsa?

7. N’chiyani chimakuchititsani chidwi ndi kudzichepetsa kwa Yesu?

7 Yesu amalimbikitsa khalidwe la kudzichepetsa mwa zochita zake. Mwachitsanzo, iye amaonetsetsa kuti ulemerero wonse ukupita kwa Atate wake osati kwa iyeyo. (Maliko 10:17, 18; Yoh. 5:19) Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira kudzichepetsa koteroko? Kodi sizimakuchititsani kuti muzikonda Mwana wa Mulungu komanso kumutsanzira? N’zosachita kufunsa. N’chifukwa chiyani Yesu ali wodzichepetsa? Chifukwa amakonda komanso kutsanzira Atate wake omwe ndi odzichepetsa. (Sal. 18:35; Aheb. 1:3) Kodi zimenezi sizikukuchititsani kuti muzikonda kwambiri Yesu yemwe amasonyeza bwino kwambiri makhalidwe a Yehova?

8. N’chifukwa chiyani timakonda Yesu monga Mfumu yathu?

8 Timakonda Yesu monga Mfumu yathu chifukwa ndi Wolamulira wabwino kwambiri. Yehova anaphunzitsa Mwana wakeyu ndipo anamuika kuti azilamulira. (Yes. 50:4, 5) Ganiziraninso chikondi chololera kuvutikira ena chimene Yesu anasonyeza. (Yoh. 13:1) Monga Mfumu yanu, Yesu ndi woyenerera kuti muzimukonda. Iye anafotokoza kuti anthu amene amamukondadi, omwe amawatchula kuti ndi anzake, amasonyeza chikondicho pomvera malamulo ake. (Yoh. 14:15; 15:14, 15) Ndi mwayitu waukulu kukhala anzake a Mwana wa Yehova.

9. Kodi ubatizo wa Akhristu umafanana bwanji ndi wa Khristu?

9 Limodzi mwa malamulo a Yesu ndi lakuti otsatira ake ayenera kubatizidwa. (Mat. 28:19, 20) Iye anapereka chitsanzo pa nkhaniyi. Komabe ubatizo wake umasiyana m’njira zina ndi wa otsatira ake. (Onani bokosi lakuti “ Kusiyana kwa Ubatizo wa Yesu ndi wa Otsatira Ake.”) Koma m’njira zina ndi wofanana. Pamene anabatizidwa, Yesu anadzipereka kuchita chifuniro cha Atate wake. (Aheb. 10:7) Mofanana ndi zimenezi, otsatira a Khristu amabatizidwa pofuna kusonyeza poyera kuti adzipereka kwa Yehova Mulungu. Apa tsopano chinthu chofunika kwambiri pa moyo wawo chimakhala kuchita chifuniro cha Mulungu osati chawo. Choncho iwo amakhala akutsatira chitsanzo cha Mbuye wawo.

10. N’chifukwa chiyani kukonda Yesu kuyenera kukuchititsani kubatizidwa?

10 Mumavomereza Yesu monga Mwana wobadwa yekha wa Yehova komanso Mfumu imene Mulungu wasankha kuti idzatilamulire. Timadziwa kuti Yesu ndi wodzichepetsa ndipo amatsanzira ndendende makhalidwe a Atate wake. Munaphunzira kuti anadyetsa anjala, analimbikitsa ofooka komanso anachiritsa odwala. (Mat. 14:14-21) Mwaonanso mmene amatsogolerera mpingo wake masiku ano. (Mat. 23:10) Ndipo mukudziwa kuti adzachita zambiri kuposa pamenepo m’tsogolomu monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ndiye kodi mungasonyeze bwanji kuti mumamukonda? Mungachite zimenezo potengera chitsanzo chake. (Yoh. 14:21) Mungayambe ndi kudzipereka kwa Yehova kenako n’kubatizidwa.

KUKONDA YEHOVA MULUNGU

11. Kodi chifukwa chachikulu chokuchititsani kubatizidwa ndi chiyani, nanga n’chifukwa chiyani mukutero?

11 Kodi chifukwa chachikulu chotichititsa kubatizidwa chiyenera kukhala chiyani? Yesu anatchula lamulo lalikulu kwambiri la Mulungu pomwe ananena kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Kodi umu ndi mmene chilili chikondi chanu kwa Mulungu?

Yehova ndi amene amakupatsani zinthu zilizonse zabwino zomwe mumasangalala nazo komanso zimene mudzasangalale nazo m’tsogolo (Onani ndime 12-13)

12. N’chifukwa chiyani mumakonda Yehova? (Onaninso chithunzi.)

12 Pali zifukwa zambiri zokuchititsani kukonda Yehova. Mwachitsanzo, mwafika pomvetsa bwino kuti iye ndi “kasupe wa moyo” komanso kuti ndi amene amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Sal. 36:9; Yak. 1:17) Chilichonse chabwino chomwe mumasangalala nacho chimachokera kwa Mulungu wathu wowolowa manja komanso wachikondi.

13. N’chiyani chimene chimachititsa kuti dipo likhale mphatso yamtengo wapatali?

13 Dipo ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova anatipatsa. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani za ubwenzi wabwino kwambiri wa Yehova ndi Mwana wake. Yesu anati: ‘Atate amandikonda’ komanso “ndimakonda Atate.” (Yoh. 10:17; 14:31) Ubwenziwu unalimba kwambiri chifukwa anakhala limodzi kwa zaka mabiliyoni. (Miy. 8:22, 23, 30) Ndiye taganizani mmene zinamupwetekera Mulungu polola kuti Mwana wakeyu avutike komanso kufa. Yehova amakonda kwambiri anthu kuphatikizapo inuyo moti mpaka analolera kupereka Mwana wake wokondedwa monga nsembe n’cholinga choti inuyo komanso anthu ena mudzakhale ndi moyo mpaka kalekale. (Yoh. 3:16; Agal. 2:20) Chimenechitu ndi chifukwa chachikulu kwambiri chotichititsa kukonda Mulungu.

14. Kodi ndi cholinga chabwino chiti chomwe muyenera kukhala nacho pa moyo wanu?

14 Chikondi chanu kwa Yehova chakula pamene mwakhala mukuphunzira zambiri zokhudza iye. Mosakayikira mumafuna kukhala naye pa ubwenzi wolimba panopa komanso mpaka kalekale. Ndipo n’zotheka. Mokoma mtima iye amakulimbikitsani kuti muzichita zinthu zosangalatsa mtima wake. (Miy. 23:15, 16) Mungachite zimenezi osati ndi mawu okha komanso ndi zochita zanu. Zimene mumachita pa moyo wanu zingasonyeze ngati mumakondadi Yehova. (1 Yoh. 5:3) Chimenechi ndi cholinga chabwino kwambiri chimene mungasankhe pa moyo wanu.

15. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakonda Yehova?

15 Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakonda Yehova? Choyamba muyenera kupereka pemphero panokha losonyeza kuti mukudzipereka kwa Mulungu woona yekha. (Sal. 40:8) Kenako muyenera kusonyeza poyera kudziperekako pobatizidwa. Monga tafotokozera kumayambiriro kwa nkhaniyi, nthawiyi imakhala yosangalatsa komanso yofunika kwambiri pa moyo wanu. Mumayamba moyo watsopano osati wongochita zofuna zanu zokha koma za Yehova. (Aroma 14:8; 1 Pet. 4:1, 2) Imeneyitu ingaoneke ngati nkhani yaikulu ndipo ndi mmene ililidi. Komatu kuchita zimenezi kumakutsegulirani mwayi woti mukhale ndi moyo wabwino kwambiri. Motani?

16. Monga mmene lemba la Salimo 41:12 likusonyezera, kodi Yehova adzawachitira chiyani anthu omwe amadzipereka kuti amutumikire?

16 Yehova ndi wowolowa manja kwambiri. Posatengera zimene inuyo mumamupatsa, nthawi zonse amakupatsani zinthu zambiri. (Maliko 10:29, 30) Iye adzakupatsani moyo wosangalatsa, watanthauzo komanso wokhutiritsa ngakhale panopa m’dziko loipali. Ndipotu ichi n’chiyambi chabe. Moyo umene munayamba mutangobatizidwawu ulibe malire. Mungapitirizebe kutumikira Atate wanu wokondedwa mpaka kalekale. Chikondi pakati pa inu ndi Atate wanu chidzapitiriza kukula. Ndipo pamapeto pake mudzakhala ndi moyo ngati iyeyo, mpaka kalekale.​—Werengani Salimo 41:12.

17. Kodi ndi chiyani chomwe mungamupatse Yehova chomwe alibe?

17 Mukadzipereka komanso kubatizidwa mumakhala ndi mwayi wopereka kwa Atate wanu chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Iye wakupatsani chilichonse chabwino chomwe mumasangalala nacho. Posonyeza kuyamikira inunso mungamupatse Mwiniwake wakumwamba ndi dzikoli chinachake chomwe alibe, chimene ndi kufunitsitsa kwanu kumutumikira modzipereka. (Yobu 1:8; 41:11; Miy. 27:11) Umenewu ndi moyo wabwino kwambiri womwe mungakhale nawo. Mosakayikira, kukonda kwanu Yehova ndi chifukwa chabwino kwambiri chokuchititsani kubatizidwa.

MUKUDIKIRA CHIYANI?

18. Kodi mungadzifunse mafunso ati?

18 Ndiye kodi mungayankhe bwanji funso ili, Kodi mubatizidwa? Ndinu nokha amene mungayankhe funsoli. Komabe zingakhale bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikudikira chiyani?’ (Mac. 8:36) Kumbukirani zifukwa zitatu zimene takambirana. Choyamba n’chakuti mumakonda choonadi komanso chilungamo. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimafuna kudzaona nthawi imene aliyense azidzalankhula choonadi komanso kuchita chilungamo?’ Chachiwiri n’chakuti mumakonda Yesu Khristu. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimafuna kuti Mwana wa Mulungu akhale Mfumu yanga komanso ndimafuna kutsatira chitsanzo chake?’ Ndipo chachitatu komanso choposa zonse ndi chakuti mumakonda Yehova. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimafuna kusangalatsa mtima wa Yehova pomutumikira monga Mulungu wanga?’ Ngati mayankho anu pa mafunsowa ndi akuti inde, ndiye n’chifukwa chiyani simukufuna kubatizidwa? Mukudikira chiyani?​—Mac. 16:33.

19. N’chifukwa chiyani simuyenera kuzengereza pa nkhani yobatizidwa? Perekani chitsanzo. (Yohane 4:34)

19 Ngati mukuzengereza kubatizidwa taganizirani chitsanzo chimene Yesu anagwiritsa ntchito. (Werengani Yohane 4:34.) Palembali Yesu anayerekezera kuchita chifuniro cha Atate wake ndi chakudya. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti chakudya n’chabwino kwa tonsefe. Yesu amadziwa kuti zilizonse zimene Yehova amatiuza kuti tichite zimakhala zabwino kwa ifeyo. Yehova safuna kuti tichite chilichonse chomwe chingativulaze. Kodi zimene Yehova amafuna kuti inuyo muchite zimaphatikizapo kubatizidwa? Inde. (Mac. 2:38) Choncho mungakhale otsimikiza kuti kumvera lakuti mubatizidwe n’kothandiza kwa inuyo. Ngati simungazengereze kudya chakudya chabwino kwambiri, kodi pali chifukwa chilichonse chomwe chingakuchititseni kuti muzengereze kubatizidwa?

20. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

20 Kodi mukudikira chiyani? Ambiri angayankhe kuti, “Panopa sindinakonzeke.” Mfundo ndi yakuti kusankha kuti mudzipereke kwa Yehova komanso kubatizidwa, ndi nkhani yofunika kwambiri pa moyo wanu. Choncho pamafunika nthawi, kuganizira mosamala komanso khama kuti mukhale okonzeka. Koma ngati mukufunitsitsa kubatizidwa, kodi mungatani panopo kuti mukonzekere? Tidzakambirana yankho la funso limeneli munkhani yotsatira.

NYIMBO NA. 28 Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova

a Ubatizo ndi wofunika kwambiri kwa wophunzira Baibulo aliyense. Kodi n’chiyani chingathandize wophunzira Baibulo kuti abatizidwe? Mawu amodzi, chikondi. Kukonda chiyani komanso ndani? Munkhaniyi tipeza mayankho a mafunso amenewa komanso tikambirana mmene moyo wa Mkhristu wobatizidwa umayenera kukhalira.