Yehova Amakonda Anthu Amene ‘Amabereka Zipatso’ Mopirira

Yehova Amakonda Anthu Amene ‘Amabereka Zipatso’ Mopirira

‘Zogwera panthaka yabwino, ndi anthu amene amabereka zipatso mwa kupirira.’​LUKA 8:15.

NYIMBO: 68, 72

1, 2. (a) Kodi anthu amene amalalikirabe mwakhama m’madera omwe anthu ambiri alibe chidwi amatilimbikitsa bwanji? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi Yesu ananena chiyani pa nkhani yolalikira m’dera la kwawo? (Onani mawu a m’munsi.)

SERGIO ndi mkazi wake Olinda ndi apainiya a ku United States, omwe ali ndi zaka za m’ma 80. Masiku ano, amavutika kuyenda chifukwa cha vuto la miyendo. Koma amapitabe pamalo ena pafupi ndi pokwerera basi pamene pamadutsa anthu ambiri ndipo akhala akuchita zimenezi kwa zaka zambiri. Amafika pamalowa 7 koloko m’mawa kuti azigawira mabuku ndi magazini kwa anthu odutsa. Anthu ambiri amangodutsa osawasamala koma iwo sasiya ndipo amamwetulira munthu aliyense amene angawayang’ane. Amachokapo cha m’ma 12 koloko masana n’kumayenda pang’onopang’ono pobwerera kunyumba kwawo. Kukacha m’mawa amapitanso. Banjali limachita zimenezi masiku 6 pa mlungu kwa chaka chonse.

2 Mofanana ndi banjali, abale ndi alongo ambiri akhala akulalikira kwa zaka zambiri m’madera amene anthu ambiri alibe chidwi. Mwina nanunso mumalalikira m’gawo ngati limeneli. Ngati ndi choncho, tikukuthokozani kwambiri chifukwa cha kupirira kwanu. * Dziwani kuti mukamatumikira Yehova mokhulupirika mumalimbikitsa anthu ambiri, kuphatikizapo amene atumikira Yehova kwa nthawi yaitali. Pa nkhani imeneyi, woyang’anira dera wina ananena kuti: “Ndikamalalikira ndi abale ndi alongo okhulupirika chonchi ndimalimbikitsidwa kwambiri.” Woyang’anira dera winanso anati: “Kukhulupirika kwawo kumandithandiza kuti ndisabwerere m’mbuyo komanso ndizilalikira molimba mtima.” Komanso woyang’anira dera wina anati: “Ndimamva bwino kwambiri ndikaganizira chitsanzo chawo.”

3. Kodi tikambirana mafunso atatu ati, nanga kukambirana mafunsowo kungatithandize bwanji?

3 Tiyeni tsopano tikambirane mafunso atatu amene angatithandize kuti tikhalebe ndi mtima wofuna kumaliza nawo ntchito imene Yesu anatipatsa. Mafunso ake ndi akuti: N’chifukwa chiyani tikhoza kukhumudwa nthawi zina? Kodi tingabereke bwanji zipatso? Nanga n’chiyani chingatithandize kuti tiziberekabe zipatso mopirira?

N’CHIFUKWA CHIYANI TIKHOZA KUKHUMUDWA?

4. (a) Kodi Paulo ankamva bwanji pamene Ayuda ankakana uthenga wake? (b) N’chifukwa chiyani Paulo ankamva choncho?

4 Ngati munakhumudwapo chifukwa cholalikira m’dera limene anthu ambiri safuna kumvetsera, mungamvetse bwino zimene mtumwi Paulo ananena. Pa zaka pafupifupi 30 zimene ankalalikira, anathandiza anthu ambiri kuti akhale Akhristu. (Mac. 14:21; 2 Akor. 3:2, 3) Komabe sanathe kuthandiza Ayuda ambiri kuti ayambe kulambira Mulungu m’njira yoyenera. Ayuda ambiri sankamumvera ndipo ena ankamuzunza. (Mac. 14:19; 17:1, 4, 5, 13) Kodi zimenezi zinamukhudza bwanji Paulo? Iye ananena kuti: “Ndikunena zoona mwa Khristu . . . kuti ndili ndi chisoni chachikulu ndiponso mtima ukundipweteka nthawi zonse.” (Aroma 9:1-3) N’chifukwa chiyani Paulo ankamva chonchi? Iye ankalalikira ndi mtima wonse ndipo ankalalikira Ayuda chifukwa chowakonda. Choncho zinkamupweteka kwambiri chifukwa Ayuda ankakana kulandira chifundo cha Mulungu.

5. (a) N’chifukwa chiyani timalalikira kwa anthu? (b) N’chifukwa chiyani nthawi zina timakhumudwa?

5 Mofanana ndi Paulo, timalalikira anthu chifukwa chowakonda. (Mat. 22:39; 1 Akor. 11:1) Timatero chifukwa chodziwa kuti anthu amene ayamba kutumikira Yehova amadalitsidwa kwambiri. Tikaona anthu a m’gawo lathu, timaganiza kuti, ‘Zikanakhala bwino tikanawathandiza kuzindikira madalitso amene angalandire.’ Choncho timapitiriza kulimbikitsa anthu kuti aphunzire za Yehova ndiponso cholinga chake chokhudza anthu. Zili ngati timauza anthuwo kuti: ‘Takubweretserani mphatso yamtengo wapatali kwambiri. Chonde ilandireni.’ M’pake kuti anthu akakana uthenga wathu ‘mtima umatipweteka.’ Tikamamva choncho sikuti tikusowa chikhulupiriro koma zimasonyeza kuti timalalikira chifukwa chokonda anthu. Choncho ngakhale kuti nthawi zina timakhumudwa, timalalikirabe mopirira. Mlongo wina dzina lake Elena, yemwe wakhala akuchita upainiya kwa zaka 25, ananena zimene ambirife tingagwirizane nazo. Iye anati: “Ntchito yolalikira imandivuta koma palibe ntchito ina yabwino kuposa imeneyi.”

KODI TINGABEREKE BWANJI ZIPATSO?

6. Kodi tikambirana funso liti, ndipo tiyankha bwanji funsoli?

6 N’chifukwa chiyani tinganene kuti tikhoza kubereka zipatso mu utumiki ngakhale m’gawo lovuta? Kuti tiyankhe funso lofunikali, tiyeni tikambirane mafanizo awiri a Yesu osonyeza kufunika ‘kobereka zipatso.’ (Mat. 13:23) Fanizo loyamba ndi lonena za mtengo wa mpesa.

7. (a) Mufanizo la Yesu, kodi “mlimi,” “mtengo wa mpesa” komanso “nthambi” zikuimira ndani? (b) Kodi tikambirana funso liti?

7 Werengani Yohane 15:1-5, 8Pavesi 8, Yesu anauza atumwi ake kuti: “Atate amalemekezeka mukapitiriza kubala zipatso zambiri ndi kusonyeza kuti mulidi ophunzira anga.” Mufanizoli, Yesu anati Yehova ali ngati “mlimi,” Yesuyo ali ngati “mtengo wa mpesa weniweni” ndipo ophunzira ake ali ngati “nthambi.” * Ndiye kodi zipatso zimene Akhristu ayenera kubereka zikuimira chiyani? Mufanizoli, Yesu sananene kuti zipatsozi zikuimira chiyani koma anatchula mfundo ina imene ingatithandize kuyankha funso limeneli.

8. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zipatso zamufanizo la Yesu sizikuimira anthu amene tawathandiza kukhala ophunzira ake? (b) Kodi nthawi zonse Yehova amatipempha kuchita zinthu zotani?

8 Yesu ananena kuti Atate ake amadula ‘nthambi iliyonse yosabala zipatso.’ Apa ankatanthauza kuti Yehova amaona kuti ndife atumiki ake enieni pokhapokha ngati timabereka zipatso. (Mat. 13:23; 21:43) Mfundo imeneyi ikusonyeza kuti zipatso zimene Mkhristu aliyense ayenera kubereka sizingaimire anthu amene tinawathandiza kuti akhale ophunzira a Yesu. (Mat. 28:19) Zikanakhala choncho, ndiye kuti Akhristu amene sathandiza anthu kukhala ophunzira chifukwa choti amalalikira m’madera ovuta, akanakhala m’gulu la nthambi zosabereka zipatso. Komatu zimenezo sizingakhale zomveka. Tikutero chifukwa sitingakakamize anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Yehova, yemwe ndi wachikondi, sangakane atumiki ake chifukwa choti alephera kuchita zinthu zimene sangakwanitse. Paja chilichonse chimene Yehova amatipempha kuti tichite chimakhala choti tingachikwanitse.​—Deut. 30:11-14.

9. (a) Kodi timabereka zipatso tikamagwira ntchito iti? (b) Kodi tikambirana fanizo liti, ndipo n’chifukwa chiyani?

9 Ndiye kodi zipatso zimene tiyenera kubereka zikuimira chiyani? Zikuonekeratu kuti zipatsozi zikuimira zinthu zimene aliyense akhoza kukwanitsa. Choncho tinganene kuti “kubereka zipatso” kukuimira kugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. * (Mat. 24:14) Fanizo la Yesu la wofesa mbewu limatsimikiziranso mfundo imeneyi. Tiyeni tsopano tikambirane fanizo limeneli.

10. (a) Mufanizo la Yesu, kodi mbewu komanso nthaka zikuimira chiyani? (b) Kodi mapesi a tirigu amabereka chiyani?

10 Werengani Luka 8:5-8, 11-15. Mufanizo la wofesa mbewu, mbewuzo zikuimira “mawu a Mulungu” kapena kuti uthenga wa Ufumu. Nthaka ikuimira mtima wophiphiritsa wa munthu. Mbewu zimene zimagwera panthaka yabwino zimazika mizu kenako n’kukula. Pamenepa tingati zimakula n’kukhala mapesi a tirigu. Kenako zimabereka “zipatso kuwirikiza maulendo 100.” Koma kodi mapesi a tiriguwo amabereka zipatso zotani? Kodi amakhala mapesi ena? Ayi, timakhala tinjere ta tirigu tomwe tikhoza kudzameranso n’kukhala mapesi ena. Mufanizoli, mbewu imodzi inabereka tinjere 100. Ndiye kodi zimenezi zikugwirizana bwanji ndi utumiki wathu?

Kodi tingabereke bwanji zipatso mopirira? (Onani ndime 11)

11. (a) Kodi fanizo la wofesa mbewu likugwirizana bwanji ndi utumiki wathu? (b) Kodi timabereka bwanji mbewu zatsopano za Ufumu?

11 Kuti timvetse kugwirizana kwake, tiyerekeze kuti zaka zambiri m’mbuyomo, a Mboni ena kapena makolo athu anatiuza uthenga wabwino wa Ufumu. Ndiyeno anasangalala kuona kuti mtima wathu walandira bwino uthengawo, womwe uli ngati mbewu. Mofanana ndi nthaka yabwino ya mufanizoli, tinalandira uthengawo n’kuugwiritsitsa. Ndiye tinganene kuti uthengawo unazika mizu n’kukula ndipo linakhala phesi la tirigu lomwe likhoza kubereka zipatso. Mofanana ndi phesi la tirigu lomwe limabereka tinjere osati mapesi ena, ifenso zipatso zimene timabereka sizikhala ophunzira atsopano koma mbewu zatsopano za Ufumu. * Ndiye kodi timabereka bwanji mbewu zatsopano za Ufumu? Nthawi iliyonse imene timauza anthu uthenga wa Ufumu, timakhala ngati tikuchulukitsa ndiponso kumwaza mbewu imene inafesedwa mumtima mwathu. (Luka 6:45; 8:1) Choncho fanizoli limasonyeza kuti tikamapitiriza kuuza anthu uthenga wa Ufumu, timakhala ‘tikubereka zipatso mopirira.’

12. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la Yesu la mtengo wa mpesa komanso la wofesa mbewu? (b) Kodi inuyo mukumva bwanji ndi zimene mwaphunzira pa mafanizowa?

12 Ndiye kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la Yesu la mtengo wa mpesa komanso la wofesa mbewu? Tikuphunzirapo kuti kubereka zipatso sikudalira zimene anthu amachita akamva uthenga wathu, koma kukhulupirika kwathu pa ntchitoyi. Paulo anatchulanso mfundo yomweyi pamene ananena kuti: “Aliyense payekha adzalandira mphoto yake mogwirizana ndi ntchito yake.” (1 Akor. 3:8) Ananena kuti munthu adzalandira mphoto mogwirizana ndi ntchito yake, osati mogwirizana ndi zotsatira za ntchitoyo. Mlongo wina dzina lake Matilda, amene wakhala akuchita upainiya kwa zaka 20, anati: “Ndimasangalala kwambiri kudziwa kuti Yehova amatipatsa mphoto mogwirizana ndi khama lathu.”

KODI TINGATANI KUTI TIZIPIRIRA POBEREKA ZIPATSO?

13, 14. Malinga ndi Aroma 10:1, 2, kodi ndi zifukwa ziti zimene zinachititsa kuti Paulo asasiye kulalikira anthu amene ankakana uthenga wa Ufumu?

13 N’chiyani chingatithandize kuti tipitirize kubereka zipatso mopirira? Monga tanena kale, Paulo anakhumudwa chifukwa choti Ayuda ankakana uthenga wa Ufumu. Komabe sankawaona ngati anthu okanika. Onani zimene iye anauza Akhristu a ku Roma zokhudza mmene ankaonera Ayuda. Iye anati: “Chimene ndikufunitsitsa mumtima mwanga ndiponso pembedzero langa kwa Mulungu ndi lakuti Aisiraeli apulumutsidwe. Pakuti ndikuwachitira umboni kuti ndi odzipereka potumikira Mulungu, koma samudziwa molondola.” (Aroma 10:1, 2) Kodi Paulo anatchula zifukwa ziti zomwe zinkamuchititsa kuti apitirize kulalikira?

14 Choyamba, Paulo ananena kuti ndi zimene ‘ankafunitsitsa mumtima mwake.’ Iye ankafunitsitsa kuti Ayuda ena adzapulumuke. (Aroma 11:13, 14) Chachiwiri, Paulo anatchula za ‘pembedzero lake kwa Mulungu.’ Iye ankachonderera Mulungu m’pemphero kuti athandize Ayuda kuti azilandira uthenga wa Ufumu. Chachitatu, Paulo ananena kuti Ayuda anali “odzipereka potumikira Mulungu.” Izi zikusonyeza kuti ankaona zinthu zabwino zimene anthu ankachita. Paulo ankadziwa kuti anthu amtima wabwino, omwe ndi odzipereka pa zinthu zina, akhoza kusintha n’kukhala odzipereka potsatira Khristu.

15. Kodi tingatsanzire bwanji Paulo? Perekani zitsanzo.

15 Kodi tingatsanzire bwanji Paulo? Choyamba, tiyenera kukhalabe ndi mtima wofuna kupeza anthu amene ali ndi “maganizo abwino.” Chachiwiri, tiyenera kuchonderera Yehova m’pemphero kuti atsegule mitima ya anthu oterewa. (Mac. 13:48; 16:14) Silvana, yemwe wachita upainiya kwa zaka pafupifupi 30, ananena kuti, “Ndisanapite kunyumba iliyonse mu utumiki, ndimapempha Yehova kuti andithandize kuona anthuwo moyenera.” Tiyeneranso kupempha Mulungu kuti angelo azititsogolera kwa anthu ofuna kumva uthenga wabwino. (Mat. 10:11-13; Chiv. 14:6) M’bale wina dzina lake Robert, yemwe wachita upainiya kwa zaka zoposa 30, anati, “Kugwira ntchito limodzi ndi angelo omwe amadziwa zimene zikuchitikira anthu n’kosangalatsa kwambiri.” Chachitatu, tiyenera kuyesetsa kuona zabwino mwa anthu amene timawalalikira. M’bale wina dzina lake Carl, yemwe ndi mkulu ndipo anabatizidwa zaka zoposa 50 zapitazo, ananena kuti: “Ndimayesetsa kuona zabwino mwa munthu aliyense ngakhale zitakhala zochepa. Ndimaona ngati munthuyo akumwetulira, ngati akuoneka wokoma mtima kapena ngati wafunsa funso labwino.” Mofanana ndi Paulo, nafenso tikhoza kupirira n’kumabereka zipatso.

“DZANJA LAKO LISAPUME”

16, 17. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa malangizo a pa Mlaliki 11:6? (b) Perekani chitsanzo chotsimikizira kuti anthu ena amakhudzidwa akaona tikulalikira.

16 Ngakhale pamene zikuoneka kuti uthenga wa Ufumu sukuwafika anthu pamtima, sitiyenera kuganiza kuti ntchito yathu yofesa mbewu ikupita pachabe. (Werengani Mlaliki 11:6.) N’zoona kuti anthu ambiri samvetsera uthenga wathu koma amaona zimene timachita. Amaona kuti timavala bwino, ndife aulemu komanso timakonda kumwetulira. Anthu akaona khalidwe lathu labwino akhoza kuzindikira kuti zinthu zoipa zimene ankatiganizira si zoona. Zoterezi n’zimene zinachitikira Sergio ndi Olinda amene tawatchula kumayambiriro kwa nkhaniyi.

17 Sergio anati: “Pa nthawi ina sitinkamva bwino m’thupi ndipo sitinapite pamalo aja kwa nthawi ndithu. Titayambiranso kupita, anthu ena anatifunsa kuti, ‘Munasowatu. Chinachitika n’chiyani?’” Nayenso Olinda ananena uku akumwetulira kuti: “Madalaivala a basi ankatibayibitsa ndipo ena ankanena kuti ‘Anthu inu mumachita bwino kwabasi.’ Ena anafika mpaka popempha magazini.” Chodabwitsa kwambiri n’chakuti munthu wina anabwera pamene panali banjali, n’kuwapatsa maluwa powathokoza kuti amagwira ntchito yabwino.

18. N’chifukwa chiyani inuyo mukufunitsitsa ‘kubereka zipatso mopirira’?

18 Choncho ngati timachita khama, osalola kuti dzanja lathu lipume pa ntchito yofesa mbewu za Ufumu, timathandiza kwambiri pochitira “umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Koposa zonse, timasangalala kwambiri podziwa kuti tikusangalatsa Yehova chifukwa iye amakonda anthu onse amene ‘amabereka zipatso mopirira.’

^ ndime 2 Ngakhale Yesu anazindikira kuti zimakhala zovuta kuti munthu azilalikira m’dera la kwawo. Ndipo mfundo imeneyi inatchulidwa ndi anthu 4 onse amene analemba Uthenga Wabwino.​—Mat. 13:57; Maliko 6:4; Luka 4:24; Yoh. 4:44.

^ ndime 7 Ngakhale kuti nthambizi zikuimira anthu opita kumwamba, atumiki a Mulungu onse akhoza kuphunzirapo kanthu pa fanizoli.

^ ndime 9 N’zoona kuti “kubereka zipatso” kungatanthauzenso kukhala ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” Koma munkhaniyi ndiponso yotsatira tikambirana kwambiri za “chipatso cha milomo yathu,” kapena kuti kulalikira za Ufumu.​—Agal. 5:22, 23; Aheb. 13:15.

^ ndime 11 Palinso maulendo ena amene Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo cha kufesa ndi kukolola pofotokoza za ntchito yothandiza anthu kuti akhale ophunzira.​—Mat. 9:37; Yoh. 4:35-38.