NKHANI YOPHUNZIRA 21

Yehova Amatipatsa Mphamvu

Yehova Amatipatsa Mphamvu

“Pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu.”​2 AKOR. 12:10.

NYIMBO NA. 73 Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi ndi mavuto otani amene a Mboni ambiri amakumana nawo?

MTUMWI Paulo analimbikitsa Timoteyo komanso Akhristu onse kuti azichita zonse zomwe angathe pa utumiki wawo. (2 Tim. 4:5) Tonsefe timaona kuti kutsatira malangizo a Paulo n’kofunika kwambiri. Koma nthawi zina kuchita zimenezi kumakhala kovuta. Tikutero chifukwa abale ndi alongo ambiri amafunika kuchita zinthu molimba mtima kuti agwire ntchito yolalikira. (2 Tim. 4:2) Mwachitsanzo, taganizirani za abale athu amene akukhala m’mayiko omwe ntchito yathu ndi yoletsedwa. Iwo amalalikirabe ngakhale kuti zimenezi zingachititse kuti amangidwe.

2 Atumiki a Yehova amakumana ndi mavuto osiyanasiyana omwe akhoza kuwafooketsa. Mwachitsanzo, ena amafunika kugwira ntchito maola ambiri kuti athe kupeza zinthu zofunika posamalira mabanja awo. Iwo amafunitsitsa atachita zambiri pa ntchito yolalikira koma pofika kumapeto kwa mlungu amakhala atatopa. Ndipo ena amalephera kuchita zambiri chifukwa akudwala matenda aakulu kapenanso chifukwa cha uchikulire moti sangathe kuchoka pakhomo. Ndiye pali enanso omwe amavutika ndi maganizo odziona ngati opanda pake. Mlongo wina dzina lake Mary, * yemwe amakhala ku Middle East ananena kuti: “Ndimafunika kuyesetsa kulimbana ndi maganizo odziona ngati wopanda pake omwe amandifooketsa, amene amaononga nthawi komanso mphamvu zomwe ndikanagwiritsa ntchito mu utumiki ndipo zikatero ndimangokhalira kudziimba mlandu.”

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, Yehova angatipatse mphamvu kuti tithe kupirira mavuto athu n’kupitirizabe kumutumikira mmene tingathere. Tisanakambirane mmene iye angatithandizire, tiyeni tione mmene anathandizira Paulo ndi Timoteyo powapatsa mphamvu zoti athe kukwaniritsa utumiki wawo ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto.

AMATIPATSA MPHAMVU KUTI TIZILALIKIRABE

4. Kodi Paulo ankakumana ndi mavuto otani?

4 Paulo ankakumana ndi mavuto ambiri. Iye ankafunika kuti Yehova amuthandize makamaka pa nthawi imene anamenyedwa, kuponyedwa miyala komanso kutsekeredwa m’ndende. (2 Akor. 11:23-25) Paulo anavomerezanso kuti ankalimbana ndi maganizo ofooketsa. (Aroma 7:18, 19, 24) Ankapiriranso vuto lina lomwe analitchula kuti “munga m’thupi,” limene ankafunitsitsa kuti Mulungu alichotse.​—2 Akor. 12:7, 8.

Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kuti akwaniritse utumiki wake (Onani ndime 5-6) *

5. Kodi Paulo anakwanitsa kuchita zinthu ziti ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto?

5 Ngakhale kuti Paulo ankakumana ndi mavuto, Yehova anamupatsa mphamvu kuti akwanitse kuchita utumiki wake. Mwachitsanzo, taganizirani zimene Paulo anakwanitsa kuchita. Pa nthawi imene anali pa ukaidi wosachoka panyumba ku Roma, iye ankachita khama kuteteza uthenga wabwino polankhula ndi atsogoleri a Chiyuda komanso akuluakulu a boma. (Mac. 28:17; Afil. 4:21, 22) Iye analalikiranso Asilikali Oteteza Mfumu komanso anthu omwe ankabwera kudzamuona. (Mac. 28:30, 31; Afil. 1:13) Pa nthawiyi, Paulo analembanso makalata amene akuthandiza Akhristu oona mpaka pano. Chitsanzo cha Paulo chinalimbikitsa mpingo wa ku Roma moti abale anayamba kuonetsa “kulimba mtima kowonjezereka polankhula mawu a Mulungu mopanda mantha.” (Afil. 1:14) Ngakhale kuti Paulo ankalephera kuchita zinthu zina, iye anachita zonse zomwe akanatha ‘pothandiza kupititsa patsogolo uthenga wabwino.’​—Afil. 1:12.

6. Mogwirizana ndi 2 Akorinto 12:9, 10, kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kuti akwanitse utumiki wake?

6 Paulo anazindikira kuti Yehova ndi amene ankamuthandiza pa zonse zimene ankakwanitsa kuchita pomutumikira. Iye anavomereza kuti mphamvu ya Mulungu ‘inkakhala yokwanira iye akakhala wofooka.’ (Werengani 2 Akorinto 12:9, 10.) Ngakhale kuti Paulo ankazunzidwa, kuikidwa m’ndende komanso kukumana ndi mavuto ena, Yehova ankagwiritsa ntchito mzimu wake woyera pomuthandiza kuti akwanitse utumiki wake.

Kodi n’chiyani chinathandiza Timoteyo kuti akwaniritse utumiki wake? (Onani ndime 7) *

7. Kodi Timoteyo ankafunika kulimbana ndi mavuto ati kuti akwanitse utumiki wake?

7 Timoteyo yemwe anali wachinyamata komanso mnzake wa Paulo, ankafunika mphamvu zochokera kwa Mulungu kuti akwanitse utumiki wake. Iye ankayenda ndi Paulo pa maulendo ataliatali a umishonale. Kuwonjezera pamenepo, Paulo ankamutuma kukachezera komanso kulimbikitsa mipingo. (1 Akor. 4:17) N’kutheka kuti nthawi zina Timoteyo ankaona kuti sangakwanitse kuchita zimenezi. Mwina n’chifukwa chake Paulo anamulimbikitsa kuti: “Usalole kuti munthu aliyense akuderere poona kuti ndiwe wamng’ono.” (1 Tim. 4:12) Komanso pa nthawiyi Timoteyo ‘ankadwaladwala,’ zomwe zinali ngati munga m’thupi mwake. (1 Tim. 5:23) Koma iye ankadziwa kuti Yehova angamuthandize pogwiritsa ntchito mzimu wake kuti athe kupitiriza kulalikira uthenga wabwino komanso kutumikira abale ake.​—2 Tim. 1:7.

AMATIPATSA MPHAMVU KUTI TIKHALEBE OKHULUPIRIKA NGAKHALE TIKUMANE NDI MAVUTO

8. Kodi Yehova amapereka bwanji mphamvu kwa atumiki ake masiku ano?

8 Masiku ano Yehova amapatsa atumiki ake “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti apitirize kumutumikira mokhulupirika. (2 Akor. 4:7) Tsopano tiyeni tikambirane zinthu 4, zimene Yehova amatipatsa kuti tikhalebe okhulupirika kwa iye zomwe ndi pemphero, Baibulo, Akhristu anzathu komanso ntchito yolalikira.

Yehova amatipatsa mphamvu pogwiritsa ntchito pemphero (Onani ndime 9)

9. Kodi pemphero lingatithandize bwanji?

9 Pemphero limatipatsa mphamvu. Pa Aefeso 6:18, Paulo amatilimbikitsa kupemphera kwa Mulungu “pa chochitika chilichonse” ndipo iye amatiyankha potipatsa mphamvu. Jonnie, yemwe amakhala ku Bolivia, amaona kuti Yehova anamuthandiza pa nthawi imene anakumana ndi mavuto motsatizanatsatizana. Mkazi wake komanso makolo ake anadwala kwambiri pa nthawi imodzi. Iye ankavutika kwambiri kuti asamalire anthu atatu onsewa. Mayi ake anamwalira ndipo panatenga nthawi yaitali kuti mkazi wake komanso bambo ake ayambenso kupeza bwino. Pokumbukira zimene zinachitikazi, Jonnie ananena kuti, “Chimene chinandithandiza pa nthawi yovutayi ndi kumuuza Yehova m’pemphero mmene ndinkamvera.” Yehova anapatsa Jonnie mphamvu zimene ankafunikira kuti athe kupirira. Amayi ake a Ronald, yemwe ndi mkulu ku Bolivia, anapezeka ndi khansa. Patapita mwezi umodzi iwo anamwalira. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza Ronald kuti apirire? Iye anati: “Kupemphera kwa Yehova kunandithandiza kuti ndizimufotokozera zamumtima mwanga komanso mmene ndinkamvera. Ndimadziwa kuti Yehova amandidziwa bwino kuposa aliyense komanso kuposa mmene ineyo ndimazidziwira.” Nthawi zina tikhoza kupanikizika ndi mavuto mwinanso kufika posowa chonena m’pemphero. Komabe Yehova amatiuza kuti tizipemphera kwa iye pamene tikulephera kufotokoza bwinobwino mmene tikumvera.​—Aroma 8:26, 27.

Yehova amatipatsa mphamvu pogwiritsa ntchito Baibulo (Onani ndime 10)

10. Mogwirizana ndi Aheberi 4:12, kodi kuwerenga Baibulo komanso kuganizira mozama zimene tawerengazo n’kofunika bwanji?

10 Baibulo limatipatsa mphamvu. Paulo ankadalira Malemba kuti azimupatsa mphamvu komanso kumulimbikitsa ndipo ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. (Aroma 15:4) Tikamawerenga komanso kuganizira mozama Mawu a Mulungu, Yehova angatithandize ndi mzimu wake kumvetsa mmene Malembawo angatithandizire pa zimene zikutichitikira. (Werengani Aheberi 4:12.) Ronald, yemwe tamutchula uja ananena kuti: “Ndimaona kuti ndinachita bwino kukhala ndi chizolowezi chowerenga Baibulo usiku uliwonse. Ndimaganizira kwambiri makhalidwe a Yehova komanso mmene amachitira zinthu mwachikondi ndi atumiki ake. Zimenezi zimandithandiza kuti ndipezenso mphamvu.”

11. Kodi Baibulo linathandiza bwanji mlongo wina?

11 Kuganizira mozama zimene tawerenga m’Mawu a Mulungu kungatithandize kukhala ndi maganizo oyenera pa mavuto amene takumana nawo. Tiyeni tione mmene Baibulo linathandizira mlongo wina wamasiye yemwe anali ndi chisoni chachikulu. Mkulu wina anamuuza kuti angapeze mfundo zothandiza ngati atawerenga buku la Yobu. Atangoyamba kuwerenga bukuli, mlongoyu ankaona kuti Yobu anali ndi maganizo olakwika ndipo mumtima mwake anayamba kumudzudzula kuti: “Yobu, amenewotu si maganizo abwino.” Koma kenako anazindikira kuti nayenso anali ndi maganizo olakwika ngati Yobu. Zimenezi zinamuthandiza kuti asinthe n’kuyamba kuona zinthu moyenera komanso zinamupatsa mphamvu kuti athe kupirira ululu umene ankamva chifukwa cha imfa ya mwamuna wake.

Yehova amatipatsa mphamvu pogwiritsa ntchito Akhristu anzathu (Onani ndime 12)

12. Kodi Yehova amatipatsa bwanji mphamvu kudzera mwa olambira anzathu?

12 Akhristu anzathu amatipatsa mphamvu. Njira ina imene Yehova amatipatsira mphamvu ndi kudzera mwa olambira anzathu. Paulo analemba kuti ankalakalaka atakumana ndi abale ndi alongo n’cholinga choti ‘alimbikitsane.’ (Aroma 1:11, 12) Mary, yemwe tamutchula kale uja amasangalala kukhala limodzi ndi abale ndi alongo. Iye anati: “Yehova wandithandizapo pogwiritsa ntchito abale ndi alongo amene sankadziwa n’komwe mavuto omwe ndikukumana nawo. Iwo ankalankhula mawu ondilimbikitsa kapenanso kunditumizira khadi ndipo ndi zimene ndinkafunikiradi. Chinanso chimene chinandithandiza ndi kucheza ndi alongo amene anakumana ndi mavuto ngati anga n’kuphunzirapo pa zimene anachita. Komanso nthawi zonse akulu amandithandiza kuti ndiziona kuti ndine wofunika mumpingo.”

13. Kodi tingalimbikitsane bwanji tikakhala pamisonkhano?

13 Malo ena abwino amene tingakalimbikitsane ndi kumisonkhano yathu. Mukapita kumisonkhano, muzikhala oyamba kulimbikitsa anzanu komanso kuwayamikira kuchokera pansi pa mtima. Mwachitsanzo, pa nthawi ina misonkhano isanayambe, Peter amene ndi mkulu, anauza mlongo wina yemwe mwamuna wake si wa Mboni kuti: “Timalimbikitsidwa kwambiri kuona kuti nthawi zonse mumafika pamisonkhano. Ana anu onse 6 amakhala akuoneka bwino komanso amakhala okonzeka kupereka ndemanga.” Mlongoyo anayankha kwinaku akugwetsa misozi yachisangalalo kuti: “Simungamvetse kuti ndimafunikiradi kumva mawu ngati amenewa lero.”

Yehova amatipatsa mphamvu pogwiritsa ntchito ntchito yolalikira (Onani ndime 14)

14. Kodi kugwira ntchito yolalikira kumatithandiza bwanji?

14 Ntchito yolalikira imatipatsa mphamvu. Tikamauza ena choonadi cha m’Baibulo, timamva bwino komanso timalimbikitsidwa kaya anthuwo amvetsera kapena ayi. (Miy. 11:25) Mlongo wina dzina lake Stacy anaona mmene kugwira ntchito yolalikira kunamulimbikitsira. Wachibale wake atachotsedwa anakhumudwa ndipo nthawi zambiri ankadzifunsa kuti, ‘Kodi pali zinazake zimene ndikanachita kuti ndimuthandize?’ Zinkamuvuta kuti aiwale zimene zinachitikazi. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza? Kugwira ntchito yolalikira. Akamagwira ntchito yolalikira, ankaganizira kwambiri mmene angathandizire anthu a m’gawo lake. Iye ananena kuti: “Pa nthawi imeneyi Yehova anandithandiza kupeza wophunzira Baibulo amene ankapita patsogolo kwambiri ndipo zimenezi zinandilimbikitsa. Panopa chimene chimandithandiza kwambiri ndi kugwira ntchito yolalikira.”

15. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Mary ananena?

15 Chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wawo, ena angamaone kuti sakuchita zambiri mu utumiki. Ngati inunso mumamva choncho muzikumbukira kuti Yehova amasangalala mukamachita zonse zomwe mungathe pomutumikira. Taganizirani chitsanzo cha Mary, yemwe tamutchula kale uja. Atasamukira kugawo limene anthu ake amalankhula chinenero china, ankaona kuti sakuchita zambiri. Iye anati: “Kwa kanthawi, zomwe ndinkakwanitsa ndi kungopereka ndemanga yachidule, kuwerenga lemba kapena kugawira kapepala basi.” Zimenezi zinamuchititsa kuti azidziona ngati sakuchita zambiri poyerekezera ndi anthu omwe amadziwa bwino chinenerocho. Komabe iye anasintha mmene ankaonera zinthu. Anazindikira kuti Yehova angamugwiritse ntchito ngakhale kuti satha kulankhula bwino chinenero cha kuderalo. Iye ananena kuti: “Mfundo zachoonadi ndi zosavuta ndipo ndi zimene zimasintha anthu.”

16. N’chiyani chingathandize anthu amene sangathe kuchoka panyumba kuti apezenso mphamvu?

16 Yehova amayamikira akamaona kuti timafunitsitsa kugwira ntchito yolalikira ngakhale kuti sitingathe kuchoka panyumba. Iye angatithandize kuti tizilalikira kwa madokotala kapena anthu ena amene amatisamalira. Tikamayerekezera zimene tikuchita panopa ndi zimene tinkachita kale, tikhoza kufooka. Koma tikamaganizira mmene Yehova akutithandizira tidzapeza mphamvu zimene zingatithandize kuti tizipirira mayesero alionse mosangalala.

17. Mogwirizana ndi Mlaliki 11:6, n’chifukwa chiyani tiyenera kupitirizabe kulalikira ngakhale pamene sitikuona zotsatira zake nthawi yomweyo?

17 Sitingadziwiretu kuti ndi mbewu ziti zachoonadi zimene tadzala, zomwe zingamere n’kukula. (Werengani Mlaliki 11:6.) Mwachitsanzo, mlongo wina wazaka 80 dzina lake Barbara, nthawi zambiri amalalikira pafoni komanso kulemba makalata. M’kalata ina anaikamo Nsanja ya Olonda ya March 1, 2014, yomwe munali nkhani ya mutu wakuti, “Kodi ndi Zinthu Ziti Zimene Mulungu Wakuchitirani?” Mosadziwa iye anatumiza kalatayo kwa banja lina lomwe linali litasiya choonadi. Banjali linawerenga magaziniyo mobwerezabwereza. Mwamuna wa m’banjali ankangomva ngati Yehova akumulankhula mwachindunji. Pambuyo pa zaka 27 kuchokera pamene anasiya choonadi, iwo anayambiranso kupezeka pamisonkhano n’kukhalanso a Mboni za Yehova. Tangoganizani mmene Barbara analimbikitsidwira kuona mmene kalata imodzi yokha imene analemba inathandizira banjali.

Yehova amatipatsa mphamvu pogwiritsa ntchito (1) pemphero, (2) Baibulo, (3) Akhristu anzathu, and (4) ntchito yolalikira (Onani ndime 9-10, 12, 14)

18. Kodi tingatani kuti Mulungu azitipatsa mphamvu?

18 Yehova amatipatsa mphamvu kudzera m’njira zosiyanasiyana. Tikamagwiritsa ntchito zinthu zimene amatipatsa monga pemphero, Baibulo, Akhristu anzathu komanso ntchito yolalikira timasonyeza kuti timakhulupirira kuti iye ndi wofunitsitsa kutithandiza. Choncho tiyeni nthawi zonse tizidalira Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi wokonzeka “kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.”​—2 Mbiri 16:9.

NYIMBO NA. 61 Pitani Patsogolo Mboninu

^ ndime 5 Tikukhala mu nthawi yovuta kwambiri, koma Yehova amatithandiza kupirira. Munkhaniyi tikambirana mmene anathandizira mtumwi Paulo ndi Timoteyo kuti apitirizebe kumutumikira ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto. Tikambirananso zinthu 4 zimene Yehova watipatsa kuti tithe kupirira masiku ano.

^ ndime 2 Dzina lasinthidwa.

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Pa nthawi imene Paulo ali pa ukaidi wosachoka panyumba ku Roma, akulembera mipingo makalata komanso akulalikira uthenga wabwino kwa anthu omwe abwera kudzamuona.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI:Timoteyo akuchezera mipingo n’kumalimbikitsa abale.