NKHANI YOPHUNZIRA 21

Mmene Yehova Amayankhira Mapemphero Athu

Mmene Yehova Amayankhira Mapemphero Athu

“Timadziwa kuti amatimvera tikapempha chilichonse, timakhala ndi chikhulupiriro kuti tilandira zinthu zimene tamupemphazo.”​—1 YOH. 5:15.

NYIMBO NA. 41 Mulungu Imvani Pemphero Langa

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1-2. Kodi nthawi zina tingadzifunse chiyani pa nkhani ya mapemphero athu?

 KODI munadzifunsapo ngati Yehova amayankha mapemphero anu? Ngati ndi choncho dziwani kuti si inu nokha. Abale ndi alongo enanso anadzifunsapo zimenezi, makamaka pa nthawi yomwe ankakumana ndi mavuto. Ngati ifenso tikukumana ndi mavuto, zingakhale zovuta kuzindikira mmene Yehova akuyankhira mapemphero athu.

2 Tiyeni tikambirane chifukwa chake sitiyenera kukayikira kuti Yehova amayankha mapemphero a atumiki ake. (1 Yoh. 5:15) Tikambirananso mafunso awa: N’chifukwa chiyani nthawi zina zingaoneke ngati Yehova sakuyankha mapemphero athu? Kodi Yehova amayankha bwanji mapemphero athu masiku ano?

NTHAWI ZINA YEHOVA SANGAYANKHE M’NJIRA IMENE TIMAYEMBEKEZERA

3. N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizipemphera kwa iye?

3 Malemba amatitsimikizira kuti Yehova amatikonda kwambiri komanso ndife a mtengo wapatali kwa iye. (Hag. 2:7; 1 Yoh. 4:10) N’chifukwa chake amatiuza kuti tizimupempha kuti azitithandiza. (1 Pet. 5:6, 7) Iye amafuna kutithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba komanso tizipirira mavuto amene tikukumana nawo.

Yehova anayankha mapemphero a Davide pomupulumutsa kwa adani ake komanso (Onani ndime 4)

4. Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amayankha mapemphero a atumiki ake? (Onaninso chithunzi.)

4 Nthawi zambiri timawerenga m’Baibulo kuti Yehova anayankha mapemphero a atumiki ake. Kodi ndi chitsanzo chiti chomwe mukuchiganizira? Bwanji za Mfumu Davide? Iye anakumana ndi adani ambiri oopsa pa moyo wake, ndipo nthawi zambiri ankapemphera kwa Yehova kuti amuthandize. Pa nthawi ina iye anachonderera Yehova kuti: “Inu Yehova, imvani pemphero langa. Tcherani khutu pamene ndikuchonderera. Ndiyankheni mogwirizana ndi kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu.” (Sal. 143:1) Yehova anayankha mapemphero a Davide oti amupulumutse. (1 Sam. 19:10, 18-20; 2 Sam. 5:17-25) Mpake kuti Davide ananena motsimikiza kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.” Ifenso tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza.​—Sal. 145:18.

Yehova anayankha mapemphero a Paulo pomupatsa mphamvu zimene ankafunikira kuti apirire (ndime 5)

5. Kodi nthawi zonse Yehova ankayankha mapemphero a atumiki ake m’njira imene iwo ankayembekezera? Perekani chitsanzo. (Onaninso chithunzi.)

5 Nthawi zina Yehova sangayankhe mapemphero athu m’njira imene timayembekezera. Izi ndi zimenenso zinachitikira mtumwi Paulo. Iye anapempha Mulungu kuti amuchotsere “munga m’thupi.” Katatu konse anapempherera za vuto limeneli. Kodi Yehova anayankha mapemphero amenewo? Inde, koma osati m’njira imene Paulo ankayembekezera. M’malo mochotsa vutolo, Yehova anamupatsa mphamvu zomwe ankafunikira kuti apitirize kumutumikira mokhulupirika.​—2 Akor. 12:7-10.

6. N’chifukwa chiyani nthawi zina zingaoneke ngati Yehova sakuyankha mapemphero athu?

6 Nthawi zina ifenso tingayankhidwe mapemphero athu m’njira imene sitimayembekezera. Koma tingakhale otsimikiza kuti Yehova amadziwa njira yabwino kwambiri yotithandizira. Iye “angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.” (Aef. 3:20) Pa chifukwa chimenechi, iye angayankhe mapemphero athu pa nthawi komanso m’njira imene sitimayembekezera.

7. N’chifukwa chiyani nthawi zina timafunika kusintha zimene timapempherera? Perekani chitsanzo.

7 Pamene tikumvetsa bwino cholinga cha Mulungu, nthawi zina tingafunike kusintha zomwe tikupempherera. Taganizirani zimene zinachitikira M’bale Martin Poetzinger. Atangokwatira kumene, M’bale Poetzinger anatsekeredwa mundende yozunzirako anthu ya Nazi. Poyamba iye anapempha Yehova kuti amuthandize kutuluka mundendeyi n’cholinga choti azikasamalira mkazi wake komanso kupitiriza kugwira ntchito yolalikira. Koma patapita milungu iwiri, iye sanaone chizindikiro chilichonse chosonyeza kuti Yehova amuthandiza kutuluka. Choncho anayamba kupemphera kuti: “Yehova, chonde ndidziwitseni zimene mukufuna kuti ndichite.” Kenako anayamba kuganizira mavuto amene abale ambiri mundendemo ankakumana nawo. Ambiri ankadera nkhawa akazi ndi ana awo. Ndiyeno M’bale Poetzinger anapemphera kuti: “Yehova, zikomo kwambiri chifukwa chondipatsa utumiki watsopano. Ndithandizeni kuti ndizilimbikitsa abale anga.” Izi ndi zomwe ankachita pa zaka 9 zimene anali mundende.

8. Kodi tiyenera kukumbukira mfundo yofunika iti tikamapemphera?

8 Tizikumbukira kuti Yehova ali ndi cholinga, ndipo adzachikwaniritsa pa nthawi yake. Cholinga chakechi chikuphatikizapo kuchotseratu mavuto onse omwe anthu amakumana nawo monga ngozi zam’chilengedwe, matenda komanso imfa. Yehova adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito Ufumu wake. (Dan. 2:44; Chiv. 21:3, 4) Komabe panopa walola kuti Satana azilamulira dzikoli. b (Yoh. 12:31; Chiv. 12:9) Ngati Yehova atati azithetsa mavuto a anthu panopa, mwa njira inayake zingaoneke ngati Satana akulamulira bwino. Komabe pamene tikuyembekezera kuti Yehova akwaniritse malonjezo ake, sizikutanthauza kuti tikakumana ndi mavuto satithandiza. Tiyeni tikambirane njira zina zimene Yehova amatithandizira.

MMENE YEHOVA AMAYANKHIRA MAPEMPHERO ATHU MASIKU ANO

9. Kodi Yehova angatithandize bwanji pamene tikufunika kusankha zochita? Perekani chitsanzo.

9 Amatipatsa nzeru. Yehova amalonjeza kuti azitipatsa nzeru zomwe timafunikira kuti tizisankha bwino pa nkhani zosiyanasiyana. Timafunika nzeru za Mulungu makamaka tikamasankha zochita pa nkhani zomwe zidzatikhudze kwa moyo wathu wonse, monga nkhani yokhudza kukhala pabanja kapena kusakhala pabanja. (Yak. 1:5) Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina wosakwatiwa dzina lake Maria. c Iye anali akusangalala kuchita upainiya pamene anakumana ndi m’bale wina. Maria anati: “Titayamba kugwirizana kwambiri tinayambanso kukondana. Ndinkadziwa kuti ndiyenera kusankha zochita ndipo ndinapempherera za nkhaniyi kwa nthawi yayitali. Ndinkafunika kutsogoleredwa ndi Yehova koma ndinkadziwanso kuti iye sangandisankhire zochita.” Maria amaona kuti Yehova anayankha pemphero lake loti amuthandize kusankha zochita mwanzeru. Motani? Pamene ankafufuza m’mabuku athu, anapeza nkhani zimene zinkayankha mafunso omwe anali nawo. Iye anatsatiranso malangizo a nzeru omwe mayi ake anamupatsa. Malangizowo anamuthandiza kuti aganizire mmene ankamvera. Pamapeto pake iye anasankha zinthu mwanzeru.

Kodi Yehova amatipatsa bwanji mphamvu kuti tipirire? (Onani ndime 10)

10. Mogwirizana ndi Afilipi 4:13, kodi Yehova adzachita chiyani pothandiza atumiki ake? Perekani chitsanzo. (Onaninso chithunzi.)

10 Amatipatsa mphamvu kuti tipirire. Monga mmene anachitira ndi Paulo, Yehova angatipatsenso mphamvu kuti tipirire mayesero amene tikukumana nawo. (Werengani Afilipi 4:13.) Taganizirani mmene Yehova anathandizira m’bale wina dzina lake Benjamin kuti apirire mavuto omwe ankakumana nawo. Kwa nthawi yaitali ali wachinyamata, iye ndi makolo ake ankakhala m’malo osiyanasiyana osungirako anthu othawa kwawo, ku Africa. Benjamin anati: “Ndinkapemphera pafupipafupi kwa Yehova, kumupempha kuti andipatse mphamvu zoti zindithandize kuchita zomwe zimamusangalatsa. Yehova anayankha mapemphero anga pondipatsa mtendere wamumtima, kundithandiza kuti ndisasiye kulalikira komanso kundipatsa mabuku omwe anandithandiza kuti ndikhale pa ubwenzi wolimba ndi iye.” Iye anapitiriza kuti: “Kuwerenga zimene zinachitikira a Mboni ena komanso kuphunzira mmene Yehova anawathandizira kupirira, kunandithandiza kuti nditsimikize mtima kupitirizabe kukhala wokhulupirika.”

Kodi Yehova anakuthandizanipo pogwiritsa ntchito Akhristu anzanu? (Onani ndime 11-12) d

11-12. Kodi Yehova angagwiritse ntchito bwanji abale ndi alongo kuyankha mapemphero athu? (Onaninso chithunzi.)

11 Amagwiritsa ntchito abale ndi alongo athu. Pa usiku wake womaliza asanapereke moyo wake monga nsembe, Yesu anapemphera mochokera pansi pamtima. Iye anachonderera Yehova kuti asalole kuti anthu ena azimuona ngati wonyoza Mulungu. Koma m’malo mochita zomwe anapemphazo, Yehova anathandiza Yesu pomutumizira mmodzi mwa angelo ake kuti akamulimbikitse. (Luka 22:42, 43) Ifenso Yehova angatithandize kudzera mwa m’bale kapena mlongo yemwe watiimbira foni kapena kutiyendera kuti atilimbikitse. Tonsefe tikhoza kupeza mipata yoti tizilankhula “mawu abwino” kwa Akhristu anzathu.​—Miy. 12:25.

12 Taganizirani zomwe zinachitikira mlongo wina dzina lake Miriam. Patapita milungu ingapo kuchokera pamene mwamuna wake anamwalira, iye anali yekha kunyumba ndipo anali ndi chisoni chachikulu komanso anasokonezeka maganizo. Ankangolira ndipo ankafuna atalankhula ndi winawake. Iye anati: “Ndinalibe mphamvu zoti n’kuimbira foni aliyense, choncho ndinapemphera kwa Yehova. Pamene ndinkalira komanso kupemphera, ndinangomva foni yanga ikuitana, ndipo yemwe anaimbayo anali mkulu yemwenso tinkagwirizana naye.” Mkuluyu ndi mkazi wake anamulimbikitsa Miriam. Iye amakhulupirira kuti Yehova ndi amene anachititsa kuti mkuluyu amuimbire.

Kodi Yehova angagwiritse ntchito bwanji anthu ena kuti atithandize? (Onani ndime 13-14)

13. Fotokozani chitsanzo chosonyeza mmene Yehova angagwiritsire ntchito anthu omwe samutumikira poyankha mapemphero athu.

13 Angagwiritse ntchito anthu omwe si atumiki ake. (Miy. 21:1) Nthawi zina Yehova amayankha mapemphero a atumiki ake polimbikitsa anthu omwe samutumikira kuti awathandize. Mwachitsanzo, iye analimbikitsa Mfumu Aritasasita kuti avomere zimene Nehemiya anapempha, zoti abwerere ku Yerusalemu kukathandiza pa ntchito yomanganso mzindawo. (Neh. 2:3-6) Masiku anonso Yehova angachititse anthu omwe samutumikira kuti atithandize pomwe tikufunika thandizo.

14. Kodi zimene zinachitikira Soo Hing zakulimbikitsani bwanji? (Onaninso chithunzi.)

14 Mlongo wina dzina lake Soo Hing, amaona kuti Yehova anamuthandiza kudzera mwa dokotala wake. Mwana wake wamwamuna amadwala matenda osiyanasiyana a maganizo. Mwana wawoyo atachita ngozi, mlongoyo ndi mwamuna wake anasiya ntchito kuti azimusamalira. Zimenezi zinachititsa kuti iwo akumane ndi vuto la zachuma. Soo Hing anaona kuti zinafika poti sangathe kupiriranso. Iye anapemphera kwa Yehova kuchokera pansi pamtima kuti amuthandize. Dokotala wawo uja anayesetsa kufufuza njira zoti awathandizire. Chifukwa cha zimenezi, iwo analandira thandizo kuchokera kuboma komanso anapeza malo okhala. Pambuyo pake Soo Hing ananena kuti: “Tinaona mmene Yehova ankatithandizira pa nkhaniyi. Kunena zoona, iye ndi ‘Wakumva pemphero.’”​—Sal. 65:2.

PAMAFUNIKA CHIKHULUPIRIRO KUTI TIFUFUZE NDI KUVOMEREZA MMENE YEHOVA AKUYANKHIRA MAPEMPHERO ATHU

15. Kodi n’chiyani chimene chinathandiza mlongo wina kudziwa kuti Yehova ankayankha mapemphero ake?

15 Si nthawi zonse pamene mapemphero athu amayankhidwa m’njira yodabwitsa. Koma mayankho amene Yehova amapereka amatithandiza kuti tikhalebe okhulupirika kwa Atate wathu wakumwambayu. Choncho muzikhala tcheru kuti muone mmene Yehova akuyankhira mapemphero anu. Mlongo wina dzina lake Yoko ankaona kuti Yehova sankayankha mapemphero ake, koma kenako anayamba kumalemba m’buku lake zimene wapempha. Patapita kanthawi, iye anayang’ananso m’buku lake lija ndipo anazindikira kuti Yehova anali atayankha mapemphero ake ambiri ngakhalenso ena omwe anali atawaiwala. Nthawi ndi nthawi timafunika kumaima kaye n’kuganizira mmene Yehova akuyankhira mapemphero athu.​—Sal. 66:19, 20.

16. Kodi tingasonyeze bwanji chikhulupiriro pa nkhani ya pemphero? (Aheberi 11:6)

16 Timasonyeza chikhulupiriro, osati popemphera kwa Yehova yekha, koma povomerezanso yankho la pemphero lathu kaya yankholo likhale lotani. (Werengani Aheberi 11:6.) Taganizirani chitsanzo cha Mike ndi mkazi wake Chrissy. Iwo ankafuna atakatumikira pa Beteli. Mike anati, “Kwa zaka zambiri tinafunsira utumikiwu komanso kupemphera kwa Yehova mobwerezabwereza kuti atithandize kukwaniritsa cholinga chathuchi koma sitinaitanidwe ku Beteli.” Mike ndi Chrissy sankakayikira kuti Yehova amadziwa mmene angawagwiritsire bwino ntchito pa utumiki wake. Choncho iwo anapitiriza kuchita zonse zomwe angathe pochita upainiya wokhazikika komwe kunkafunika olalikira ambiri komanso kuthandiza pantchito zomangamanga. Panopa Mike ndi woyang’anira dera. Iye anati, “Si nthawi zonse pamene Yehova wakhala akuyankha mapemphero athu m’njira imene timayembekezera koma wakhala akuwayankha m’njira yabwino kwambiri kuposa mmene timaganizira.”

17-18. Mogwirizana ndi Salimo 86:6, 7, kodi tiyenera kukhala otsimikiza za chiyani?

17 Werengani Salimo 86:6, 7. Wolemba masalimo Davide ankakhulupirira kuti Yehova amva komanso kuyankha mapemphero ake. Inunso mungamakhulupirire zimenezi. Zitsanzo zomwe takambirana munkhaniyi, zikutitsimikizira kuti Yehova angatipatse nzeru komanso mphamvu zimene timafunikira kuti tipirire. Iye angagwiritse ntchito abale ndi alongo kapenanso anthu omwe panopa sakumutumikira kuti atithandize mwanjira inayake.

18 Ngakhale kuti sinthawi zonse pamene Yehova angayankhe mapemphero athu m’njira imene timayembekezera, timadziwa kuti adzatiyankha. Iye adzatipatsa zenizeni zimene tikufunikira komanso pa nthawi yomwe zikufunikira. Choncho pitirizani kupemphera muli ndi chikhulupiriro choti Yehova azikusamalirani panopa komanso kuti ‘adzakhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse’ m’dziko latsopano lomwe likubwera.​—Sal. 145:16.

NYIMBO NA. 46 Timakuyamikirani Yehova

a Yehova amatitsimikizira kuti adzayankha mapemphero athu ngati ali ogwirizana ndi chifuniro chake. Pamene tikukumana ndi mayesero, sitingakayikire kuti adzatithandiza kukhalabe okhulupirika kwa iye. Tiyeni tione mmene Yehova amayankhira mapemphero athu.

b Kuti mudziwe chifukwa chake Yehova walola kuti Satana azilamulira dzikoli, onani nkhani yakuti “Musamaiwale Nkhani Yofunika Kwambiri,” mu Nsanja ya Olonda ya June 2017.

c Mayina ena asinthidwa.

d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mayi ndi mwana wake afika m’dziko lina monga anthu othawa kwawo. Akhristu anzawo awalandira mwachikondi komanso akuwathandiza m’njira zosiyanasiyana.