NKHANI YOPHUNZIRA 22

Pitirizani Kuyenda pa “Msewu wa Chiyero”

Pitirizani Kuyenda pa “Msewu wa Chiyero”

“Kumeneko kudzakhala msewu waukulu, . . . Msewu wa Chiyero.”​—YES. 35:8.

NYIMBO NA. 31 Yendani ndi Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1-2. Kodi Ayuda omwe ankakhala ku Babulo ankafunika kusankha pa nkhani yofunika iti? (Ezara 1:2-4)

 PANALI pataperekedwa chilengezo choti Ayuda omwe anali akapolo kwa zaka 70 ku Babulo, akanatha kubwerera kwawo ku Isiraeli. (Werengani Ezara 1:2-4.) Yehova yekha ndi amene akanachititsa kuti zimenezi zitheke. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Ababulo sankamasula akapolo. (Yes. 14:4, 17) Koma mzinda wa Babulo unali utagonjetsedwa ndipo mfumu yatsopano inauza Ayuda kuti akhoza kuchoka m’dzikolo. Chifukwa cha zimenezi, Myuda aliyense, makamaka mitu ya mabanja, ankafunika kusankha zochita kuti achoke ku Babulo kapena ayi. Komatu kusankha zochita pa nkhaniyi sikunali kophweka. Chifukwa chiyani?

2 Ayuda ena anali achikulire kwambiri moti zikanakhala zovuta kuyenda ulendo wovutawu. Komanso Ayuda ambiri anabadwira ku Babulo komweko ndipo anali asanakhalepo kwina kulikonse. Choncho kwa iwowa, ku Isiraeli kunali kwawo kwa makolo awo. Ayuda enanso zinthu zinkawayendera bwino ku Babulo, choncho zikanakhala zovuta kusiya nyumba zawo zabwino komanso mabizinesi awo n’kumakakhala m’dziko lachilendo.

3. Kodi Ayuda okhulupirika omwe akanabwerera ku Isiraeli akanapeza madalitso otani?

3 Kwa Ayuda okhulupirika, kubwerera ku Isiraeli kunali kofunika kwambiri kuposa chilichonse chomwe akanasiya. Chofunika kwambiri chinali chakuti zinthu zikanayambiranso kuwayendera bwino pa nkhani ya kulambira. Ngakhale kuti ku Babulo kunali akachisi achikunja oposa 50, kunalibeko kachisi wa Yehova. Kunalibe guwa limene Aisiraeli akanamaperekapo nsembe zomwe zinkafunika malinga ndi Chilamulo cha Mose. Komanso kunalibe ansembe omwe akanamapereka nsembezo. Kuwonjezera pamenepo, anthu a Yehova anali ochepa kwambiri poyerekeza ndi amuna ndi akazi achikunja omwe sankalemekeza Yehova kapenanso mfundo zake. Choncho Ayuda ambiri okhulupirika ankafunitsitsa atabwerera kwawo kuti akabwezeretse kulambira koona.

4. Kodi Yehova analonjeza kuti akanathandiza bwanji Ayuda pobwerera kwawo?

4 Ulendo wovuta wochokera ku Babulo kupita ku Isiraeli ukanawatengera Ayuda miyezi pafupifupi 4. Koma Yehova anali atalonjeza kuti adzachotsa chilichonse chomwe chinkaoneka kuti chingawalepheretse kubwerera. Yesaya analemba kuti: “Konzani njira ya Yehova anthu inu! Wongolani msewu wa Mulungu wathu wodutsa m’chipululu. . . . Malo okumbikakumbika asalazidwe ndipo malo azitundazitunda akhale chigwa.” (Yes. 40:3, 4) Yerekezerani kuti mukuona msewu waukulu wa m’chipululu womwe ukudutsa m’chigwa. Anthu angasangalaletu kuyenda mumsewu woterewu. Zikanakhala zosavuta kwa Ayudawa kuyenda mumsewu waukulu wowongoka, m’malo momakwera kapena kutsika mapiri kapenanso zitunda. Iwo akanayendanso mwachangu.

5. Kodi msewu waukulu wophiphiritsa wochoka ku Babulo kupita ku Isiraeli unkatchedwa chiyani?

5 Masiku ano, misewu yambiri ikuluikulu imadziwika ndi dzina kapena nambala. Msewu waukulu wophiphiritsa umene Yesaya anafotokoza unalinso ndi dzina. Timawerenga kuti: “Kumeneko kudzakhala msewu waukulu ndipo udzatchedwa Msewu wa Chiyero. Munthu wodetsedwa sadzayendamo.” (Yes. 35:8) Kodi lonjezo limeneli linkatanthauza chiyani kwa Aisiraeli? Nanga limatanthauza chiyani kwa ife masiku ano?

“MSEWU WA CHIYERO” PA NTHAWIYO KOMANSO PANOPA

6. N’chifukwa chiyani msewuwu unkatchedwa woyera?

6 Dzina lakuti “Msewu wa Chiyero” ndi lokongolatu. N’chifukwa chiyani msewuwu unkatchedwa woyera? Pakati pa Ayuda obwerera kwawo sipakanapezeka “munthu wodetsedwa” yemwe sankafuna kusiya chiwerewere, kulambira mafano kapena machimo ena akuluakulu. Ayudawo akanakhala “anthu oyera” kwa Mulungu wawo. (Deut. 7:6) Komabe zimenezi sizinkatanthauza kuti Ayuda omwe anachoka ku Babulowo sankafunika kusintha zinthu zina kuti azisangalatsa Yehova.

7. Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe Ayuda ankafunika kusintha? Perekani chitsanzo.

7 Monga taonera kale, ambiri mwa Ayudawa anabadwira ku Babulo ndipo ambirinso ankatsatira kaganizidwe ndi mfundo za anthu akumeneko. Patapita zaka zambiri kuchokera pamene Ayuda oyambirira anabwerera ku Isiraeli, Ezara anamva kuti Ayuda ena anali atakwatira akazi achikunja. (Eks. 34:15, 16; Ezara 9:1, 2) Ndipo patapita nthawi, Bwanamkubwa Nehemiya anadabwa atapeza kuti ana ena omwe anabadwira ku Isiraeli, sankadziwa chilankhulo cha Ayuda. (Deut. 6:6, 7; Neh. 13:23, 24) Kodi ana amenewa akanaphunzira bwanji kukonda komanso kulambira Yehova ngati sankadziwa Chiheberi, chilankhulo chomwe chinagwiritsidwa ntchito polemba Mawu a Mulungu? (Ezara 10:3, 44) Choncho panali zinthu zambiri zomwe Ayuda ankafunika kusintha. Koma zikanakhala zosavuta kusintha ngati akanakhala ku Isiraeli kumene kulambira koona kunkabwezeretsedwa pang’onopang’ono.​—Neh. 8:8, 9.

Kungoyambira mu 1919 C.E., amuna, akazi ndi ana ambirimbiri akhala akutuluka mu Babulo Wamkulu ndipo ayamba kuyenda pa “Msewu wa Chiyero” (Onani ndime 8)

8. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi ndi zinthu zomwe zinachitika kalekale? (Onani chithunzi chapachikuto.)

8 Ena angaganize kuti, ‘Zimenezitu n’zochititsa chidwi. Koma kodi zomwe zinachitikira Ayuda kalekalezi zikutikhudza bwanji?’ Tinganene kuti zimatikhudza chifukwa nafenso tikuyenda pa “Msewu wa Chiyero.” Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” tiyenera kupitiriza kuyenda pa “Msewu wa Chiyero” chifukwa umatithandiza kukhalabe m’Paradaiso wauzimu komanso udzatithandiza kupeza madalitso amene Ufumu udzabweretse m’tsogolo. b (Yoh. 10:16) Kungoyambira mu 1919 C.E., amuna, akazi komanso ana mamiliyoni akhala akutuluka mu Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga, ndipo ayamba kuyenda pamsewu wophiphiritsawu. N’zosakayikitsa kuti inuyo muli m’gulu limeneli. Ngakhale kuti anthu anayamba kuyenda pamsewu umenewu zaka pafupifupi 100 zapitazo, ntchito youkonza inayamba zaka zambiri m’mbuyo mwake.

KUKONZA MSEWU

9. Mogwirizana ndi Yesaya 57:14, kodi ntchito yokonza “Msewu wa Chiyero” inachitika bwanji?

9 Kwa Ayuda omwe ankachoka ku Babulo, Yehova anaonetsetsa kuti wawachotsera zopinga zonse. (Werengani Yesaya 57:14.) Nanga bwanji za “Msewu wa Chiyero” wa masiku ano? Kwa zaka zambiri chisanafike chaka cha 1919, Yehova anagwiritsa ntchito amuna omwe ankamulemekeza kuti akonze njira yotulukira mu Babulo Wamkulu. (Yerekezerani ndi Yesaya 40:3.) Iwo anagwira ntchito yofunika yokonza msewu wauzimu ndipo zimenezi zinathandiza kuti anthu a maganizo abwino atuluke mu Babulo Wamkulu n’kulowa m’paradaiso wauzimu, momwe kulambira koona kunali kutabwezeretsedwa. Kodi “ntchito yokonza msewuyi” inaphatikizapo chiyani? Taganizirani zinthu zina zomwe zinachitika.

Kwa zaka zambiri chisanafike chaka cha 1919, amuna oopa Mulungu anathandiza kukonza msewu wotulukira m’Babulo Wamkulu (Onani ndime 10-11)

10-11. Kodi kusindikiza komanso kumasulira Baibulo, kwathandiza bwanji kuti anthu adziwe zambiri zokhudza Baibulo? (Onaninso chithunzi.)

10 Kusindikiza. Baibulo linakhala likukoperedwa pamanja mpaka chapakatikati pa zaka m’ma 1400. Ntchitoyi inkatenga nthawi yaitali ndipo Mabaibulo anali osowa komanso odula kwambiri. Koma anthu atapanga makina osindikizira, Baibulo linayamba kupangidwa mosavuta komanso linkapezeka ndi anthu ambiri.

11 Kumasulira. Kwa zaka zambiri, Baibulo linkapezeka m’Chilatini, chilankhulo chomwe anthu ophunzira okha ndi amene ankachimva. Komabe pamene ntchito yosindikiza mabuku inkafalikira, anthu oopa Mulungu anapititsa patsogolo ntchito yomasulira Baibulo m’zilankhulo zomwe anthu ambiri ankalankhula. Tsopano anthu owerenga Baibulo ankatha kuyerekezera zimene atsogoleri achipembedzo ankawaphunzitsa ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.

Amuna oopa Mulungu anathandiza kukonza msewu wotulukira m’Babulo Wamkulu (Onani ndime 12-14) c

12-13. Fotokozani mmene ophunzira Baibulo oona mtima anathandizira anthu m’zaka za m’ma 1800 kudziwa ziphunzitso zabodza.

12 Zinthu zothandiza pophunzira Baibulo. Anthu omwe ankaphunzira Baibulo mosamala, anadziwa zambiri pa zimene ankawerenga m’Mawu a Mulungu. Koma atsogoleri achipembedzo ambiri anakwiya chifukwa anthuwo ankauza ena zomwe aphunzira m’Baibulo. Mwachitsanzo, m’zaka za m’ma 1800, anthu ena oona mtima anayamba kupanga timapepala tomwe tinkafotokoza ziphunzitso zabodza zomwe matchalitchi ankaphunzitsa.

13 Cha mu 1835, munthu wina woopa Mulungu dzina lake Henry Grew, anafalitsa kapepala komwe kanafotokoza mmene akufa alili. M’kapepalako anafotokoza kuchokera m’Malemba kuti moyo wosafa ndi mphatso yochokera kwa Mulungu osati umene aliyense amabadwa nawo ngati mmene matchalitchi ambiri ankaphunzitsira. Mu 1837, m’busa wina dzina lake George Storrs anapeza kapepalaka ali musitima. Iye anakawerenga ndipo anatsimikizira kuti wapeza mfundo yofunika ya choonadi ndipo anaganiza zouza ena zomwe anaphunzirazo. Mu 1842, iye anakamba nkhani zotsatizana pamutu wochititsa chidwi wakuti, “Kufufuza​—Kodi Anthu Oipa Amakhala Osafa?” Zimene George Storrs analemba, zinathandiza kwambiri mnyamata wina dzina lake Charles Taze Russell.

14. Kodi ntchito yauzimu yokonza msewu, yomwe inali itachitika kale, inathandiza bwanji M’bale Russell ndi anzake? (Onaninso chithunzi.)

14 Kodi ntchito yauzimu yokonza msewu, yomwe inali itayamba kale kuchitika, inathandiza bwanji M’bale Russell ndi anzake? Akamaphunzira Malemba, ankatha kufufuza m’mabuku osiyanasiyana komanso Mabaibulo ena omwe anatulutsidwa iwo asanayambe ntchito yawo. Anapindulanso ndi zomwe anthu monga Henry Grew, George Storrs ndi ena anafufuza m’Baibulo. Nayenso M’bale Russell ndi anzake anathandiza nawo pa ntchito yauzimu yokonza msewu potulutsa mabuku ambiri komanso timapepala tofotokoza nkhani za m’Baibulo.

15. Kodi ndi zinthu zofunika ziti zomwe zinachitika mu 1919?

15 Mu 1919, anthu a Mulungu anatuluka mu Babulo Wamkulu. Pa nthawi imeneyi, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anaikidwa ndipo inali nthawi yoyenera chifukwa iye anayamba kuthandiza anthu a mtima wabwino kuti ayambe kuyenda pa “Msewu wa Chiyero,” womwe unali utangotsegulidwa kumene. (Mat. 24:45-47) Chifukwa choti atumiki okhulupirika anali atagwira ntchito yokonza msewuwu m’mbuyomu, anthu amene ankayenda pamsewu waukuluwu, akanatha kudziwa zambiri zokhudza zolinga za Yehova. (Miy. 4:18) Akanathanso kusintha moyo wawo kuti uzigwirizana ndi zimene Yehova amafuna. Yehova sayembekezera kuti anthu ake asinthe kamodzin’kamodzi. M’malomwake, iye wakhala akuwathandiza mwapang’onopang’ono. (Onani bokosi lakuti, “Yehova Wakhala Akuthandiza Anthu Ake Mwapang’onopang’ono.”) Tonsefe tidzasangalala kwambiri pamene tizidzasangalatsa Mulungu wathu pa chilichonse.​—Akol. 1:10.

“MSEWU WA CHIYERO” UDAKALI WOTSEGUKA

16. Kuyambira mu 1919, kodi ndi ntchito iti yomwe yakhala ikuchitika pokonza “Msewu wa Chiyero”? (Yesaya 48:17; 60:17)

16 Msewu uliwonse umafunika kumakonzedwa pafupipafupi. Kungochokera mu 1919, ntchito yokonza “Msewu wa Chiyero” yakhala ikupitirira n’cholinga chofuna kuthandiza anthu ambiri kutuluka mu Babulo Wamkulu. Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene anali atangosankhidwa kumene, anayamba kugwira ntchito ndipo mu 1921, anatulutsa buku lothandiza kuphunzira Baibulo pofuna kuthandiza atsopano kuti aphunzire choonadi. Bukuli, lomwe ndi Zeze wa Mulungu, linagawidwa pafupifupi mabuku 6 miliyoni m’zinenero 36, ndipo linathandiza anthu ambiri kuphunzira choonadi. Posachedwapa patulutsidwa buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale lomwe ndi labwino pochititsa maphunziro a Baibulo. M’masiku otsiriza ano, Yehova wakhala akugwiritsa ntchito gulu lake potipatsa chakudya chauzimu n’cholinga choti tonsefe tipitirizebe kuyenda pa “Msewu wa Chiyero.”​—Werengani Yesaya 48:17; 60:17.

17-18. Kodi “Msewu wa Chiyero” ukupita kuti?

17 Tinganene kuti munthu akavomera kuphunzira Baibulo, amakhala ndi mwayi woyamba kuyenda pa “Msewu wa Chiyero.” Ena amangoyenda pamsewuwu kwa kanthawi kochepa kenako n’kuchokapo. Pomwe ena atsimikiza kupitirizabe kuyenda pamsewuwu mpaka atafika komwe akupita. Kodi akupita kuti?

18 Kwa amene ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba, “Msewu wa Chiyero” umakawafikitsa “m’paradaiso wa Mulungu” kumwamba. (Chiv. 2:7) Kwa amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli, msewuwu umawathandiza kuti adzafike pokhala angwiro kumapeto kwa zaka 1,000. Ngati mukuyenda pamsewu umenewu musamayang’ane kumbuyo, ndipo musachokepo mpaka mutafika m’dziko latsopano. Tikukufunirani “ulendo wabwino.”

NYIMBO NA. 24 Bwerani Kuphiri la Yehova

a Yehova anatchula msewu wophiphiritsa wochoka ku Babulo kupita ku Isiraeli kuti “Msewu wa Chiyero.” Kodi masiku anonso Yehova wakonzera anthu ake msewu ngati umenewu? Inde. Kungochokera mu 1919, anthu mamiliyoni akhala akutuluka mu Babulo Wamkulu n’kuyamba kuyenda pa “Msewu wa Chiyero.” Tonsefe tiyenera kupitiriza kuyenda pamsewu umenewu mpaka tikafike kumene tikupita.

b Onani buku lakuti, Ulosi wa Yesaya​—Muuni wa Anthu Onse 2, tsamba 56-57.

c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale Russell ndi anzake akugwiritsa ntchito mabuku othandiza pophunzira Baibulo omwe analembedwa iwo asanayambe ntchito yawo.