NKHANI YOPHUNZIRA 20

Zimene Tingachite Kuti Mapemphero Athu Azikhala Abwino Kwambiri

Zimene Tingachite Kuti Mapemphero Athu Azikhala Abwino Kwambiri

“Mukhuthulireni za mumtima mwanu.”​—SAL. 62:8.

NYIMBO NA. 45 Kusinkhasinkha kwa Mtima Wanga

ZIMENE TIPHUNZIRE a

Tingapemphere kwa Yehova nthawi zonse komanso kumupempha kuti azititsogolera pa mbali zonse za moyo wathu (Onani ndime 1)

1. Kodi Yehova amauza atumiki ake kuti azichita chiyani? (Onaninso chithunzi.)

 KODI tingapite kwa ndani tikamafuna malangizo komanso kulimbikitsidwa? Tikudziwa yankho la funso limeneli. Tikhoza kupemphera kwa Yehova. Ndipotu iye amatiuza kuti tizichita zimenezo. Amafuna kuti tizipemphera kwa iye nthawi zonse, kapena kuti “mosalekeza.” (1 Ates. 5:17) Tingapemphere kwa iye momasuka komanso kumupempha kuti azititsogolera pa mbali iliyonse ya moyo wathu. (Miy. 3:5, 6) Popeza Yehova ndi Mulungu woolowa manja, satiikira malire a nthawi zomwe tingapemphere kwa iye.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Timaona kuti pemphero ndi mphatso ya mtengo wapatali. Komabe chifukwa chotanganidwa, mwina zingamativute kupeza nthawi yopemphera. Mwinanso tingaone kuti tikufunika kukonza mapemphero athu kuti azikhala omveka bwino. N’zosangalatsa kuti Malemba angatilimbikitse komanso kutitsogolera pa nkhaniyi. Munkhaniyi, tiona mmene chitsanzo cha Yesu chingatithandizire kuti tizipeza nthawi yopemphera. Tionanso zinthu 5 zomwe tingatchule m’mapemphero athu kuti azikhala abwino.

YESU ANKAPEZA NTHAWI YOPEMPHERA

3. Kodi Yesu ankadziwa zotani zokhudza kupemphera?

3 Yesu ankadziwa kuti Yehova amaona kuti kupemphera n’kofunika kwambiri. Asanabwere padziko lapansi, iye ankaona Atate wake akuyankha mapemphero a amuna ndi akazi okhulupirika. Mwachitsanzo, Yesu anali pambali pa Atate wake pomwe iwo ankayankha mapemphero ochokera pansi pa mtima a Hana, Davide, Eliya komanso anthu ena. (1 Sam. 1:10, 11, 20; 1 Maf. 19:4-6; Sal. 32:5) Choncho n’zosadabwitsa kuti Yesu anauza ophunzira ake kuti azipemphera pafupipafupi komanso ndi chikhulupiriro.​—Mat. 7:7-11.

4. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yesu pa nkhani yopemphera?

4 Kudzera m’mapemphero ake kwa Yehova, Yesu anapereka chitsanzo choti otsatira ake azitengera. Pa nthawi yonse ya utumiki wake, Yesu ankapemphera pafupipafupi. Iye ankafunika kukonza nthawi yoti apemphere chifukwa nthawi zambiri ankakhala wotanganidwa komanso ankazunguliridwa ndi anthu ambiri. (Maliko 6:31, 45, 46) Iye ankadzuka m’mawa kwambiri kuti akakhale payekha n’kupemphera. (Maliko 1:35) Pa nthawi ina anapemphera usiku wonse asanasankhe zochita pa nkhani yofunika kwambiri. (Luka 6:12, 13) Ndipo pa usiku wake womaliza, iye anapemphera mobwerezabwereza poganizira mbali yomaliza ya utumiki wake padzikoli, yomwe inali yovuta kwambiri.​—Mat. 26:39, 42, 44.

5. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu tikamapemphera?

5 Chitsanzo cha Yesu chikutiphunzitsa kuti kaya timatanganidwa bwanji, timafunika kupeza nthawi yopemphera. Mofanana ndi Yesu, mwina ifenso tingafunike kudzuka m’mawa kwambiri kapena kugona mochedwa kuti tipeze nthawi yopemphera. Tikamachita zimenezi, timasonyeza kuti timayamikira Yehova potipatsa mphatso yapaderayi. Mlongo wina dzina lake Lynne, amakumbukirabe mmene anakhudzidwira atadziwa kwa nthawi yoyamba zokhudza mwayi wa pemphero. Iye anati: “Nditaphunzira kuti ndikhoza kulankhula ndi Yehova nthawi iliyonse, zinandithandiza kuti ndizimuona monga Mnzanga wapamtima ndipo ndinkafuna kuti mapemphero anga azikhala abwino.” Mosakayikira ndi mmenenso ambirife timamvera. Ndiye tiyeni tikambirane mfundo 5 zofunika zomwe tingatchule m’mapemphero athu.

MFUNDO 5 ZOFUNIKA KUTCHULA POPEMPHERA

6. Mogwirizana ndi Chivumbulutso 4:10, 11, kodi Yehova ndi woyenera kulandira chiyani?

6 Kutamanda Yehova. M’masomphenya ochititsa chidwi, mtumwi Yohane anaona akulu 24 kumwamba akulambira Yehova. Iwo ankatamanda Mulungu podziwa kuti ndi woyenera kulandira ‘mphamvu, ulemerero ndi ulemu.’ (Werengani Chivumbulutso 4:10, 11.) Angelo okhulupirika alinso ndi zifukwa zowachititsa kutamanda ndi kulemekeza Yehova. Iwo amakhala naye limodzi kumwamba ndipo anafika pomudziwa bwino kwambiri. Amaonanso makhalidwe ake kudzera m’zochita zake. Akamaona mmene Yehova amachitira zinthu, zimawachititsa kuti azimutamanda.​—Yobu 38:4-7.

7. Kodi tingatamande Yehova pa zifukwa ziti?

7 Ifenso timafuna kutamanda Yehova m’mapemphero athu n’kumafotokoza zimene timakonda komanso kuyamikira zokhudza iye. Mukamawerenga komanso kuphunzira Baibulo, muziyesa kupeza makhalidwe ake omwe amakusangalatsani kwambiri. (Yobu 37:23; Aroma 11:33) Kenako muzimuuza Yehova mmene mukumvera chifukwa cha makhalidwewo. Tingamutamandenso chifukwa chotithandiza ifeyo komanso abale ndi alongo athu. Nthawi zonse iye amatisamalira ndiponso kutiteteza.​—1 Sam. 1:27; 2:1, 2.

8. Kodi zina mwa zifukwa zotichititsa kuyamikira Yehova ndi ziti? (1 Atesalonika 5:18)

8 Kuyamikira Yehova. Tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuyamikira Yehova m’mapemphero athu. (Werengani 1 Atesalonika 5:18.) Tingamuyamikire chifukwa cha zabwino zimene tili nazo. Ndipotu mphatso iliyonse yabwino imachokera kwa iye. (Yak. 1:17) Mwachitsanzo, tingamuthokoze chifukwa cha dziko lokongolali komanso zinthu zochititsa chidwi zam’chilengedwe. Tingamuthokozenso chifukwa chotipatsa moyo, banja, anzathu komanso chiyembekezo. Timafunanso kuyamikira Yehova chifukwa chotilola kusangalala ndi ubwenzi wamtengo wapatali womwe tili nawo ndi iye.

9. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tiziyamikira Yehova?

9 Tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti tiziganizira zifukwa zomwe zimatichititsa kuti tiziyamikira Yehova. Anthu ambiri m’dzikoli ndi osayamika. Nthawi zambiri iwo amangoganizira zimene akufuna, osati zimene angachite kuti asonyeze kuyamikira zimene ali nazo. Ngati titatengera maganizo amenewa, ndiye kuti mapemphero athu akhoza kukhala omangopempha. Kuti zimenezi zisatichitikire, tiyenera kumayesetsa kukhala ndi mtima woyamikira zonse zimene Yehova amatichitira.​—Luka 6:45.

Kuyamikira Yehova kungatithandize kuti tizipirira (Onani ndime 10)

10. Kodi kuyamikira kunathandiza bwanji mlongo wina kuti apirire? (Onaninso chithunzi.)

10 Mtima woyamikira ungatithandize kuti tizipirira mavuto. Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Kyung-sook, zomwe zinafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2015. Iye anapezeka ndi khansa ya m’mapapo. Mlongoyu ananena kuti: “Zimenezi zinandikhumudwitsa kwambiri. Ndinaona kuti ndataya chilichonse ndipo ndinkachita mantha kwambiri.” Kodi n’chiyani chinamuthandiza kupirira? Iye ananena kuti madzulo aliwonse asanakagone ankapita pamalo ochezera padenga la nyumba yake ndipo ankapemphera motulutsa mawu n’kutchula zinthu 5 zomwe akuyamikira pa tsikulo. Zimenezi zinamuthandiza kuti asamadere nkhawa kwambiri ndipo zinamulimbikitsa kuti azikonda Yehova. Anaona mmene Yehova amathandizira atumiki ake okhulupirika akamakumana ndi mayesero ndipo anazindikira kuti timapeza madalitso ambiri kuposa mavuto amene timakumana nawo. Mofanana ndi Kyung-sook, tili ndi zifukwa zambiri zoyamikirira Yehova ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto. Kumuyamikira popemphera kungatithandize kuti tipirire komanso tipitirizebe kukhala osangalala.

11. Yesu atabwerera kumwamba, n’chifukwa chiyani ophunzira ake ankafunika kukhala olimba mtima?

11 Kupempha Yehova kuti atithandize kuti tizilalikira molimba mtima. Asanabwerere kumwamba, Yesu anakumbutsa ophunzira ake kuti ayenera kuchitira umboni za iye “mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8; Luka 24:46-48) Pasanapite nthawi yaitali, atsogoleri a Chiyuda anagwira mtumwi Petulo ndi Yohane n’kupita nawo kukhoti lalikulu la Ayuda ndipo anawalamula kuti asiye kulalikira ndiponso anawaopseza. (Mac. 4:18, 21) Ndiye kodi Petulo ndi Yohane anatani?

12. Mogwirizana ndi Machitidwe 4:29, 31, kodi ophunzira a Yesu anachita chiyani?

12 Poyankha atsogoleri a chipembedzo a Chiyuda omwe ankawaopsezawo, Petulo ndi Yohane anati: “Weruzani nokha, ngati n’koyenera pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. Koma ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:19, 20) Petulo ndi Yohane atamasulidwa, ophunzirawo anapemphera kwa Yehova mokweza mawu kuti awathandize kukwaniritsa chifuniro chake. Iwo anapemphera kuti: “Lolani kuti akapolo anu apitirize kulankhula mawu anu molimba mtima.” Yehova anayankha pemphero lochokera pansi pa mtimali.​—Werengani Machitidwe 4:29, 31.

13. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Jin-hyuk?

13 Tingatsanzire ophunzirawa, popitiriza kulalikira ngakhale pamene akuluakulu a boma aletsa ntchito yathu. Taganizirani chitsanzo cha M’bale Jin-hyuk, yemwe anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali. Ali m’ndende, iye anapatsidwa ntchito yoti azisamalira akaidi ena omwe anali muselo ya okha. Koma sankaloledwa kuti azikambirana nawo nkhani zina kuphatikizapo zokhudza Baibulo. Iye anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize kukhala wolimba mtima komanso kupeza njira zouzira ena choonadi pa mpata uliwonse umene ungapezeke. (Mac. 5:29) Iye anati: “Yehova anayankha mapemphero anga pondithandiza kukhala wolimba mtima komanso kundipatsa nzeru kuti ndiyambitse maphunziro a Baibulo ambiri, omwe ndinkachititsa kwa 5 minitsi muselo iliyonse. Kenako usiku ndinkalemba makalata amene ndinkapatsa akaidi anzanga tsiku lotsatira.” Ifenso tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza kuti tikwaniritse utumiki wathu. Mofanana ndi Jin-hyuk, tingamupemphe kuti atithandize kukhala olimba mtima komanso atipatse nzeru.

14. N’chiyani chingatithandize tikamakumana ndi mavuto? (Salimo 37:3, 5)

14 Kupempha Yehova kuti atithandize kupirira mavuto. Ambirife tikukumana ndi mavuto okhudza thanzi kapena maganizo, imfa ya okondedwa athu, mavuto a m’banja, kuzunzidwa kapenanso mavuto ena. Ndipo zinthu monga miliri komanso nkhondo zachititsa kuti zikhale zovuta kwambiri kulimbana ndi mavutowa. Choncho muzipemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima. Muzimuuza zimene zikuchitika pa moyo wanu ngati mmene mungachitire ndi mnzanu wapamtima. Muzikhulupirira kuti Yehova “adzachitapo kanthu.”​—Werengani Salimo 37:3, 5.

15. Kodi pemphero lingatithandize bwanji ‘kupirira chisautso’? Perekani chitsanzo.

15 Kulimbikira kupemphera kungatithandize ‘kupirira chisautso.’ (Aroma 12:12) Yehova amadziwa zimene zikuchitikira atumiki ake ndipo ‘amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.’ (Sal. 145:18, 19) Mpainiya wina wazaka 29, dzina lake Kristie, anaona kuti zimenezi n’zoona. Mosayembekezereka, iye anayamba kudwala matenda aakulu. Zimenezi zinamukhumudwitsa kwambiri. Kenako anamvanso kuti mayi ake apezeka ndi matenda oopsa. Kristie anati: “Ndinkapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima kuti andipatse mphamvu kuti ndithe kupirira tsiku lililonse. Nthawi zonse ndinkayesetsa kuchita zinthu zokhudza kulambira monga kupezeka pamisonkhano komanso kuphunzira pandekha.” Iye anawonjezera kuti: “Pemphero linandithandiza pa nthawi zovuta kwambiri. Ndinkadziwa kuti nthawi zonse Yehova ali nane, ndipo zimenezi zinkanditonthoza kwambiri. Ngakhale kuti mavuto okhudza thanzi langa sanathe nthawi yomweyo, Yehova ankayankha mapemphero anga pondipatsa mtendere wamumtima.” Tisamaiwale kuti “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.”​—2 Pet. 2:9.

Kuti tipewe mayesero, (1) tiyenera kupemphera kwa Yehova kuti atithandize, (2) kuchita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athu komanso (3) kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova (Onani ndime 16-17)

16. N’chifukwa chiyani timafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti tilimbane ndi mayesero?

16 Kupempha Yehova kuti atithandize kupewa mayesero. Popeza kuti si ife angwiro, nthawi zambiri timalimbana ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Satana amayesetsa kuchita zonse zomwe angathe potichititsa kuti tizivutika kuchita zoyenera. Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndi kusokoneza maganizo athu pogwiritsa ntchito zosangalatsa zoipa. Zikatere, tingayambe kumaganizira zinthu zoipa zomwe zingachititse kuti tisakhale oyera pamaso pa Yehova komanso tichite tchimo lalikulu.​—Maliko 7:21-23; Yak. 1:14, 15.

17. Tikapempha Yehova kuti atithandize, kodi tingatani kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi zomwe tapemphazo? (Onaninso chithunzi.)

17 Timafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti tithe kulimbana ndi maganizo ofuna kuchita zoipa. M’pemphero lake la chitsanzo, Yesu anatchulamonso mfundo yakuti: “Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo.” (Mat. 6:13) Yehova amafuna kutithandiza, koma tiyenera kumupempha kuti atithandize. Tiyeneranso kumachita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athu. Tingachitenso zinthu zina zomwe zingatithandize kupewa maganizo ndi mfundo zoipa zomwe ndi zofala m’dziko la Satanali. (Sal. 97:10) Kuwerenga komanso kuphunzira Baibulo kungatithandize kuti tiziganizira zinthu zabwino. Kupezeka pamisonkhano komanso kugwira nawo ntchito yolalikira kungatetezenso maganizo athu. Tikatero, Yehova amatilonjeza kuti sadzalola kuti tiyesedwe kufika pamene sitingathe kupirira.​—1 Akor. 10:12, 13.

18. Pa nkhani ya pemphero, kodi tonsefe tikufunika kuchita chiyani?

18 Tonsefe tiyenera kumapemphera kwambiri kuposa kale kuti tikhalebe okhulupirika m’masiku otsiriza ovutawa. Tsiku lililonse muzipeza nthawi yoti muzipemphera kuchokera pansi pa mtima. Yehova amafuna kuti ‘tizimukhuthulira za mumtima mwathu.’ (Sal. 62:8) Muzitamanda Yehova ndipo muzimuyamikira chifukwa cha zonse zimene amachita. Muzimupempha kuti azikuthandizani kukhala wolimba mtima polalikira. Muzimuchonderera kuti akuthandizeni kulimbana ndi mavuto komanso mayesero alionse omwe mukukumana nawo. Musamalole kuti chilichonse kapena aliyense akulepheretseni kupemphera kwa Yehova nthawi zonse. Koma kodi Yehova amayankha bwanji mapemphero athu? Tidzakambirana funso lofunikali munkhani yotsatira.

NYIMBO NA. 42 Pemphero la Mtumiki wa Mulungu

a Timafuna kuti mapemphero athu azikhala ngati makalata osangalatsa, omwe talembera mnzathu wapamtima. Komabe si nthawi zonse pamene zimakhala zophweka kupeza nthawi yoti tipemphere. Ndiponso nthawi zina zingativute kudziwa nkhani zoti titchule m’mapemphero athu. Munkhaniyi tikambirana mfundo zofunika zimenezi.