NKHANI YOPHUNZIRA 45

Pitirizani Kusonyezana Chikondi Chokhulupirika

Pitirizani Kusonyezana Chikondi Chokhulupirika

“Muzisonyezana kukoma mtima kosatha [chikondi chokhulupirika] ndi chifundo.”​—ZEK. 7:9.

NYIMBO NA. 107 Tizitsanzira Chikondi cha Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi ndi zifukwa ziti zimene zimatichititsa kuti tizisonyezana chikondi chokhulupirika?

TILI NDI zifukwa zomveka zotichititsa kuti tizisonyezana chikondi chokhulupirika. Kodi zina mwa zifukwazi ndi ziti? Taonani mmene miyambi ya m’Baibulo yotsatirayi ikuyankhira funsoli: “Usasiye kukoma mtima kosatha ndi choonadi. . . . Ukachita zimenezi, Mulungu ndi anthu adzakukomera mtima ndipo adzakuona kuti ndiwe wozindikira.” “Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake.” “Amene akufunafuna chilungamo ndiponso kukoma mtima kosatha adzapeza moyo.”​—Miy. 3:3, 4; 11:17; 21:21

2 Miyambiyi ikutchula zifukwa zitatu zotichititsa kuti tizisonyeza chikondi chokhulupirika. Choyamba, kusonyeza chikondi chokhulupirika kumatichititsa kukhala amtengo wapatali kwa Mulungu. Chachiwiri, zinthu zimatiyendera bwino tikamasonyeza chikondi chokhulupirika. Mwachitsanzo, timagwirizana kwambiri ndi anzathu. Ndipo chachitatu, tidzapeza madalitso m’tsogolo kuphatikizapo moyo wosatha. Choncho tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kutsatira malangizo a Yehova akuti: “Muzisonyezana kukoma mtima kosatha ndi chifundo.”​—Zek. 7:9.

3. Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

3 Munkhaniyi tikambirana mayankho a mafunso 4 awa: Kodi tiyenera kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa ndani? Kodi tingaphunzire chiyani m’buku la Rute pankhani yosonyeza chikondi chokhulupirika? Nanga tingatani kuti tizisonyeza chikondi chokhulupirika masiku ano? Kodi anthu amene amasonyeza chikondi chimenechi amapindula bwanji?

KODI TIYENERA KUSONYEZA CHIKONDI CHOKHULUPIRIKA KWA NDANI?

4. Kodi tingatsanzire bwanji Mulungu pankhani yosonyeza chikondi chokhulupirika? (Maliko 10:29, 30)

4 Monga mmene tinaphunzirira munkhani yapita ija, Yehova amapitirizabe kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu amene amamukonda komanso kumutumikira. (Dan. 9:4) Timafuna ‘kutsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.’ (Aef. 5:1) Choncho timafunitsitsa kuti tizikonda kwambiri abale ndi alongo athu mumpingo.​—Werengani Maliko 10:29, 30.

5-6. Kodi mawu akuti “kukhulupirika” angatanthauze chiyani?

5 Mungavomereze kuti tikamvetsa bwino tanthauzo la chikondi chokhulupirika ndi pamene tingachisonyeze bwino kwa olambira anzathu. Kuti timvetse bwino za chikondichi, tiyeni tione kusiyana kwake ndi mawu akuti kukhulupirika omwe anthu amatchula kawirikawiri. Taganizirani chitsanzo ichi.

 6 Masiku ano timatha kunena za munthu amene wagwira ntchito zaka zambiri pakampani kuti ndi wokhulupirika kukampaniyo. Koma n’kutheka kuti pa zaka zonsezo sanakumanepo ndi eniake a kampaniyo ndipo mwinanso sagwirizana ndi malamulo ake. Iye samaikonda kampaniyo koma amasangalala chifukwa ntchitoyo imamupatsa ndalama zomwe amafunikira. Komabe akupitiriza kugwira ntchitoyo mpaka pamene adzapume kapena kupeza ntchito yabwino kwina.

7-8. (a) Kodi n’chiyani chimachititsa kuti munthu azisonyeza chikondi chokhulupirika? (b) N’chifukwa chiyani tikufuna kukambirana zinthu zina zimene zili m’buku la Rute?

7 Kusiyana kumene kulipo pakati pa kukhulupirika ndi chikondi chokhulupirika chimene chatchulidwa  mundime 6 ndi zolinga zomwe zimachititsa munthu kuti azisonyeza makhalidwewa. Munkhani zimene timawerenga m’Baibulo, kodi ndi chiyani chimene chinkachititsa anthu a Mulungu kuti azisonyeza chikondi chokhulupirika? Iwo ankatero osati chifukwa chakuti ndi zimene ankafunika kuchita, koma ndi zimene ankafuna kuchita. Taganizirani chitsanzo cha Davide. Iye ankafunitsitsa kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa mnzake wapamtima Yonatani ngakhale kuti bambo ake a Yonatani ankafuna kupha Davideyo. Patapita zaka zambiri Yonatani atamwalira, Davide anapitiriza kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa Mefiboseti mwana wa Yonatani.​—1 Sam. 20:9, 14, 15; 2 Sam. 4:4; 8:15; 9:1, 6, 7

8 Tingadziwe zambiri pankhani yosonyeza chikondi chokhulupirika tikamaphunzira buku la m’Baibulo la Rute. Kodi tingaphunzire zotani pankhani yosonyeza chikondichi kuchokera kwa anthu otchulidwa m’bukuli? Nanga tingagwiritse ntchito bwanji mfundo zake mumpingo mwathu? *

KODI TINGAPHUNZIRE CHIYANI M’BUKU LA RUTE PANKHANI YOSONYEZA CHIKONDI CHOKHULUPIRIKA?

9. N’chifukwa chiyani Naomi ankaona kuti Yehova sakusangalala naye?

9 M’buku la Rute timawerengamo nkhani ya Naomi, mpongozi wake Rute komanso munthu wina woopa Mulungu dzina lake Boazi yemwe anali wachibale wa mwamuna wa Naomi. Chifukwa chakuti ku Isiraeli kunali njala, Naomi, mwamuna wake komanso ana awo amuna awiri anasamukira ku Mowabu. Ali kumeneko mwamuna wake wa Naomi anamwalira. Ana ake awiri aja anakwatira koma n’zomvetsa chisoni kuti nawonso anamwalira. (Rute 1:3-5; 2:1) Zomwe zinachitikazi zinachititsa kuti Naomi afooke kwambiri. Zimenezi zinamusokoneza kwambiri maganizo mpaka anafika poyamba kuona kuti Yehova sakusangalala naye. Taonani mmene anafotokozerera momwe ankamvera zokhudza Mulungu: “Dzanja la Yehova landiukira.” “Wamphamvuyonse wachititsa moyo wanga kukhala wowawa kwambiri.” “Ndi Yehova amene wandichititsa kukhala wonyozeka, ndipo ndi Wamphamvuyonseyo amene wandigwetsera tsokali.”​—Rute 1:13, 20, 21.

10. Kodi Yehova anatani ndi zimene Naomi ananena chifukwa chopwetekedwa mtima?

10 Kodi Yehova anatani ndi zimene Naomi analankhula chifukwa chopwetekedwa mtima? Iye sanasiye kumukonda mtumiki wakeyu. M’malomwake anamusonyeza chifundo. Yehova amadziwa kuti “kuponderezedwa kumapangitsa munthu wanzeru kuchita zinthu zopanda nzeru.” (Mlal. 7:7) Komabe Naomi ankafunika kuthandizidwa kuti aone kuti Yehova sanamusiye. Ndiye kodi Mulungu anamuthandiza bwanji? (1 Sam. 2:8) Iye anachititsa kuti Rute amuthandize komanso kumusonyeza chikondi chokhulupirika. Mofunitsitsa komanso mokoma mtima, Rute anathandiza apongozi akewo kuti ayambirenso kuona kuti Yehova sanawasiye ndipo ankawakonda. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Rute?

11. N’chifukwa chiyani abale ndi alongo okoma mtima amathandiza Akhristu anzawo omwe akumana ndi mavuto?

11 Chikondi chokhulupirika chimatichititsa kuti tizithandiza anthu amene akumana ndi mavuto. Mofanana ndi Rute yemwe sanamusiye Naomi, masiku ano abale ndi alongo okoma mtima amafunitsitsa kuthandiza ena mumpingo omwe akumana ndi mavuto. Iwo amakonda abale ndi alongo awo ndipo amafuna kuchita zonse zimene angathe kuti awathandize. (Miy. 12:25; 24:10) Izi ndi zogwirizana ndi zimene Paulo anatilimbikitsa pomwe anati: “Lankhulani molimbikitsa kwa amtima wachisoni, thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.”​—1 Ates. 5:14.

Tingathandize m’bale kapena mlongo amene wakhumudwa pomumvetsera (Onani ndime 12)

12. Kodi ndi njira yabwino iti imene tingathandizire m’bale kapena mlongo amene ali ndi nkhawa?

12 Nthawi zambiri njira yabwino imene tingathandizire m’bale kapena mlongo amene ali ndi nkhawa ndi kumumvetsera akamalankhula komanso kumutsimikizira kuti timamukonda. Mulungu amaona zimene mumachita pothandiza atumiki ake amtengo wapatali. (Sal. 41:1) Pa Miyambo 19:17 pamati: “Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.”

Rute sakufuna kusiyana ndi apongozi ake a Naomi, pamene Olipa akubwerera ku Mowabu. Rute akuuza Naomi kuti: “Kumene inu mupite inenso ndipita komweko” (Onani ndime 13)

13. Kodi Rute anali wosiyana bwanji ndi Olipa, nanga n’chifukwa chiyani zimene anachita zinasonyeza kuti anali ndi chikondi chokhulupirika? (Onani chithunzi chapachikuto.)

13 Timamvetsanso zokhudza chikondi chokhulupirika tikaganizira zimene zinachitikira Naomi pambuyo pa imfa ya mwamuna wake ndi ana ake awiri. Iye atamva kuti “Yehova wakumbukira anthu ake powapatsa chakudya,” anaganiza zobwerera kwawo. (Rute 1:6) Pa nthawiyi apongozi ake onse awiri ananyamuka naye limodzi. Koma ali m’njira Naomi anauza azimayiwa maulendo atatu kuti abwerere ku Mowabu. Ndiye kodi chinachitika n’chiyani? Timawerenga kuti: “Olipa anapsompsona apongozi ake powatsanzika. Koma Rute anawaumirirabe.” (Rute 1:7-14) Posankha kuti abwerere, Olipa anatsatira malangizo a Naomi ndipo ndi zimene ankayembekezeredwa kuti achite. Koma Rute anachita zoposa pamenepo. Iye analinso ndi ufulu wobwerera koma chifukwa chikuti anali ndi chikondi chokhulupirika, anasankha kukhalabe ndi apongozi akewo omwe ankafunika kuthandizidwa. (Rute 1:16, 17) Rute anasankha kukhalabe ndi Naomi osati chifukwa chakuti ndi zimene ankafunika kuchita, koma ndi zimene ankafuna kuchita. Zimene Rute anachita zinasonyeza kuti anali ndi chikondi chokhulupirika. Kodi tikuphunzira chiyani pankhaniyi?

14. (a) Kodi masiku ano abale ndi alongo amtima wachikondi amasankha kuchita chiyani? (b) Mogwirizana ndi Aheberi 13:16, kodi ndi nsembe ziti zimene Mulungu amasangalala nazo?

14 Chikondi chokhulupirika chimapangitsa munthu kuchita zoposa zimene zimayembekezeredwa. Masiku ano abale ndi alongo ambiri amasankha kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa Akhristu anzawo ngakhale amene sakuwadziwa. Mwachitsanzo, pakachitika ngozi za m’chilengedwe, mwansanga iwo amafunitsitsa kudziwa zimene angachite kuti athandizepo. Ngati wina mumpingo wakumana ndi vuto lobwera chifukwa cha mavuto azachuma, iwo amachitapo kathu mwansanga kuti amuthandize kupeza zimene akufunikira. Mofanana ndi Akhristu a ku Makedoniya a m’nthawi ya atumwi, iwo amachita zoposa zimene zikuyembekezeredwa. Amagwiritsa ntchito nthawi komanso zinthu zawo ndipo amachita “ngakhale zoposa pamenepo,” kuti athandize abale awo amene akumana ndi mavuto. (2 Akor. 8:3) Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri chifukwa cha mtima wachikondi umene amasonyezawo.​—Werengani Aheberi 13:16.

KODI TINGATANI KUTI TIZISONYEZA CHIKONDI CHOKHULUPIRIKA MASIKU ANO?

15-16. Kodi Rute anasonyeza bwanji kuti ankayesetsabe kuti athandize apongozi ake?

15 Tingaphunzire mfundo zabwino kwambiri pa zimene Rute anachita pothandiza Naomi. Tiyeni tione zina zimene tingaphunzire.

16 Muziyesetsabe kuti muthandizepo. Pamene Rute ankafuna kupita ndi apongozi ake ku Yuda, poyamba apongozi akewo anamukaniza. Koma Rute sanabwerere m’mbuyo. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Naomi “ataona kuti walimbikira zoti apite naye limodzi, anasiya kumuuza kuti abwerere.”​—Rute 1:15-18.

17. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiyesetsebe kuthandiza winawake?

17 Zimene tikuphunzirapo: Pamafunika kuleza mtima kuti tithandize anthu amene ali ndi nkhawa chifukwa cha mavuto, koma tiyenera kuyesetsabe kuti tiwathandize. Mlongo amene akufunika kuthandizidwa, poyamba angakane kuti timuthandize. * Komabe chikondi chokhulupirika chingatipangitse kuchita zimene tingathe kuti tisamusiye. (Agal. 6:2) Timayembekezera kuti m’kupita kwa nthawi, iye angavomere kuti timuthandize komanso timulimbikitse.

18. Kodi n’chiyani chimene chiyenera kuti chinamuthandiza kwambiri Rute?

18 Musamakhumudwe. Naomi ndi Rute atafika ku Betelehemu, Naomi anakumana ndi anzake amene anawasiya. Iye anawauza kuti: “Ndinali ndi zonse pochoka kuno, koma Yehova wandibweza wopanda kanthu.” (Rute 1:21) Tangoganizani mmene Rute anamvera Naomi atalankhula zimenezi. Iye anali atachita zonse zimene akanatha kuti athandize Naomi. Ankalira naye, kumutonthoza komanso anali atayenda naye masiku ambiri. Koma ngakhale kuti iye anachita zonsezi, Naomi ananena kuti: “Yehova wandibweza wopanda kanthu.” Ngakhale kuti Rute anali naye nthawi zonse, zimene Naomi analankhulazi zinasonyeza ngati sankayamikira zonse zimene Rute anamuchitira. Zimenezitu ziyenera kuti zinali zopweteka kwambiri kwa Rute. Koma iye anapitirizabe kumuthandiza Naomi.

19. N’chiyani chingatithandize kuti tizipitirizabe kuthandiza munthu amene wakhumudwa?

19 Zimene tikuphunzirapo: Masiku anonso mlongo amene wakhumudwa akhoza kutilankhula zinthu zimene zingatipweteke mumtima, ngakhale kuti tachita zonse zimene tingathe kuti timuthandize. Koma zikatero sitiyenera kukhumudwa. Tiyenera kupitirizabe kumuthandiza n’kumapempha Yehova kuti atithandize kupeza njira yabwino yomutonthozera.​—Miy. 17:17.

Kodi akulu masiku ano angatsanzire bwanji Boazi? (Onani ndime 20-21)

20. Kodi n’chiyani chinathandiza Rute kupeza mphamvu zimene ankafunikira kuti asafooke?

20 Muzilimbikitsa ena mukaona kuti akufunika kulimbikitsidwa. Rute anali atasonyeza chikondi chokhulupirika kwa Naomi koma pa nthawiyi nayenso ankafunika kulimbikitsidwa. Ndipo Yehova anachititsa kuti Boazi amulimbikitse. Iye anauza Rute kuti: “Yehova akudalitse chifukwa cha zimene wachita, ndipo Yehova, Mulungu wa Isiraeli akufupe mokwanira. Iye amene m’mapiko mwake wathawiramo ndi kupezamo chitetezo.” Mawu okhudza mtimawa anamulimbikitsa kwambiri Rute. Poyankha iye anauza Boazi kuti: “Mwanditonthoza mtima, komanso mwalankhula mondilimbitsa mtima ngati kuti ndine mtsikana wanu wantchito.” (Rute 2:12, 13) Mawu apanthawi yake amene Boazi analankhula, anapatsa Rute mphamvu zimene ankafunikira.

21. Mogwirizana ndi Yesaya 32:1, 2, kodi akulu achikondi amatani?

21 Zimene tikuphunzirapo. Anthu amene amasonyeza ena chikondi chokhulupirika, nthawi zina nawonso amafunika kulimbikitsidwa. Mofanana ndi Boazi amene anatsimikizira Rute kuti Mulungu ndi anthu ankaona zimene ankachita pothandiza Naomi, akulu atcheru masiku ano, amayamikira abale ndi alongo amene amathandiza ena. Abale ndi alongowa akamayamikiridwa motere, amapeza mphamvu kuti apitirizebe kuchita zabwino.​—Werengani Yesaya 32:1, 2.

KODI ANTHU AMENE AMASONYEZA CHIKONDI CHOKHULUPIRIKA AMAPEZA MADALITSO OTANI?

22-23. Kodi Naomi anasintha bwanji mmene ankaonera zinthu, nanga n’chifukwa chiyani? (Salimo 136:23, 26)

22 Boazi anapereka mowolowa manja chakudya kwa Rute ndi Naomi. (Rute 2:14-18) Kodi Naomi anatani ataona zimene Boazi anawachitira? Iye anati: “Yehova amene sanaleke kusonyeza kukoma mtima kosatha kwa amoyo ndi akufa, am’dalitse munthu ameneyu.” (Rute 2:20a) Apatu Naomi anasintha kwambiri mmene ankaonera zinthu. Poyamba iye ananena kuti: “Yehova . . . wandichititsa kukhala wonyozeka,” koma apa anafuula mosangalala kuti: “Yehova . . . sanaleke kusonyeza kukoma mtima kosatha.” Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Naomi asinthe mmene ankaonera zinthu?

23 Naomi anali atayamba kuzindikira kuti Yehova sanamusiye. Yehova anagwiritsa ntchito Rute kuti amuthandize pobwerera ku Yuda. (Rute 1:16) Anazindikiranso kuti anagwiritsa ntchito Boazi yemwe anali mmodzi wa ‘owawombola’ kuti athandize iyeyo ndi Rute. * (Rute 2:19, 20b) Iye ayenera kuti anaganiza kuti, ‘Tsopano ndazindikira kuti Yehova sanandisiye ndipo wakhala ali nane nthawi yonseyi.’ (Werengani Salimo 136:23, 26.) Naomi ayenera kuti anayamikira kwambiri kuti Rute ndi Boazi sanataye mtima n’kusiya kumuthandiza. N’zosachita kufunsa kuti anthu onse atatuwa anasangalala kwambiri kuona kuti Naomi wapezanso mphamvu n’kupitiriza kutumikira Yehova.

24. N’chifukwa chiyani tikufunika kupitirizabe kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa Akhristu anzathu?

24 Kodi taphunzira chiyani m’buku la Rute pankhani yosonyeza chikondi chokhulupirika? Chikondi chokhulupirika chimatichititsa kuti tisamataye mtima n’kusiya kuthandiza abale ndi alongo athu omwe akhumudwa. Chimatichititsanso kuti tizichita zonse zomwe tingathe kuti tiwathandize. Pafupipafupi, akulu ayenera kumalimbikitsa anthu amene amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa ena. Tikaona kuti anthu amene anakhumudwa apezanso mphamvu n’kuyamba kutumikira Yehova, timasangalala kwambiri. (Mac. 20:35) Koma kodi chifukwa chachikulu chotichititsa kuti tizisonyezabe chikondi chokhulupirika n’chiyani? Timafuna kutsanzira komanso kusangalatsa Yehova yemwe ndi “wodzaza ndi kukoma mtima kosatha,” kapena kuti chikondi chokhulupirika.​—Eks. 34:6; Sal. 33:22.

NYIMBO NA. 130 Muzikhululuka

^ ndime 5 Yehova amafuna tizisonyeza chikondi chokhulupirika kwa abale ndi alongo athu mumpingo. Tingamvetse bwino zimene munthu amene ali ndi chikondi chokhulupirika amachita, tikaganizira mmene atumiki ena a Mulungu m’mbuyomu ankasonyezera khalidweli. Munkhaniyi tiona zimene tingaphunzire pachitsanzo cha Rute, Naomi komanso Boazi.

^ ndime 8 Kuti mumvetse bwino zimene zili munkhaniyi, tikukulimbikitsani kuti muwerenge panokha Rute chaputala 1 ndi 2.

^ ndime 17 Tikufotokoza za alongo amene amafunika kuwathandiza chifukwa chakuti munkhaniyi tikugwiritsa ntchito chitsanzo cha Naomi. Komabe mfundo zake n’zothandizanso kwa abale.

^ ndime 23 Kuti mudziwe zambiri pa udindo wa Boazi monga wowawombola, onani nkhani yakuti “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo​—‘Anali Mkazi Wabwino Kwambiri,’” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2012, tsamba 20.