NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA October 2018

Magaziniyi ili ndi nkhani zophunzira kuyambira pa December 3 mpaka 30, 2018.

Tizilankhula Zoona Zokhazokha

N’chifukwa chiyani anthu amakonda kunama, nanga zotsatira zake n’zotani? Tingatani kuti tizilankhula zoona zokhazokha?

Tiziphunzitsa Mfundo za Choonadi

Nthawi yatsalayi tiyenera kuigwiritsa ntchito poyambitsa maphunziro a Baibulo ndipo tiziphunzitsa anthu choonadi. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa tikakhala mu utumiki?

Tizikhulupirira Khristu Yemwe Ndi Mtsogoleri Wathu

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Yesu yemwe ndi mtsogoleri wathu pamene zinthu zikusintha kwambiri m’gulu la Yehova masiku ano?

Tizikhalabe ndi Mtendere Wamumtima Zinthu Zikasintha

Zinthu zikasintha mosayembekezereka pa moyo wathu, tikhoza kuda nkhawa. Kodi ‘mtendere wa Mulungu’ ungatithandize bwanji pa nthawi ngati imeneyi?