NKHANI YOPHUNZIRA 41

Timatumikira Mulungu “Wachifundo Chochuluka”

Timatumikira Mulungu “Wachifundo Chochuluka”

“Yehova amakomera mtima aliyense, ndipo ntchito zake zonse amazichitira chifundo.”​—SAL. 145:9.

NYIMBO NA. 44 Pemphero la Munthu Wovutika

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi timaganizira za munthu wotani tikamanena za munthu wachifundo?

TIKAMANENA za munthu wachifundo, timaganizira za munthu yemwe ndi wokoma mtima, wachikondi komanso wowolowa manja. Mwinanso tingakumbukire nkhani imene Yesu ananena yokhudza Msamariya wachifundo. Munthu wamtundu wina ameneyu, ‘anachitira chifundo’ Myuda wina yemwe anamenyedwa ndi achifwamba. Msamariyayo “anagwidwa chifundo” ataona Myuda wovulazidwayo ndipo anamusamalira mwachikondi. (Luka 10:29-37) Fanizo limeneli limasonyeza khalidwe labwino la Mulungu wathu lomwe ndi chifundo. Yehova amatisonyeza khalidweli chifukwa chotikonda. Iye amatichitira chifundo m’njira zambiri tsiku lililonse.

2. Kodi njira ina yosonyezera chifundo ndi iti?

2 Palinso njira ina yosonyezera chifundo. Munthu wachifundo, nthawi zina akhoza kusankha kuti asapereke chilango kwa munthu amene amayenera kulandira chilangocho. Poganizira zimenezi, tingaone kuti Yehova wakhala akutichitira tonsefe chifundo. Monga mmene wolemba masalimo ananenera, iye “sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu.” (Sal. 103:10) Komabe, nthawi zina Yehova amapereka chilango chokhwima kwa munthu yemwe wachita tchimo.

3. Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Munkhaniyi tikambirana mafunso atatu awa: N’chifukwa chiyani Yehova amasonyeza chifundo? Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kupereka chilango chokhwima kwa munthu ndi kumusonyeza chifundo? Nanga n’chiyani chingatithandize kuti tizisonyeza chifundo? Tiyeni tione mmene Mawu a Mulungu amayankhira mafunso amenewa?

CHIFUKWA CHAKE YEHOVA AMASONYEZA CHIFUNDO

4. N’chifukwa chiyani Yehova amasonyeza chifundo?

4 Yehova amakonda kuchita zinthu mwachifundo. Mtumwi Paulo analemba kuti Mulungu ndi “wachifundo chochuluka.” Pamene ankalemba zimenezi, Paulo ankafotokoza mmene Mulungu anasonyezera chifundo popereka chiyembekezo choti atumiki ake odzozedwa, omwe si angwiro akakhale kumwamba. (Aef. 2:4-7) Koma sikuti Yehova anangosonyeza chifundo kwa atumiki ake odzozedwa okha. Wolemba masalimo Davide anati, “Yehova amakomera mtima aliyense, ndipo ntchito zake zonse amazichitira chifundo.” (Sal. 145:9) Chifukwa chakuti Yehova amakonda anthu, iye amawachitira chifundo pakakhala chifukwa chomveka chochitira zimenezo.

5. Kodi Yesu anadziwa bwanji za chifundo cha Yehova?

5 Kuposa wina aliyense, Yesu amadziwa bwino mmene Yehova amakondera kusonyeza chifundo. Yehova ndi Yesu anakhala limodzi kumwamba kwa zaka zambiri Yesuyo asanabwere padzikoli. (Miy. 8:30, 31) Yesu ankaona mmene Atate wake ankasonyezera chifundo kambimbiri kwa anthu ochimwa. (Sal. 78:37-42) Akamaphunzitsa, iye nthawi zambiri ankafotokoza za khalidwe labwino la Atate wakeli.

Bambo sanachititse manyazi mwana wake amene analowerera, koma anamulandira ndi manja awiri (Onani ndime 6) *

6. Kodi Yesu anatithandiza bwanji kumvetsa chifundo cha Atate wake?

6 Monga tinanenera munkhani yapita ija, Yesu anagwiritsa ntchito fanizo la mwana wolowerera pofuna kutithandiza kumvetsa kuti Yehova amakonda kwambiri kusonyeza chifundo. Mwana ameneyu anachoka kwawo ndipo “anasakaza chuma chake chonse mwa kulowerera m’makhalidwe oipa.” (Luka 15:13) Kenako analapa n’kusiya makhalidwe ake oipawo, anadzichepetsa ndipo anabwerera kwawo. Ndiye kodi bambo ake anachita chiyani? Sipanatenge nthawi yaitali kuti mnyamatayo adziwe mmene bambo akewo ankamvera. Yesu anati: “Ali chapatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa chifundo. Pamenepo anamuthamangira ndi kumukumbatira ndipo anamupsompsona mwachikondi.” Bambowo sanachititse manyazi mwana wawoyo. M’malomwake, iwo anamukhululukira mwachifundo ndipo anamulandiranso m’banja lawo. Mwana wolowererayo anali atachita zoipa kwambiri koma chifukwa choti analapa, bambo akewo anamukhululukira. Bambo achifundowo mu fanizoli akuimira Yehova. Pofotokoza fanizoli, Yesu anasonyeza kuti Atate wake ndi wofunitsitsa kukhululukira ochimwa omwe alapa ndi mtima wonse.​—Luka 15:17-24.

7. Kodi nzeru za Yehova zikugwirizana bwanji ndi chifundo chimene amasonyeza?

7 Yehova amasonyeza chifundo chifukwa cha nzeru zake zopanda malire. Sikuti Yehova wangokhala wanzeru chifukwa choti amadziwa zinthu zambiri. Koma m’malomwake, Baibulo limati: “Nzeru yochokera kumwamba” ndi “yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino.” (Yak. 3:17) Mofanana ndi kholo lachikondi, Yehova amadziwa kuti chifundo chake chimathandiza kwambiri ana ake. (Sal. 103:13; Yes. 49:15) Popeza Yehova amasonyeza chifundo anthu ake, iwo akuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo ngakhale kuti si angwiro. Choncho nzeru zopanda malire za Yehova, zimamuchititsa kuti azisonyeza chifundo pakakhala chifukwa chochitira zimenezo. Koma iye amadziwanso nthawi imene sayenera kusonyeza chifundo. Popeza ndi wanzeru, iye salekerera zoipa pongofuna kusonyeza chifundo.

8. Kodi nthawi zina pamafunika kuchita chiyani ndi munthu yemwe wachita tchimo, nanga n’chifukwa chiyani?

8 Tiyerekeze kuti mtumiki wa Mulungu mwadala wasankha kuti azichita machimo. Kodi tiyenera kuchita chiyani? Yehova anauzira Paulo kulemba kuti: “Muleke kuyanjana” naye. (1 Akor. 5:11) Anthu amene achita machimo koma osalapa amachotsedwa mumpingo. Kuchita zimenezi n’kofunika chifukwa kumateteza abale ndi alongo athu okhulupirika komanso kumasonyeza kuti Yehova ndi woyera. Komabe ena amaganiza kuti ngati munthu wachotsedwa mumpingo ndiye kuti Mulungu sanamuchitire chifundo. Kodi zimenezi ndi zoona? Tiyeni tione.

KODI KUCHOTSA MUNTHU MUMPINGO KUMASONYEZA CHIFUNDO?

Nkhosa yomwe ikudwala ingaikidwe kwayokha koma m’busa amapitirizabe kuisamalira (Onani ndime 9-11)

9-10. Mogwirizana ndi Aheberi 12:5, 6, n’chifukwa chiyani tinganene kuti kuchotsa mumpingo osalapa kumasonyeza chifundo cha Yehova? Perekani chitsanzo.

9 Tikamva chilengezo pamisonkhano chonena kuti munthu wina amene timamudziwa komanso kumukonda “salinso wa Mboni za Yehova,” timamva chisoni kwambiri. Mwina tingamakayikire ngati kunali koyeneradi kuti munthuyo achotsedwe. Ndiye kodi n’zoona kuti kuchotsa munthu mumpingo kumasonyeza chifundo? Inde ndi choncho. Kusapereka chilango kwa munthu yemwe akufunikira chilangocho ndi kupanda nzeru, chifundo komanso chikondi. (Miy. 13:24) Kodi kuchotsa munthu wosalapa mumpingo kungamuthandize kuti asinthe? Inde. Abale ndi alongo ambiri omwe ankachita machimo aakulu ananena kuti kuchotsedwa mumpingo n’kumene kunawathandiza kuzindikira kulakwa kwawo, kulapa komanso kusintha khalidwe lawo n’kubwerera kwa Yehova.​—Werengani Aheberi 12:5, 6.

10 Taganizirani chitsanzo izi: Tiyerekeze kuti m’busa wazindikira kuti nkhosa yake ina ikudwala. Pofuna kuthandiza kuti nkhosayo ichire, iye akudziwa kuti ayenera kuichotsa kaye pakati pa zinzake. Komabe nkhosa zimakonda kukhala pamodzi ndipo zikhoza kusokonezeka ngati munthu atazilekanitsa. Kodi pamenepa tinganene kuti m’busayo akuchita nkhanza popatula nkhosa yodwalayo? Ayi si choncho. Iye akudziwa kuti ngati atalola nkhosayo kumayendabe ndi zinzake, ikhoza kupatsira nkhosa zinazo matenda akewo. Choncho kupatula nkhosa yodwalayo kungateteze gulu lonselo.​—Yerekezerani ndi Levitiko 13:3, 4.

11. (a) Kodi munthu wochotsedwa amafanana bwanji ndi nkhosa yomwe ikudwala? (b) Kodi wochotsedwa angachite zinthu ziti nanga angathandizidwe bwanji?

11 Mkhristu akachotsedwa mumpingo, tingamuyerekezere ndi nkhosa yomwe ikudwala. Tinganene kuti iye akudwala mwauzimu. (Yak. 5:14) Mofanana ndi matenda opatsirana, munthu yemwe wawononga ubwenzi wake ndi Yehova akhoza kulimbikitsa anthu enanso kuti azichita zoipa. Choncho n’chifukwa chake nthawi zina pangafunike kuchotsa mumpingo munthu yemwe akudwala mwauzimu. Chilango chimenechi chimasonyeza kuti Yehova amakonda nkhosa zake zokhulupirika ndiponso chikhoza kuthandiza wochimwayo kuzindikira kulakwa kwake n’kulapa. Pamene ali wochotsedwa iye angamapite kumisonkhano, kumene angamakalandire malangizo omuthandiza kulimbitsanso chikhulupiriro chake. Akhozanso kumapeza mabuku oti aziwerenga ndi kuphunzira. Ndiponso angamaonere pulogalamu ya JW Broadcasting®. Akulu akaona mmene akusinthira, angamamupatse malangizo nthawi ndi nthawi omuthandiza kuti akonzenso ubwenzi wake ndi Yehova n’cholinga choti abwezeretsedwe n’kukhalanso wa Mboni za Yehova. *

12. Kodi ndi njira iti imene akulu angasonyezere chikondi komanso chifundo kwa munthu wosalapa?

12 Tiyenera kumakumbukira kuti ndi anthu ochimwa osafuna kulapa okha, omwe amachotsedwa mumpingo. Akulu amazindikira kuti nkhani imeneyi ndi yaikulu ndipo saiona mopepuka. Iwo amadziwa kuti Yehova amapereka chilango “pa mlingo woyenera.” (Yer. 30:11) Amakonda abale awo ndiponso safuna kuchita chilichonse chimene chingawononge ubwenzi wawo ndi Yehova. Komabe nthawi zina pofuna kusonyeza chikondi komanso chifundo, akulu angachotse mumpingo munthu yemwe wachita tchimo.

13. N’chifukwa chiyani Mkhristu wina ku Korinto ankafunika kuchotsedwa mumpingo?

13 Taganizirani mmene mtumwi Paulo anachitira zinthu ndi munthu yemwe anachita tchimo koma osalapa. Mkhristu wina ku Korinto anatenga mkazi wa bambo ake. Zimenezi zinali zoipa kwambiri. Pa nkhani imeneyi, Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Mwamuna wogona ndi mkazi wa bambo ake, wavula bambo ake. Mwamuna ndi mkaziyo aziphedwa ndithu.” (Lev. 20:11) N’zoona kuti Paulo sakanapereka chigamulo choti munthuyo aphedwe. Koma anauza Akhristu a ku Korinto kuti amuchotse mumpingo. Khalidwe loipa la munthuyo linkasokoneza anthu ena mumpingo moti anthu enanso sankaona kuti limeneli ndi tchimo lalikulu.​—1 Akor. 5:1, 2, 13.

14. Kodi Paulo anasonyeza bwanji chifundo kwa munthu wochotsedwa ku Korinto, nanga n’chifukwa chiyani? (2 Akorinto 2:5-8, 11)

14 Patapita nthawi, Paulo anamva zoti munthu uja wasintha kwambiri. Munthu wochimwayo anali atalapa kuchokera pansi pa mtima. Ngakhale kuti munthuyo anachititsa manyazi mpingo, Paulo anauza akulu kuti sankafunika kuchita zinthu “mwamphamvu kwambiri” kapena kuti mokhwimitsa zinthu. Iye anawalangiza kuti: “Mukhululukireni ndi mtima wonse ndi kumutonthoza.” Ndipo anapereka chifukwa chimene anawauzira zimenezi ponena kuti: “Kuopera kuti mwina wotereyu angamezedwe ndi chisoni chake chopitirira malire.” Paulo anamvera chisoni munthu amene analapayo. Iye sankafuna kuona munthuyo akuvutika kwambiri mumtima chifukwa cha zoipa zimene anachita mpaka kumaona kuti sangakhululukidwenso.​—Werengani 2 Akorinto 2:5-8, 11.

15. Kodi akulu angatani kuti aziona moyenera nkhani yopereka chilango komanso kusonyeza chifundo?

15 Mofanana ndi Yehova, akulu amakonda kuchitira ena chifundo. Iwo amapereka chilango chokhwima ngati pakufunika kutero koma amasonyezanso chifundo ngati n’zotheka ndiponso pakakhala zifukwa zomveka zochitira zimenezo. Koma ngati akulu atangomusiya munthu wochimwa osamupatsa chilango chilichonse, sichingakhale chifundo koma kulekerera zinthu. Komabe kodi ndi akulu okha omwe amafunika kusonyeza chifundo?

N’CHIYANI CHINGATHANDIZE KUTI TONSEFE TIZISONYEZA CHIFUNDO?

16. Mogwirizana ndi Miyambo 21:13, kodi Yehova amachita chiyani kwa anthu amene amalephera kusonyeza chifundo?

16 Akhristu onse amayesetsa kutsanzira chifundo cha Yehova. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’chakuti Yehova samvetsera mapemphero a anthu amene sachitira chifundo anzawo. (Werengani Miyambo 21:13.) Palibe yemwe angafune kuti Yehova asamamvetsere mapemphero ake. Choncho tizipewa kukhala anthu ouma mtima. M’malo mokana kumvetsera Mkhristu mnzathu akamatifotokozera mavuto ake, nthawi zonse tiyenera kukhala okonzeka kumvetsera “kudandaula kwa munthu wonyozeka.” Choncho tiziyesetsa kukumbukira mfundo yakuti: “Wosachita chifundo adzaweruzidwa mopanda chifundo.” (Yak. 2:13) Tikamazindikira kuti ifenso tikufunikira kusonyezedwa chifundo ndi pamenenso zimakhala zosavuta kusonyeza ena chifundo. Tiyenera kusonyeza chifundo makamaka pamene munthu walapa n’kubwerera mumpingo.

17. Kodi Mfumu Davide anasonyeza bwanji chifundo chochokera pansi pa mtima?

17 Zitsanzo za m’Baibulo, zingatithandize kuti tikhale achifundo n’kupewa kukhala anthu ouma mtima. Mwachitsanzo, taganizirani za Mfumu Davide. Nthawi zambiri, iye ankachitira ena chifundo chochokera pansi pa mtima. Ngakhale kuti Sauli ankafuna kupha Davide, iye ankachitira chifundo mfumu yodzozedwa ndi Mulunguyi ndipo sanayese kuibwezera kapena kuivulaza.​—1 Sam. 24:9-12, 18, 19.

18-19. Kodi ndi pa nthawi ziwiri ziti pamene Davide analephera kusonyeza chifundo?

18 Komabe si nthawi zonse pamene Davide ankasonyeza chifundo. Mwachitsanzo, Nabala, yemwe anali wouma mtima atalankhula zamwano komanso kukana kupatsa chakudya Davide ndi amuna amene anali naye, iye anakwiya ndipo anaganiza zokapha Nabalayo ndi amuna onse a m’nyumba yake. Koma mkazi wa Nabala Abigayeli, yemwe anali wokoma mtima, anachita zinthu mofulumira ndipo anathandiza Davide kuti asapalamule mlandu wa magazi.​—1 Sam. 25:9-22, 32-35.

19 Pa nthawi ina, mneneri Natani anauza Davide za munthu wina wolemera yemwe analanda nkhosa ya munthu wina wosauka. Atamva nkhaniyi, mokwiya Davide ananena kuti: “Ndithu, pali Yehova Mulungu wamoyo, munthu wochita zimenezi ayenera kufa!” (2 Sam. 12:1-6) Davide ankadziwa kuti Chilamulo cha Mose chimanena kuti munthu akaba nkhosa imodzi ankafunika kubweza nkhosa 4. (Eks. 22:1) Ndiye mpaka kunena kuti munthuyo aphedwe? Chimenechitu chinali chilango chankhanza. Kwenikweni Natani ankafotokoza fanizo limeneli pofuna kusonyeza machimo akuluakulu amene Davideyo anachita. Koma Yehova anamuchitira Davide chifundo chachikulu kuposa mmene Davideyo akanachitira ndi munthu woba nkhosa wa m’fanizo la Natani.​—2 Sam. 12:7-13.

Mfumu Davide analephera kusonyeza chifundo kwa munthu wa m’fanizo la Natani (Onani ndime 19-20) *

20. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Davide?

20 Onani kuti Davide atakwiya kwambiri, anaganiza kuti Nabala ndi amuna omwe anali naye ankayenera kuphedwa. Ndipo kenako Davide anaweruza kuti munthu wa m’fanizo la Natani ankayeneranso kuphedwa. Koma Davide anali munthu wachikondi. Ndiye n’chifukwa chiyani anaweruza munthu wakuba nkhosa uja mwankhanza choncho? Taganizirani zimene zinali zitangomuchitikira kumene. Pa nthawiyo Davide sanali ndi chikumbumtima chabwino. Munthu akamachita nkhanza komanso kumangoweruza ena, amasonyeza kuti moyo wake wauzimu suli bwino. Yesu anachenjeza mwamphamvu otsatira ake kuti: “Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe, pakuti chiweruzo chimene mukuweruza nacho ena inunso mudzaweruzidwa nacho.” (Mat. 7:1, 2) Choncho tiyeni tiziyesetsa kupewa kukhala ouma mtima ndipo tizitsanzira Mulungu wathu yemwe ndi “wachifundo chochuluka.”

21-22. Kodi ndi njira zina ziti zimene tingasonyezere chifundo?

21 Chifundo sichitanthauza kungomvera anthu ena chisoni. M’malomwake anthu achifundo amachitapo kanthu pofuna kuthandiza ena. Choncho tonsefe tizikhala tcheru kuti tidziwe zimene anthu a m’banja lathu, mumpingo kapena m’dera lathu akufunikira. Kunena zoona, tili ndi mipata yambiri imene tingasonyezere ena chifundo. Kodi pali munthu wina amene akufunika kulimbikitsidwa? Kodi tingamuthandize mwina pomupatsa chakudya kapena kumuchitira zinthu zosonyeza kuti timamuganizira? Kodi pali Mkhristu amene wangobwezeretsedwa kumene yemwe angafunike kumutonthoza komanso kumulimbikitsa? Kodi tingauze ena uthenga wabwino wolimbikitsa? Imeneyi ndi imodzi mwa njira zabwino kwambiri zosonyezera chifundo kwa aliyense amene takumana naye.​—Yobu 29:12, 13; Aroma 10:14, 15; Yak. 1:27.

22 Ngati titakhala tcheru, tingaone kuti pali mipata yambiri imene tingasonyezere chifundo kwa ena. Tikamasonyeza chifundo, timasangalatsa kwambiri Atate wathu wakumwamba yemwe ndi Mulungu “wachifundo chochuluka.”

NYIMBO NA. 43 Pemphero Loyamikira Mulungu

^ ndime 5 Chifundo ndi limodzi mwa makhalidwe abwino kwambiri a Yehova ndiponso ndi khalidwe limene tonsefe tiyenera kukhala nawo. Munkhaniyi tikambirana zimene zimachititsa Yehova kuti azisonyeza chifundo, chifukwa chake tinganene kuti chilango chimasonyeza chifundo chake komanso zimene tingachite kuti tizitsanzira khalidwe labwinoli.

^ ndime 11 Kuti mudziwe zimene anthu amene abwezeretsedwa angachite kuti akonzenso ubwenzi wawo ndi Mulungu komanso mmene akulu angawathandizire, onani nkhani yakuti, “Yesetsani Kukonzanso Ubwenzi Wanu ndi Yehova,” yomwe ili m’magaziniyi.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Ali padenga la nyumba yake, bambo akuona mwana wake wolowerera akubwerera kunyumba ndipo akuthamanga kukamukumbatira.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Chifukwa chovutika ndi chikumbumtima, Mfumu Davide akukwiya ndi munthu wolemera wa m’fanizo la Natani ndipo akuweruza kuti ayenera kuphedwa.