1923​—⁠Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo

1923​—⁠Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo

“TIKUYEMBEKEZERA kuti chaka cha 1923 chikhala chosangalatsa kwambiri. Ndi mwayi waukulu kuuza anthu omwe akuvutika panopa kuti zinthu zikhala bwino posachedwapa.” Izi ndi zomwe Nsanja ya Olonda ya January 1, 1923 inanena. M’chaka chimenecho Ophunzira Baibulo anasintha mmene ankachitira misonkhano komanso mmene ankagwirira ntchito yolalikira. Izi zinachititsa kuti ayambe kugwirizana kwambiri ndipo mgwirizano umenewo ndi umene ulipo mpaka lero.

MISONKHANO INATHANDIZA KUTI AZIGWIRIZANA KWAMBIRI

Kalendala yomwe pankakhala malemba komanso manambala a nyimbo

M’chaka chimenechi gulu linasintha zinthu zina ndipo izi zinathandiza kuti Ophunzira Baibulo azigwirizana kwambiri. Bungwe la Watchtower linayamba kukonza malemba oti abale ndi alongo azikambirana mlungu uliwonse pamsonkhano womwe ankautchula kuti Kupemphera, Kutamanda Komanso Kupereka Maumboni. Kuonjezera pamenepo, Ophunzira Baibulo anakonza kalendala yomwe pankakhala lemba lomwe abale ndi alongo akanatha kukambirana mlungu uliwonse komanso nyimbo yomwe angamaimbe pophunzira paokha kapena pakulambira kwa pabanja.

Pamsonkhanowu Ophunzira Baibulo ankafotokoza “maumboni” a zimene zawachitikira pamene amalalikira, zinthu zimene akuyamikira Yehova, nyimbo ngakhalenso pemphero. Eva Barney, yemwe anabatizidwa mu 1923 ali ndi zaka 15, ananena kuti: “Munthu ukafuna kupereka umboni unkaimirira, n’kuyamba kufotokoza ndi mawu ngati akuti, ‘Ndikufuna ndithokoze Ambuye chifukwa cha zabwino zonse zimene andichitira.’” Abale ena ankakonda kwambiri kupereka maumboni. Mlongo Barney anaonjezera kuti: “M’bale wathu wokondedwa Godwin, yemwe anali wachikulire, ankakhala ndi zambiri zoti athokozere Ambuye. Koma mkazi wake akaona kuti yemwe akutsogolera akuoneka kuti watopa nazo, ankamukoka jekete mwamuna wakeyo ndipo ankakhala pansi.”

Kamodzi pa mwezi, mpingo uliwonse unkakhala ndi msonkhano wapadera wa Kupemphera, Kutamanda Komanso Kupereka Maumboni. Pofotokoza za msonkhano wapaderawu, Nsanja ya Olonda ya April 1, 1923, inanena kuti: “Hafu ya msonkhanowu ndi kuchitira maumboni za ntchito yolalikira komanso kulimbikitsa ofalitsa. . . . Tikukhulupirira kuti kuchita misonkhano mwa njira imeneyi kuthandiza kuti abale ndi alongo azigwirizana kwambiri.”

Charles Martin, yemwe anali wofalitsa wazaka 19 ndipo anali wa ku Vancouver ku Canada, anapindula kwambiri ndi misonkhanoyi. Iye anati: “Kumisonkhano imeneyi ndi komwe ndinaphunzira zoyenera kunena ndikafika pa nyumba ya munthu. Nthawi zambiri sipankalephera kukhala winawake woti afotokoze zimene anakumana nazo polalikira nyumba ndi nyumba. Zimenezi zinkandithandiza kudziwa zimene ndinganene komanso mmene ndingayankhire anthu otsutsa.”

NTCHITO YOLALIKIRA INATHANDIZA KUTI AZIGWIRIZANA KWAMBIRI

Kabuku komwe panopa timati Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu, ka May 1, 1923

“Masiku olalikira” anathandizanso kuti abale ndi alongo azigwirizana. Mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1923, munali chilengezo chakuti: “Kuti tizigwirizana pa ntchito yathu, tsiku la 1 May 1923 lasankhidwa kuti lidzakhale la utumiki. Ndi mmenenso zizikhalira ndi Lachiwiri loyamba la mwezi uliwonse. . . . Aliyense mumpingo azifunika kugwira nawo ntchito pa tsikuli.”

Ngakhale Ophunzira Baibulo achinyamata ankagwira nawo ntchitoyi. Hazel Burford yemwe anali ndi zaka 16 pa nthawiyo ananena kuti: “Kabuku komwe panopa timati Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu kankakhala ndi mfundo zofanana ndi zitsanzo za ulaliki zomwe tinkafunika kuloweza. a Ndinkachita zinthu zonsezi mwakhama limodzi ndi agogo anga.” Komabe mlongo Burford anatsutsidwa ndi munthu amene sankayembekezera. Iye anati: “M’bale wina wachikulire ankatsutsa kwambiri zoti ndizilankhula ndi anthu. Pa nthawiyo ena sankamvetsa zoti Ophunzira Baibulo onse, kuphatikizapo anyamata ndi atsikana, ayenera kugwira nawo ntchito yotamanda Mlengi Wamkulu.” (Sal. 148:​12, 13) Koma Mlongo Burford sanasiye kulalikira. Iye anakalowa kalasi yachiwiri ya Sukulu ya Giliyadi ndipo anakatumikira ku Panama ngati mmishonale. Patapita nthawi abalewo anasintha maganizo awo pa nkhani yakuti achinyamata azilalikira nawo.

MISONKHANO IKULUIKULU INATHANDIZA KUTI AZIGWIRIZANA KWAMBIRI

Misonkhano yadera komanso yachigawo inathandiza kuti abale azigwirizana kwambiri. Yambiri mwa misonkhanoyi inkakhala ndi masiku olalikira ngati mmene zinalili ndi msonkhano wa ku Winnipeg, ku Canada. Pa 31 March, ku Winnipeg kunachitika ntchito yapadera yolalikira ndipo anthu onse omwe anasonkhana anapemphedwa kuti agwire nawo ntchitoyi. Pa masiku ngati amenewa anthu ambiri ankamva uthenga wabwino ndipo pankakhala zotsatira zabwino. Pa 5 August, anthu pafupifupi 7,000 anapezeka pamsonkhano wina ku Winnipeg. Pa nthawiyo chimenechi chinali chiwerengero chokwera kwambiri poyerekezera ndi misonkhano ina yomwe inachitika ku Canada.

Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wofunika kwambiri mu 1923, unachitika pa 18 mpaka pa 26 August ku Los Angeles, ku California. Kutatsala milungu yochepa kuti msonkhanowo uchitike, manyuzipepala analengeza za msonkhanowo ndipo Ophunzira Baibulo anagawa timapepala toitanira anthu toposa 500,000. Zikwangwani zoitanira anthu kumsonkhanowu zinaikidwanso pamagalimoto ambiri.

Msonkhano wa Ophunzira Baibulo wa mu 1923 ku Los Angeles

Loweruka pa 25 August, M’bale Rutherford anakamba nkhani ya mutu wakuti “Nkhosa ndi Mbuzi,” yomwe inafotokoza momveka bwino kuti nkhosa ndi anthu omwe adzakhale m’paradaiso padziko lapansi. Pamsonkhanowu iye anawerenganso chigamulo chamutu wakuti “Chenjezo.” Chigamulochi chinatsutsa matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu ndipo chinalimbikitsa anthu amaganizo abwino kuti atuluke mu “Babulo Wamkulu.” (Chiv. 18:​2, 4) Pambuyo pake, Ophunzira Baibulo akhama padziko lonse anagawa kapepala kokhala ndi chigamulochi.

“Zimenezi zithandiza kuti abale azigwirizana kwambiri”

Pa tsiku lomaliza la msonkhanowu, anthu oposa 30,000 anamvetsera nkhani ya M’bale Rutherford yamutu wakuti “Mitundu Yonse Ikupita ku Aramagedo, Koma Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali ndi Moyo Sadzafa.” Chifukwa chakuti ankayembekezera kuti pamsonkhanowo padzakhala anthu ambiri, Ophunzira Baibulo anachita lendi bwalo lina la masewera lomwe linali litangomangidwa kumene ku Los Angeles. Kuti aliyense azidzamva bwinobwino, abale anagwiritsa ntchito masipika a m’bwalo la maseweralo ndipo njira imeneyi yogwiritsa ntchito zokuzira mawu inali itangoyamba kumene. Anthu ena ambiri anamvetsera msonkhanowo kudzera pa wailesi.

NTCHITO YOLALIKIRA INAWONJEZEREKA M’MAYIKO ENA

Mu 1923, ntchito yolalikira inawonjezereka kwambiri ku Africa, Europe, India, komanso South America. Ku India, M’bale A. J. Joseph yemwe anali ndi mkazi ndi ana 6 ankathandiza pantchito yosindikiza mabuku a Chihindi, Chitamili, Chitelugu ndi Chiudu.

William R. Brown ndi banja lake

Alfred Joseph ndi Leonard Blackman, omwe anali Ophunzira Baibulo a ku Sierra Leone, analemba kalata n’kuitumiza kulikulu lathu yopempha kuti awathandize. Pempho lawo linayankhidwa pa 14 April, 1923. Alfred anati: “Loweruka lina usiku ndinalandira foni.” Pa foniyo anamva mawu amphamvu akuti, “Kodi ndi inu amene munalemba kalata kulikulu lathu yopempha anthu odzalalikira?” Alfred anayankha kuti, “Inde.” Munthuyo anati: “Ndiyetu anditumiza ineyo.” Amene anaimbayo anali William R. Brown. Pa nthawiyi anali atangofika kumene kuchokera ku Caribbean ndipo anali ndi mkazi wake Antonia ndi ana awo aakazi awiri Louise ndi Lucy. Sipanapite nthawi yaitali kuti abalewa akumane ndi M’bale Brown ndi banja lake.

Alfred anapitiriza kuti: “Kutacha m’mawa, ine ndi Leonard tikuphunzira Baibulo monga mmene tinkachitira mlungu uliwonse, tinangoona chimunthu chachitali chitaima pakhomo. Anali M’bale Brown. Iye anali wakhama moti ankafuna atakamba nkhani ya onse tsiku lotsatira.” Mwezi usanathe, iye anali atagawira mabuku onse amene anabwera nawo. Pasanapite nthawi yaitali, analandira mabuku enanso 5,000 koma sanachedwenso kutha. Koma sikuti iye ankadziwika monga wogulitsa mabuku. Pa nthawi yonse yomwe anakhala akutumikira Yehova mwakhama, anagwiritsa ntchito Malemba pokamba nkhani zake, zomwe zinachititsa kuti apatsidwe dzina lakuti Baibulo Brown.

Beteli ya ku Magdeburg m’ma 1920

Pa nthawiyo, ofesi ya nthambi yomwe inali mumzinda wa Barmen ku Germany inali yaing’ono, komanso zinkaonekeratu kuti asilikali a dziko la France akhoza kulowa mumzindawo. Ophunzira Baibulo anapeza malo ena ku Magdeburg, ndipo zinkaoneka kuti ntchito yosindikiza mabuku ikhoza kumayenda bwino kumeneko. Pa 19 June abale anamaliza kupakira mashini ndi zinthu zina ndipo anasamukira ku Beteli ya ku Magdeburg. Atangouza abale kulikulu lathu kuti amaliza kusamuka, tsiku lotsatira nyuzipepala inalengeza kuti dziko la France lalanda mzinda wa Barmen. Abale anaona kuti umenewu unali umboni wakuti Yehova akuwadalitsa komanso kuwateteza.

George Young ndi Sarah Ferguson (kumanja) komanso mchemwali wake

Ku Brazil, M’bale George Young, yemwe anayenda m’mayiko ambiri kukalalikira uthenga wabwino anatsegula ofesi ya nthambi ndipo anayamba kusindikiza magazini a Nsanja ya Olonda mu Chipwitikizi. Pa miyezi yochepa chabe, iye anagawa magazini ndi timabuku zoposa 7,000. Sara Ferguson anasangalala kwambiri pamene M’bale Young anapita kukachezera banja lake. Mlongo Ferguson anakhala akuwerenga magazini a Nsanja ya Olonda kuyambira mu 1899, koma anali asanapeze mwayi wobatizidwa posonyeza kuti wadzipereka kwa Yehova. Patangopita miyezi yochepa, Mlongo Ferguson ndi ana ake 4 anabatizidwa.

KUTUMIKIRA MULUNGU MWAKHAMA KOMANSO MOSANGALALA

Chakumapeto kwa chaka, Nsanja ya Olonda ya December 15, 1923, inafotokoza mmene kusintha pa nkhani ya mmene ankagwirira ntchito yolalikira komanso mmene ankachitira misonkhano, zinathandizira kuti abale azigwirizana kwambiri. Nsanjayo inati: “Zikuonekeratu kuti moyo wauzimu wa mipingo . . . uli bwino kwambiri . . . Tiyeni tivale zida zonse ndipo tizitumikira Mulungu mwakhama komanso motsimikiza mtima m’chaka chikubwerachi. Tizichita zimenezi mosangalala.

Chaka cha 1924 chinalinso chosangalatsa kwa Ophunzira Baibulo. Kwa miyezi ingapo, abale a ku Beteli anali akugwira ntchito yomanga pamalo ena pachilumba cha Staten pafupi ndi ku Brooklyn. Nyumba zomwe zinkamangidwa pamalo atsopanowa zinamalizidwa kumayambiriro kwa chaka cha 1924, ndipo zimenezi zinathandiza kuti abale azigwirizana komanso uthenga wabwino ulalikidwe kwambiri.

Ogwira ntchito yomanga pachilumba cha Staten

a Panopa timati Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu.