NKHANI YOPHUNZIRA 40

‘Kuthandiza Anthu Ambiri Kuti Akhale Olungama’

‘Kuthandiza Anthu Ambiri Kuti Akhale Olungama’

“Amene akuthandiza anthu ambiri kukhala olungama adzawala ngati nyenyezi mpaka kalekale, inde, kwamuyaya.”​—DAN. 12:3.

NYIMBO NA. 151 Iye Adzaitana

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi ndi zinthu zosangalatsa ziti zomwe tikuyembekezera mu Ulamuliro wa Zaka 1,000?

 ZIDZAKHALATU zosangalatsa kwambiri anthu akadzayamba kuukitsidwa padzikoli mu Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000. Anthu onse omwe okondedwa awo anamwalira amafunitsitsa kudzawaonanso. Umu ndi mmenenso Yehova amamvera. (Yobu 14:15) Tangoganizani mmene zidzakhalire zosangalatsa kuona anthu padziko lonse akukumananso ndi okondedwa awo omwe anamwalira. Monga tinaonera munkhani yapita ija, “olungama” omwe mayina awo analembedwa m’buku la moyo, “adzauka kuti alandire moyo.” (Mac. 24:15; Yoh. 5:29) N’kutheka kuti ambiri mwa okondedwa athuwa adzakhala m’gulu la anthu oyambirira kuukitsidwa kuti akhale ndi moyo padzikoli Aramagedo ikadzangotha. b Kuwonjezera pamenepo, “osalungama” omwe analibe mwayi wodziwa Yehova ndi kumutumikira mokhulupirika pa nthawi imene anali ndi moyo, “adzauka kuti aweruzidwe.”

2-3. (a) Mogwirizana ndi Yesaya 11:9, 10, kodi ndi ntchito yaikulu yophunzitsa iti yomwe idzachitike? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Anthu onse omwe adzaukitsidwe adzafunika kuphunzitsidwa. (Yes. 26:9; 61:11) Choncho padzafunika pakhale ntchito yaikulu yophunzitsa anthu yomwe sinachitikepo ndi kale lonse. (Werengani Yesaya 11:9, 10.) Chifukwa chiyani? Mwa zina, osalungama omwe adzaukitsidwe adzafunika kuphunzitsidwa zokhudza Yesu Khristu, Ufumu wa Mulungu, dipo, kufunika kwa dzina la Yehova komanso chifukwa chake iye yekha ndi amene ali woyenera kulamulira. Ngakhalenso olungama adzafunika kuti adziwe zimene Yehova wakhala akuphunzitsa anthu ake za cholinga chake chokhudza dzikoli. Ndipotu ambiri mwa okhulupirikawa anafa Baibulo lisanamalizidwe kulembedwa. Choncho pali zambiri zomwe olungama ndi osalungama omwe angadzafunike kuphunzira.

3 Munkhaniyi, tikambirana mafunso awa: Kodi ntchito yaikulu yophunzitsayi idzachitika bwanji? Nanga idzakhudza bwanji nkhani yakuti mayina awo akhalebe m’buku la moyo kapena afufutidwemo? Mayankho a mafunso amenewa ndi ofunika kwambiri kwa ife masiku ano. Monga mmene tionere, maulosi ena ochititsa chidwi omwe ali m’buku la Danieli ndi la Chivumbulutso atithandiza kumvetsa zomwe zidzachitike anthu akadzaukitsidwa. Choyamba tiyeni tione zinthu zosangalatsa zomwe zinanenedweratu mu ulosi wa pa Danieli 12:1, 2.

“AMENE AGONA MUNTHAKA ADZAUKA”

4-5. Kodi lemba la Danieli 12:1, limatchula zinthu ziti zokhudza nthawi ya mapeto?

4 Werengani Danieli 12:1. Buku la Danieli limatiuza zinthu zosangalatsa zomwe zidzachitike m’nthawi ya mapeto. Mwachitsanzo, pa Danieli 12:1 amatiuza kuti Mikayeli, yemwe ndi Yesu Khristu, “waimirira kuti athandize anthu a [Mulungu].” Mbali ya ulosi imeneyi inayamba kukwaniritsidwa mu 1914, pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba.

5 Komabe Danieli anauzidwanso kuti Yesu “adzaimirira” pa “nthawi ya masautso imene sinakhalepo kuyambira pamene mtundu woyambirira wa anthu unakhalapo kufikira nthawi imeneyo.” Apatu “nthawi ya masautso” imeneyi, ndi “chisautso chachikulu” chotchulidwa pa Mateyu 24:21. Yesu adzaimirira kapena kuti adzachitapo kanthu kuti ateteze anthu a Mulungu kumapeto kwa nthawi ya masautsoyi yomwe ndi pa Aramagedo. Buku la Chivumbulutso limanena kuti anthuwa ndi khamu lalikulu lomwe ‘lidzatuluke m’chisautso chachikulu.’​—Chiv. 7:9, 14.

6. Kodi n’chiyani chidzachitike a khamu lalikulu akadzapulumuka chisautso chachikulu? Fotokozani. (Onaninso nkhani yakuti, “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” m’magaziniyi, kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya kuukitsidwa kwa omwe adzakhale padzikoli.)

6 Werengani Danieli 12:2. Kodi chidzachitike n’chiyani khamu lalikulu likadzapulumuka pa nthawi ya masautsoyi? Ulosiwu sukunena za kuukitsidwa kophiphiritsa kapena kwauzimu komwe kukuchitika masiku otsiriza ano, monga mmene tinkakhulupirira m’mbuyomu. c M’malomwake, mawuwa akunena za kuukitsidwa kwa anthu komwe kudzachitike m’dziko latsopano. N’chifukwa chiyani tikutero? Mawu akuti “munthaka,” kapena kuti m’fumbi, omwe agwiritsidwanso ntchito pa Yobu 17:16, ndi ofanana ndi mawu akuti “manda.” Choncho lemba la Danieli 12:2, likunena za kuukitsidwa kumanda komwe kudzachitike masiku otsiriza akadzatha komanso pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo.

7. (a) Kodi kuukitsidwa kwa anthu ena kuti adzalandire “moyo wosatha” kumatanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kumeneku ndi “kuuka kwabwino kwambiri”?

7 Kodi lemba la Danieli 12:2, limatanthauza chiyani likamati ena adzaukitsidwa kuti alandire “moyo wosatha”? Limatanthauza kuti pa nthawi ya zaka 1,000 anthu oukitsidwa omwe adzadziwe kapena kupitiriza kudziwa ndi kumvera Yehova ndi Yesu, adzapatsidwa moyo wosatha. (Yoh. 17:3) Kumenekutu kudzakhala “kuuka kwabwino kwambiri” kuposa kwa anthu amene anaukitsidwapo m’mbuyomu. (Aheb. 11:35) N’chifukwa chiyani? Chifukwa anthuwa sanali angwiro ndipo anamwaliranso.

8. Kodi zikutanthauza chiyani kuti ena adzauka kuti alandire ‘chitonzo ndiponso kudedwa mpaka kalekale’?

8 Koma si oukitsidwa onse omwe adzavomereze kuphunzitsidwa ndi Yehova. Ulosi wa Danieli unanena kuti ena adzauka kuti ‘alandire chitonzo ndipo adzadedwa mpaka kalekale.’ Chifukwa chakuti adzasonyeza kusamvera, mayina awo sadzalembedwa m’buku la moyo ndipo sadzapatsidwa moyo wosatha. M’malomwake, iwo “adzadedwa mpaka kalekale” kapena kuti adzawonongedwa. Choncho lemba la Danieli 12:2, likufotokoza zimene zidzachitikire oukitsidwa onse potengera zimene azidzachita pambuyo pa kuukitsidwa kwawoko. d (Chiv. 20:12) Ena adzalandira moyo wosatha pomwe ena adzawonongedwa.

‘KUTHANDIZA ANTHU AMBIRI KUKHALA OLUNGAMA’

9-10. Kodi n’chiyaninso chidzachitike pambuyo pa chisautso chachikulu, nanga ndi ndani ‘adzawale ngati kuwala kwa kuthambo’?

9 Werengani Danieli 12:3. Kodi n’chiyaninso chidzachitike pambuyo pa “nthawi ya masautso” ikubwerayi? Kuwonjezera pa zimene lemba la Danieli 12:2 limanena, vesi 3 limafotokoza chinthu china chomwe chidzachitike pambuyo pa chisautso chachikulu.

10 Kodi ndi ndani amene “adzawala ngati kuwala kwa kuthambo”? Mawu a Yesu a pa Mateyu 13:43, akutithandiza kupeza yankho la funsoli, omwe amati: “Pa nthawi imeneyo olungama adzawala kwambiri ngati dzuwa mu ufumu wa Atate wawo.” Pamenepa Yesu ankanena za “ana a ufumu” omwe ndi abale ake odzozedwa amene adzalamulire naye limodzi mu Ufumu wa kumwamba. (Mat. 13:38) Choncho lemba la Danieli 12:3, liyenera kuti likunena za odzozedwa komanso ntchito yomwe adzagwire mu Ulamuliro wa Zaka 1,000.

A 144,000 adzagwira ntchito limodzi ndi Yesu Khristu potsogolera ntchito yophunzitsa anthu yomwe idzachitike mu zaka 1,000 (Onani ndime 11)

11-12. Kodi ntchito iti yomwe a 144,000, adzagwire pa nthawi ya zaka 1,000?

11 Kodi odzozedwa adzathandiza bwanji “anthu ambiri kukhala olungama”? Iwo adzagwira ntchito limodzi ndi Yesu Khristu potsogolera ntchito yophunzitsa yomwe idzachitike padzikoli pa nthawi ya zaka 1,000. Sikuti a 144,000, adzangokhala mafumu, koma adzatumikiranso monga ansembe. (Chiv. 1:6; 5:10; 20:6) Iwo adzathandiza “pochiritsa mitundu ya anthu,” zomwe zikutanthauza kuwathandiza pang’onopang’ono kuti akhalenso angwiro. (Chiv. 22:1, 2; Ezek. 47:12) Odzozedwa adzasangalalatu kwambiri ndi ntchito imeneyi.

12 Kodi ndi enanso ati omwe ali m’gulu la “anthu ambiri” omwe adzathandizidwe kukhala olungama? Anthu amenewa akuphatikizapo omwe adzaukitsidwe, amene adzapulumuke pa Aramagedo komanso ana onse omwe angadzabadwe m’dziko latsopano. Pofika kumapeto kwa zaka 1,000, anthu onse adzakhala angwiro. Ndiye kodi ndi pa nthawi iti pamene mayina a anthu sangadzafufutidwenso m’buku la moyo ngati kuti alembedwa ndi inki?

MAYESERO OMALIZA

13-14. Kodi anthu onse angwiro adzafunika kuchita chiyani asanalandire moyo wosatha?

13 Tiyenera kukumbukira kuti kukhala wangwiro sikutanthauza kuti basi munthu adzalandira moyo wosatha. Taganizirani zimene zinachitikira Adamu ndi Hava. Iwo anali angwiro, koma ankafunika kupitirizabe kumvera Yehova Mulungu kuti apatsidwe moyo wosatha. N’zomvetsa chisoni kuti analephera kumumvera.​—Aroma 5:12.

14 Kodi zinthu zidzakhala bwanji kwa anthu padzikoli pofika kumapeto kwa zaka 1,000? Onse adzakhala angwiro. Kodi iwo adzakhala kumbali ya ulamuliro wa Yehova mpaka kalekale? Kapena kodi ena adzakhala ngati Adamu ndi Hava omwe sanamvere Mulungu ngakhale kuti anali angwiro? Padzafunika kupeza mayankho a mafunso amenewa. Koma kodi adzapezeka bwanji?

15-16. (a) Kodi ndi pa nthawi iti pomwe anthu onse adzapatsidwe mwayi wosonyeza kuti ndi okhulupirika kwa Yehova? (b) Kodi zotsatira za mayesero omaliza zidzakhala zotani?

15 Satana adzamangidwa kwa zaka 1,000. Pa nthawiyo, iye sadzatha kusocheretsa aliyense. Komabe zikadzatha zaka 1,000, Satana adzamasulidwa ndipo adzayesa kusocheretsa anthu angwiro. Pa nthawi ya mayeserowa, anthu onse angwiro adzakhala ndi mwayi wosonyeza mbali yomwe ali, pa nkhani ya dzina la Mulungu ndi ulamuliro wake. (Chiv. 20:7-10) Zimene aliyense adzachite pa nthawiyi, zidzasonyeza ngati ali woyenera kuti dzina lake lipitirizebe kukhala m’buku la moyo.

16 Anthu ena omwe chiwerengero chawo sichikudziwika adzakhala ngati Adamu ndi Hava ndipo adzakana ulamuliro wa Yehova. Ndiye kodi n’chiyani chidzawachitikire? Lemba la Chivumbulutso 20:15, limatiuza kuti: “Aliyense amene sanapezeke atalembedwa m’buku la moyo anaponyedwa m’nyanja yamoto.” Choncho anthu osamverawa adzawonongedwa kuti asakhalekonso. Koma anthu ambiri angwiro adzapambana mayesero omalizawa. Zikadzatero mayina awo sadzafufutidwanso m’buku la moyo.

“NTHAWI YAMAPETO”

17. Kodi Danieli anauzidwa kuti n’chiyani chidzachike m’nthawi yathu ino? (Danieli 12:4, 8-10)

17 N’zosangalatsa kwambiri kuganizira zinthu zomwe zidzachitike m’tsogolozi. Komabe mngelo anauza Danieli uthenga wina wofunika kwambiri wokhudza nthawi yathu ino, yomwe ndi “nthawi yamapeto.” (Werengani Danieli 12:4, 8-10; 2 Tim. 3:1-5) Mngeloyo anauza Danieli kuti: “Anthu . . . adzadziwa zinthu zambiri zoona.” Anthu a Mulungu anali kudzamvetsa bwino maulosi opezeka m’buku lake. Mngeloyo anawonjezera kuti pa nthawiyo “anthu oipa adzachita zinthu zoipa ndipo palibe munthu woipa aliyense amene adzamvetsetse mawu amenewa.”

18. Kodi n’chiyani chichitikire anthu oipa posachedwapa?

18 Masiku ano zingaoneke ngati anthu amene amachita zoipa salangidwa. (Mal. 3:14, 15) Koma posachedwapa Yesu adzaweruza anthu omwe ali ngati mbuzi n’kuwasiyanitsa ndi anthu omwe ali ngati nkhosa. (Mat. 25:31-33) Anthu oipawa sadzapulumuka pa chisautso chachikulu, ndipo sadzaukitsidwa kuti akhale m’dziko latsopano. Mayina awo sadzapezeka mu “buku la chikumbutso” lotchulidwa pa Malaki 3:16.

19. Kodi panopa ndi nthawi yoti tizichita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani? (Malaki 3:16-18)

19 Panopa ndi nthawi yoti tizisonyeza kuti sitili m’gulu la anthu oipa. (Werengani Malaki 3:16-18.) Yehova akusonkhanitsa anthu omwe amawaona kuti ndi “chuma chapadera,” kapena kuti anthu ake amtengo wapatali. N’zosakayikitsa kuti tikufuna kukhala m’gulu la anthu amenewa.

Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri kuona Danieli, okondedwa athu komanso anthu ena ambiri ‘akuuka’ kuti alandire gawo lawo m’dziko latsopano (Onani ndime 20)

20. Kodi ndi lonjezo liti limene Danieli anapatsidwa, nanga n’chifukwa chiyani mukuyembekezera mwachidwi kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli?

20 Kunena zoona, panopa tikukhala munthawi yosangalatsa kwambiri. Koma zina zosangalatsanso kwambiri zatsala pang’ono kuchitika. Posachedwapa tiona zinthu zonse zoipa zikuthetsedwa. Pambuyo pa zimenezi tidzaona kukwaniritsidwa kwa zomwe Yehova analonjeza Danieli kuti: “Udzauka kuti ulandire gawo lako pa mapeto a masikuwo.” (Dan. 12:13) Kodi mukuyembekezera mwachidwi nthawi imene Danieli limodzi ndi okondedwa anu ‘adzaukitsidwe’? Ngati zili choncho, panopa muzichita zonse zomwe mungathe kuti mukhalebe okhulupirika. Mukatero mungakhale otsimikiza kuti dzina lanu lidzapitirizabe kukhala m’buku la moyo la Yehova.

NYIMBO NA. 80 “Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova Ndi Wabwino”

a Nkhaniyi ifotokoza kamvedwe kathu katsopano kokhudza ntchito yaikulu yophunzitsa yofotokozedwa pa Danieli 12:2, 3. Tiona nthawi yomwe ntchitoyi idzagwiridwe komanso amene adzaigwire. Tionanso mmene ntchito yophunzitsayi idzathandizire anthu okhala padzikoli kukonzekera mayesero omaliza kumapeto kwa Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000.

b N’kutheka kuti kuukitsidwaku kudzayamba ndi anthu omwe akumwalira ali okhulupirika m’masiku otsiriza ano, n’kumabwerera m’mbuyo m’badwo ndi m’badwo. Ngati umu ndi mmene zidzakhalire, ndiye kuti m’badwo uliwonse udzakhala ndi mwayi wolandira anthu oukitsidwa omwe ankadziwana nawo. Kaya zinthu zidzakhala bwanji, Malemba amafotokoza kuti kuukitsidwa kwa anthu omwe adzapite kumwamba, kudzachitika mwadongosolo kapena kuti “aliyense pamalo pake.” Choncho tinganenenso kuti kuukitsidwa kwa anthu omwe adzakhale padzikoli kudzachitikanso chimodzimodzi.​—1 Akor. 14:33; 15:23.

c Zimenezi zikusintha zomwe tinafotokoza m’buku la Samalani Ulosi wa Danieli! mutu 17, komanso mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1987, tsamba 21-25.

d Mosiyana ndi zimenezi, mawu akuti “olungama” ndi “osalungama” opezeka pa Machitidwe 24:15, komanso akuti “amene anali kuchita zabwino” ndi “amene anali kuchita zoipa” opezeka pa Yohane 5:29, akunena za zochita za oukitsidwawo asanamwalire.