NKHANI YOPHUNZIRA 37

Muzikhulupirira Abale Anu

Muzikhulupirira Abale Anu

“Chikondi . . . chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse.”​—1 AKOR. 13:4, 7.

NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. N’chifukwa chiyani n’zosadabwitsa kuona kuti anthu ambiri m’dzikoli zimawavuta kukhulupirira ena?

 ANTHU m’dziko la Satanali sadziwa amene ayenera kumukhulupirira. Nthawi zambiri iwo amakhumudwitsidwa ndi amalonda, andale komanso atsogoleri azipembedzo. Zimenezi zimachititsa kuti asamakhulupirirenso anzawo, anthu oyandikana nawo ngakhalenso achibale awo. Izitu siziyenera kutidabwitsa. Baibulo linaneneratu kuti: “Masiku otsiriza . . . anthu adzakhala . . . osakhulupirika, . . . onenera anzawo zoipa, . . . ndiponso achiwembu.” M’mawu ena, anthu amasonyeza makhalidwe a mulungu wa nthawi ino, yemwe ndi wosadalarika.​—2 Tim. 3:1-4; 2 Akor. 4:4.

2. (a) Kodi tingamakhulupirire kwambiri ndani? (b) Kodi ena akhoza kumakayikira za chiyani?

2 Monga Akhristu, timadziwa kuti tingakhulupirire kwambiri Yehova. (Yer. 17:7, 8) Sitikayikira kuti iye amatikonda ndiponso kuti ‘sadzasiya’ anthu omwe ndi anzake. (Sal. 9:10) Tingakhulupirirenso Khristu Yesu chifukwa anapereka moyo wake kuti atiwombole. (1 Pet. 3:18) Ndiponso zimene zakhala zikuchitika pa moyo wathu zimatithandiza kukhulupirira kuti Baibulo limapereka malangizo odalirika. (2 Tim. 3:16, 17) Ndife otsimikiza kuti tizikhulupirira Yehova, Yesu komanso Baibulo. Komabe ena angamakayikire ngati angamakhulupirire abale ndi alongo awo mumpingo. Ndiye ngati tiyenera kuwakhulupirira, n’chifukwa chiyani?

TIMAFUNIKIRA ABALE NDI ALONGO ATHU

Padziko lonse, tili ndi abale ndi alongo odalirika omwe nawonso amakonda Yehova (Onani ndime 3)

3. Kodi ndi mwayi wamtengo wapatali uti womwe tili nawo? (Maliko 10:29, 30)

3 Yehova anatisankha kuti tikhale m’banja la anthu ake, omwe amamutumikira padziko lonse. Umenewutu ndi mwayi waukulu umene umachititsa kuti tipeze madalitso ambiri. (Werengani Maliko 10:29, 30.) Mofanana ndi ifeyo, padziko lonse pali abale ndi alongo omwenso amakonda Yehova ndipo amayesetsa kutsatira mfundo zake. Tingasiyane nawo chilankhulo, chikhalidwe komanso mmene timavalira. Komabe timawakonda ngakhale pamene takumana nawo kwa nthawi yoyamba. Timasangalala tikamatamanda komanso kulambira limodzi Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi.​—Sal. 133:1.

4. N’chifukwa chiyani timafunikira abale ndi alongo athu?

4 Panopo kuposa kale, tiyenera kukhala ogwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo athu. Nthawi zambiri amatithandiza polimbana ndi mavuto athu. (Aroma 15:1; Agal. 6:2) Iwo amatilimbikitsanso kuti tipitirizebe kukhala akhama pa utumiki wathu komanso kukhalabe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. (1 Ates. 5:11; Aheb. 10:23-25) Tangoganizani mmene tikanamvera zikanakhala kuti panalibe mpingo woti uzitithandiza kulimbana ndi adani athu, omwe ndi Satana Mdyerekezi ndi dziko lake loipali. Posachedwapa Satana ndi anthu omwe amawalamulira aukira atumiki a Mulungu. Pa nthawiyitu tidzayamikira kwambiri kuthandizidwa ndi abale ndi alongo athu.

5. N’chifukwa chiyani ena zingamawavute kukhulupirira abale ndi alongo awo?

5 Ena zimawavuta kukhulupirira abale ndi alongo awo, mwina chifukwa choti Mkhristu wina sanawasungire chinsinsi kapena sanakwaniritse zimene analonjeza. Kapenanso mwina wina mumpingo analankhula kapena kuchita zinthu zimene zinawakhumudwitsa kwambiri. Zinthu ngati zimenezi zingachititse kuti ziziwavuta kukhulupirira ena. Ndiye n’chiyani chingatithandize kuti tizikhulupirira Akhristu anzathu?

CHIKONDI CHIMATITHANDIZA KUTI TIZIKHULUPIRIRA ENA

6. Kodi chikondi chingatithandize bwanji kuti tizikhulupirira ena? (1 Akorinto 13:4-8)

6 Chikondi ndi chimene chimatithandiza kuti tizikhulupirira ena. Chaputala 13 cha 1 Akorinto chimafotokoza mbali zambiri za chikondi zomwe zingatithandize kuti tizikhulupirira kapena tiyambirenso kukhulupirira anthu ena. (Werengani 1 Akorinto 13:4-8.) Mwachitsanzo, vesi 4 limanena kuti “chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.” Yehova amaleza nafe mtima ngakhale pamene tamuchimwira. Choncho ifenso tingamalezere mtima abale athu ngati alankhula kapena kuchita zinthu zimene zatikhumudwitsa. Vesi 5 limawonjezera kuti: “[Chikondi] sichikwiya. Sichisunga zifukwa.” Choncho sitingafune kuti ‘tizisunga zifukwa,’ kapena kuti kumangokumbukirabe zimene abale athu atilakwira. Lemba la Mlaliki 7:9, limanena kuti ‘tisamafulumire kukwiya mumtima mwathu.’ Tingachite bwino kwambiri kutsatira malangizo a pa Aefeso 4:26 akuti: “Dzuwa lisalowe muli chikwiyire.”

7. Kodi mfundo za pa Mateyu 7:1-5, zingatithandize bwanji kuti tizikhulupirira ena?

7 Chinthu china chimene chingatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri abale ndi alongo athu ndi kuwaona mmene Yehova amawaonera. Mulungu amawakonda ndipo samangokhalira kufufuza zolakwa zawo. Ifenso tiyenera kumutsanzira. (Sal. 130:3) M’malo momangoganizira zolakwa zawo, tiziyesetsa kuona makhalidwe abwino amene ali nawo komanso kumaona kuti angachite zinthu zabwino. (Werengani Mateyu 7:1-5.) Tiziona kuti amafuna kuchita zabwino ndipo sichinali cholinga chawo kuti atikhumudwitse, chifukwa chikondi “chimakhulupirira zinthu zonse.” (1 Akor. 13:7) Koma zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova amayembekezera kuti tizikhulupirira ena popanda zifukwa zomveka. M’malomwake amafuna tiziwakhulupirira chifukwa choti asonyeza kuti ndi odalirika. b

8. Kodi mungatani kuti muzikhulupirira abale anu?

8 Mofanana ndi kulemekeza ena, pamatenga nthawi kuti tiyambe kukhulupirira munthu. Ndiye kodi mungatani kuti muzikhulupirira abale anu? Muyenera kuwadziwa bwino. Muzilankhula nawo kumisonkhano ya mpingo, muzilowa nawo mu utumiki, muzileza nawo mtima komanso muziwapatsa mpata woti asonyeze kuti ndi odalirika. Mwina poyamba mungafunike kusankha nkhani zimene mungauze munthu amene mukumudziwa kumene. Mukayamba kudziwana kwambiri, mwina mungamasuke n’kuyamba kumufotokozera mmene mukumvera. (Luka 16:10) Koma kodi mungatani ngati m’bale wachita zinthu zosonyeza kuti si wodalirika? Musamafulumire kusiya kugwirizana naye. Musamalole kuti zochita za ena zikuchititseni kuti musamakhulupirire abale ndi alongo onse. Pa nkhaniyi, tiyeni tione zitsanzo za atumiki ena okhulupirika a Yehova, omwe ngakhale kuti anakhumudwitsidwa sanasiye kukhulupirira ena.

MUZIPHUNZIRA KWA ANTHU AMENE SANASIYE KUKHULUPIRA ENA

Ngakhale kuti poyamba Eli sanalankhule bwino, Hana anapitirizabe kukhulupirira dongosolo la Yehova lokhudza kulambira (Onani ndime 9)

9. (a) Kodi Hana anatani kuti apitirizebe kutsatira dongosolo la Yehova lokhudza kulambira ngakhale kuti anthu ena audindo ankalakwitsa zinthu? (b) Kodi zimene zinachitikira Hana zakuphunzitsani chiyani pa nkhani yokhulupirira Yehova? (Onani chithunzi.)

9 Kodi munakhumudwitsidwapo ndi zochita za m’bale wina waudindo? Ngati ndi choncho, kuganizira chitsanzo cha Hana kungakuthandizeni. Pa nthawiyo, Eli monga mkulu wa ansembe ndi amene ankatsogolera kulambira Yehova ku Isiraeli. Koma banja lake silinali la chitsanzo chabwino. Ana ake, omwe ankatumikira monga ansembe, nthawi zambiri ankachita zinthu zoipa koma bambo awo sankawadzudzula. Yehova sanachotse Eli pa udindo wake nthawi yomweyo. Koma Hana sanasiye kutsatira dongosolo la Mulungu lokhudza kulambira pachihema pa nthawi imene Eli anali mkulu wa nsembe. Pa nthawi ina Eli ataona Hana yemwe anali wokhumudwa kwambiri akupemphera, anaganiza kuti waledzera. M’malo mofufuza zoona pa nkhaniyo, iye anayamba kumudzudzula. (1 Sam. 1:12-16) Ngakhale zinali choncho, Hana analonjeza kuti akadzakhala ndi mwana wamwamuna adzam’pereka kuti azidzatumikira kuchihema, komwe akanamasamalidwa ndi Eli. (1 Sam. 1:11) Koma kodi Yehova anali atathetsa kale nkhani yokhudza ana a Eli? Ayi, koma iye anachitapo kanthu pa nthawi yoyenera. (1 Sam. 4:17) Poyembekezera nthawiyo, Mulungu anam’patsa Hana mwana wamwamuna dzina lake Samueli.​—1 Sam. 1:17-20.

10. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti sanasiye kukhulupirira ena ngakhale kuti ena anamukhumudwitsa?

10 Kodi mnzanu wapamtima anayamba wakukhumudwitsanipo? Ngati ndi choncho, ganizirani zimene zinachitikira Mfumu Davide. Iye anali ndi mnzake wapamtima dzina lake Ahitofeli. Koma pamene Abisalomu ankafuna kulanda ufumu wa bambo ake Davide, Ahitofeli anagwirizana naye pa kuukirako. Tangoganizani mmene Davide anamvera chifukwa choukiridwa ndi mwana wake komanso munthu amene ankamuona kuti ndi mnzake. Komabe Davide sanalole kuti zimenezi zimuchititse kusiya kukhulupirira ena. Iye anapitiriza kukhulupirirabe mnzake wina dzina lake Husai yemwe sanakhale kumbali youkirayo. Apatu Davide sanalakwitse kumukhulupirira. Husai anasonyeza kuti anali mnzake wabwino chifukwa analolera ngakhale kuika moyo wake pangozi kuti athandize Davide.​—2 Sam. 17:1-16.

11. Kodi wantchito wa Nabala anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira ena?

11 Taganiziraninso chitsanzo cha mmodzi wa antchito a Nabala. Mokoma mtima Davide limodzi ndi amuna omwe anali nawo, anateteza antchito a Mwisiraeli wina dzina lake Nabala. Pa nthawi ina, Davide anapempha Nabala kuti agawire amuna omwe anali nawo chakudya chomwe akanakwanitsa. Nabala atakana, Davide anakwiya kwambiri ndipo anaganiza zokapha mwamuna aliyense m’nyumba ya Nabala. Wantchito uja anakauza mkazi wa Nabala dzina lake Abigayeli zomwe zinachitikazo. Monga mmodzi wa anthu a m’nyumba ya Nabala, iye ankadziwa kuti Abigayeli akanatha kupulumutsa moyo wake. M’malo mothawa, iye ankakhulupirira kuti Abigayeli angathe kukonza zinthu. Sankakayikira zimenezi chifukwa Abigayeli ankadziwika kuti anali mkazi wanzeru. Zomwe zinachitika pambuyo pake zimasonyeza kuti iye sanalakwitse kumukhulupirira. Mayi ameneyu anachita zinthu molimba mtima polepheretsa Davide kuti asachite zoipa zomwe anakonza. (1 Sam. 25:2-35) Abigayeli ankakhulupirira kuti Davide achita zinthu mwanzeru.

12. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira ophunzira ake ngakhale kuti iwo ankalakwitsa zinthu zina?

12 Yesu ankakhulupirira ophunzira ake ngakhale kuti iwo ankalakwitsa zinthu zina. (Yoh. 15:15, 16) Yakobo ndi Yohane atamupempha malo apadera mu Ufumu, Yesu sanakayikire zolinga zawo potumikira Yehova kapena kuwakana kuti asakhalenso atumwi ake. (Maliko 10:35-40) Patapita nthawi, ophunzira ake onse anamuthawa pa usiku umene anagwidwa. (Mat. 26:56) Komabe Yesu sanasiye kuwakhulupirira. Iye ankadziwa bwino zofooka zawo, komabe “anawakonda mpaka pa mapeto a moyo wake.” (Yoh. 13:1) Ataukitsidwa, Yesu anapatsa atumwi ake 11 okhulupirika udindo wofunika kwambiri wotsogolera pa ntchito yophunzitsa anthu komanso kusamalira nkhosa zake za mtengo wapatali. (Mat. 28:19, 20; Yoh. 21:15-17) Iyetu sanalakwitse pokhulupirira anthu omwe sanali angwirowa. Iwo anapitirizabe kukhala okhulupirika mpaka pamapeto a moyo wawo wapadzikoli. Choncho Hana, Davide, wantchito wa Nabala, Abigayeli ndi Yesu ndi zitsanzo zabwino kwambiri pa nkhani yokhulupirira anthu omwe si angwiro.

KUYAMBIRANSO KUKHULUPIRIRA ENA

13. Kodi n’chiyani chingatilepheretse kuti tizikhulupirira ena?

13 Kodi munayamba mwafotokozerapo m’bale wina nkhani yachinsinsi kenako n’kudzazindikira kuti iye sanasunge chinsinsicho? Zimenezitu zingakhale zokhumudwitsa kwambiri. Pa nthawi ina mlongo wina anafotokozera nkhani yake mkulu wina. Tsiku lotsatira mkazi wa mkuluyo anamuimbira foni kuti amulimbikitse, zomwe zinangosonyezeratu kuti anadziwa nkhani yachinsinsiyo. N’zomveka kuti mlongoyo zinayamba kumuvuta kuti azikhulupirira mkuluyo. Komabe mlongoyo anachita zoyenera popempha kuti athandizidwe. Iye anakambirana ndi mkulu wina yemwe anamuthandiza kuti ayambirenso kukhulupirira akulu.

14. Kodi n’chiyani chinathandiza m’bale wina kuti ayambirenso kukhulupirira ena?

14 M’bale wina anakhala akusemphana maganizo kwa nthawi yaitali ndi akulu ena awiri omwe ankaona kuti sangawakhulupirirenso. Komabe iye anayamba kuganizira mawu achidule koma amphamvu amene ananena m’bale wina yemwe amamulemekeza kwambiri, akuti: “Mdani wathu ndi Satana osati abale athu.” M’baleyo anapemphera komanso kuganizira kwambiri mawuwo ndipo pambuyo pake anakwanitsa kukhalanso pa mtendere ndi akulu awiri aja.

15. N’chifukwa chiyani zingatitengere nthawi kuti tiyambirenso kukhulupirira ena? Perekani chitsanzo.

15 Kodi munayamba mwasiyitsidwapo mwayi wina wautumiki? Zimenezitu zingakhale zowawa kwambiri. Grete ndi mayi ake anali Mboni zokhulupirika pa nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi ku Germany m’ma 1930, pomwe ntchito yathu inali yoletsedwa. Iye anali ndi mwayi wokopera magazini a Nsanja ya Olonda oti aziperekedwa kwa Akhristu ena. Koma abale atazindikira kuti bambo ake ankatsutsa choonadi, anamusiyitsa kuchita zimenezi poopa kuti bambo akewo angakauze otsutsa zinthu zokhudza mpingo. Komatu si mayesero okhawo omwe anakumana nawo. Pa nthawi yonse ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, abale sankapatsa Grete ndi mayi ake magazini ndipo ankapewa kuwalankhula akakumana nawo pamsewu. Zimenetu zinali zopweteka kwambiri. Iwo anakhumudwa kwambiri, moti Grete anafotokoza kuti zinamutengera nthawi yaitali kuti akhululuke n’kuyambiranso kukhulupirira abalewo. Komabe patapita nthawi, iye anazindikira kuti Yehova ayenera kuti anawakhululukira choncho nayenso ankafunika kutero. c

“Mdani wathu ndi Satana osati abale athu”

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita khama kuti tizikhulupirira abale ndi alongo?

16 Ngati inunso munakhumudwitsidwapo, muziyesetsa kuti muyambirenso kukhulupirira anthu ena. N’zoona kuti pangafunike nthawi, komabe khama lanu lingakhale ndi zotsatirapo zabwino. Mwachitsanzo, ngati munayamba mwadyapo zakudya za poizoni mungayambe kukhala osamala ndi zimene mumadya. Chakudya cha poizonicho sichingakuchititseni kuti musiye kudya zakudya zina zonse. Mofanana ndi zimenezi, sitiyenera kulola kuti zimene zinatichitikira zitichititse kusiya kukhulupirira abale ndi alongo athu omwe timadziwa kuti si angwiro. Tikayambiranso kukhulupirira ena tidzakhala osangalala ndipo tidzayamba kuganizira zimene ifeyo tingachite pothandiza ena mumpingo kuti azikhulupiriranso anthu ena.

17. N’chifukwa chiyani kukhulupirirana kuli kofunika, nanga tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

17 M’dziko la Satanali anthu ambiri sakhulupirira anzawo. Koma ifeyo tingakhulupirire abale ndi alongo athu chifukwa timawakonda ndipo nawonso amatikonda. Kukhulupirirana kotereku kungatithandize kuti tizisangalala komanso tikhale ogwirizana panopa ndipo kudzatiteteza pa nthawi yovuta m’tsogolomu. Koma bwanji ngati munakhumudwapo chifukwa cha kusadalirika kwa anthu ena? Muziona zinthu mmene Yehova amazionera, muzigwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo, muzikonda kwambiri abale anu komanso muziphunzira pa zitsanzo za anthu otchulidwa m’Baibulo. Tikhoza kusiya kukhala okhumudwa n’kuyambiranso kukhulupirira ena. Tikamachita zimenezi tingakhale ndi anzathu abwino ambiri omwe amamatirira ‘kuposa m’bale wathu.’ (Miy. 18:24) Komabe si zokwanira kuti tizingokhulupirira anthu ena. Nafenso tiyenera kukhala anthu oti ena azitikhulupirira. Munkhani yotsatira, tidzakambirana mmene ifeyo tingasonyezere kuti ndife odalirika kwa abale athu.

NYIMBO NA. 99 Khamu la Abale

a Tiyenera kumadalira abale ndi alongo athu. Komatu kuchita zimenezi si kophweka nthawi zonse chifukwa nthawi zina angatikhumudwitse. Munkhaniyi, tikambirana mmene kugwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo komanso kuganizira zitsanzo za anthu akale, kungatithandizire kuti tizidalira Akhristu anzathu kapena kuyambiranso kuwakhulupirira pambuyo poti atikhumudwitsa.

b Baibulo limatichenjeza kuti pali ena mumpingo omwe sitiyenera kuwadalira. (Yuda 4) Nthawi zina abale achinyengo angayese kupotoza ena polankhula “zinthu zopotoka.” (Mac. 20:30) Sitiyenera kuwakhulupirira anthu amenewa kapena kumvetsera zolankhula zawo.

c Kuti mudziwe zambiri zomwe zinachitikira Grete, onani Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 1974 la Chingelezi, tsamba 129-131.