NKHANI YOPHUNZIRA 37

NYIMBO NA. 118 “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”

Kalata Imene Ingatithandize Kupirira Mokhulupirika Mpaka Mapeto

Kalata Imene Ingatithandize Kupirira Mokhulupirika Mpaka Mapeto

“Zinthu zimene tinkadalira poyamba tazigwira mwamphamvu mpaka mapeto.”AHEB. 3:14.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi, tiona zimene tikuphunzira m’kalata imene mtumwi Paulo analembera Aheberi. Kalatayi itithandiza kuti tizipirira mokhulupirika mpaka mapeto.

1-2. (a) Kodi zinthu zinali bwanji ku Yudeya pamene mtumwi Paulo ankalembera kalata Aheberi? (b) N’chifukwa chiyani kalatayi inali ya pa nthawi yake?

 AKHRISTU a Chiheberi omwe ankakhala ku Yerusalemu ndi ku Yudeya anakumana ndi mavuto aakulu pambuyo poti Yesu waphedwa. Mpingo wa Chikhristu utakhazikitsidwa, Akhristuwo anayamba kuzunzidwa kwambiri. (Mac. 8:1) Kenako patapita zaka 20, otsatira a Khristu ankakumana ndi mavuto a zachuma, mwina chifukwa cha njala yomwe inagwa m’dzikolo. (Mac. 11:​27-30) Koma cha m’ma 61 C.E., Akhristu sankazunzidwa kwambiri poyerekezera ndi zimene akanakumana nazo m’tsogolo. Pa nthawi imeneyi iwo analandira kalata youziridwa ya Paulo, yomwe inali ya pa nthawi yake.

2 Kalata yopita kwa Aheberiwa inali ya pa nthawi yake chifukwa mtendere womwe Akhristuwo anali nawo unali wosakhalitsa. Paulo anapereka malangizo kwa Akhristuwo omwe akanawathandiza kupirira mayesero amene amayembekezeka kukumana nawo. Kuwonongedwa kwa mzinda wa Yerusalemu komwe Yesu ananeneratu kunali kutatsala pang’ono kuchitika. (Luka 21:20) Komabe Paulo kapena Akhristu a ku Yudeyawo sankadziwa nthawi yeniyeni yomwe mzindawo uwonongedwe. Ngakhale zinali choncho, Akhristuwo akanatha kugwiritsa ntchito nthawi imeneyo podzikonzekeretsa komanso kuyesetsa kuti akhale ndi makhalidwe monga chikhulupiriro ndi kupirira.—Aheb. 10:25; 12:​1, 2.

3. N’chifukwa chiyani buku la Aheberi lili lothandizanso kwa Akhristu masiku ano?

3 Posachedwapa tikumana ndi chisautso chachikulu kwambiri kuposa chimene Akhristu a Chiheberi ankayembekezera. (Mat. 24:21; Chiv. 16:​14, 16) Choncho tiyeni tikambirane malangizo amene Yehova anapereka kwa Akhristuwo omwe angatithandizenso masiku ano.

‘TIYESETSE MWAKHAMA KUTI TIKHALE AAKULU MWAUZIMU’

4. Kodi Ayuda omwe anadzakhala Akhristu anakumana ndi mavuto otani? (Onaninso chithunzi.)

4 Ayuda, omwe anadzakhala Akhristu, anakumana ndi mavuto aakulu. Pa nthawi ina iwo anali mtundu wosankhidwa ndi Mulungu. Mzinda wa Yerusalemu unali likulu la Ufumu wa Mulungu padziko lapansi ndipo kachisi anali likulu la kulambira koyera. Ayuda onse okhulupirika ankatsatira Chilamulo cha Mose chimene atsogoleri awo achipembedzo ankaphunzitsa. Zimene ankaphunzitsazo zinkakhudza nkhani ya zakudya, mdulidwe komanso mmene ankayenera kuchitira zinthu ndi anthu a mitundu ina. Koma Yesu atafa, Yehova sankavomerezanso nsembe zimene Ayuda ankapereka. Zimenezi zinali zovuta kwambiri kwa Akhristu a Chiyuda omwe poyamba ankatsatira Chilamulo. (Aheb. 10:​1, 4, 10) Ngakhalenso Akhristu olimba mwauzimu ngati mtumwi Petulo anavutika kuti asinthe zinthu zina. (Mac. 10:​9-14; Agal. 2:​11-14) Chifukwa chakuti ankakhulupirira mfundo zatsopano, Akhristuwo ankazunzidwa ndi atsogoleri achipembedzo a Chiyuda.

Akhristu ankafunika kugwiritsitsa choonadi n’kumapewa mfundo zabodza za atsogoleri achipembedzo a Chiyuda omwe ankawatsutsa (Onani ndime 4-5)


5. N’chifukwa chiyani Akhristu ankafunika kukhala osamala?

5 Akhristu a Chiheberi ankazunzidwa ndi magulu awiri a anthu. Kumbali ina kunali atsogoleri achipembedzo a Chiyuda omwe ankaona Akhristuwa ngati ampatuko. Pomwe kumbali ina, ena ankalimbikitsa otsatira a Khristu kuti azitsatira zinthu zina za m’Chilamulo cha Mose, mwina pofuna kuti asamazunzidwe. (Agal. 6:12) Ndiye kodi n’chiyani chikanathandiza Akhristuwa kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova?

6. Kodi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti azichita chiyani? (Aheberi 5:14–6:1)

6 M’kalata imene analembera Aheberi, Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti aziphunzira komanso kuganizira mozama Mawu a Mulungu. (Werengani Aheberi 5:14–6:1.) Pogwiritsa ntchito Malemba a Chiheberi, Paulo anafotokozera abale akewo kuti njira yolambirira ya Akhristu inali yapamwamba kuposa ya Ayuda. a Paulo ankadziwa kuti kudziwa bwino komanso kumvetsa mfundo za choonadi kukanathandiza Akhristuwo kuti azindikire komanso kupewa kupusitsidwa ndi mfundo zabodza.

7. Kodi masiku ano timakumana ndi mavuto otani?

7 Mofanana ndi m’nthawi ya Akhristu a Chiheberi, masiku anonso pali anthu amene amafalitsa nkhani zabodza zosemphana ndi mfundo zolungama za Yehova. Nthawi zambiri anthu amatsutsa mfundo za m’Baibulo zimene timakhulupirira pa nkhani ya makhalidwe. Iwo amanena kuti ndife ankhanza komanso osalolera. Maganizo a anthu ambiri ndi osiyana kwambiri ndi mmene Mulungu amaonera zinthu. (Miy. 17:15) Choncho tiyenera kuyesetsa kuti tizizindikira komanso kukana mfundo zimene otsutsa amagwiritsa ntchito pofuna kutifooketsa kapenanso kutisocheretsa.—Aheb. 13:9.

8. Kodi tingatani kuti tipitirize kukula mwauzimu?

8 Tingachite bwino kutsatira malangizo amene Paulo anapereka kwa Akhristu a Chiheberi oti apitirize kukula mwauzimu. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kumaphunzira mozama mfundo za choonadi komanso kumaganiza mmene Yehova amaganizira. Munthu amafunika kupitiriza kuchita zimenezi ngakhale pambuyo poti wadzipereka komanso kubatizidwa. Kaya takhala m’choonadi kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tiyenera kumawerenga komanso kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse. (Sal. 1:2) Kuphunzira patokha kungatithandize kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Khalidwe limeneli ndi lomwe Paulo anatsindika kwambiri m’kalata imene analembera Aheberi.—Aheb. 11:1, 6.

‘TIZIKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO CHIMENE CHINGATITHANDIZE KUDZAPEZA MOYO’

9. N’chifukwa chiyani Akhristu a Chiheberi ankafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba?

9 Akhristu a Chiheberi ankafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kuti apulumuke chisautso chomwe chinkabwera ku Yudeya. (Aheb. 10:​37-39) Yesu anachenjeza otsatira ake kuti adzathawire kumapiri akadzaona mzinda wa Yerusalemu utazunguliridwa ndi asilikali. Akhristu onse ankayenera kutsatira malangizowa kaya ankakhala mumzindawo kapena ayi. (Luka 21:​20-24) Kale asilikali akabwera kudzaukira, anthu ankathawira mumzinda wokhala ndi mpanda, ngati mmene zinalili ndi mzinda wa Yerusalemu. Choncho kuthawira kumapiri kukanaoneka ngati kusaganiza bwino ndipo zikanafunika kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro cholimba.

10. Kodi chikhulupiriro cholimba chikanathandiza Akhristu kuti achite chiyani? (Aheberi 13:17)

10 Akhristu a Chiheberi ankafunikanso kukhulupirira kwambiri anthu amene Yesu ankawagwiritsa ntchito potsogolera mpingo. Anthu amene ankatsogolerawo, ayenera kuti anapereka malangizo omwe akanathandiza Akhristuwo kudziwa nthawi yoyenera kuthawa komanso mmene akanachitira zimenezo. (Werengani Aheberi 13:17.) Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “muzimvera” pa Aheberi 13:​17, amanena za munthu amene amalimbikitsidwa kumvera chifukwa chakuti akukhulupirira yemwe akumupatsa malangizowo. Sikuti amangomvera chifukwa chakuti winayo ali ndi udindo wopereka malangizo. Choncho Akhristu a Chiheberiwo ankafunika kuti azikhulupirira kwambiri anthu amene ankawatsogolera chisautso chisanayambe. Ngati Akhristuwo ankamvera amene ankawatsogolera pa nthawi ya mtendere, zikanakhalanso zosavuta kuti adzamvere pa nthawi yovuta.

11. N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba masiku ano?

11 Masiku ano tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro, ngati mmene zinalili ndi Akhristu a Chiheberi. Tikukhala m’nthawi imene anthu ambiri amakana komanso kunyoza chenjezo la m’Baibulo lonena za mapeto a dziko loipali. (2 Pet. 3:​3, 4) Kuwonjezera pamenepo, ngakhale kuti Baibulo limafotokoza zambiri zokhudza zimene zidzachitike pa chisautso chachikulu, pali zambiri zimene sitikuzidziwa. Choncho tiyenera kukhulupirira kwambiri kuti mapeto adzafika pa nthawi yoyenera komanso kuti Yehova adzatisamalira.—Hab. 2:3.

12. Kodi n’chiyani chimene chidzatithandize kuti tipulumuke pa chisautso chachikulu?

12 Ifenso tiyenera kumakhulupirira kwambiri “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru,” amene Yehova akumugwiritsa ntchito potipatsa malangizo masiku ano. (Mat. 24:45) Chisautso chachikulu chikadzayamba tingadzalandire malangizo otithandiza kuti tipulumuke ngati mmene Akhristu a Chiheberi analandirira malangizo Aroma atabwera. Panopa m’pamene tiyenera kumakhulupirira kwambiri malangizo amene anthu omwe akutsogolera gulu la Yehova amatipatsa. Ngati panopa zimativuta kuwamvera, tisamayembekezere kuti tidzawakhulupirira komanso kuwamvera pa nthawi ya chisautso chachikulu.

13. N’chifukwa chiyani malangizo a pa Aheberi 13:5 anali ofunika?

13 Pamene ankayembekezera chizindikiro chakuti athawe, Akhristu a Chiheberi ankafunikanso kumapewa ‘kukonda ndalama’ kapena chuma. (Werengani Aheberi 13:5.) Ena mwa iwo anavutika chifukwa cha njala komanso umphawi. (Aheb. 10:​32-34) Ngakhale kuti iwo ankafunitsitsa kupirira mavuto amene ankakumana nawo chifukwa cha uthenga wabwino, ena anayamba kuona kuti chuma ndi chimene chingawateteze. Koma ngakhale akanakhala ndi ndalama zochuluka bwanji, sizikanawateteza. (Yak. 5:3) Ndipotu amene ankakonda chuma zikanawavuta kuti athawe n’kusiya nyumba ndi zinthu zawo.

14. Kodi kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kungatithandize bwanji kuti tikhale ndi maganizo oyenera pa nkhani ya chuma?

14 Tikhoza kupewa mtima wokonda chuma ngati timakhulupirira kwambiri kuti mapeto a dzikoli ali pafupi. Ndipotu anthu ‘adzataya siliva wawo m’misewu’ chifukwa adzazindikira kuti “siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku limene Yehova adzasonyeze mkwiyo wake waukulu.” (Ezek. 7:19) M’malo mofuna kukhala ndi ndalama zambiri, tizichita zinthu zimene zingatithandize kuti tizipeza zinthu zofunika kwambiri, uku tikutumikira Yehova. Izi zikuphatikizapo kupewa ngongole zosafunika kapenanso kutanganidwa ndi kusamalira zinthu zambiri zimene tili nazo. Tidzapewanso kukonda kwambiri zinthu zimene tili nazo kale. (Mat. 6:​19, 24) Pamene mapeto a dzikoli akuyandikira, chikhulupiriro chathu chingayesedwe pa nkhani ya chuma komanso zinthu zina.

“MUKUFUNIKA KUKHALA OPIRIRA”

15. N’chifukwa chiyani Akhristu a Chiheberi ankafunika kukhala opirira?

15 Akhristu a Chiheberi ankafunika kupirira mayesero pamene zinthu zinkaipiraipira ku Yudeya. (Aheb. 10:36) Ngakhale kuti Akhristu ena anazunzidwa m’mbuyomo, ambiri anakhala Akhristu pa nthawi imene kunali kamtendere. Paulo ananena kuti ngakhale kuti iwo anapirira mayesero ovuta, sanapirire ngati Yesu yemwe anafika pophedwa. (Aheb. 12:4) Chifukwa chakuti anthu ambiri ankalowa Chikhristu, Ayuda otsutsa anayamba kukwiya kwambiri komanso kuwazunza. Zaka zochepa m’mbuyomo, Paulo atafika ku Yerusalemu kunayamba chisokonezo. Ayuda oposa 40 ‘analumbira pochita kudzitemberera kuti saadya kapena kumwa chilichonse mpaka atapha Paulo.’ (Mac. 22:22; 23:​12-14) Ngakhale kuti ankadedwa komanso kuzunzidwa, Akhristuwo ankafunika kumasonkhana, kulalikira uthenga wabwino komanso kumalimbitsa chikhulupiriro chawo.

16. Kodi kalata yopita kwa Aheberi ingatithandize bwanji kuti tizikhala ndi maganizo oyenera tikamazunzidwa? (Aheberi 12:7)

16 Kodi n’chiyani chomwe chikanathandiza Akhristu a Chiheberi pa nthawi yomwe ankazunzidwa? Paulo ankadziwa kuti iwo ankafunika kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya mayesero omwe ankakumana nawo. Choncho iye anawafotokozera kuti Mulungu analola kuti iwo akumane ndi mayeserowo n’cholinga chofuna kuwaphunzitsa. (Werengani Aheberi 12:7.) Kuphunzitsidwa mwa njira imeneyi kumathandiza kuti munthu akhale ndi makhalidwe abwino. Kuganizira zimene zikanachitika pambuyo pa mayeserowo kukanathandiza Akhristuwo kuti apirire.—Aheb. 12:11.

17. Kodi Paulo anaphunzira chiyani pa nkhani yopirira mayesero?

17 Paulo analimbikitsa Akhristu a Chiheberi kuti azipirira mayesero ndipo sankayenera kutaya mtima. Zinali zomveka kuti Paulo awapatse malangizo amenewa. Popeza kuti anazunzako Akhristu, iye ankadziwa zimene Akhristuwo angakumane nazo. Komanso anali atapirirako kuzunzidwa chifukwa atakhala Mkhristu anazunzidwa m’njira zambiri. (2 Akor. 11:​23-25) Choncho Paulo analankhula motsimikiza chifukwa ankadziwa zimene zimafunika kuti munthu apirire. Anakumbutsa Akhristuwo kuti akamapirira mayesero sayenera kudzidalira okha, koma kudalira Yehova. Paulo akanatha kunena molimba mtima kuti: “Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa.”—Aheb. 13:6.

18. Kodi tiyenera kudziwa zinthu ziti za m’tsogolo kuti tizipirira tikamazunzidwa?

18 Panopa abale athu ena akuzunzidwa. Tikhoza kuwathandiza powapempherera, komanso nthawi zina kuwapatsa zimene akufunikira. (Aheb. 10:33) Komabe Baibulo limanena momveka bwino kuti “onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mogwirizana ndi Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Tim. 3:12) Choncho tonsefe tiyenera kukonzekera zimene tingakumane nazo m’tsogolo. Tiyeni tipitirize kukhulupirira Yehova ndipo tisamakayikire kuti adzatithandiza kupirira mayesero alionse omwe tingakumane nawo. Pa nthawi yake, iye adzathetsa mavuto onse omwe atumiki ake akukumana nawo.—2 Ates. 1:​7, 8.

19. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingatithandize kukonzekera chisautso chachikulu? (Onaninso chithunzi.)

19 Sitikukayikira kuti kalata imene Paulo analembera Akhristu a Chiheberi inathandiza Akhristuwo kukonzekera chisautso chimene chinkabwera. Paulo analimbikitsa abale ake kuti ayenera kuphunzira Malemba mozama komanso kuwamvetsa. Kuchita zimenezi kukanawathandiza kuti azizindikira komanso kupewa mfundo zomwe zikanasokoneza chikhulupiriro chawo. Anawalimbikitsanso kuti ayenera kulimbitsa chikhulupiriro chawo kuti adzatsatire malangizo a Yesu komanso a amene ankatsogolera mumpingo. Iye anathandiza Akhristuwo kuti azikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya mayesero n’cholinga choti awapirire komanso kuti aziona mayeserowo ngati njira imene Atate wawo wachikondi akuwaphunzitsira. Tiyeni nafenso tizitsatira malangizo ouziridwa amenewa. Tikatero tidzatha kupirira mpaka mapeto.—Aheb. 3:14.

Akhristu okhulupirika anadalitsidwa chifukwa chopirira. Atathawa ku Yudeya, iwo anapitiriza kusonkhana. Kodi tikuphunzirapo chiyani? (Onani ndime 19)

NYIMBO NA. 126 Khalani Maso, Limbani M’chikhulupiriro, Khalani Amphamvu

a M’chaputala choyamba chokha, Paulo anafotokoza mfundo za m’Malemba a Chiheberi maulendo pafupifupi 7 pofuna kusonyeza kuti njira yolambirira ya Akhristu inali yapamwamba kuposa ya Ayuda.—Aheb. 1:​5-13.