NKHANI YOPHUNZIRA 38

NYIMBO NA. 25 Chuma Chapadera

Kodi Mumamvera Machenjezo?

Kodi Mumamvera Machenjezo?

“Mmodzi adzatengedwa ndipo winayo adzasiyidwa.”MAT. 24:40.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tikambirana mafanizo atatu a Yesu komanso mmene akugwirizanirana ndi chiweruzo chomwe chidzachitike kumapeto a dziko loipali.

1. Kodi Yesu achita chiyani posachedwapa?

 TIKUKHALA munthawi imene tikuyembekezera kuti zinthu zisintha kwambiri. Posachedwapa Yesu aweruza anthu onse okhala padzikoli. Iye anafotokoza zimene zichitike tsiku lachiweruzo lisanafike. Anapatsa ophunzira ake ‘chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha mapeto a nthawi ino.’ (Mat. 24:3) Ulosiwu umapezeka m’machaputala 24 ndi 25 a buku la Mateyu komanso mu Maliko 13 ndi Luka 21.

2. Kodi tsopano tikambirana chiyani, nanga zimenezi zitithandiza bwanji?

2 Yesu anapereka mafanizo atatu othandiza komanso otichenjeza: Fanizo la nkhosa ndi mbuzi, la anamwali ochenjera ndi opusa komanso la matalente. Fanizo lililonse limatithandiza kumvetsa mmene zochita za munthu aliyense zidzakhudzire chiweruzo chomwe adzalandire. Tikamakambirana mafanizowa tiona zimene tikuphunzirapo komanso mmene tingazigwiritsire ntchito. Fanizo loyamba lomwe tikambirane ndi la nkhosa ndi mbuzi.

NKHOSA NDI MBUZI

3. Kodi ndi liti pomwe Yesu adzaweruze anthu?

3 Mufanizo la nkhosa ndi mbuzi, Yesu anafotokoza kuti adzaweruza anthu potengera mmene anachitira zinthu atamva uthenga wabwino komanso ngati anathandiza abale ake odzozedwa. (Mat. 25:​31-46) Pa nthawi ya “chisautso chachikulu,” iye adzapereka chiweruzochi Aramagedo isanachitike. (Mat. 24:21) Mofanana ndi mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi, Yesu adzalekanitsa anthu amene anathandiza mokhulupirika otsatira ake odzozedwa ndi anthu omwe sanawathandize.

4. Mogwirizana ndi Yesaya 11:​3, 4, n’chifukwa chiyani sitikayikira kuti Yesu adzaweruza anthu mwachilungamo? (Onaninso chithunzi chapachikuto.)

4 Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti, monga Woweruza wosankhidwa ndi Yehova, Yesu adzaweruza mwachilungamo. (Werengani Yesaya 11:​3, 4.) Iye amaona zochita, zoganiza ndi zolankhula za anthu komanso mmene anachitira zinthu ndi abale ake odzozedwa. (Mat. 12:​36, 37; 25:40) Yesu adzadziwa amene ankathandiza abale ake odzozedwa komanso kugwira nawo ntchito yolalikira. a Njira yaikulu imene a nkhosa zina amathandizira abale ake a Khristu, ndi kugwira nawo ntchito yolalikira. Amene anathandiza odzozedwa mwa njira imeneyi adzaweruzidwa kuti ndi “olungama” ndipo adzapatsidwa mwayi wokhala ndi “moyo wosatha” padziko lapansi. (Mat. 25:46; Chiv. 7:​16, 17) Imeneyitu ndi mphoto yaikulu kwa anthu amene akupitirizabe kukhala okhulupirika. Akadzapitiriza kukhala okhulupirika pa chisautso chachikulu komanso pambuyo pake, mayina awo adzakhalabe “mʼbuku la moyo.”—Chiv. 20:15.

Posachedwapa Yesu adzaweruza anthu kuti ali ngati nkhosa kapena mbuzi (Onani ndime 4))


5. Kodi tikuphunzira chiyani mufanizo la nkhosa ndi mbuzi, nanga ndi ndani amene ayenera kuchita chidwi ndi fanizoli?

5 Muzikhala okhulupirika. Fanizo la nkhosa ndi mbuzi limakhudza kwambiri anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo padzikoli. Sikuti iwo amangosonyeza chikhulupiriro pothandiza abale ake a Yesu pa ntchito yolalikira. Koma amamveranso mokhulupirika kagulu ka abale ake odzozedwa omwe Yesu wawasankha. (Mat. 24:45) Nawonso amene ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba amafunika kumvera chenjezo la m’fanizoli. Chifukwa chiyani? Chifukwa Yesu amaona zochita, zoganiza komanso zolankhula zawo. Iwonso amafunika kukhala okhulupirika. Ndipotu Yesu anapereka mafanizo ena awiri ochenjeza Akhristu odzozedwa. Mafanizowa alinso mu Mateyu chaputala 25. Tsopano tiyeni tikambirane fanizo la anamwali ochenjera ndi opusa.

ANAMWALI OCHENJERA NDI OPUSA

6. Kodi anamwali 5 anasonyeza bwanji kuti anali ochenjera? (Mateyu 25:​6-10)

6 Yesu anafotokoza fanizo la anamwali 10 omwe anapita kukachingamira mkwati. (Mat. 25:​1-4) Iwo ankafuna kuperekeza mkwatiyo kuphwando la ukwati wake. Yesu anafotokoza kuti anamwali 5 anali “ochenjera” pomwe 5 enawo anali “opusa.” Anamwali ochenjerawo anali tcheru komanso okonzeka. Iwo anali okonzeka kudikira mkwatiyo ngakhale mpaka usiku. Anatenga nyale kuti asakhale mumdima ndipo anatenganso mafuta owonjezera kuti mwina mkwati angachedwe kubwera. Choncho iwo anakonzekera kuti nyale zawo zisazime. (Werengani Mateyu 25:​6-10.) Mkwatiyo atafika anamwali ochenjerawo analowa naye limodzi m’nyumba yaphwando. Mofanana ndi zimenezi, Akhristu odzozedwa omwe asonyeza kuti ndi okonzeka, ali tcheru komanso ndi okhulupirika mpaka kubwera kwa Khristu, adzaonedwa kuti ndi oyenera kulowa ndi mkwati, yemwe ndi Yesu, mu Ufumu wakumwamba. b (Chiv. 7:​1-3) Nanga bwanji za anamwali 5 opusa?

7. Kodi n’chiyani chinachitikira anamwali 5 opusa, ndipo n’chifukwa chiyani?

7 Mosiyana ndi anamwali ochenjera aja, anamwali 5 opusa sanali okonzeka pamene mkwati ankafika. Nyale zawo zinali zitatsala pang’ono kuzima ndipo sanatenge mafuta ena owonjezera. Iwo atamva kuti mkwati watsala pang’ono kufika anapita kukagula mafuta. Pamene mkwatiyo amafika iwo anali asanabwerere. Pa nthawi imeneyo “anamwali amene anali atakonzeka aja analowa naye limodzi mʼnyumba imene munali phwando laukwati ndipo chitseko chinatsekedwa.” (Mat. 25:10) Pambuyo pake anamwali opusa aja atafika n’kumafuna kulowa, mkwatiyo anawauza kuti: “Sindikukudziwani.” (Mat. 25:​11, 12) Anamwali amenewa sanakonzekere mokwanira kubwera kwa mkwati. Kodi odzozedwa akuphunzirapo chiyani?

8-9. Kodi odzozedwa angaphunzire chiyani pa fanizo la anamwali? (Onaninso chithunzi.)

8 Muzikhala tcheru komanso okonzeka. Yesu sankalosera kuti padzakhala magulu awiri a odzozedwa, lina lomwe lidzakhale lokonzeka mpaka mapeto pomwe linalo ayi. M’malomwake ankafotokoza zomwe zidzachitikire odzozedwa ngati sangapirire mokhulupirika mpaka mapeto. Ngati zimenezi zitachitika sangadzalandire mphoto yawo. (Yoh. 14:​3, 4) Imeneyitu ndi nkhani yaikulu kwambiri. Kaya chiyembekezo chathu ndi cha kumwamba kapena cha padzikoli, tonsefe tiyenera kumvera chenjezo la m’fanizo la anamwali. Aliyense wa ife ayenera kukhala tcheru komanso wokonzeka mpaka mapeto.—Mat. 24:13.

9 Atafotokoza fanizo la anamwali pofuna kutsindika kufunika kokhala tcheru komanso okonzeka, Yesu ananenanso fanizo la matalente. Fanizoli limasonyeza kufunika kokhala akhama.

Tonsefe tingachite bwino kuganizira chenjezo la mufanizo la anamwali pokhala okonzeka, atcheru komanso kupirira mpaka mapeto (Onani ndime 8-9)


MATALENTE

10. Kodi akapolo awiri anasonyeza bwanji kuti anali okhulupirika? (Mateyu 25:​19-23)

10 Mufanizo la matalente, Yesu ananena kuti akapolo awiri anali okhulupirika kwa mbuye wawo ndipo mmodzi anali wosakhulupirika. (Mat. 25:​14-18) Akapolo awiriwo anagwira ntchito mwakhama pochulukitsa chuma cha mbuye wawo. Mbuyeyo asanachoke kupita kudziko lina anapatsa akapolowo matalente, zomwe zinali ndalama zambiri. Akapolo awiri okhulupirikawo anagwira ntchito mwakhama ndipo anagwiritsa ntchito ndalamazo mwanzeru. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Mbuyeyo pobwera anapeza kuti akapolowo achulukitsa ndalamazo kuwirikiza kawiri ndipo anawayamikira. Iye anawauza kuti ‘asangalale limodzi naye.’ (Werengani Mateyu 25:​19-23.) Koma nanga bwanji za kapolo wachitatu uja? Kodi anachita chiyani ndi ndalama zimene mbuye wake anamupatsa?

11. Kodi n’chiyani chimene chinachitikira kapolo “waulesi,” nanga n’chifukwa chiyani?

11 Kapolo mmodzi analandira talente imodzi koma anali “waulesi.” Mbuye wake ankayembekezera kuti iye agwiritsa ntchito talenteyo mwanzeru. Koma iye anakwirira talenteyo munthaka. Kapoloyo anangopereka talente yomwe anamupatsayo popanda yowonjezera. Iye analibe maganizo abwino. M’malo mopepesa chifukwa cholephera kuwonjezera ndalama ya mbuye wake, kapoloyo anatchula mbuye wakeyo kuti “munthu wovuta.” Mbuyeyo sanasangalale ndi kapoloyo. Kuwonjezera pamenepo, anamulanda talenteyo n’kumuthamangitsa panyumba ya mbuye wake.—Mat. 25:​24, 26-30.

12. Kodi akapolo awiri okhulupirika akuimira ndani masiku ano?

12 Akapolo awiri okhulupirika akuimira Akhristu odzozedwa okhulupirika. Mbuye wawo yemwe ndi Yesu, amawaitana kuti ‘asangalale limodzi naye.’ Iwo amalandira mphoto yawo yakumwamba pa kuuka koyamba. (Mat. 25:​21, 23; Chiv. 20:5b) Zimene zinachitikira kapolo waulesi zimapereka chenjezo kwa odzozedwa onse. N’chifukwa chiyani tikutero?

13-14. Kodi odzozedwa angaphunzire chiyani pa fanizo la matalente? (Onaninso chithunzi.)

13 Muzikhala akhama. Mufanizo la matalente, monganso mmene zilili mufanizo la anamwali, Yesu sankalosera kuti odzozedwa adzakhala aulesi. M’malomwake ankangofotokoza zimene zingachitike ngati iwo atasiya kukhala akhama. Iwo angalephere kukhala “pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana ndi kuwasankha” ndipo sangaloledwe kulowa mu Ufumu wakumwamba.—2 Pet. 1:10.

14 Mafanizo a Yesu onena za anamwali ndi matalente amasonyeza kuti Akhristu onse ayenera kukhala maso, okonzeka komanso akhama. Koma kodi Yesu ananenanso mawu ena ochenjeza odzozedwa? Inde. Mawu a Yesu a pa Mateyu 24:​40, 41 amanenanso za chiweruzo cha odzozedwa.

Yesu amafuna kuti odzozedwa akhalebe akhama mpaka mapeto (Onani ndime 13-14) d


KODI NDI NDANI AMENE “ADZATENGEDWA”?

15-16. Kodi lemba la Mateyu 24:​40, 41 likusonyeza bwanji kufunika koti odzozedwa akhale maso?

15 Asananene mafanizo atatu amene takambiranawa, Yesu ananena za chiweruzo chomaliza cha odzozedwa chomwe chidzasonyeze oyenera kutengedwa. Iye ananena za amuna awiri omwe ankagwira ntchito m’munda komanso akazi awiri omwe ankapera pamphero. Anthu awiri ankagwira ntchito zofanana koma Yesu ananena kuti “mmodzi adzatengedwa ndipo winayo adzasiyidwa.” (Werengani Mateyu 24:​40, 41.) Kenako anauza otsatira ake kuti: “Choncho khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwere.” (Mat. 24:42) Yesu ananenanso zofanana ndi zimenezi atapereka fanizo la anamwali. (Mat. 25:13) Kodi zimene ananenazo ndi zogwirizana? Zikuoneka choncho. Tikutero chifukwa odzozedwa okhulupirika okha ndi amene ‘adzatengedwe’ kapena kuti kulandiridwa ndi Yesu mu Ufumu wakumwamba.—Yoh. 14:3.

16 Muzikhala maso. Wodzozedwa aliyense amene sadzapitiriza kukhalabe maso sadzatengedwa limodzi ndi “osankhidwa ake.” (Mat. 24:31) Komabe anthu a Mulungu onse, kaya ali ndi chiyembekezo chotani, ayenera kuona mawu a Yesu monga chenjezo lowathandiza kupitiriza kukhala maso komanso okhulupirika.

17. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukhumudwa ngati Yehova wasankha kudzoza anthu ena ndi mzimu wake m’nthawi yathu ino?

17 Pofika pano timamudziwa bwino Mulungu wathu, choncho sitikayikira zimene amasankha. Sitimakhumudwa ngati Yehova wasankha kudzoza anthu ena okhulupirika m’masiku athu ano. c Timakumbukira fanizo la Yesu lonena za anthu omwe anabwera kudzagwira ntchito m’munda wampesa cha m’ma 5 koloko madzulo. (Mat. 20:​1-16) Anthu omwe anaitanidwa kudzagwira ntchito m’munda wampesawo mochedwa, analandira ndalama zofanana ndi anthu omwe anayamba kugwira ntchitoyo m’mawa. Mofanana ndi zimenezi, kaya odzozedwa asankhidwa pa nthawi iti, iwo adzalandira mphoto yawo yakumwamba ngati atakhalabe okhulupirika.

MUZIMVERA MACHENJEZO

18-19. Kodi takambirana mafanizo komanso machenjezo ati?

18 Kodi takambirana chiyani? Kwa anthu amene akuyembekezera moyo wosatha padziko lapansi, fanizo la nkhosa ndi mbuzi lasonyeza kufunika kokhalabe okhulupirika kwa Yehova panopa komanso pa chisautso chachikulu. Pa nthawi imeneyo, Yesu adzaweruza anthu okhulupirika kuti ndi oyenera kupita “kumoyo wosatha.”—Mat. 25:46.

19 Takambirananso mafanizo awiri omwe akupereka chenjezo kwa odzozedwa. Mufanizo la Yesu la anamwali ochenjera ndi opusa, 5 anali anzeru. Iwo anali atcheru komanso okonzekera kubwera kwa mkwati ngakhale kuti mkwatiyo anachedwa kubwera. Koma anamwali opusa sanali okonzeka. Choncho mkwati sanawalole kulowa m’nyumba ya phwando. Ifenso tiyenera kukhala okonzeka kudikira ngakhale kwa nthawi yaitali mpaka pamene Yesu adzabwere kudzawononga dziko loipali. Komanso mufanizo la Yesu la matalente takambirana za akapolo awiri okhulupirika omwe anali akhama. Iwo anagwira mwakhama ntchito imene mbuye wawo anawapatsa ndipo iye anasangalala nawo. Koma kapolo waulesi anakanidwa. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiyenera kutumikira Yehova mwakhama mpaka mapeto. Pomaliza takambirana zimene odzozedwa angachite kuti akhalebe maso n’cholinga choti ‘adzatengedwe’ ndi Yesu kuti akalandire mphoto yawo kumwamba. Iwo akuyembekezera mwachidwi nthawi imene Yesu ‘adzawasonkhanitse’ kupita kumwamba. Pambuyo pa Aramagedo, iwo adzakhala mkwatibwi pa ukwati wa Mwanawankhosa.—2 Ates. 2:1; Chiv. 19:9.

20. Kodi Yehova adzawachitira chiyani anthu amene amamvera machenjezo ake?

20 Ngakhale kuti tsiku la chiweruzo likubwera mofulumira, palibe chifukwa chochitira mantha. Ngati tingakhalebe okhulupirika, Atate wathu wakumwamba adzatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti ‘tidzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.’ (2 Akor. 4:7; Luka 21:36) Kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi, tidzasangalatsa Atate wathu ngati titamvera machenjezo opezeka m’mafanizo a Yesu. Chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova, mayina athu ‘adzalembedwa mʼbuku’ la moyo.—Dan. 12:1; Chiv. 3:5.

NYIMBO NA. 26 Munachitira Ine Amene

a Onani nkhani yakuti “Kodi Tikudziwa Chiyani pa Nkhani ya Mmene Yehova Adzaweruzire Anthu?” mu Nsanja ya Olonda ya May 2024.

b Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti “Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?” mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2015.

[Mawu a M’munsi]

d MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlongo wodzozedwa akuphunzira Baibulo ndi mtsikana yemwe wamupeza mu utumiki.