Kodi ophunzira 70 omwe Yesu anawatuma kukalalikira aja, anali kuti pomwe iye ankayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye? Kodi anali atamusiya?
Popeza kuti ophunzira 70 amenewa panalibe pamene Yesu ankayambitsa mwambowu, sitiyenera kuganiza kuti iye sankasangalala nawo kapenanso kuti anamuthawa. Iye ankangofuna kukhala ndi atumwi ake 12 okha pamwambowu.
Yesu ankasangalala ndi atumwi 12 komanso ophunzira 70 amenewa. Poyamba Yesu anasankha amuna 12 pakati pa ophunzira ake ambiri n’kuwatchula kuti atumwi. (Luka 6:12-16) Iye anali ku Galileya pomwe “anasonkhanitsa atumwi 12” ndipo “anawatumiza kuti azikalalikira za Ufumu wa Mulungu ndiponso kuchiritsa anthu.” (Luka 9:1-6) Pambuyo pake ali ku Yudeya, Yesu “anasankha anthu ena 70 nʼkuwatumiza awiriawiri.” (Luka 9:51; 10:1) Apa n’zoonekeratu kuti Yesu anali ndi anthu omutsatira m’madera osiyanasiyana omwe uthenga wake unkalalikidwa.
Ayuda omwe anakhala ophunzira a Yesu ayenera kuti chaka chilichonse ankachitabe mwambo wa Pasika limodzi ndi mabanja awo. (Eks. 12:6-11, 17-20) Imfa yake itatsala pang’ono, Yesu ndi atumwi ake anapita ku Yerusalemu. Koma sanafune kuti ophunzira ake onse ochokera ku Yudeya, Galileya ndi Pereya asonkhane pamodzi kudzachita Pasika. Apa n’zoonekeratu kuti Yesu ankafuna kuti akhale ndi atumwi ake okha pa nthawiyi. Iye anawauza kuti: “Ndakhala ndikulakalaka kwambiri kuti ndidye Pasika uyu limodzi ndi inu ndisanayambe kuzunzika.”—Luka 22:15.
Yesu anali ndi chifukwa chabwino chochitira zimenezi. Iye anali atatsala pang’ono kufa ngati “Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko.” (Yoh. 1:29) Zimenezi zinkayenera kuchitikira ku Yerusalemu komwe kwa nthawi yaitali Aisiraeli ankaperekerako nsembe kwa Mulungu. Imfa ya Yesu ikanamasula kwambiri anthu kuposa mmene akanachitira mwana wa nkhosa amene mabanja a Chiisiraeli anadya usiku umene ankachoka ku Iguputo. (1 Akor. 5:7, 8) Zimene Yesu anachitazi zikanathandiza atumwi 12 amenewa kuti akhale maziko a mpingo wa Chikhristu. (Aef. 2:20-22) N’zochititsa chidwi kuti mzinda woyera wa Yerusalemu uli ndi “miyala yomangira maziko yokwana 12” ndipo pamiyalayo panalembedwa “mayina 12 a atumwi 12 a Mwanawankhosa.” (Chiv. 21:10-14) Choncho atumwi okhulupirikawo akanakhala ndi udindo wofunika kwambiri pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Ndiye m’pomveka kuti Yesu ankafuna kukhala ndi atumwi akewa pa Pasika wake womaliza komanso pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye womwe anauyambitsa pambuyo pake.
Ophunzira 70 aja limodzi ndi ena sanakhale nawo pa chakudya chamadzulocho limodzi ndi Yesu. Koma ophunzira onse, omwe akanapitirizabe kukhala okhulupirika, akanapindula ndi mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye umene Yesu anayambitsa. Onse amene pambuyo pake akanadzozedwa, akanalowa m’pangano la Ufumu lomwe Yesu anauza atumwi ake usikuwo.—Luka 22:29, 30.