“Ufumu Wanga Suli Mbali ya Dziko Lino”

“Ufumu Wanga Suli Mbali ya Dziko Lino”

“Chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi.”​—YOH. 18:37.

NYIMBO: 15, 74

1, 2. (a) Kodi n’chiyani chikuchititsa kuti anthu azisiyana maganizo m’dzikoli? (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

MLONGO wina wa kum’mwera kwa Europe anafotokoza zimene zinamuchitikira kuti: “Kuyambira ndili wamng’ono ndakhala ndikuona zinthu zopanda chilungamo zokhazokha. Choncho ndinayamba kudana ndi boma n’kumagwirizana ndi anthu otsutsa bomalo. Ndinakhala pa chibwenzi ndi chigawenga chinachake kwa zaka zambiri.” M’bale winanso wa kum’mwera kwa Africa ankaona kuti si kulakwa kuchita zachiwawa. Iye anati: “Ndinkaona kuti mtundu wathu ndi wapamwamba kuposa mitundu ina ya anthu ndipo ndinalowa chipani chinachake. Tinkauzidwa kuti tizipha adani athu ndi mikondo ngakhalenso anthu amtundu wathu amene anali mu zipani zina.” Mlongo wina wa m’chigawo chapakati cha ku Europe anati: “Ndinali munthu watsankho. Ndinkadana ndi munthu aliyense amene ndinkasiyana naye mtundu kapena chipembedzo.”

2 Maganizo amene anthu atatuwa anali nawo ndi amene afala kwambiri masiku ano. Anthu ambiri amakonda kutsutsa boma, kulimbana pa nkhani zandale komanso kudana ndi anthu ochokera m’mayiko ena. Mogwirizana ndi zimene Baibulo linaneneratu, m’masiku otsiriza ano anthu ambiri safuna “kugwirizana ndi anzawo.” (2 Tim. 3:1, 3) Popeza anthu ambiri m’dzikoli sakugwirizana, kodi Akhristu angatani kuti azigwirizanabe? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane zimene Yesu anachita pa nthawi imene anthu ambiri ankasiyana maganizo pa nkhani zandale. Tikambirana mafunso atatu awa: N’chifukwa chiyani Yesu ankapewa kuchita nawo zandale? Kodi iye anasonyeza bwanji kuti atumiki a Mulungu sayenera kukhala mbali inayake ya ndale? Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti sitiyenera kuchita zachiwawa ngakhale anthu ena atatichitira zopanda chilungamo?

MAGANIZO A YESU PA NKHANI ZANDALE

3, 4. (a) Kodi Ayuda ankayembekezera kuti Mesiya adzachita zotani? (b) Kodi zimene Ayuda ankayembekezerazi zinakhudza bwanji ophunzira a Yesu?

3 Ayuda ambiri amene Yesu ankawalalikira sankafuna kuti azilamuliridwa ndi Aroma. Gulu linalake la Ayuda ndi limene linkalimbikitsa anthu kuti azidana ndi ufumu wa Aroma. Ambiri mwa Ayudawo ankatsatira mfundo za Yudasi wa ku Galileya. Iye anali mesiya wachinyengo ndipo ankapusitsa anthu ambiri. Wolemba mbiri ya Ayuda dzina lake Josephus ananena kuti Yudasi “ankalimbikitsa Ayuda anzake kuti aukire boma komanso ankanena kuti Ayuda amene ankalipira msonkho kwa Aroma anali amantha.” Ndipo Aroma analamula kuti Yudasi aphedwe. (Mac. 5:37) Ayuda ena a m’gulu loukira lija anafika pochita zachiwawa n’cholinga choti akwaniritse zolinga zawo.

4 Panalinso Ayuda ena ambiri amene ankayembekezera kuti Mesiya akadzabwera adzawamasula ku ulamuliro wa Aroma komanso kuchititsa kuti mtundu wachiyuda ukhale wolemekezeka. (Luka 2:38; 3:15) Ambiri ankakhulupirira kuti Mesiya adzakhazikitsa ufumu ku Isiraeli ndipo zimenezi zikachitika, Ayuda okhala m’mayiko osiyanasiyana adzatha kubwerera kwawo. Kumbukirani kuti nthawi ina Yohane Mbatizi anafunsa Yesu kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndinu kapena tiyembekezere wina?” (Mat. 11:2, 3) N’kutheka kuti Yohane ankafuna kudziwa ngati panali wina amene adzachite zonse zimene Ayuda ankayembekezera. Nawonso ophunzira awiri a Yesu amene anakumana naye pamsewu wopita ku Emau ankayembekezera kuti Mesiya achita zinthu zinazake zothandiza Isiraeli. (Werengani Luka 24:21.) Atumwi a Yesu anamufunsanso kuti: “Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?”​—Mac. 1:6.

5. (a) N’chifukwa chiyani anthu a ku Galileya ankafuna kuti Yesu akhale mfumu yawo? (b) Kodi Yesu anawathandiza bwanji kuti akhale ndi maganizo oyenera?

5 N’zosakayikitsa kuti zimene Ayuda ankayembekezerazi n’zimene zinachititsa anthu a ku Galileya kufuna kuti Yesu akhale mfumu yawo. Ayenera kuti ankaganiza kuti Yesu akhala mfumu yabwino kwambiri chifukwa chakuti ankatha kuchiritsa odwala, kudyetsa anthu anjala komanso ankaphunzitsa bwino. Yesu atadyetsa amuna pafupifupi 5,000 anazindikira zimene anthuwo ankaganiza. Baibulo limati: “Yesu atadziwa kuti iwo akufuna kumugwira kuti amuveke ufumu, anachoka ndi kupitanso kuphiri yekhayekha.” (Yoh. 6:10-15) Tsiku lotsatira, Yesu ali kutsidya lina la nyanja ya Galileya, anaona kuti ndi nthawi yabwino yowafotokozera za cholinga cha ntchito yake. Iye anawafotokozera kuti anabwera kudzathandiza anthu mwauzimu osati kungowapatsa zinthu monga chakudya. Yesu anawauza kuti: “Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka, koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha.”​—Yoh. 6:25-27.

6. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti sankafuna kukhala wolamulira wapadziko lapansi? (Onani chithunzi choyambirira.)

6 Atatsala pang’ono kuphedwa, Yesu anazindikira kuti otsatira ake ena ankayembekezera kuti iye akhazikitsa ufumu padzikoli ndipo likulu lake lidzakhala ku Yerusalemu. Koma Yesu anawathandiza kumvetsa zinthu powafotokozera fanizo la ndalama za mina. Fanizoli linasonyeza kuti “munthu wina wa m’banja lachifumu,” yemwe ankaimira Yesu, anapita kudziko lakutali ndipo zimenezi zikanatenga nthawi yaitali. (Luka 19:11-13, 15) Yesu anauzanso akuluakulu a Aroma maganizo ake pa nkhani zandale. Pa nthawi ina, Pontiyo Pilato anafunsa Yesu kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?” (Yoh. 18:33) Mwina Pilato ankaopa kuti Yesu akhoza kuyambitsa chisokonezo mu ufumu wake. Koma Yesu anamuyankha kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yoh. 18:36) Iye sankafuna kuchita nawo zandale chifukwa Ufumu wake unali wakumwamba. Choncho anauza Pilato kuti anabwera padziko lapansi “kudzachitira umboni choonadi.”​—Werengani Yohane 18:37.

Kodi mumaganizira kwambiri mavuto a m’dzikoli kapena Ufumu wa Mulungu? (Onani ndime 7)

7. N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kuti mtima wathu usayambe kukonda mbali inayake ya ndale?

7 Tikamamvetsa cholinga cha utumiki wathu ngati mmene Yesu ankachitira, tidzapeweratu kuchita chilichonse chosonyeza kuti tili mbali inayake pa nkhani zandale. Koma nthawi zina zimenezi zimakhala zovuta. Woyang’anira dera wina ananena kuti: “Masiku ano, anthu a m’dera lathu ali ndi mtima wofunitsitsa kusintha zinthu. Ndipo anthu ochuluka amakonda kwambiri dziko lawo moti amaona kuti zinthu zikhoza kuyamba kuwayendera bwino ngati atamalamuliridwa ndi anthu amtundu wawo. Koma n’zosangalatsa kuti abale ndi alongo amakhalabe ogwirizana chifukwa amaika maganizo awo pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Iwo amakhulupirira kuti Mulungu ndi amene angathetse zinthu zopanda chilungamo komanso mavuto ena amene timakumana nawo.”

KODI YESU ANATANI ANTHU ATAMUFUNSA NKHANI ZANDALE?

8. Perekani chitsanzo cha mavuto amene Ayuda ankakumana nawo.

8 Nthawi zambiri, zinthu zopanda chilungamo zikachitika anthu amayamba kukangana pa nkhani zandale. Mwachitsanzo, m’nthawi ya Yesu anthu ankakangana chifukwa cha nkhani yopereka msonkho. Ndipotu Yudasi wa ku Galileya, yemwe tamutchula kale uja, anaukira boma chifukwa cha lamulo loti munthu aliyense ayenera kulembedwa m’kaundula n’cholinga choti akuluakulu a boma azitha kudziwa ngati wapereka msonkho kapena ayi. Anthu amene ankalamuliridwa ndi Aroma, kuphatikizapo amene Yesu ankawalalikira, ankapereka msonkho pa zinthu zambiri monga katundu, malo ndi nyumba. Okhometsa misonkho ankachita zachinyengo ndipo zimenezi zinkapangitsa operekawo kuona kuti akuponderezedwa. Okhometsa misonkho ena ankachita kugula udindo wawowo n’cholinga choti azipeza ndalama zambiri. Mwachitsanzo, Zakeyu anali mkulu wa okhometsa misonkho ku Yeriko ndipo analemera chifukwa choti ankabera anthu. (Luka 19:2, 8) N’kutheka kuti panali anthu ambiri amene ankachita zinthu ngati zimenezi.

9, 10. (a) Kodi adani a Yesu anatani pofuna kuti Yesuyo akhale kumbali inayake pa nkhani zandale? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu anachita? (Onani chithunzi choyambirira.)

9 Adani a Yesu anamufunsa zokhudza msonkho pofuna kuti akhale kumbali inayake pa nkhani zandale. Msonkho umene ankamufunsa unali wa dinari imodzi ndipo nzika iliyonse ya mu ufumu wa Aroma inkafunika kupereka. (Werengani Mateyu 22:16-18.) Ayuda sankafuna kupereka msonkhowu chifukwa munthu akapereka ankasonyeza kuti akugonjera ulamuliro wa Aroma. Anthu “achipani cha Herode” anayambitsa nkhaniyi poganiza kuti Yesu akanena kuti anthu asamapereke msonkho akhoza kuimbidwa mlandu woukira boma. Komanso Yesu akanena kuti n’zoyenera kuti anthu azipereka msonkho, ndiye kuti anthu akhoza kusiya kumutsatira.

10 Yesu anapewa kusonyeza kuti ali kumbali inayake pa nkhani yamisonkho. Iye anangonena kuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.” (Mat. 22:21) Yesu ankadziwa kuti okhometsa misonkho ankachita zachinyengo. Koma sankafuna kuti zimenezi zimusokoneze n’kusiya nkhani yofunika kwambiri yokhudza Ufumu wa Mulungu. Iye ankadziwa kuti Ufumuwo ndi umene ungathetse mavuto onse a anthu. Pamenepatu anapereka chitsanzo chabwino kwa otsatira ake onse. Tiyenera kupewa kusonyeza kuti tili kumbali inayake pa nkhani zandale ngakhale mbaliyo itaoneka kuti ndi yabwino kwambiri. Akhristu ayenera kufunafuna Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake m’malo molimbana ndi zinthu zopanda chilungamo m’dzikoli.​—Mat. 6:33.

11. Kodi njira yabwino yothandizira anthu kupeza chilungamo ndi iti?

11 N’zosangalatsa kuti anthu amene poyamba ankakonda kwambiri zandale anasintha atakhala a Mboni za Yehova. Mlongo wina wa ku Great Britain ananena kuti: “Maphunziro amene ndinatenga kuyunivesite anachititsa kuti ndikhale ndi mtima wofuna kumenyera ufulu wa anthu akudafe chifukwa tinkachitiridwa zinthu zambiri zopanda chilungamo. Ndinkawina mikangano yambiri koma mumtimamu ndinkamvabe kuti palibe chimene ndikuchita. Sindinkazindikira kuti nkhani ya tsankhoyi imayambira mumtima. Koma nditayamba kuphunzira Baibulo ndinazindikira kuti ndiyenera kuyamba ndi kusintha mtima wanga. Ndipo mlongo amene anandithandiza kuti ndikwanitse kuchita zimenezi anali mzungu. Panopa ndikuchita upainiya wokhazikika mumpingo wachinenero chamanja ndipo ndimayesetsa kulalikira anthu amtundu uliwonse.”

“BWEZERA LUPANGA LAKO M’CHIMAKE”

12. Kodi “chofufumitsa” chimene Yesu ananena kuti ophunzira ake apewe chinali chiyani?

12 Nthawi ya Yesu, anthu achipembedzo ankachitanso zandale. Buku lina limanena kuti: “Magulu achipembedzo a Ayuda ankakhala ngati zipani zandale zamasiku ano.” (Daily Life in Palestine at the Time of Christ) N’chifukwa chake Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Khalani maso! Chenjerani ndi chofufumitsa cha Afarisi ndi cha Herode.” (Maliko 8:15) Ponena kuti “Herode” ayenera kuti ankatanthauza achipani cha Herode. Afarisi ankafuna kuti Ayuda amasuke ku ulamuliro wa Aroma. Mateyu anasonyeza kuti Yesu anatchulanso Asaduki popereka chenjezoli. Asadukiwo sankafuna kuti zinthu zisinthe chifukwa chakuti ambiri mwa iwo anali ndi maudindo mu ulamuliro wa Aroma. Choncho Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti azipewa chofufumitsa kapena kuti mfundo zimene magulu atatuwa ankaphunzitsa. (Mat. 16:6, 12) Chochititsa chidwi n’chakuti Yesu anapereka chenjezoli patangopita nthawi yochepa kuchokera pamene anthu ankafuna kuti iye akhale mfumu yawo.

13, 14. (a) Kodi chimachitika n’chiyani anthu akasakaniza ndale ndi chipembedzo? Perekani chitsanzo cha mu nthawi ya Yesu. (b) N’chifukwa chiyani si bwino kuchita ziwawa polimbana ndi zinthu zopanda chilungamo? (Onani chithunzi choyambirira.)

13 Nthawi zambiri anthu akamasakaniza ndale ndi chipembedzo, ziwawa sizichedwa kuyambika. Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti ayenera kupewa zimenezi. Chifukwa chimodzi chimene chinachititsa kuti ansembe aakulu komanso Afarisi akonze zoti aphe Yesu chinali chakuti ankaona kuti iye akhoza kuchititsa kuti achotsedwe pa udindo wawo wachipembedzo komanso wandale. Paja iwo anati: “Ngati timulekerera, onse adzakhulupirira mwa iye, ndipo Aroma adzabwera kudzatenga malo athu ndi mtundu wathu.” (Yoh. 11:48) Choncho Kayafa, yemwe anali mkulu wa ansembe, anatsogolera pokonza chiwembu choti Yesu aphedwe.​—Yoh. 11:49-53; 18:14.

14 Kayafa anatumiza asilikali kuti akagwire Yesu usiku. Yesu ankadziwa za chiwembuchi choncho pa nthawi imene ankadya chakudya chamadzulo chomaliza ndi atumwi ake, anawauza kuti apeze malupanga. Malupanga awiri anali okwanira kuti awaphunzitse mfundo ina yofunika kwambiri. (Luka 22:36-38) Usiku wa tsiku limenelo, Petulo anagwiritsa ntchito lupanga limodzi n’kuvulaza munthu wina amene anali m’gulu limene linabwera kudzagwira Yesu. N’zosachita kufunsa kuti iye anapsa mtima poona kuti anthu akugwira Yesu usikuwo. (Yoh. 18:10) Koma Yesu anauza Petulo kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mat. 26:52, 53) Zimene Yesu ananenazi zinali zogwirizana ndi mfundo imene iye anaipempherera usiku womwewo yakuti ophunzira akewo sayenera kukhala mbali ya dziko. (Werengani Yohane 17:16.) Mulungu ndi amene ali ndi udindo wolimbana ndi zinthu zopanda chilungamo.

15, 16. (a) Kodi Mawu a Mulungu athandiza bwanji Akhristu kuti apewe kulimbana ndi anthu ena? (b) Kodi Yehova amaona kusiyana kotani pakati pa anthu ake ndi anthu a m’dzikoli?

15 Mlongo wa kum’mwera kwa Europe amene tamutchula kumayambiriro uja anazindikiranso mfundo imeneyi. Iye anati: “Ndazindikira kuti ziwawa sizibweretsa chilungamo. Ndaona kuti anthu ambiri amene amayambitsa ziwawa amafa ndipo ena amangokhala okwiya basi. Ndinasangalala nditaphunzira m’Baibulo kuti Mulungu yekha ndi amene angabweretse chilungamo padzikoli. Uthenga umenewu ndi umene ndakhala ndikuulalikira kwa zaka 25 zapitazi.” M’bale wa kum’mwera kwa Africa uja anasiya kunyamula mkondo ndipo panopa amanyamula “lupanga la mzimu” lomwe ndi Mawu a Mulungu. Amagwiritsa ntchito Mawuwa polalikira uthenga wamtendere kwa anthu amtundu uliwonse. (Aef. 6:17) Nayenso mlongo wa m’chigawo chapakati cha ku Europe uja atakhala wa Mboni za Yehova, anakwatiwa ndi m’bale wamtundu umene kale ankadana nawo. Anthu atatu onsewa anasintha chonchi chifukwa choti ankafuna kutsanzira Khristu.

16 Kunena zoona anthuwa anachita bwino kwambiri kusintha chonchi. Paja Baibulo limayerekezera anthu m’dzikoli ndi nyanja yowinduka yomwe ikukanika kukhala bata. (Yes. 17:12; 57:20, 21; Chiv. 13:1) Nkhani zandale zimagawanitsa anthu ndiponso zimayambitsa chiwawa koma ifeyo timapitiriza kukhala mwamtendere komanso mogwirizana. Popeza anthu ndi ogawikana m’dzikoli, Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri akamaona mgwirizano wa anthu ake.​—Werengani Zefaniya 3:17.

17.(a) Tchulani zinthu zitatu zimene zimatithandiza kukhala ogwirizana. (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

17 Munkhaniyi taona zinthu zitatu zimene zimathandiza Akhristufe kukhala ogwirizana. (1) Timakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse zinthu zopanda chilungamo, (2) timapewa kukhala mbali inayake pa nkhani zandale komanso (3) timapewa kuchita zachiwawa. Koma nthawi zina tingavutike kukhala ogwirizana chifukwa cha tsankho. Munkhani yotsatira tidzakambirana zimene tingachite kuti tithetse vuto limeneli ngati mmene Akhristu oyambirira anachitira.