NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA February 2017

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira April 3 mpaka 30, 2017.

Cholinga cha Yehova Chidzakwaniritsidwa

Kodi cholinga cha Mulungu chokhudza anthu ndi dzikoli chinali chotani? N’chiyani chinalakwika? Nanga n’chifukwa chiyani tingati dipo la Yesu limathandiza kuti cholingacho chidzakwaniritsidwe?

Dipo ndi ‘Mphatso Yangwiro’ Yochokera kwa Atate

Dipo lidzathandiza kuti anthu adzapeze madalitso ambiri koma linathandizanso pa nkhani zokhudza chilengedwe chonse.

Yehova Amatsogolera Anthu Ake

Kale Mulungu agwiritsa ntchito anthu potsogolera anthu ake. N’chiyani chikusonyeza kuti iye ankatsogolera anthu ake pogwiritsa ntchito anthuwo?

Kodi Ndi Ndani Akutsogolera Anthu a Mulungu Masiku Ano?

Yesu analonjeza kuti adzakhala ndi Akhristu mpaka mapeto. Kodi iye akutsogolera bwanji anthu ake masiku ano?