Cholinga cha Yehova Chidzakwaniritsidwa

Cholinga cha Yehova Chidzakwaniritsidwa

“Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazichita. Ndakonza zimenezi ndipo ndidzazichitadi.”—YES. 46:11.

NYIMBO: 12, 132

1, 2. (a) Kodi Yehova watithandiza kuzindikira chiyani? (b) Kodi lemba la Yesaya 46:10, 11 ndi 55:11 limatilimbikitsa bwanji?

 BAIBULO limayamba ndi mawu akuti: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Gen. 1:1) Pa zinthu zimene Yehova analenga timangodziwapo zochepa chabe. (Mlal. 3:11) Mwachitsanzo, sitidziwa bwinobwino zokhudza kuwala, zinthu zimene zili m’mlengalenga komanso mphamvu imene imathandiza dziko kuti likhazikike m’malere. Koma Yehova watithandiza kuti tidziwe chifukwa chimene analengera dziko komanso anthu. Iye analenga dziko kenako analenga anthu m’chifanizo chake kuti azikhala m’dzikoli. (Gen. 1:26) Iye ankafuna kuti akhale Bambo ndipo anthu akhale ana ake.

2 Koma chaputala 3 cha buku la Genesis chimasonyeza kuti Satana anafuna kusokoneza cholinga cha Mulungu. (Gen. 3:1-7) Komabe zimenezi sizinatheke chifukwa palibe amene angalepheretse Yehova kukwaniritsa cholinga chake. (Yes. 46:10, 11; 55:11) Choncho cholinga choyambirira cha Mulungu chidzakwaniritsidwa pa nthawi yake ndendende.

3. (a) Kodi munthu ayenera kudziwa mfundo ziti kuti amvetse uthenga wa m’Baibulo? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kukambirana mfundo zimenezi panopa? (c) Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Panopa timadziwa bwino cholinga cha Yehova polenga dziko ndi anthu komanso udindo wa Yesu pokwaniritsa cholingachi. Mfundo zimenezi ndi zofunika kwambiri ndipo n’zimene tonsefe tinazidziwa titangoyamba kuphunzira Mawu a Mulungu. Ndiyeno timafunitsitsa kuthandizanso ena kuti adziwe mfundozi. Pamene tikuphunzira nkhaniyi, tiziganizira zimene tingachite kuti tiitanire anthu ambiri kumwambo wokumbukira imfa ya Yesu. (Luka 22:19, 20) Anthu amene adzafike pamwambowu adzaphunzira za cholinga cha Mulungu. Choncho pamene tsiku la Chikumbutso likuyandikira, tiyenera kuganizira mafunso amene tingagwiritse ntchito pothandiza anthu amene timaphunzira nawo kuti aone kufunika kwa mwambowu. M’nkhaniyi tikambirana mafunso atatu awa: Kodi cholinga cha Yehova polenga dziko ndi anthu n’chotani? Kodi chinalakwika n’chiyani kuti cholingacho chisakwaniritsidwe panopa? N’chifukwa chiyani tinganene kuti nsembe ya Yesu inatsegula njira yoti cholingacho chikwaniritsidwe?

KODI CHOLINGA CHA MULUNGU CHOYAMBIRIRA CHINALI CHOTANI?

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zinthu zimene Yehova analenga zimalengeza ulemerero wake?

4 Yehova ndi Mlengi wodabwitsa. Zinthu zonse zimene analenga n’zokongola komanso zapamwamba kwambiri. (Gen. 1:31; Yer. 10:12) Zinthuzi anazilenganso mwadongosolo. Timachita chidwi tikaona mmene Yehova analengera zinthu zosiyanasiyana, kaya zing’onozing’ono kapena zikuluzikulu. Mwachitsanzo, timadabwa ndi mmene maselo a thupi la munthu amagwirira ntchito, kukongola kwa mwana wakhanda komanso mmene dzuwa limaonekera likamalowa. Zinthu zimenezi zimatisangalatsa chifukwa tinalengedwa kuti tizitha kusangalala ndi zinthu zokongola.—Werengani Salimo 19:1; 104:24.

5. Kodi Yehova anachita chiyani kuti zinthu zonse zizichitika mwadongosolo?

5 Yehova anakhazikitsa malamulo a chilengedwe komanso malamulo a makhalidwe abwino n’cholinga choti zinthu zonse zizichitika mwadongosolo. (Sal. 19:7-9) Chilichonse m’chilengedwechi anachiika pamalo ake ndipo chimagwira ntchito yake mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu. Mwachitsanzo, mphamvu imene imachititsa kuti dziko likhazikike m’malere imathandizanso kuti madzi a m’nyanja asasefukire. Izi zimathandiza kuti padzikoli pakhale bata komanso kuti zamoyo zizisangalala. Anthu kuphatikizapo zolengedwa zonse zimatsatira malamulo amene Mulungu anakhazikitsawa. Zonsezi zimasonyeza kuti Mulungu ali nalo cholinga dzikoli komanso anthu. Choncho tikakhala mu utumiki, tingachite bwino kumafotokozera anthu za Mulungu amene amachititsa kuti zinthu zizichitika mwadongosolo chonchi.—Chiv. 4:11.

6, 7. Kodi Yehova anapatsa Adamu ndi Hava mphatso zina ziti?

6 Cholinga choyambirira cha Yehova chinali chakuti anthu azikhala ndi moyo padzikoli mpaka kalekale. (Gen. 1:28; Sal. 37:29) Iye anapatsa Adamu ndi Hava mphatso zosiyanasiyana zowathandiza kuti azisangalala. (Werengani Yakobo 1:17.) Yehova anawapatsa ufulu wosankha zochita, nzeru komanso mtima wotha kukonda anzawo. Mulungu anapereka malangizo kwa Adamu omuthandiza kuti azimumvera. Anamuphunzitsanso mmene angapezere zofunika pa moyo wake komanso mmene angasamalirire dziko ndi zinyama. (Gen. 2:15-17, 19, 20) Yehova analenganso Adamu ndi Hava m’njira yoti azitha kuona, kumva, kununkhiza, kuzindikira zimene zawakhudza komanso kumva kukoma kwa chakudya. Izi zinachititsa kuti azisangalala ndi zinthu zosiyanasiyana m’Paradaiso. Anthu oyambirirawa anali ndi ntchito zambiri zosangalatsa komanso zinthu zatsopano zoti aphunzire.

7 Kodi cholinga china cha Mulungu chinali chotani? Yehova analenga Adamu ndi Hava m’njira yoti abereke ana angwiro. Iye ankafuna kuti iwo aziberekana mpaka adzaze dziko lonse. Mulungu ankafuna kuti Adamu ndi Hava komanso makolo onse azikonda ana awo ngati mmene iyeyo ankawakondera. Iye anawapatsa dziko lapansili ndi zinthu zonse zimene zilimo kuti akhalemo mpaka kalekale.—Sal. 115:16.

KODI CHINALAKWIKA N’CHIYANI?

8. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anapatsa Adamu ndi Hava lamulo la pa Genesis 2:16, 17?

8 Koma zinthu sizinayende mmene Mulungu ankafunira. Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava lamulo losavuta kuti liwathandize kudziwa kuti ufulu wawo uli ndi malire. Iye anati: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Gen. 2:16, 17) Lamuloli linali lomveka bwino komanso losavuta kulitsatira. Ndipotu iwo anali ndi chakudya cha mwanaalirenji.

9, 10. (a) Kodi Satana anaimba Yehova mlandu uti? (b) Kodi Adamu ndi Hava anasankha kuchita chiyani? (Onani chithunzi patsamba 3.)

9 Satana Mdyerekezi anagwiritsa ntchito njoka popusitsa Hava kuti asamvere Atate wake Yehova. (Werengani Genesis 3:1-5; Chiv. 12:9) Choyamba Satana anafunsa kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” Zinali ngati akuwafunsa kuti: ‘Ndiye kuti mulibe ufulu wochita zimene mukufuna?’ Kenako ananama kuti: “Kufa simudzafa ayi.” Ndiyeno pofuna kukopa Hava kuti asamvere Mulungu anamuuza kuti: “Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu.” Apa ankatanthauza kuti Yehova akuwamana zipatsozo podziwa kuti ziwathandiza kukhala ozindikira. Pomaliza anawalonjeza zinthu zabodza kuti: “Mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.”

10 Apa tsopano Adamu ndi Hava anafunika kusankha zochita. Kodi anayenera kumvera Mulungu kapena njoka? Iwo anasankha kuti asamvere Mulungu. Atangochita zimenezi anakhala kumbali ya Satana yotsutsana ndi Mulungu. Iwo anakana zoti Yehova akhale Bambo awo. Mwayi wonse woti azitetezedwa ndi ulamuliro wake unathera pomwepo.—Gen. 3:6-13.

11. N’chifukwa chiyani Yehova salekerera anthu osamumvera?

11 Adamu ndi Hava atachimwa sanakhalenso angwiro. Izi zinachititsa kuti atalikirane ndi Mulungu. Paja iye ndi woyera kwambiri moti sangayang’ane “zinthu zoipa” ndipo sangathe “kuonerera khalidwe loipa.” (Hab. 1:13) Mulungu akanawalekerera zinthu zikanasokonekera kwambiri kumwamba ndiponso padzikoli. Komanso akanangoisiya nkhaniyi ndiye kuti sakanakhalanso Mulungu wodalirika. Koma Yehova ndi wokhulupirika ndipo saphwanya mfundo zake. (Sal. 119:142) Ufulu umene anapatsa Adamu ndi Hava sunawapatse chilolezo chophwanya malamulo ake. Kusamvera kwawoko kunachititsa kuti afe n’kubwerera kufumbi kumene anachokera.—Gen. 3:19.

12. N’chiyani chinachitikira ana a Adamu?

12 Adamu ndi Hava atangodya chipatso chija anatuluka m’banja la Mulungu. Iye anawathamangitsa m’munda wa Edeni ndipo panalibe mwayi woti angabwererenso. (Gen. 3:23, 24) Apa Yehova anapereka chilango chogwirizana ndi zimene analakwitsa. (Werengani Deuteronomo 32:4, 5.) Popeza anthuwo sanalinso angwiro, sakanatha kusonyeza bwinobwino makhalidwe a Mulungu. Adamu anataya mwayi wokhala ndi moyo wosatha ndipo anapatsira ana ake uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12) Ana ake analibenso mwayi woti n’kukhala ndi moyo wosatha. Komanso Adamu ndi Hava sakanatha kubereka ana angwiro ndipo n’chimodzimodzinso ndi ana awo. Kungoyambira nthawi imene Satana anachititsa kuti Adamu ndi Hava achimwe, iye sanasiyebe kusokoneza anthu.—Yoh. 8:44.

DIPO LINATHANDIZA KUTI ANTHU AGWIRIZANENSO NDI MULUNGU

13. Kodi Yehova amafuna kuti anthu achite chiyani?

13 Mulungu sanasiye kukonda anthu. Ngakhale kuti Adamu ndi Hava sanamumvere, iye amafuna kuti anthu akhalebe naye pa ubwenzi. Mulungu safuna kuti aliyense adzafe. (2 Pet. 3:9) Choncho nkhani ya mu Edeni itangochitika, iye anakonza zoti ana a Adamu adzathe kukhalanso naye pa ubwenzi. Koma anachita izi popanda kuphwanya mfundo zake zachilungamo. Kodi Yehova anachita bwanji zimenezi?

14. (a) Malinga ndi Yohane 3:16, kodi Mulungu anachita chiyani kuti anthu adzapeze moyo wosatha? (b) Kodi tingakambirane ndi anthu achidwi funso liti?

14 Werengani Yohane 3:16. Anthu ambiri amene timawaitanira ku Chikumbutso amalidziwa bwino lemba limeneli. Koma funso ndi loti, Kodi nsembe ya Yesu imathandiza bwanji kuti anthu adzapeze moyo wosatha? Ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso, mwambo wa Chikumbutso weniweniwo komanso kupitanso kwa anthu omwe adzabwere ku mwambowu zidzatipatsa mwayi wowafotokozera yankho la funso lofunikali. Anthu amenewa angachite chidwi kwambiri akayamba kumvetsa mmene Yehova anasonyezera chikondi ndi nzeru popereka dipo. Kodi tingakambirane ndi anthu mfundo ziti zokhudza dipo?

15. Kodi Yesu anasiyana bwanji ndi Adamu?

15 Yehova anapereka munthu wangwiro kuti akhale dipo. Munthu ameneyu anafunika kukhala wokhulupirika komanso wofunitsitsa kupereka moyo wake kuti apulumutse anthu ochimwa. (Aroma 5:17-19) Yehova anasamutsa moyo wa Mwana wake woyambirira kulengedwa kuchokera kumwamba kubwera padziko lapansili. (Yoh. 1:14) Choncho Yesu anali wangwiro ngati mmene Adamu analili. Koma mosiyana ndi Adamu, Yesu anamvera Yehova. Ngakhale pamene anakumana ndi mayesero aakulu, iye sanachimwe kapena kuphwanya malamulo a Mulungu.

16. N’chifukwa chiyani tinganene kuti dipo ndi mphatso yamtengo wapatali?

16 Popeza Yesu anali wangwiro, anapulumutsa anthu ku uchimo ndi imfa powafera. Adamu anali wangwiro ndipo akanatha kukhala wokhulupirika komanso womvera. N’chimodzimodzinso ndi Yesu. (1 Tim. 2:6) Iye anakhala nsembe ya dipo imene inathandiza kuti “anthu ambiri,” kaya amuna, akazi komanso ana, adzapeze moyo wosatha. (Mat. 20:28) Dipoli ndi limene linatsegula njira yoti cholinga choyambirira cha Mulungu chidzakwaniritsidwe. (2 Akor. 1:19, 20) Dipo limathandiza kuti anthu onse okhulupirika adzapeze moyo wosatha.

YEHOVA ANATSEGULA NJIRA YOTI TIBWERERE KWA IYE

17. Kodi dipo limatitsegulira mwayi wotani?

17 Yehova analolera kupereka Mwana wake wamtengo wapatali kuti akhale dipo. (1 Pet. 1:19) Iye amakonda kwambiri anthu moti analolera kuti Mwana wakeyu afe pofuna kuwapulumutsa. (1 Yoh. 4:9, 10) Apa tingati Yesu anatenga udindo wokhala bambo athu umene Adamu anataya. (1 Akor. 15:45) Zimene Yesu anachitazi zimathandiza kuti tidzapeze moyo wosatha komanso kuti tidzabwerere m’banja la Mulungu. Yehova amagwiritsa ntchito dipoli kuti alandirenso anthu m’banja lake popanda kuphwanya mfundo zake zachilungamo. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri anthu onse okhulupirika akadzakhalanso angwiro. Pa nthawiyo, mbali yakumwamba ya banja la Mulungu idzakhala yogwirizana kwambiri ndi mbali yapadziko lapansi. Mwachidule tingati tidzakhala ana enieni a Mulungu.—Aroma 8:21.

18. Kodi Yehova adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense” pa nthawi iti?

18 Zimene Satana anachita sizinalepheretse Yehova kusonyeza chikondi chake kwa anthu. Sizinalepheretsenso anthu ena kukhala okhulupirika kwa Yehova ngakhale kuti si angwiro. Chifukwa cha dipo, Yehova adzathandiza ana ake onse kuti akhale olungama. Tidzasangalala kwambiri anthu onse ‘okhulupirira Mwanayo akadzalandira moyo wosatha.’ (Yoh. 6:40) Popeza Yehova ndi wachikondi komanso wanzeru, adzathandiza anthu kuti akhalenso angwiro mogwirizana ndi cholinga chake choyambirira. Pa nthawiyo, Yehovayo adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense.”—1 Akor. 15:28.

19. (a) Kodi mtima woyamikira dipo uyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani? (Onani bokosi lakuti, “ Tiyeni Tipitirize Kufufuza Anthu Oyenerera.”) (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana mfundo iti yokhudza dipo?

19 Mtima woyamikira uyenera kutilimbikitsa kuthandiza anthu kudziwa kuti dipo ndi mphatso yamtengo wapatali imene ingawathandize. Anthu ayenera kudziwa kuti dipo ndi njira imene Yehova akugwiritsa ntchito popereka mwayi kwa aliyense kuti adzapeze moyo wosatha. Komatu pali zinthu zinanso zimene zikutheka chifukwa cha dipo. Nkhani yotsatira ikusonyeza kuti dipo la Yesu limaperekanso yankho pa nkhani zimene Satana anatsutsa m’munda wa Edeni.