Dipo ndi ‘Mphatso Yangwiro’ Yochokera kwa Atate

Dipo ndi ‘Mphatso Yangwiro’ Yochokera kwa Atate

“Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera . . . kwa Atate.”—YAK. 1:17.

NYIMBO: 131, 73

1. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatheke chifukwa cha dipo?

 NSEMBE ya dipo ya Yesu Khristu imathandiza kuti tidzapeze madalitso ambiri. Dipo limeneli limatsegulanso njira yoti tidzasangalale ndi moyo wosatha. Komatu si zokhazi. Yesu analolera kufa ali wokhulupirika kwa Yehova. Izi zimathandiza poyankha nkhani zofunika kwambiri zokhudza kukhulupirika kwa angelo komanso anthu.—Aheb. 1:8, 9.

2. (a) Kodi Yesu anatchula mfundo ziti zofunika kwambiri m’pemphero lachitsanzo? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

2 Kutatsala zaka ziwiri kuti Yesu aphedwe n’kupereka dipo, iye anauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mat. 6:9, 10) Tiyeni tsopano tikambirane mfundo zimene zingatithandize kuti tiziyamikira kwambiri dipoli. Tiona mmene dipo limathandizira kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe, Ufumu wake ulamulire komanso kuti chifuniro chake chichitike.

“DZINA LANU LIYERETSEDWE”

3. Kodi dzina la Yehova limasonyeza chiyani, nanga Satana analidetsa bwanji?

3 Yesu anayamba pemphero lachitsanzo ndi mfundo yoti dzina la Mulungu liyeretsedwe. Dzinali limasonyeza kuti Mulungu ndi wabwino, wamkulu komanso woyera kwambiri. M’pemphero lina, Yesu anatchula Yehova kuti “Atate Woyera.” (Yoh. 17:11) Popeza Yehova ndi woyera, mfundo zake ndi malamulo ake nazonso n’zoyera. Ngakhale zili choncho, m’munda wa Edeni, Satana anatsutsa zoti Mulungu ndi woyenera kupereka malamulo oti anthu azitsatira. Ponena zabodza zokhudza Yehova, Satana anadetsa dzina loyera la Mulungu.—Gen. 3:1-5.

4. Kodi Yesu anathandiza bwanji poyeretsa dzina la Mulungu?

4 Koma Yesu ankakonda kwambiri dzina la Yehova. (Yoh. 17:25, 26) Iye anathandiza kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe. (Werengani Salimo 40:8-10.) Ali padzikoli sanalakwitse chilichonse ndipo anasonyeza kuti Yehova ndi woyenera kupereka malamulo oti anthu ndi angelo azitsatira. Satana anachititsa kuti Yesu aphedwe mwakhanza koma iye anakhalabe wokhulupirika kwa Atate wake wakumwamba. Zimene Yesu anachita zinasonyeza kuti munthu wangwiro akhoza kumvera bwinobwino malamulo a Mulungu.

5. Kodi tingatani kuti tidziyeretsa nawo dzina la Mulungu?

5 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda dzina la Yehova? Zochita zathu ndi zimene zingasonyeze. Paja Yehova amafuna kuti tikhale oyera. (Werengani 1 Petulo 1:15, 16.) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kulambira Yehova yekha komanso kumumvera ndi mtima wonse. Ngakhale tikamazunzidwa, tiziyesetsa kutsatira mfundo zake ndi malamulo ake. Tikamachita zinthu zabwino, timaonetsa kuwala kwathu ndipo dzina la Yehova limalemekezedwa. (Mat. 5:14-16) Tikamakhala oyera, timasonyeza kuti malamulo a Yehova ndi abwino ndipo zonena za Satana ndi zabodza. Koma tikachimwa, tiyenera kulapa mochokera pansi pa mtima ndipo tisamachitenso makhalidwe alionse amene anganyozetse dzina la Yehova.—Sal. 79:9.

6. N’chifukwa chiyani Yehova amationa ngati olungama ngakhale kuti si ife angwiro?

6 Yehova amagwiritsa ntchito dipo kuti akhululukire anthu amene asonyeza chikhulupiriro. Dipo limapangitsanso kuti azilandira anthu amene adzipereka kwa iye ndipo amawaona kuti ndi olungama. Yehova amaona Akhristu odzozedwa ngati ana ake ndipo a “nkhosa zina” ngati mabwenzi ake. (Yoh. 10:16; Aroma 5:1, 2; Yak. 2:21-25) Choncho, panopa dipo limatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Atate wathu komanso kuti tiziyeretsa nawo dzina lake.

“UFUMU WANU UBWERE”

7. Kodi dipo lidzabweretsa madalitso ati mu Ufumu wa Mulungu?

7 Mfundo yachiwiri imene Yesu anaitchula m’pemphero lachitsanzo inali yakuti: “Ufumu wanu ubwere.” Kodi dipo limathandiza bwanji kuti Ufumu wa Mulungu ulamulire? Dipo linatsegula mwayi woti papezeke anthu 144,000 oti adzakhale mafumu ndi ansembe limodzi ndi Khristu kumwamba. (Chiv. 5:9, 10; 14:1) Yesu ndi anzakewo adzalamulira mu Ufumu wa Mulungu kwa zaka 1,000 ndipo adzathandiza anthu kuti apeze madalitso obwera chifukwa cha dipo. Pa nthawiyo, dzikoli lidzakhala Paradaiso. Anthu onse okhulupirika adzakhala angwiro ndipo izi zidzathandiza kuti mbali yakumwamba ndi yapadziko lapansi ya banja la Mulungu ikhale yogwirizana kwambiri. (Chiv. 5:13; 20:6) Yesu adzaphwanya mutu wa njoka ndipo adzachotseratu mavuto onse obwera chifukwa cha zochita za Satana.—Gen. 3:15.

8. (a) Kodi Yesu anathandiza bwanji ophunzira ake kuti aziona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri? (b) Kodi ifeyo tingasonyeze bwanji kuti tili kumbali ya Ufumu wa Mulungu?

8 Yesu ali padzikoli anathandiza ophunzira ake kuzindikira kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri. Atangobatizidwa anayamba kulalikira “uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu” m’madera osiyanasiyana. (Luka 4:43) Iye atatsala pang’ono kupita kumwamba, anauza ophunzira ake kuti adzakhala mboni zake “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:6-8) Ntchito yolalikira ikuthandiza anthu padziko lonse kuti adziwe za dipo komanso kuti akhale nzika za Ufumu wa Mulungu. Tikamathandiza abale a Khristu pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu, timasonyeza kuti tili kumbali ya Ufumuwo.—Mat. 24:14; 25:40.

“CHIFUNIRO CHANU CHICHITIKE”

9. Kodi tingatsimikize bwanji kuti Yehova adzakwaniritsa cholinga chake kwa anthu?

9 Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Chifuniro chanu chichitike”? Yehova ndi Mlengi ndipo zimene amalankhula sizilephereka moti zimakhala ngati zachitika kale. (Yes. 55:11) Choncho iye sangalole kuti Satana asokoneze cholinga chake kwa anthu. Kuyambira pa chiyambi, cholinga cha Yehova ndi chakuti dzikoli lidzazidwe ndi ana angwiro a Adamu ndi Hava. (Gen. 1:28) Adamu ndi Hava akanafa asanabereke mwana, cholinga cha Mulungu chimenechi sichikanakwaniritsidwa. Choncho iwo atachimwa, Yehova anawalola kuti abereke ana. Iye adzagwiritsa ntchito dipo pothandiza anthu amene asonyeza chikhulupiriro kuti adzakhale angwiro komanso kuti adzakhale ndi moyo wosatha. Yehova amakonda anthu ndipo amafuna kuti anthu omvera adzakhale ndi moyo umene iyeyo ankafuna.

10. Kodi dipo lidzathandiza bwanji anthu amene anamwalira?

10 Nanga bwanji za anthu ambirimbiri amene anamwalira asanapeze mwayi wodziwa Yehova komanso kumutumikira? Dipo limathandizanso kuti anthu amenewa adzaukitsidwe. Atate wathu wachikondi adzawaukitsa n’kuwapatsa mwayi woti aphunzire za cholinga chake kuti akhale ndi moyo wosatha. (Mac. 24:15) Yehova amafuna kuti anthu azikhala ndi moyo osati azifa. Popeza iye ndi kasupe wa moyo, adzakhala Atate wa onse amene adzaukitsidwe. (Sal. 36:9) Mpake kuti Yesu anati tizipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba.” (Mat. 6:9) Yehova wapatsa Yesu ntchito yofunika kwambiri youkitsa akufa. (Yoh. 6:40, 44) M’Paradaiso, Yesu adzakwaniritsa udindo wake wokhala “kuuka ndi moyo.”—Yoh. 11:25.

11. Kodi cholinga cha Mulungu chokhudza “khamu lalikulu” n’chiyani?

11 Yehova amasonyeza kukoma mtima kwake mopanda tsankho. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Aliyense wochita chifuniro cha Mulungu, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga ndi mayi anga.” (Maliko 3:35) Cholinga cha Mulungu n’choti “khamu lalikulu” kapena kuti anthu osawerengeka ochokera mu fuko lililonse, mtundu uliwonse komanso chinenero chilichonse azimulambira. Anthu onse amene amakhulupirira dipo la Khristu komanso amene amachita zimene Mulungu amafuna angadzakhale m’gulu lomwe lidzafuule kuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.”—Chiv. 7:9, 10.

12. Kodi pemphero lachitsanzo limatitsimikizira chiyani?

12 Pemphero lachitsanzo limasonyeza bwino cholinga cha Mulungu kwa anthu omvera. Choncho tiyeni tizichita zonse zimene tingathe kuti tiyeretse dzina la Yehova. (Yes. 8:13) Dzina la Yesu limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Chipulumutso.” Ndipo kupulumutsidwa kwathu chifukwa cha dipo, kudzalemekeza kwambiri dzina la Yehova. Ufumu wa Mulungu udzathandizanso kuti anthu omvera adalitsidwe chifukwa cha dipo. Mwachidule tingati pemphero lachitsanzo limatitsimikizira kuti palibe chimene chingalepheretse Mulungu kukwaniritsa cholinga chake.—Sal. 135:6; Yes. 46:9, 10.

TIZISONYEZA KUTI TIMAYAMIKIRA DIPO

13. Kodi munthu akabatizidwa amasonyeza chiyani?

13 Tingasonyeze kuti timayamikira dipo podzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa. Tikabatizidwa timasonyeza kuti “ndife a Yehova.” (Aroma 14:8) Timasonyezanso kuti tikufuna kuti Mulungu atithandize kukhala ndi chikumbumtima chabwino. (1 Pet. 3:21) Ndiyeno Yehova amagwiritsa ntchito magazi a Yesu kuti atiyeretse. Sitikukayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova adzatipatsa zinthu zonse zimene watilonjeza.—Aroma 8:32.

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira dipo? (Onani ndime 13 ndi 14)

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda anzathu?

14 Koma pali njira inanso imene tingasonyezere kuti timayamikira dipo. Yehova amachita zinthu zonse chifukwa cha chikondi ndipo amafuna kuti aliyense amene amamulambira azisonyeza chikondicho. (1 Yoh. 4:8-11) Ndiyeno tikamakonda anzathu timasonyeza kuti tikufuna kukhala ‘ana a Atate wathu wakumwamba.’ (Mat. 5:43-48) Paja lamulo lalikulu kwambiri ndi loti tizikonda Yehova ndipo lachiwiri lake ndi loti tizikonda anzathu. (Mat. 22:37-40) Tikamamvera lamulo loti tizilalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, timasonyeza kuti timakonda anzathu ndipo timalemekeza kwambiri Mulungu. Tikamachita zimenezi, chikondi chathu kwa Mulungu “chimakhala chokwanira.”—1 Yoh. 4:12, 20.

DIPO LIMABWERETSA “NYENGO ZOTSITSIMUTSA” KUCHOKERA KWA YEHOVA

15. (a) Kodi Yehova amatidalitsa bwanji masiku ano? (b) Nanga ndi madalitso ati amene tikuyembekezera?

15 Tikamakhulupirira dipo machimo athu onse akhoza kukhululukidwa. Paja Mawu a Mulungu amanena kuti machimo athu angathe kufafanizidwa. (Werengani Machitidwe 3:19-21.) Monga tanenera kale, dipo ndi limene limathandiza kuti Yehova aziona kuti odzozedwa ndi ana ake. (Aroma 8:15-17) Ngati ndife a “nkhosa zina” tingati Yehova walemba kale chikalata chokhala ndi dzina lathu chotilola kuti tikhale ana ake. Ndiyeno tikadzakhala angwiro n’kupambana mayesero omaliza, iye adzasainira chikalatacho n’kutitenga kuti tikhale ana ake apadzikoli. (Aroma 8:20, 21; Chiv. 20:7-9) Yehova sadzasiya kukonda ana ake ndipo madalitso amene adzawapatse chifukwa cha dipo adzakhala osatha. (Aheb. 9:12) Mphatso ya dipo ndi yosafwifwa ndipo palibe amene angatilande.

16. Kodi dipo limatithandiza bwanji?

16 Mdyerekezi sangalepheretse anthu amene alapa ndi mtima wonse kuti adzakhale m’banja la Mulungu. Paja Yesu anabwera padzikoli n’kutifera “kamodzi kokha.” Choncho dipo linalipiridwa kale. (Aheb. 9:24-26) Dipoli limafafaniziratu mlandu umene Adamu anatipalamulira. Timayamikira kwambiri kuti dipo la Khristu limatithandiza kuti tisakhale akapolo a dziko la Satanali ndiponso tisamaope imfa.—Aheb. 2:14, 15.

17. Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira za chikondi cha Mulungu?

17 Malonjezo a Mulungu ndi odalirika. Mofanana ndi malamulo ake a m’chilengedwe omwe sasintha, Yehovanso sasintha ndipo sadzatigwiritsa mwala. (Mal. 3:6) Kuwonjezera pa mphatso ya moyo iye amatipatsanso chikondi chake. Paja Baibulo limati: “Ife tikudziwa ndipo tikukhulupirira za chikondi chimene Mulungu ali nacho kwa ife. Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:16) Dziko lonseli lidzakhala Paradaiso wokongola kwambiri ndipo munthu aliyense azidzatha kukonda kwambiri Mulungu. Tiyeni nafenso tizitsanzira angelo okhulupirika amene amanena kuti: “Mulungu wathu wanzeru, wamphamvu ndi wa nyonga, atamandidwe, apatsidwe ulemerero ndi ulemu, ndipo ayamikiridwe kwamuyaya. Ame.”—Chiv. 7:12.