Kodi Anthu Ambiri Amasankha Bwanji Pakati pa Choyenera ndi Chosayenera?

Kodi Anthu Ambiri Amasankha Bwanji Pakati pa Choyenera ndi Chosayenera?

Pafupifupi aliyense amavomereza kuti zinthu zina ndi zabwino pomwe zina ndi zoipa. Mwachitsanzo, zinthu monga kupha, kugwiririra komanso kuchitira ana nkhanza zokhudza kugonana anthu ambiri amaziona kuti ndi zoipa koma amasangalala ndi makhalidwe abwino monga chilungamo, kukoma mtima komanso chifundo. Komabe, anthu ambiri amaganiza kuti zilizonse zomwe munthu angasankhe pa nkhani monga zokhudza kugonana, kuchita zinthu moona mtima kapenanso kulera ana zilibe vuto lililonse. Nthawi zambiri anthu amasankha zochita potengera mmene akumvera komanso mmene anthu ena angawaonere. Kodi amenewa ndi maganizo abwino?

KODI NDI NZERU KUSANKHA ZINTHU POTENGERA MMENE TIKUMVERA?

Nthawi zambiri anthufe timasankha zinthu potengera mmene ifeyo timaonera zinthu kapena kuti mogwirizana ndi chikumbumtima chathu. (Aroma 2:​14, 15) Ngakhale ana aang’ono nawonso amatha kudziwa ngati winawake wachita zinthu mwachilungamo kapena mopanda chilungamo komanso amatha kudziimba mlandu akalakwitsa. Tikamakula, timazindikira choyenera ndi chosayenera kuchokera kwa anthu amene timakhala nawo kapena kuchita nawo zinthu monga achibale, anzathu, aphunzitsi athu, maneba, anthu am’chipembedzo chathu kapenanso potengera chikhalidwe chathu. Choncho tikamasankha zochita, chikumbumtima chathu chimatithandiza kuzindikira ngati tasankha zinthu mogwirizana ndi mfundo zabwino zomwe tinaphunzira kapena ayi.

Ngati chikumbumtima chathu chimatithandiza kusiyanitsa pakati pa choyenera ndi chosayenera, sitingavutike kusonyeza ena chifundo, kukhala oyamikira, kuchita zinthu mwachilungamo komanso kuthandiza ena akakumana ndi mavuto. Chimatithandizanso kupewa kuchita zinthu zokhumudwitsa anthu amene timawakonda kapenanso zinthu zomwe zingatichititse manyazi, kudzimvera chisoni ngakhalenso kudziimba mlandu.

Kodi ndi nzeru nthawi zonse kusankha zinthu potengera mmene tikumvera? Wachinyamata wina dzina lake Garrick anati, “Ndinkachita chilichonse chomwe ndinkafuna.” Komabe, iye anakumana ndi mavuto ambiri chifukwa chosankha kukhala moyo woterewu. Anayamba kukhala moyo umene pambuyo pake anadzazindikira kuti sunkamusangalatsa chifukwa ankachita zachiwerewere, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza ubongo, kuledzera komanso kuchita zachiwawa.

KODI NDI NZERU KUSANKHA ZINTHU POTENGERA MMENE ENA AKUTIONERA?

Nthawi zambiri timathanso kusankha zochita potengera mmene anthu ena angaonere zomwe tasankha. Zimenezi zingathandize kuti tiphunzirepo pa zimene zinawachitikira komanso nzeru zawo. Anthu am’banja lathu, am’dera lathu komanso anzathu amatikonda kwambiri tikamachita zomwe iwo amaziona kuti ndi zoyenera.

Kodi ndi nzeru nthawi zonse kusankha zinthu potengera mmene ena akutionera? Mtsikana wina dzina lake Priscila ankakonda kuchita zimene anzake ambiri ankachita ndipo anayamba kuchita zachiwerewere. Komabe, iye anazindikira kuti kuchita zimene anthu ena ankaziona kukhala zoyenera sikunamuthandize kukhala wosangalala. Ndiye ananena kuti: “Kuchita zimene anthu ena ankaziona kuti ndi zoyenera sikunandithandize ngakhale pang’ono. Mapeto ake ndinasankha zinthu mopanda nzeru ndipo ndinakumana ndi mavuto oopsa.”

N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE KUSANKHA MWANZERU?

Tikamafuna kusankha pakati pa choyenera ndi chosayenera, si kulakwa kuganizira mmene timaonera zinthu komanso mmene anthu ena angationere. Koma sitingasankhe zinthu mwanzeru chifukwa chotsatira mfundo yokhayi. Zili choncho chifukwa nthawi zina tingakumane ndi mavuto aakulu kapenanso kukhumudwitsa anthu ena chifukwa sitinaganizire kaye tisanasankhe. (Miyambo 14:12) Ndipo ngakhale ifeyo kapenanso anthu ena ataona kuti zomwe tikufuna kuchita zilibe vuto lililonse, tingafunike kusamala chifukwa zikhoza kutibweretsera mavuto aakulu komanso tikhoza kusintha mmene timaonera zinthu. Komanso makhalidwe ena omwe kale anthu ankawaona kuti ndi olakwika, masiku ano amawaona kuti alibe vuto lililonse, pamene makhalidwe ena amene anthu ankawaona kuti alibe vuto, masiku ano amawaona kuti ndi olakwika.

Kodi ndi nzeru nthawi zonse kusankha zinthu potengera mmene ena akutionera?

Kodi pali malangizo odalirika amene angatithandize kusankha pakati pa choyenera ndi chosayenera? Kodi pali mfundo za makhalidwe abwino zomwe tingamazitsatire panopa zimene sizingadzatibweretsere mavuto m’tsogolo?

N’zosangalatsa kudziwa kuti n’zotheka kupeza malangizo othandiza komanso odalirika okhudza makhalidwe abwino omwe angathandize munthu wina aliyense padzikoli. Nkhani yotsatira ikufotokoza kumene tingapeze malangizo odalirika amene angatithandize kusankha pakati pa choyenera ndi chosayenera.