Ndi Udindo Wanu Kusankha Pakati pa Choyenera ndi Chosayenera YAMBANI Ndi Udindo Wanu Kusankha Pakati pa Choyenera ndi Chosayenera Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Zomwe timachita pa moyo wathu zingachititse kuti tidzakhale ndi moyo wosangalala kapena ayi. Ndipo Yehova Mulungu amadziwa zimenezi. N’chifukwa chake amafuna kuti tizitsatira mfundo zake pa moyo wathu. Yehova amafuna kuti tizisangalala komanso kuti tizikhala mwamtendere. “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakutsogolerani mʼnjira imene mukuyenera kuyenda. Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga! Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a mʼnyanja.”—Yesaya 48:17, 18. Popeza kuti iye ndi Mlengi wathu, Mulungu amadziwa zomwe tiyenera kuchita kuti tikhale ndi moyo wabwino kwambiri. Iye amafuna kuti tizitsatira malangizo ake n’cholinga choti zinthu zizitiyendera bwino. Tikamatsatira malamulo a Mulungu pa moyo wathu, sitidzakayikira kuti tasankha zinthu mwanzeru kapena ayi. Nthawi zonse tizisankha zinthu mwanzeru zomwe zingatithandize kuti tizikhala mwamtendere komanso mosangalala. Yehova samatipempha kuti tizichita zinthu zomwe sitingakwanitse. “Lamulo limene ndikukupatsani leroli si lovuta kwa inu kulitsatira, ndipo silili poti simungathe kulipeza.”—Deuteronomo 30:11. Kuti tizitha kutsatira mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino, tiyenera kusintha mmene timaganizira komanso zomwe timachita. Komabe, Yehova sakutipempha kuti tizichita zinthu zomwe sitingakwanitse. Ndipotu iye amadziwa bwino zomwe tingakwanitse chifukwa ndi Mlengi wathu. Tikamudziwa bwino Yehova, tidzazindikira kuti “malamulo akewo si ovuta kuwatsatira.”—1 Yohane 5:3. Yehova akulonjeza kuti adzathandiza anthu onse amene amasankha kutsatira mfundo zake. “Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja, Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’”—Yesaya 41:13. Tingakwanitse kutsatira mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino chifukwa chakuti iye ndi wokonzeka kutithandiza. Iye angatithandize pogwiritsa ntchito Mawu ake Baibulo, lomwe limatilimbikitsa komanso kutipatsa chiyembekezo. Anthu mamiliyoni ambiri padzikoli aona kuti zinthu zikuwayendera bwino kwambiri pa moyo wawo chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Inunso mungapeze malangizo othandiza kuchokera m’Baibulo. Mungachite zimenezi pophunzira kabuku kofotokoza Baibulo ka mutu wakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, komwe kakupezeka kwaulere pa jw.org/ny. Kabukuka kali ndi mitu yotsatirayi: Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji? Baibulo Limatithandiza Kukhala Ndi Chiyembekezo Kodi Muyenera Kukhulupirira Baibulo? Mukamafufuza Mawu a Mulungu, Baibulo, mudzapeza kuti si buku lachikale koma ‘ndi lodalirika nthawi zonse, kuyambira panopa mpaka kalekale.’ (Salimo 111:8) Kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu tifunika kumatsatira mfundo za makhalidwe abwino zomwe zili m’Baibulo. Komabe, Mulungu samatikakamiza kuchita zimenezi. (Deuteronomo 30:19, 20; Yoswa 24:15) Aliyense wa ife ali ndi udindo wosankha zoyenera kapena zosayenera. Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Ndi Udindo Wanu Kusankha Pakati pa Choyenera ndi Chosayenera NSANJA YA OLONDA Ndi Udindo Wanu Kusankha Pakati pa Choyenera ndi Chosayenera Chinenero Chamanja cha ku Malawi Ndi Udindo Wanu Kusankha Pakati pa Choyenera ndi Chosayenera https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/2024007/afrn/art/2024007_afrn_sqr_xl.jpg wp24.1 5