Malangizo a M’Baibulo Okhudza Zoyenera Ndi Zosayenera Ndi Othandiza

Malangizo a M’Baibulo Okhudza Zoyenera Ndi Zosayenera Ndi Othandiza

Baibulo lathandiza anthu mamiliyoni ambiri kusankha mwanzeru pa mbali 4 za moyo wawo. Tiyeni tione mbali zimenezi.

1. Moyo wa M’banja

Anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya banja komanso zomwe angachite kuti azikhala ndi banja losangalala.

BAIBULO LIMATI: “Aliyense wa inu azikonda mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.”—Aefeso 5:33.

ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA: Mulungu ndi amene anayambitsa banja, choncho iye amadziwa zimene mwamuna ndi mkazi ayenera kuchita kuti azikhala mosangalala. (Maliko 10:​6-9) Anthu okwatirana amakhala osangalala aliyense akamaganizira kwambiri zimene angachitire mnzake, osati zimene mnzakeyo angamuchitire, n’cholinga choti banja lawo likhale lolimba. Mwamuna amasonyeza kuti amakonda mkazi wake ngati amamusamalira komanso kumuchitira zinthu mokoma mtima. Mkazi amene amalemekeza mwamuna wake amachita zimenezi mwa zochita zake komanso pomulankhula mwaulemu.

MALANGIZO A M’BAIBULO OTHANDIZA: Quang ndi Thi a ku Vietnam ankaona kuti sizingatheke kuti akhale osangalala m’banja lawo chifukwa cha mavuto amene ankakumana nawo. Nthawi zambiri Quang ankachita zinthu mosaganizira mkazi wake. Iye ananena kuti: “Sindinkaganizira mmene Thi ankamvera ndipo nthawi zambiri ndinkachita zinthu zomuchititsa manyazi.” Zimenezi zinachititsa kuti Thi akhale ndi maganizo ofuna kuthetsa banja. Iye anati: “Ndinayamba kuona kuti sindingakhulupirirenso mwamuna wanga ngakhalenso kumulemekeza.”

Patapita nthawi, Quang ndi Thi anaphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa ndipo anayamba kugwiritsira ntchito mfundo za pa Aefeso 5:33 m’banja lawo. Quang ananena kuti, “Vesili linandithandiza kuona kuti ndikufunikira kumachita zinthu moganizira mkazi wanga. Ndinaonanso kuti ndifunika kusonyeza Thi kuti ndimamukonda pomamupezera zinthu zofunikira, kumusamalira komanso kumuganizira. Ndikamachita zimenezi iye amayamba kundikonda komanso kundilemekeza kwambiri. Nayenso Thi ananena kuti, “Ndikamayesetsa kugwiritsira ntchito mfundo ya pa Aefeso 5:33 komanso kumalemekeza kwambiri mwamuna wanga, ndimayamba kumva kuti amandikonda, ndimaona kuti ndine wotetezeka komanso timakhala mwamtendere.”

Kuti mudziwe zambiri zokhudza moyo wa banja, werengani Galamukani! Na. 2 2018, yamutu wakuti “Mfundo 12 Zothandiza Kuti Banja Liziyenda Bwino,” pa jw.org.

2. Mmene Tiyenera Kuchitira Zinthu Ndi Ena

Nthawi zambiri anthu amachitira nkhanza ena chifukwa cha mtundu wawo, dziko lawo, mmene amaonekera, chipembedzo chawo kapenanso chifukwa choti amagonana amuna kapena akazi okhaokha.

BAIBULO LIMATI: “Muzilemekeza anthu amitundu yonse.”—1 Petulo 2:17.

ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA: Baibulo silimalimbikitsa anthu kuti azidana chifukwa cha kusiyana mtundu, dziko kapena chifukwa choti amagonana amuna kapena akazi okhaokha. Koma limatilimbikitsa kuti tizikonda anthu amitundu yonse posatengera dziko, mtundu kapena zimene amachita pa moyo wawo. (Machitidwe 10:34) Ngakhale kuti ifeyo tingasiyane ndi anthu ena chifukwa cha zimene amakhulupirira kapenanso kuchita, tifunika kuwachitira zinthu mwachikondi ndiponso mwaulemu.—Mateyu 7:12.

MALANGIZO A M’BAIBULO OTHANDIZA: Kuyambira ali wamng’ono, Daniel anaphunzitsidwa kuti anthu a ku Asia ndi obweretsa chiopsezo kudziko lawo. Choncho, iye anayamba kudana ndi munthu aliyense wochokera ku Asia ndipo nthawi zambiri ankakonda kuwanyoza pagulu. Iye ananena kuti: “Ndinkaganiza kuti zimene ndinkachitazi zinalibe vuto lililonse chifukwa ndinkasonyeza kuti ndimakonda dziko langa. Ndipo sindinkaona kuti kuganiza komanso kuchita zimenezi kunali kulakwa.”

Patapita nthawi Daniel anayamba kuphunzira Baibulo. Daniel anati: “Nditayamba kuphunzira Baibulo ndinasinthiratu maganizo anga. Ndinayamba kuona anthu mmene Mulungu amawaonera. Iye amaona kuti anthu tonse ndife ofanana posatengera kumene tinachokera.” Pofotokoza mmene panopa amaonera anthu ena, Daniel anati: “Sindimaganiziranso kuti ndi ochokera kuti. Panopa ndimakonda anthu amitundu yonse ndipo ndili ndi anzanga m’mayiko osiyanasiyana.”

Kuti mudziwe zambiri, werengani Galamukani! Na. 3 2020, yamutu wakuti, “Kodi Tsankho Lidzatha?” pa jw.org.

3. Ndalama

Anthu ambiri amafuna kulemera poganiza kuti tsogolo lawo likhala labwino komanso akhala osangalala.

BAIBULO LIMATI: “Nzeru zimateteza mofanana ndi mmene ndalama zimatetezera. Koma ubwino wa kudziwa zinthu ndi uwu: Nzeru zimateteza moyo wa amene ali ndi nzeruzo.”—Mlaliki 7:12.

ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA: Timafunikira ndalama koma sizingatithandize kukhala ndi tsogolo labwino kapena moyo wosangalala. (Miyambo 18:11; 23:​4, 5) M’malomwake, kuti munthu akhale ndi chimwemwe chenicheni komanso tsogolo labwino, zimadalira pa kugwiritsa ntchito nzeru zochokera kwa Mulungu zomwe zimapezeka m’Baibulo.—1 Timoteyo 6:​17-19.

MALANGIZO A M’BAIBULO OTHANDIZA: Cardo, wa ku Indonesia ankangokhalira kufunafuna chuma. Iye anati: “Ndinkasangalala kukhala ndi zinthu zimene anthu amalakalaka kukhala nazo. Ndinkatha kuyenda maulendo komanso kugula katundu, magalimoto ndi nyumba zodula.” Koma chuma chakechi sichinakhalitse. Iye ananenanso kuti: “Munthu wina anandipusitsa ndipo anandilanda ndalama zonse zimene ndinazikhetsera thukuta kwa zaka zambiri ndipo zonse zinapita m’kanthawi kochepa. Moyo wanga wonse ndinkangokhalira kufunafuna chuma koma pamapeto pake ndinakhumudwa chifukwa ndinalibe kalikonse moti ndinayamba kudziona ngati munthu wachabechabe.”

Cardo anayamba kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo okhudza ndalama. Panopa samatayanso nthawi yake pofunafuna chuma, m’malomwake anasankha kukhala moyo wosalira zambiri. Iye anati: “Panopa ndimaona kuti ndili ndi chuma chenicheni chifukwa ndili pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Ndimagona tulo tokoma ndipo ndili ndi chimwemwe chenicheni.”

Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya ndalama, werengani nkhani yakuti, “Kodi Maphunziro Ndi Ndalama Zingatithandize Kukhala Ndi Tsogolo Labwino?” mu Nsanja ya Olonda Na. 3 2021, pa jw.org.

4. Kugonana

Anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya zimene n’zovomerezeka pa nkhani ya kugonana.

BAIBULO LIMATI: “Muzipewa chiwerewere. Aliyense wa inu azidziwa kulamulira thupi lake kuti likhale loyera komanso lolemekezeka pamaso pa Mulungu. Musakhale ngati anthu a mitundu ina omwe sadziwa Mulungu komanso ali ndi chilakolako chosalamulirika cha kugonana ndipo sakhutiritsidwa.”—1 Atesalonika 4:​3-5.

ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA: Baibulo limasonyeza kuti tifunika kukhala odziletsa pa chilakolako cha kugonana. Mawu akuti “chiwerewere” akuphatikizapo chigololo, kugonana kwa anthu osakwatirana, kugonana amuna kapena akazi okhaokha kapenanso kugona nyama. (1 Akorinto 6:​9, 10) Kugonana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo iye amafuna kuti mwamuna ndi mkazi okhawo omwe ndi okwatirana, azisangalala ndi mphatso imeneyi.—Miyambo 5:​18, 19.

MALANGIZO A M’BAIBULO OTHANDIZA: Mayi wina wa ku Australia dzina lake Kylie, anati: “Ndisanakwatiwe ndinkaganiza kuti ndikagonana ndi munthu, ndiyamba kuona kuti ndimakondedwa komanso kuti ndine wotetezeka. Koma sizinakhale choncho. Ndinayamba kuona kuti sindine wotetezeka komanso mtima wanga unasweka.”

Pambuyo pake, Kylie anaphunzira Baibulo ndipo anayamba kutsatira zimene limaphunzitsa pa nkhani ya kugonana. Iye anati: “Ndikuona kuti mfundo za Mulungu zimatiteteza kuti tisamve kuwawa. Panopa ndimaona kuti ndine wotetezeka komanso wokondedwa chifukwa ndikuchita zinthu zimene Mulungu amafuna. Ndapewa zinthu zambiri zoopsa chifukwa chotsatira malangizo a m’Baibulo.”

Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti, “Kodi Baibulo Limavomereza Kuti Mwamuna ndi Mkazi Azikhalira Limodzi Asanakwatirane?” pa jw.org.

Mlengi wathu amatithandiza kudziwa zoyenera ndi zosayenera. Ngakhale kuti si zophweka kutsatira malangizo okhudza makhalidwe abwino, timapindula kwambiri tikamawatsatira. Tiyenera kukhulupirira kuti tikamachita zimenezi, tidzakhala osangalala nthawi zonse.