Kodi Malangizo Odalirika Mungawapeze Kuti?

Kodi Malangizo Odalirika Mungawapeze Kuti?

Popeza kuti zinthu padzikoli zikusintha kwambiri, kodi n’chiyani chingakuthandizeni kutsimikizira kuti zimene mwasankha kuchita zidzakuthandizani? Kodi mungatsimikizire bwanji kuti zimene mungasankhe lero ndi zabwinodi moti m’tsogolo simungadzadziimbe mlandu kuti munasankha molakwika?

Baibulo lingakuthandizeni kusankha zinthu zimene simungadzanong’onoze nazo bondo. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Baibulo linachokera kwa Mlengi wathu ndipo iye amadziwa bwino zinthu zimene zingatithandize kuti tikhale osangalala komanso kuti tidzakhale ndi tsogolo labwino.

“Iye anakuuza . . . zimene zili zabwino.”—Mika 6:8.

Tiyenera kudalira malangizo othandiza amene amapezeka m’Baibulo. Malangizowa ndi “odalirika nthawi zonse, kuyambira panopa mpaka kalekale.”—Salimo 111:8.

Mungachite bwino kwambiri kufufuza nokha kuti muone mmene Baibulo lingakuthandizireni pamene zinthu zikusintha kwambiri m’dzikoli.