Tizikhulupirira Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Zoyenera Ndi Zosayenera

Tizikhulupirira Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Zoyenera Ndi Zosayenera

Tikamasankha zoyenera kuchita pa nkhani ya makhalidwe abwino, sitingakhale otsimikiza kuti zimene tasankhazo zidzatiyenderadi bwino ngati tikungotsatira maganizo athu komanso a anthu ena. Tikutero chifukwa cha zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi ndi nkhani zinanso zambiri. Baibulo lili ndi malangizo othandiza kudziwa zoyenera ndi zosayenera ndipo timakhala ndi moyo wabwino komanso wosangalala tikamatsatira malangizo amenewa.

TIMAFUNIKIRA MALANGIZO OCHOKERA KWA MULUNGU

Baibulo limasonyeza kuti Yehova a Mulungu analenga anthu n’cholinga choti azipatsidwa malangizo ndi iyeyo, osati kuti azidzitsogolera okha. (Yeremiya 10:23) N’chifukwa chake iye anapereka malangizo okhudza makhalidwe abwino ndipo malangizowa amapezeka m’Baibulo. Iye amatikonda kwambiri ndipo amafuna kutiteteza kuti tisakumane ndi mavuto chifukwa chosankha zinthu molakwika. (Deuteronomo 5:29; 1 Yohane 4:8) Koposa zonse, monga Mlengi wathu, iye ali ndi nzeru komanso amadziwa malangizo abwino kwambiri omwe angatithandize pa moyo wathu. (Salimo 100:3; 104:24) Komabe, Mulungu sakakamiza anthu kuti aziyendera mfundo zake.

Yehova anapatsa Adamu ndi Hava, omwe anali anthu oyambirira, zinthu zonse zofunikira kuti azikhala moyo wosangalala. (Genesis 1:28, 29; 2:8, 15) Anawapatsanso malangizo osavuta ndipo ankayembekezera kuti savutika kuwamvera. Komabe, iye anawapatsa ufulu woti akhoza kusankha kutsatira malangizo ake kapena ayi. (Genesis 2:9, 16, 17) N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava anasankha kuyendera mfundo zawo m’malo moyendera mfundo za Mulungu. (Genesis 3:6) Ndiye kodi zinthu zinawayendera bwanji? Kodi anthu padzikoli zinthu zikuwayendera bwino chifukwa choti akusankha okha zoyenera ndi zosayenera? Ayi ndithu. Anthu akhala akukana kutsatira mfundo za Mulungu kwa zaka zambiri, ndipo zotsatira zake ndi zakuti alibe mtendere komanso sakukhala mosangalala.—Mlaliki 8:9.

Baibulo lili ndi malangizo omwe timafunikira kuti tizitha kusankha zinthu mwanzeru posatengera mmene tilili kapena komwe timachokera. (2 Timoteyo 3:16, 17; onani bokosi lakuti “ Buku la Anthu Onse.”) Taonani mmene Baibulo lingakuthandizireni.

Onani chifukwa chake Baibulo ndi loyeneradi kutchedwa kuti “Mawu a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13. Onerani vidiyo yakuti, Kodi Analemba Baibulo Ndi Ndani? pa jw.org.

BAIBULO LIMATIUZA ZIMENE MULUNGU AMAFUNA KUTI TIZICHITA

Baibulo lili ndi nkhani zolondola zofotokoza zimene Yehova wakhala akuchitira anthu kungoyambira pamene anawalenga. Zimene limanena zimatithandiza kuzindikira zinthu zimene Mulungu amaona kuti ndi zoyenera ndi zosayenera, zothandiza kapenanso zimene zingatibweretsere mavuto. (Salimo 19:7, 11) Mfundo zimene timaphunzira m’Baibulo zimakhala zolondola nthawi zonse ndipo zimatithandiza kusankha mwanzeru pa nkhani ya makhalidwe abwino.

Mwachitsanzo, taonani malangizo opezeka pa Miyambo 13:​20, omwe amati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma amene amachita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” Mfundo imeneyi si yachikale ndipo ikugwirabe ntchito mpaka pano, mofanana ndi mmene zinaliri pa nthawi imene inalembedwa. Baibulo lili ndi mfundo zothandiza zambiri. Onani bokosi lakuti, “ Nzeru za M’Baibulo Ndi Zothandiza Mpaka Kalekale.”

Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingadziwe bwanji kuti malangizo a m’Baibulo okhudza makhalidwe abwino ndi othandizadi masiku ano? Nkhani yotsatirayi ifotokoza mmene linathandizira anthu ena.

a Yehova ndi dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.