Tisamaweruze Poona Maonekedwe Akunja
“Lekani kuweruza poona maonekedwe akunja, koma muziweruza ndi chiweruzo cholungama.”—YOH. 7:24.
NYIMBO: 142, 123
1. Kodi Yesaya analosera zotani zokhudza Yesu, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zili zolimbikitsa?
ZIMENE Yesaya analosera zokhudza Yesu Khristu ndi zolimbikitsa kwambiri. Iye ananena kuti Yesu “sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake.” Ananenanso kuti Yesu “adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka.” (Yes. 11:3, 4) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimenezi ndi zolimbikitsa? Chifukwa chakuti m’dzikoli anthu ambiri ndi okondera ndiponso atsankho. Tonsefe timafuna kukhala ndi woweruza wabwino yemwe sangatiweruze potengera maonekedwe akunja.
2. Kodi Yesu anapereka lamulo liti, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Tsiku lililonse timaweruza anthu. Koma popeza si ife angwiro, sitiweruza molondola ngati mmene Yesu amachitira. Nthawi zambiri timaweruza potengera zimene timaona. Koma Yesu ali padzikoli analamula kuti: “Lekani kuweruza poona maonekedwe akunja, koma muziweruza ndi chiweruzo cholungama.” (Yoh. 7:24) Apa n’zodziwikiratu kuti Yesu amafuna kuti tizimutsanzira n’kumapewa kuweruza anthu potengera maonekedwe awo. Munkhaniyi tikambirana zinthu zitatu zimene zimachititsa anthu kuweruza anzawo molakwika. Zinthu zake ndi (1) mtundu, (2) chuma komanso (3) msinkhu. Tikamakambirana chinthu chilichonse tiziona zimene tingachite potsatira lamulo la Yesuli.
TISAMAWERUZE ANTHU POTENGERA MTUNDU WAWO
3, 4. (a) Kodi n’chiyani chinapangitsa kuti Petulo asinthe maganizo ake okhudza anthu amitundu ina? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi Yehova anathandiza Petulo kuzindikira mfundo yatsopano iti?
3 Kodi mukuganiza kuti mtumwi Petulo ankaganiza zinthu zotani atauzidwa kuti apite kunyumba kwa Koneliyo ku Kaisareya? (Mac. 10:17-29) Mofanana ndi Ayuda ena, Petulo ankakhulupirira kuti anthu amene sanali Ayuda anali odetsedwa. Koma Petulo anakumana ndi zinthu zimene zinamupangitsa kuti asinthe maganizo ake pa nkhaniyi. Mwachitsanzo, anali atangoona kumene masomphenya odabwitsa. (Mac. 10:9-16) Iye anaona chinthu chooneka ngati chinsalu chimene chinali ndi nyama zambiri zodetsedwa chitatsika ndipo anamva mawu ochokera kumwamba akuti: “Nyamuka Petulo, ipha udye!” Koma Petulo anakana ndipo mawu ochokera kumwamba aja anamuuza kuti: “Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa usiyiretu kuzinena kuti n’zoipitsidwa.” Ataona masomphenyawo anathedwa nzeru ndipo sankamvetsa zimene mawuwo ankatanthauza. Nthawi yomweyo panafika anthu amene Koneliyo anawatuma. Ndiye Petulo atalandira malangizo ochokera kwa mzimu woyera, anapita ndi anthuwo kunyumba kwa Koneliyo.
4 Ngati Petulo akanatengera zinthu zongooneka ndi maso, sakanalowa m’nyumba ya Koneliyo. Zili choncho chifukwa Ayuda sankalowa m’nyumba za anthu amitundu ina. Ndiye n’chifukwa chiyani Petulo anasintha maganizo n’kukalowa m’nyumba ya Koneliyo? Anatero chifukwa cha masomphenya amene anawaona komanso malangizo amene mzimu woyera unamupatsa. N’zosakayikitsa kuti Petulo anakhudzidwa mtima atamvetsera zimene Koneliyo ananena moti anati: “Ndazindikira ndithu kuti Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Mac. 10:34, 35) Apatu Petulo anamvetsa mfundo yatsopano ya choonadi imene inasintha zinthu kwambiri. Kodi mfundo imeneyi imakhudza bwanji Akhristu onse?
5. (a) Kodi Yehova amafuna kuti Mkhristu aliyense azindikire mfundo iti? (b) Ngakhale kuti timadziwa choonadi, kodi tikhoza kukhalabe ndi chiyani mumtima mwathu?
5 Yehova anagwiritsa ntchito Petulo pothandiza Akhristu onse kuzindikira kuti iye alibe tsankho. Saweruza anthu potengera mtundu, dziko, fuko kapena chilankhulo chawo. Iye amalandira munthu aliyense amene amamuopa komanso kuchita zimene amafuna. (Agal. 3:26-28; Chiv. 7:9, 10) N’zosachita kufunsa kuti nanunso mumakhulupirira mfundo imeneyi. Koma bwanji ngati munabadwira m’dziko kapena m’banja latsankho? Mwina mungamaganize kuti mulibe tsankho pomwe mumtima mwenimwenimo mudakali tsankho. Ngakhale Petulo, amene anagwiritsidwa ntchito pouza anthu kuti Mulungu alibe tsankho, pa nthawi ina anachita zinthu mwatsankho. (Agal. 2:11-14) Ndiye kodi tingatsatire bwanji malangizo a Yesu n’kumapewa kuweruza anthu potengera maonekedwe awo?
6. (a) Kodi tingatani kuti tichotseretu tsankho mumtima mwathu? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene m’bale wina waudindo anachita?
6 Tonsefe tiyenera kudzifufuza pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kuti tione ngati tidakali ndi kamtima katsankho. (Sal. 119:105) Tizivomerezanso ngati anzathu akutiuza kuti tili ndi kamtima kameneka ngakhale kuti ifeyo tikuganiza kuti tilibe. (Agal. 2:11, 14) N’zotheka kuti tsankholo linatilowerera kwambiri moti sitizindikira n’komwe kuti tili nalo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi lipoti limene m’bale wina waudindo analemba lokhudza banja lina labwino limene linkachita utumiki wa nthawi zonse. Mwamuna wa m’banjalo anali wamtundu winawake umene anthu ena ankaunyoza. Zikuoneka kuti m’baleyo sankazindikira kuti nayenso amasankha anthu amtunduwo. Mulipotilo analemba zinthu zabwino kwambiri zokhudza mwamunayo koma anamaliza ndi mawu akuti: “Ngakhale kuti m’baleyu ndi wamtundu [wakutiwakuti] khalidwe lake limathandiza anthu kudziwa kuti kukhala munthu wa mtunduwu sikutanthauza kuti ndiwe wauve kapena wotayirira ngati mmene anthu ambiri amtunduwu alili.” Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kaya tili ndi udindo wotani, tiyenera kudzifufuza kwambiri komanso kukhala ololera kuthandizidwa n’cholinga choti tichotseretu kamtima kalikonse katsankho kamene tatsala nako. Kodi n’chiyaninso chimene tingachite?
7. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikuyesetsa kuti tikhale ndi chikondi mumtima mwathu?
7 Tiyenera kuyesetsa kuti tikhale ndi chikondi mumtima mwathu m’malo mwa tsankho. (2 Akor. 6:11-13) Ndi bwino kudzifunsa kuti, Kodi ndimakonda kumangocheza ndi anthu amtundu wanga, dziko langa, fuko langa kapena chilankhulo changa? Ngati zili choncho, tiyenera kusintha mtima wathu. Tingachite bwino kumaitana anthu osiyana ndi ifeyo kuti tidzadyere limodzi kunyumba kwathu, tidzacheze nawo kapena kulowa nawo mu utumiki. (Mac. 16:14, 15) Tikamatero, chikondi chidzawonjezeka kwambiri mumtima mwathu moti simudzakhalanso malo oti tsankho lipezekemo. Koma nthawi zina anthufe timaweruzanso anthu potengera kusauka kapena kulemera kwawo. Tiyeni tsopano tikambirane zimenezi.
TISAMAWERUZE ANTHU POTENGERA KUSAUKA KAPENA KULEMERA KWAWO
8. Kodi lemba la Levitiko 19:15 limapereka malangizo otani pa nkhani ya kuweruza anthu?
8 Tiyenera kupewanso kuweruza anthu potengera kusauka kapena kulemera kwawo. Paja lemba la Levitiko 19:15 limati: “Musamaweruze mopanda chilungamo. Musamakondere munthu wosauka, ndiponso musamakondere munthu wolemera. Mnzako uzimuweruza mwachilungamo.” Kodi zingatheke bwanji kuweruza munthu potengera kusauka kapena kulemera kwake?
9. Kodi Solomo analemba mfundo yomvetsa chisoni iti, nanga tikuphunzirapo chiyani?
9 Mzimu woyera unathandiza Solomo kuti alembe mfundo yokhudza anthu ochimwafe yomwe ndi yoona koma yomvetsa chisoni. Pa Miyambo 14:20, iye anati: “Munthu wosauka amadedwa ngakhale ndi mnzake, koma munthu wolemera amakhala ndi anzake ambiri.” Kodi tikuphunzirapo chiyani palemba limeneli? Tikapanda kusamala, tingayambe kumangogwirizana ndi anthu olemera n’kumapewa osauka. Koma n’chifukwa chiyani kuona kuti munthu ndi wofunika potengera chuma chake n’koopsa kwambiri?
10. Kodi Yakobo anatchula vuto liti?
10 Tikamaweruza anthu malinga ndi kusauka kapena kulemera kwawo tingasokoneze mgwirizano mumpingo. Yakobo ananena kuti vuto limeneli linkagawanitsa anthu m’mipingo ya mu nthawi yake. (Werengani Yakobo 2:1-4.) Choncho tiyenera kusamala kuti vutoli lisasokoneze mipingo yathu masiku ano. Kodi tingatani kuti tipewe kuweruza anthu poona maonekedwe akunja?
11. Kodi zinthu zimene munthu ali nazo zimakhudza ubwenzi wake ndi Yehova? Fotokozani.
11 Tiyenera kuona abale athu ngati mmene Yehova amawaonera. Yehova sakonda munthu chifukwa choti ndi wosauka kapena wolemera. Ubwenzi wathu ndi Yehova sudalira ngati tili ndi chuma kapena ayi. N’zoona kuti Yesu ananena zoti ‘zidzakhala zovuta kuti munthu wolemera adzalowe mu ufumu wakumwamba.’ Koma sananene kuti n’zosatheka. (Mat. 19:23) Yesu ananenanso kuti: “Odala ndinu osaukanu, chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.” (Luka 6:20) Koma sankatanthauza kuti anthu onse osauka anali odala ndipo ankamvetsera uthenga wake. Osauka ambiri anakana kumvetsera uthenga wa Yesu. Apatu mfundo ndi yakuti, Sitinganene kuti munthu ali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova kapena ayi potengera zinthu zimene ali nazo.
12. Kodi Malemba amapereka malangizo otani kwa anthu olemera komanso osauka?
12 Chosangalatsa n’chakuti m’gulu lathu muli abale ndi alongo ambiri, olemera komanso osauka, omwe amatumikira Yehova ndi mtima wonse. Malemba amauza anthu olemera kuti “asamadalire chuma chosadalirika, koma adalire Mulungu.” (Werengani 1 Timoteyo 6:17-19.) Baibulo limalimbikitsanso anthu a Mulungu, kaya akhale olemera kapena osauka, kuti asamakonde ndalama. (1 Tim. 6:9, 10) Kunena zoona tikamayesetsa kuona abale athu ngati mmene Yehova amawaonera, sitingayambe kuweruza anthu potengera kusauka kapena kulemera kwawo. Koma nanga bwanji za kuweruza munthu potengera msinkhu wake? Kodi kuweruza chonchi n’koyenera? Tiyeni tsopano tikambirane zimenezi.
TISAMAWERUZE ANTHU POTENGERA MSINKHU WAWO
13. Kodi Malemba amanena zotani zokhudza kulemekeza achikulire?
13 Malemba ambiri amatiuza kuti tiyenera kulemekeza anthu achikulire. Mwachitsanzo lemba la Levitiko 19:32 limati: “Anthu aimvi uziwagwadira, munthu wachikulire uzim’patsa ulemu ndipo uziopa Mulungu wako.” Lemba la Miyambo 16:31 limanenanso kuti: “Imvi ndizo chisoti chachifumu cha ulemerero zikapezeka m’njira yachilungamo.” Nayenso Paulo anauza Timoteyo kuti asamadzudzule amuna achikulire mokalipa koma aziwaona ngati abambo ake. (1 Tim. 5:1, 2) Ngakhale kuti Timoteyo anali ndi udindo woyang’anira, ankayenera kuchita zinthu mwachifundo komanso mwaulemu ndi abale achikulire.
14. N’chifukwa chiyani nthawi zina tingafunike kupereka malangizo kapena uphungu kwa munthu amene ndi wamkulu kwa ife?
14 Koma kodi malangizo okhudza anthu achikulirewa tiyenera kuwatsatira bwanji? Mwachitsanzo, kodi tiyenera kumverabe munthu wachikulire ngakhale pamene akuchita machimo mwadala kapena akulimbikitsa zinthu zimene Yehova sasangalala nazo? Yehova saweruza potengera maonekedwe ndipo sangalekerere munthu wochimwa chifukwa choti ndi wachikulire. Taganizirani mfundo yopezeka pa Yesaya 65:20 imene imati: “Wochimwa, ngakhale ali ndi zaka 100, temberero lidzamugwera.” M’masomphenya amene Ezekieli anaona muli mfundo yofanananso. (Ezek. 9:5-7) Choncho chofunika kwambiri ndi kulemekeza “Wamasiku Ambiri,” yemwe ndi Yehova Mulungu. (Dan. 7:9, 10, 13, 14) Tikamachita zimenezi sitingaope kupereka malangizo kwa munthu wachikulire.—Agal. 6:1.
15. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Paulo pa nkhani yolemekeza abale achinyamata?
15 Nanga mumawaona bwanji abale achinyamata mumpingo? Paulo analembera Timoteyo, yemwe anali wachinyamata, kuti: “Usalole kuti munthu aliyense akuderere poona kuti ndiwe wamng’ono. M’malomwake, ukhale chitsanzo kwa okhulupirika m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, ndi pa khalidwe loyera.” (1 Tim. 4:12) Pa nthawi imene Paulo analemba mawuwa, Timoteyo ayenera kuti anali ndi zaka za m’ma 30. Komabe Paulo anamupatsa udindo waukulu. Kaya anamulembera malangizowa chifukwa chiyani, mfundo yake ndi yomveka bwino. Sitiyenera kuweruza abale achinyamata pongotengera msinkhu wawo. Tiyeneranso kukumbukira kuti ngakhale Ambuye wathu Yesu anachita utumiki wake padzikoli ali ndi zaka za m’ma 30 zokha.
16, 17. (a) Kodi akulu ayenera kuona chiyani kuti adziwe ngati m’bale ndi woyenerera kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu? (b) Kodi maganizo a munthu kapena chikhalidwe chake zingasiyane bwanji ndi Malemba?
16 Mwina m’chikhalidwe chathu anthu amaderera amuna achinyamata. Ngati zili choncho, akulu mumpingo mwina sangafune kuti abale achinyamata omwe ndi oyenerera akhale atumiki othandiza kapena akulu. Akulu onse angachite bwino kukumbukira kuti Malemba sanena kuti munthu angakhale mtumiki wothandiza kapena mkulu akakwanitsa zaka zinazake. (1 Tim. 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9) Ngati mkulu angaike lamulo linalake chifukwa cha mmene zilili m’chikhalidwe cha kwawo, ndiye kuti sakuchita zinthu mogwirizana ndi Malemba. Abale achinyamata ayenera kuweruzidwa mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, osati potengera chikhalidwe kapena maganizo a anthu.—2 Tim. 3:16, 17.
17 Taganizirani mmene chikhalidwe kapena maganizo a anthu angachititsire kuti abale oyenera asaikidwe pa udindo. M’dziko lina, mtumiki wothandiza wina yemwe anali woyenerera anapatsidwa maudindo akuluakulu. Ngakhale kuti akulu mumpingowo anaona kuti m’bale wachinyamatayo anali woyenerera mogwirizana ndi Malemba kuti akhale mkulu, sanaikidwe kukhala mkulu. Zinali choncho chifukwa akulu ena achikulire ankaona kuti m’baleyo ankaoneka wamng’ono kwambiri moti sangakhale mkulu. N’zomvetsa chisoni kuti m’bale wachinyamatayo sanaikidwe kukhala mkulu chifukwa choti ankaoneka wamng’ono basi. Ngakhale kuti tangofotokoza nkhani imodzi yokha, malipoti akusonyeza kuti anthu m’mipingo yambiri padziko lonse ali ndi maganizo olakwikawa. Choncho tiyenera kudalira Malemba osati chikhalidwe kapena maganizo athu. Tikamatero ndiye kuti tikumvera Yesu komanso kupewa kuweruza anthu poona maonekedwe awo.
TIZIWERUZA MWACHILUNGAMO
18, 19. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tiziona anthu mmene Yehova amawaonera?
18 Ngakhale kuti si ife angwiro, tikhoza kumaona anthu mosakondera ngati mmene Yehova amawaonera. (Mac. 10:34, 35) Koma kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuchita khama komanso kuphunzira Mawu a Mulungu pafupipafupi. Tikamatsatira mfundo zimene takambirana munkhaniyi tidzapitiriza kumvera lamulo la Yesu loti tizipewa kuweruza anthu poona maonekedwe akunja.—Yoh. 7:24.
19 Posachedwapa, Mfumu yathu Yesu Khristu adzaweruza anthu mwachilungamo ndipo sadzatengera zimene wangoona ndi maso kapena kumva ndi makutu ake. (Yes. 11:3, 4) Zimenezitu zidzakhala zosangalatsa kwambiri.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA