Tizigwira Ntchito ndi Yehova Tsiku Lililonse
“Ndife antchito anzake a Mulungu.”—1 AKOR. 3:9.
NYIMBO: 64, 111
1. Kodi tingagwire ntchito ndi Yehova m’njira ziti?
MLENGI wathu ankafuna kuti anthu angwiro azigwira naye ntchito pokwaniritsa cholinga chake. Ngakhale kuti panopa anthufe si angwiro, tikhoza kugwirabe ntchito ndi Yehova tsiku lililonse. Mwachitsanzo, timakhala “antchito anzake a Mulungu” tikamalalikira ndiponso kuphunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu. (1 Akor. 3:5-9) Ndi mwayi waukulu kwambiri kuti Mlengi wa chilengedwe chonse amationa kuti ndife oyenera kugwira naye ntchito imene iye amaiona kuti ndi yofunika kwambiri. Koma kuwonjezera pa kulalikira ndi kuphunzitsa anthu, palinso njira zina zimene timagwirira ntchito ndi Yehova. Munkhaniyi tikambirana njira monga (1) kuthandiza banja lathu komanso Akhristu anzathu, (2) kukhala ochereza, (3) kudzipereka kugwira nawo ntchito zosiyanasiyana m’gulu lathu komanso (4) kuwonjezera zimene timachita mu utumiki.—Akol. 3:23.
2. N’chifukwa chiyani si bwino kuyerekezera zimene mumachita potumikira Yehova ndi zimene ena amachita?
2 Tikamakambirana mfundo za munkhaniyi, musamayerekezere zimene mumachita potumikira Yehova ndi zimene anthu ena amachita. Tizikumbukira kuti anthu amasiyana msinkhu, thanzi, maluso komanso mmene zinthu zilili pa moyo wawo. M’pake kuti mtumwi Paulo ananena kuti: “Aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera ndi munthu wina.”—Agal. 6:4.
MUZITHANDIZA BANJA LANU KOMANSO AKHRISTU ANZANU
3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu amene amasamalira mabanja awo akuchita zinthu mogwirizana ndi Mulungu?
3 Yehova amafuna kuti atumiki ake azisamalira mabanja awo. Mwachitsanzo, mwina muyenera kugwira ntchito kuti muzipezera banja lanu zofunika pa moyo. Azimayi ambiri amafunika kukhala pakhomo n’cholinga choti azisamalira ana awo ang’onoang’ono. Ndipo anthu ena amafunika kusamalira makolo awo amene ndi odwala. Ntchito zonsezi ndi zofunika kwambiri. Paja Mawu a Mulungu amati: “Ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira, makamaka a m’banja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.” (1 Tim. 5:8) Ngati muli ndi udindo wosamalira banja lanu, mwina simungakhale ndi nthawi yambiri yochita zonse zimene mungafune m’gulu la Yehova. Koma musadandaule. Yehova amasangalala mukamasamalira banja lanu.—1 Akor. 10:31.
4. Kodi makolo angaike bwanji zofuna za Yehova pamalo oyamba, nanga zotsatira zake ndi zotani?
4 Makolo amagwiranso ntchito ndi Yehova akamathandiza ana awo kuti akhale ndi zolinga zofuna kumutumikira. Ana ambiri amene makolo awo anachita zimenezi anasamukira kutali ndi kwawo kuti akachite utumiki wa nthawi zonse. Ena mwa iwo ndi amishonale, ena akuchita upainiya m’gawo limene kukufunika ofalitsa ambiri ndipo ena akutumikira pa Beteli. N’kutheka kuti ana amene akutumikira kutali ndi makolo awo sangamacheze nawo pafupipafupi ngati mmene angafunire. Komabe, makolo amene amaika kutumikira Yehova pamalo oyamba amalimbikitsa ana awo kuti asasiye utumiki wawo. Zili choncho chifukwa chakuti amasangalala kwambiri podziwa kuti ana awowo akuika za Ufumu pamalo oyamba. (3 Yoh. 4) Mwina ambiri mwa makolowa amamva ngati mmene Hana ankamvera. Iye ankaona kuti ‘anapereka’ mwana wake, Samueli, kwa Yehova. Choncho makolowo amaona kuti ndi mwayi waukulu kwambiri kulola kuti ana awo azitumikira Yehova ndipo sangafune kuti asiye utumiki wawowo.—1 Sam. 1:28.
5. Kodi mungathandize bwanji anthu amumpingo wanu? (Onani chithunzi choyambirira.)
5 Ngati mulibe udindo waukulu wosamalira banja, kodi mungathandize Akhristu anzanu amene ndi achikulire, odwala, ali ndi mavuto ena kapena amasamalira anthu ena? Mungachite bwino kuona ngati mumpingo wanu muli anthu amene amafunika kuthandizidwa. Mwina pali mlongo wina amene amasamalira mayi kapena bambo ake achikulire ndipo mukhoza kumakacheza nawo kuti mlongoyo akhale ndi mpata wochita zinthu zina zofunika. Apo ayi, mungathandize anthu ovutika kuti azifika kumisonkhano, kukawagulira chakudya, kupita nawo kukaona ena kuchipatala kapena kuwagwirira ntchito zina. Mukamachita zimenezi mungakhale kuti mukugwira ntchito ndi Yehova pothandiza kuyankha pemphero la munthu wina.—Werengani 1 Akorinto 10:24.
MUZIKHALA OCHEREZA
6. Kodi kukhala ochereza kumatanthauza chiyani?
6 Antchito anzake a Yehova amadziwika kuti ndi ochereza. M’Malemba Achigiriki, mawu amene anamasuliridwa kuti “kuchereza” amatanthauza “kukomera mtima alendo.” (Aheb. 13:2) M’Mawu a Mulungu muli nkhani zambiri zotsimikizira kuti kusonyeza chikondi n’kofunika. (Gen. 18:1-5) Choncho tiyenera kumayesetsa kuthandiza anthu ena, kaya ndi “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro” kapena ayi.—Agal. 6:10.
7. N’chifukwa chiyani ndi bwino kuchereza anthu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse omwe abwera mumpingo wanu?
7 Kodi mungagwire ntchito ndi Mulungu pochereza anthu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse omwe abwera mumpingo wanu? (Werengani 3 Yohane 5, 8.) Tikamachita zimenezi ‘timalimbikitsana.’ (Aroma 1:11, 12) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Olaf. Iye akukumbukira kuti nthawi ina m’mbuyomu panalibe munthu mumpingo mwawo amene akanakwanitsa kuti woyang’anira dera, yemwe sanali pa banja, afikire kwawo. Pa nthawiyo Olaf anali wachinyamata ndipo anapempha makolo ake, omwe sanali a Mboni, ngati zingatheke kuti woyang’anira derayo afikire kunyumba kwawo. Iwo anavomera koma ananena kuti Olaf ayenera kugona pabalaza kuti woyang’anira derayo agone kuchipinda kwake. Olaf sanadandaule ndipo anati: “Tinasangalala kwambiri mlungu umenewo. Ine ndi woyang’anira derayo tinkadzuka m’mawa kwambiri n’kumakambirana nkhani zambiri zosangalatsa pa nthawi ya chakudya cham’mawa. Anandilimbikitsa kwambiri moti ndinayamba kufunitsitsa kuchita utumiki wa nthawi zonse.” Pa zaka 40 zapitazi, Olaf wakhala akuchita umishonale m’mayiko osiyanasiyana.
8. N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza kukoma mtima ngakhale pamene anthu sakuyamikira? Perekani chitsanzo.
8 Mukhoza kuchereza alendo m’njira zosiyanasiyana ngakhale kuti poyamba ena sangayamikire. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina ku Spain. Pamene iye ankaphunzitsa Baibulo mzimayi wina wa ku Ecuador, dzina lake Yesica, anaona kuti mzimayiyo akulira. Mlongoyo anafunsa Yesica chifukwa chake akulira. Yesica anafotokoza kuti asanasamukire ku Spain ankavutika kwambiri kupeza zinthu moti tsiku lina analibiretu chakudya. Anali ndi madzi okha kuti apatse mwana wake. Iye anayesetsa kunyengerera mwana wake kuti agone ndipo ankapemphera kuti Mulungu amuthandize. Pambuyo pake, a Mboni awiri anabwera kunyumba yake koma Yesica sanawalandire bwino ndipo anang’amba magazini amene alongowo ankafuna kumupatsa. Iye anawafunsa mopsa mtima kuti: “Mwana wanga angadye zimenezi?” Iwo anayesetsa kumukhazika mtima pansi, koma sizinathandize. Kenako alongowo anakasiya chakudya pakhomo lake. Kukoma mtima kwawo kunamukhudza kwambiri ndipo anadandaula kuti sanawalandire bwino. Anadandaulanso kuti sanazindikire kuti Mulungu ankayankha pemphero lake. Koma pambuyo pa zimenezi anayamba kufunitsitsa kuti azitumikira Yehova. Mtima wopatsa wa alongowo unathandiza kwambiri.—Mlal. 11:1, 6.
MUZIDZIPEREKA KUGWIRA NTCHITO ZOSIYANASIYANA M’GULU LA YEHOVA
9, 10. (a) Kodi atumiki a Mulungu akale ankafunika kudzipereka kuti athandize pa zinthu monga ziti? (b) Kodi masiku ano abale angathandize pa zinthu zotani mumpingo?
9 Kale ku Isiraeli, pankafunika anthu odzipereka kuti athandize pa zinthu zosiyanasiyana. (Eks. 36:2; 1 Mbiri 29:5; Neh. 11:2) Masiku ano palinso njira zambiri zimene tingathandizire abale ndi alongo athu pogwiritsa ntchito nthawi, chuma komanso maluso athu. Ngati mutachita zimenezi mudzakhala osangalala komanso mudzapeza madalitso ambiri.
10 Mawu a Mulungu amalimbikitsa abale kuti azigwira ntchito ndi Yehova poyesetsa kuti ayenerere udindo mumpingo. (1 Tim. 3:1, 8, 9; 1 Pet. 5:2, 3) Abale amene amachita zimenezi amafunitsitsa kuti azithandiza anthu m’njira zosiyanasiyana. (Mac. 6:1-4) Kodi akulu anayamba akupemphanipo kuti muthandize pa zinthu monga kulandira alendo, kusamalira mabuku, magawo kapena kukonza zinthu pa Nyumba ya Ufumu? Abale amene amathandiza pa zinthu zimenezi angavomereze kuti amasangalala kwambiri chifukwa chothandiza anthu ena.
11. Kodi mlongo wina wathandizidwa bwanji ndi anzake amene anawapeza pa nthawi imene ankagwira ntchito zomangamanga?
11 Anthu amene amadzipereka kuti agwire ntchito zosiyanasiyana m’gulu la Yehova amakhala ndi mwayi wopeza anzawo atsopano. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Margie, yemwe wakhala akugwira nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu kwa zaka 18. Pa zaka zimenezi, iye ankathandiza alongo achitsikana kuti adziwe zinthu zosiyanasiyana. Mlongoyu amaona kuti kudzipereka kugwira ntchitoyi kunamupatsa mwayi wolimbikitsana ndi Akhristu anzake. (Aroma 1:12) Margie akakumana ndi mavuto, anzake amene anawapeza pogwira ntchito zomangamanga akhala akumulimbikitsa kwambiri. Kodi munayamba mwadzipereka kugwira nawo ntchito zomangamanga? Kodi mungachite zimenezi ngakhale kuti mulibe luso lomanga?
12. Kodi mungathandize bwanji anthu amene akhudzidwa ndi ngozi?
12 Pakachitika ngozi, timakhala ndi mwayi wogwira ntchito ndi Mulungu pothandiza abale ndi alongo athu m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, tikhoza kuwathandiza ndi ndalama zathu. (Yoh. 13:34, 35; Mac. 11:27-30) Tingawathandizenso pokonza zinthu zimene zinaonongeka pa ngoziyo. Nyumba ya mlongo wina wa ku Poland dzina lake Gabriela, inawonongeka chifukwa cha kusefukira kwa madzi. Iye anasangalala kwambiri pamene abale ndi alongo a m’mipingo yapafupi ndi kwawo anabwera kudzamuthandiza. Mlongoyo ananena kuti: “Sindifotokoza za zinthu zimene zinawonongeka chifukwa si zofunika kwenikweni. Koma ndikufuna kufotokoza za madalitso amene ndinapeza. Zimene ndakumana nazozi zandithandiza kuzindikira kuti kukhala mumpingo wachikhristu ndi mwayi waukulu komanso kumakuthandiza kukhala wosangalala.” Anthu ambiri amene anathandizidwa atakumana ndi ngozi amanena kuti analimbikitsidwa kwambiri. Komanso abale ndi alongo amene amagwira ntchito ndi Yehova pothandiza anthuwa amasangalala kwambiri.—Werengani Machitidwe 20:35; 2 Akorinto 9:6, 7.
13. Kodi kudzipereka pa ntchito zosiyanasiyana kungalimbitse bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova? Perekani chitsanzo.
13 Mlongo wina dzina lake Stephanie limodzi ndi ofalitsa ena anasangalala kugwira ntchito ndi Yehova pothandiza Akhristu anzawo amene anathawa kwawo n’kubwera ku United States. Iwo anathandiza pa ntchito yopezera anthuwo malo okhala komanso zinthu zina zofunika. Stephanie ananena kuti: “Tinalimbikitsidwa kwambiri titaona kuti abalewo akusangalala komanso kuyamikira chikondi chimene abale ndi alongo apadziko lonse amasonyezana. Ngakhale kuti abale ndi alongowo anaona kuti tinawathandiza, ifeyo ndi amene tinathandizidwa kwambiri. Tikutero chifukwa tinaona abale akusonyeza chikondi, kugwirizana, chikhulupiriro komanso kudalira Yehova. Zimenezi zinatithandiza kuti tizikonda kwambiri Yehova komanso kuyamikira zimene gulu lake limatichitira.”
MUNGAWONJEZERE ZIMENE MUMACHITA MU UTUMIKI
14, 15. (a) Kodi mneneri Yesaya anasonyeza mtima wotani? (b) Kodi tingatsanzire bwanji mtima wa Yesaya?
14 Kodi mukufuna kugwira ntchito kwambiri ndi Yehova? Ngati zili choncho, kodi mungasamukire kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri? Sikuti atumiki a Mulungu amafunika kusamukira kwina kuti asonyeze mtima wopatsa. Koma abale ndi alongo amatha kudzipereka kuti akatumikire kudera lakutali ndi kwawo. Iwo ali ndi mtima wofanana ndi wa mneneri Yesaya. Yehova atamufunsa kuti: “Kodi nditumiza ndani, ndipo ndani apite m’malo mwa ife?” iye anayankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (Yes. 6:8) Kodi inunso mungakwanitse kudzipereka kukagwira ntchito kumene kukufunika thandizo? Koma kodi ndi kuti kumene tingathandize?
15 Ponena za ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa, Yesu ananena kuti: “Zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.” (Mat. 9:37, 38) Kodi mungakachite upainiya kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri? Kapena mwina mungathandize munthu wina kuti akachite zimenezi? Abale ndi alongo ambiri aona kuti njira yabwino yosonyezera kuti amakonda Mulungu ndi anzawo ndi kukachita upainiya kudera limene kukufunika olalikira ambiri. Nanga pali njira zinanso zimene mungawonjezere utumiki wanu? Mukachita zimenezi mudzakhala osangalala kwambiri.
16, 17. Kodi mungachite chiyani kuti muwonjezere zimene mumachita potumikira Yehova?
16 Kodi mungadzipereke kutumikira ku Beteli kapena kugwira ntchito zomangamanga? Mwina mungadzipereke kuchita zimenezi kwa kanthawi kapena mungamayendere kuchokera kunyumba kwanu. Nthawi zonse pamafunika anthu amene angatumikire Yehova pa ntchito iliyonse imene apemphedwa kugwira. Mwina angapemphedwe kugwira ntchito imene ikufunika kwambiri ngakhale kuti luso limene ali nalo si la ntchito imeneyo. Koma Yehova amayamikira mtima wodzipereka kugwira ntchito kulikonse kumene kungafunike antchito ambiri.—Sal. 110:3.
17 Kodi mungafune kuphunzira zinthu zina zimene zingakuthandizeni kutumikira bwino Yehova? Ngati zili choncho, mwina mukhoza kupita ku Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Sukuluyi imathandiza abale ndi alongo amene akuchita utumiki wa nthawi zonse kuti awonjezere utumiki wawo. Anthu amene amapita ku sukuluyi ayenera kukhala okonzeka kutumizidwa kulikonse akamaliza maphunzirowo. Kodi mungakonde kupita kusukulu imeneyi kuti muwonjezere utumiki wanu?—1 Akor. 9:23.
18. Kodi mungapeze zinthu ziti mukamagwira ntchito ndi Yehova tsiku lililonse?
18 Atumiki a Yehovafe timayesetsa tsiku lililonse kukhala opatsa. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti ndife abwino, okoma mtima komanso achikondi. Ndiye tikamasonyeza makhalidwe amenewa timakhala mosangalala komanso mwamtendere. (Agal. 5:22, 23) Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wanu, mukhoza kukhalabe osangalala mukamatsanzira mtima wopatsa wa Yehova komanso mukamagwira ntchito limodzi naye.—Miy. 3:9, 10.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA