NKHANI YOPHUNZIRA 34

Ndinu Amtengo Wapatali Mumpingo wa Yehova

Ndinu Amtengo Wapatali Mumpingo wa Yehova

“Mofanana ndi thupi lomwe ndi limodzi koma lili ndi ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonse za thupi, ngakhale ndi zambiri, zimapanga thupi limodzi, ndi mmenenso Khristu alili.”​—1 AKOR. 12:12.

NYIMBO NA. 101 Tizigwira Ntchito Mogwirizana

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi tili ndi mwayi wotani?

TILI ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala mumpingo wa Yehova. Timakhala mwamtendere komanso mosangalala tikamalambira limodzi ndi abale ndi alongo athu. Koma kodi ndinu ofunika bwanji mumpingo?

2. Kodi mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo chotani pamene ankalemba ena mwa makalata ake?

2 Tingaphunzire zambiri zokhudza nkhaniyi kuchokera m’chitsanzo chimene mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito pamene ankalemba ena mwa makalata ake. M’makalata amenewa, Paulo anayerekezera mpingo ndi thupi la munthu. Anayerekezeranso anthu amumpingo ndi ziwalo zathupi.​—Aroma 12:4-8; 1 Akor. 12:12-27; Aef. 4:16.

3. Kodi tikambirana mfundo zitatu ziti munkhaniyi?

3 Munkhaniyi, tikambirana zinthu zofunika zitatu zimene tingaphunzire m’chitsanzo chimene Paulo anagwiritsa ntchito. Choyamba, tiona kuti aliyense wa ife ndi wofunika * kwambiri mumpingo. Chachiwiri, tikambirana zimene tingachite ngati timaona kuti si ife ofunika mumpingo. Chachitatu, tikambirana chifukwa chimene tiyenera kumayesetsa kuchita zonse zomwe tingathe tikamatumikira Yehova mumpingo.

ALIYENSE NDI WOFUNIKA KWAMBIRI MUMPINGO

4. Kodi tikuphunzira chiyani pa Aroma 12:4, 5?

4 Mfundo yoyamba imene tikuphunzira kuchokera m’chitsanzo cha Paulo ndi yakuti aliyense ndi wofunika kwambiri mumpingo. Paulo anayamba chitsanzo chakechi ndi mawu akuti: “Monga tilili ndi ziwalo zambiri m’thupi limodzi, koma ziwalozo sizigwira ntchito yofanana, momwemonso ifeyo, ngakhale kuti ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndipo aliyense payekha ndi chiwalo cha mnzake.” (Aroma 12:4, 5) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamenepa? Ankatanthauza kuti aliyense amakhala ndi zochita zosiyana ndi za mnzake mumpingo, koma tonsefe ndi amtengo wapatali kwa Yehova.

Tili ndi zochita zosiyanasiyana mumpingo, koma tonsefe ndi ofunika (Onani ndime 5-12) *

5. Kodi Yehova wapereka chiyani mumpingo?

5 N’kutheka kuti mukamva za anthu amene ndi ofunika mumpingo, mumaganizira za amene ali ndi udindo. (1 Ates. 5:12; Aheb. 13:17) Ndi zoona kuti kudzera mwa Khristu, Yehova anapereka “mphatso za amuna” mumpingo. (Aef. 4:8) Mphatso za amuna zimenezi zikuphatikizapo abale a m’Bungwe Lolamulira, othandizira abale a m’Bungwe Lolamulira, abale a m’Makomiti a Nthambi, oyang’anira madera, abale amene amaphunzitsa sukulu zophunzitsa Baibulo, akulu mumpingo komanso atumiki othandiza. Abale onsewa amasankhidwa ndi mzimu woyera kuti azisamalira nkhosa za Yehova zomwe ndi zamtengo wapatali komanso kulimbikitsa abale ndi alongo mumpingo.​—1 Pet. 5:2, 3.

6. Mogwirizana ndi 1 Atesalonika 2:6-8, kodi abale amene anasankhidwa ndi mzimu woyera amayesetsa kuchita chiyani?

6 Abale amasankhidwa ndi mzimu woyera kuti azisamalira maudindo osiyanasiyana mumpingo. Ziwalo zosiyanasiyana zathupi monga manja ndi mapazi, zimagwira ntchito kuti zithandize thupi lonse. Mofanana ndi zimenezi, abale amene amasankhidwa ndi mzimu woyera amagwira ntchito mwakhama kuti athandize mpingo wonse. Iwo samachita zimenezi kuti anthu ena aziwapatsa ulemu. M’malomwake, cholinga chawo chimakhala kulimbikitsa abale ndi alongo awo. (Werengani 1 Atesalonika 2:6-8.) Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha abale amenewa, omwe amaganizira kwambiri zofuna za ena m’malo mwa zofuna zawo.

7. Kodi anthu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse amapeza madalitso otani?

7 Ena amatha kusankhidwa kukhala amishonale, apainiya apadera kapena apainiya okhazikika. Ndipotu abale ndi alongo ena padziko lonse anasankha kuti nthawi zonse azigwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Chifukwa cha zimenezi athandiza anthu ambiri kuti akhale ophunzira a Khristu Yesu. Ngakhale kuti ambiri mwa anthu amenewa sakhala ndi ndalama kapena zinthu zambiri, Yehova wawadalitsa kwambiri. (Maliko 10:29, 30) Abale ndi alongo amenewa timawakonda kwambiri ndipo timayamikira kukhala nawo mumpingo.

8. N’chifukwa chiyani tinganene kuti wofalitsa aliyense ndi wamtengo wapatali kwa Yehova?

8 Kodi abale amene ali ndi udindo komanso amene ali mu utumiki wa nthawi zonse ndi okhawo amene ali ofunika mumpingo? Ayi. Wofalitsa aliyense ndi wofunika kwa Mulungu komanso mumpingo. (Aroma 10:15; 1 Akor. 3:6-9) Tikutero chifukwa ntchito yofunika kwambiri imene mpingo umagwira ndi kupanga ophunzira a ambuye wathu Yesu Khristu. (Mat. 28:19, 20; 1 Tim. 2:4) Ofalitsa onse, kaya obatizidwa kapena osabatizidwa, amaona ntchito yolalikira kukhala yofunika kwambiri pa moyo wawo.​—Mat. 24:14.

9. N’chifukwa chiyani timaona kuti alongo ndi amtengo wapatali?

9 Yehova amasonyezanso kuti alongo ndi amtengo wapatali powapatsa ntchito yofunika kwambiri mumpingo. Ena mwa alongowa ali pabanja, ali ndi ana, ndi amasiye ndipo ena ndi osakwatiwa koma amamutumikira mokhulupirika. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za akazi amene anakondweretsa Mulungu. Akazi amenewa anali zitsanzo zabwino pankhani yosonyeza chikhulupiriro, nzeru, kudzipereka, kulimba mtima, kupatsa ndi ntchito zina zabwino. (Luka 8:2, 3; Mac. 16:14, 15; Aroma 16:3, 6; Afil. 4:3; Aheb. 11:11, 31, 35) Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa m’mipingo yathu muli alongo amene amasonyeza makhalidwe abwino amenewa.

10. N’chifukwa chiyani timaona kuti achikulire ndi ofunika kwambiri mumpingo?

10 Timasangalalanso kuti tili ndi achikulire ambiri m’mipingo yathu. M’mipingo ina muli abale ndi alongo amene atumikira Yehova mokhulupirika kwa moyo wawo wonse. Palinso achikulire ena omwe aphunzira choonadi posachedwapa. Komabe onsewa amavutika ndi matenda amene amabwera chifukwa cha ukalamba. Zimenezi zimachititsa kuti asamachite zambiri mumpingo komanso pa ntchito yolalikira. Ngakhale zili choncho, achikulirewa amayesetsa kuchita zonse zomwe angathe mu utumiki ndipo amagwiritsa ntchito mphamvu zawo kuti alimbikitse komanso kuphunzitsa ena. Anthu amenewa akumana ndi zambiri pa moyo wawo ndipo tingapindule kwambiri ndi zitsanzo zawo. Kunena zoona anthuwa ndi ofunika kwambiri kwa Yehova komanso kwa ife.​—Miy. 16:31.

11-12. Kodi achinyamata amumpingo wanu amakulimbikitsani bwanji?

11 Tilinso ndi achinyamata m’mipingo yathu. Iwo amakumana ndi mavuto ambiri chifukwa akukulira m’dziko limene wolamulira wake ndi Satana Mdyerekezi, yemwe amasokoneza maganizo a anthu. (1 Yoh. 5:19) Komabe timasangalala tikaona achinyamatawa akuyankha pamisonkhano, kulalikira komanso kufotokoza molimba mtima zimene amakhulupirira. Achinyamatanu, dziwani kuti ndinu ofunika kwambiri mumpingo wa Yehova.​—Sal. 8:2.

12 Komabe abale ndi alongo ena amadziona kuti ndi osafunika mumpingo. Ndiye kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tizidziona kuti ndife ofunika? Tiyeni tione.

MUZIDZIONA KUTI NDINU OFUNIKA MUMPINGO

13-14. N’chiyani chimachititsa kuti ena azidziona kuti ndi osafunika mumpingo?

13 Mfundo yachiwiri imene tikupeza m’chitsanzo cha Paulo ikutipangitsa kuganizira vuto limene anthu ambiri ali nalo masiku ano. Vuto lake ndi lakuti ambiri amadziona kuti ndi osafunika mumpingo. Paulo analemba kuti: “Ngati phazi linganene kuti: ‘Popeza sindine dzanja, sindili mbali ya thupi,’ chimenecho si chifukwa chopangitsa phazi kusakhala mbali ya thupi. Ndipo ngati khutu linganene kuti: ‘Popeza sindine diso, sindili mbali ya thupi,’ chimenecho si chifukwa chopangitsa khutu kusakhala mbali ya thupi.” (1 Akor. 12:15, 16) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamenepa?

14 Mukamadziyerekezera ndi ena mumpingo mungayambe kudziona kuti ndinu osafunika. Anthu ena mumpingo amaphunzitsa mwaluso, ndi adongosolo kapena amadziwa kulimbikitsa ena. Mwina mumaona kuti mulibe luso lochita zinthu ngati mmene iwo amachitira. Zimenezi zingasonyeze kuti ndinu odzichepetsa. (Afil. 2:3) Koma muyenera kukhala osamala. Ngati mumangokhalira kudziyerekezera ndi anthu ena omwe amachita bwino kwambiri zinthu zina, mukhoza kukhumudwa. Monga mmene Paulo ananenera, mungamadzione kuti ndinu osafunika mumpingo. N’chiyani chingakuthandizeni kuti musamadzione choncho?

15. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 12:4-11, kodi tiyenera kuzindikira chiyani pankhani ya maluso amene tingakhale nawo?

15 Taganizirani izi: Yehova anapereka mphatso za mzimu woyera kwa Akhristu ena amunthawi ya atumwi, koma mphatso zimene analandirazi sizinali zofanana. (Werengani 1 Akorinto 12:4-11.) Yehova anawapatsa mphatso komanso maluso osiyanasiyana komabe Mkhristu aliyense anali wofunika. Masiku ano sitilandira mphatso za mzimu woyera zomwe zingatithandize kuchita zinthu zodabwitsa. Koma mfundo yake ingatithandize. Tingakhale ndi maluso osiyana koma tonsefe ndi amtengo wapatali kwa Yehova.

16. Kodi ndi malangizo ati a mtumwi Paulo amene tiyenera kutsatira?

16 M’malo modziyerekezera ndi Akhristu ena, tiyenera kutsatira malangizo amene mtumwi Paulo ananena akuti: “Aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera ndi munthu wina.”​—Agal. 6:4.

17. Kodi tingapindule bwanji tikamatsatira malangizo a mtumwi Paulo?

17 Tikamatsatira malangizo a Paulo n’kumaona zimene timachita pa moyo wathu, tingayambe kuona kuti tili ndi maluso amene anthu ena alibe. Mwachitsanzo, mkulu angakhale kuti alibe luso lokamba nkhani koma angakhale ndi luso lothandiza anthu kuyamba kutumikira Yehova. Kapena sachita zinthu mwadongosolo ngati akulu ena koma ndi wokoma mtima ndipo abale ndi alongo amamasuka kumufunsa malangizo a m’Malemba. Kapenanso amakonda kuchereza alendo. (Aheb. 13:2, 16) Tikazindikira zinthu zimene timachita bwino, tingakhale osangalala podziwa kuti pali zimene tingachite mumpingo. Ndipo sitingamachitire nsanje abale amene ali ndi maluso osiyana ndi athu.

18. N’chiyani chingatithandize kuti tiziphunzitsa mwaluso?

18 Kaya timachita zotani mumpingo, tonse tiyenera kukulitsa maluso athu komanso kuchita bwino utumiki umene tapatsidwa. Pofuna kutithandiza kukwaniritsa cholinga chimenechi, Yehova amatiphunzitsa kudzera m’gulu lake. Mwachitsanzo, pamsonkhano wa mkati mwa mlungu, timalandira malangizo amene angatithandize tikamalalikira. Kodi mumayesetsa kugwiritsa ntchito zimene mumaphunzira pamsonkhanowu?

19. Kodi mungatani kuti mukwanitse kukalowa nawo Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu?

19 Yehova amatiphunzitsanso kudzera mu Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Amene angalowe sukuluyi ndi abale ndi alongo omwe amachita utumiki wa nthawi zonse ndipo ali ndi zaka kuyambira 23 mpaka 65. Koma mwina mukuona kuti simungakwanitse kulowa nawo sukuluyi. M’malo momangopeza zifukwa zimene zingakulepheretseni kulowa sukuluyi, muziganizira zifukwa zomwe zingakuchititseni kufuna kulowa sukuluyi. Kenako muziganizira zimene mungachite kuti muyenerere kukalowa sukuluyi. Ngati mutayesetsa kuchita zomwe mungathe, Yehova angakuthandizeni kuchita zimene poyamba munkaona kuti simungakwanitse.

MUZIGWIRITSA NTCHITO MALUSO ANU POLIMBIKITSA MPINGO

20. Kodi tikuphunzira chiyani pa Aroma 12:6-8?

20 Mfundo yachitatu imene tingaphunzire kuchokera m’chitsanzo cha Paulo ikupezeka pa Aroma 12:6-8. (Werengani.) Palembali Paulo anasonyezanso kuti Akhristu mumpingo amakhala ndi mphatso zosiyanasiyana. Koma ulendo uno, anatsindika mfundo yakuti tiyenera kugwiritsa ntchito mphatso zimenezi polimbikitsa mpingo.

21-22. Kodi tikuphunzira chiyani kwa M’bale Robert ndi M’bale Felice?

21 Taganizirani chitsanzo cha m’bale wina yemwe tangomutchula kuti Robert. Poyamba ankatumikira m’dziko lina koma kenako anauzidwa kuti azikatumikira pa Beteli m’dziko lakwawo. Ngakhale kuti abale anamutsimikizira kuti si kuti walakwitsa zinazake kuti asinthidwe utumiki, iye anati: “Kwa miyezi yambiri sindinkasangalala chifukwa ndinkaganiza kuti pali zinazake zimene ndinkalephera. Nthawi zina ndinkangoona kuti bola ndingosiya utumiki wa pa Beteli.” Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti ayambenso kusangalala ndi utumiki wake? Mkulu mnzake anamukumbutsa mfundo yakuti Yehova anatipatsa utumiki winawake pofuna kutikonzekeretsa kuti tidzachite bwino utumiki umene tikuchita panopa. Robert anazindikira kuti ankafunika kusiya kuganizira zam’mbuyo ndi kuyamba kuona zimene angachite panopa.

22 M’bale winanso dzina lake Felice Episcopo, anakumana ndi vuto ngati lomweli. Iye ndi mkazi wake anamaliza maphunziro a Giliyadi mu 1956 ndipo anatumikira ngati woyang’anira dera ku Bolivia. M’chaka cha 1964 anakhala ndi mwana. M’baleyu anati: “Zinali zovuta kuti tisiye utumiki umene tinkaukonda kwambiri. Kwa chaka chathunthu ndinkangokhala wokhumudwa. Koma Yehova anandithandiza kuyamba kuona zinthu moyenera ndipo ndinayamba kuyesetsa kukwaniritsa udindo wanga ngati kholo.” Kodi nanunso mumamva ngati mmene Robert kapena Felice anamvera? Kodi mumakhumudwa chifukwa munasiya utumiki umene munkachita poyamba? Ngati ndi choncho, mungakhale osangalala ngati mutasintha mmene mumaonera zinthu n’kumaganizira kwambiri zimene mungachite panopa potumikira Yehova ndi abale anu. Muzigwiritsa ntchito mphatso komanso maluso anu pothandiza ena ndipo mungamasangalale kwambiri polimbikitsa mpingo.

23. Kodi tiyenera kuchita chiyani, nanga munkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

23 Tonsefe ndi amtengo wapatali kwa Yehova. Iye amafuna kuti tikhale m’banja lake. Tikamaganizira kwambiri zimene tingachite kuti tilimbikitse abale ndi alongo n’kumayesetsa kuchita zomwe tingathe, sitingadzione kuti ndife osafunika mumpingo. Koma bwanji za mmene timaonera anthu ena mumpingo? Kodi tingasonyeze bwanji kuti timawakonda komanso kuwalemekeza? Munkhani yotsatira, tidzakambirana nkhani imeneyi.

NYIMBO NA. 24 Bwerani Kuphiri la Yehova

^ ndime 5 Tonsefe timafuna kuti Yehova azitiona kuti ndife amtengo wapatali kwa iye. Mwina nthawi zina tingamadzione ngati osafunika. Nkhaniyi itithandiza kudziwa kuti tonsefe ndi ofunika mumpingo.

^ ndime 3 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Kukhala wofunika mumpingo wa Yehova kukutanthauza zimene aliyense angachite kuti azilimbikitsa abale ndi alongo mumpingo. Zimenezi sizidalira mtundu wathu, ndalama zimene tili nazo, banja limene timachokera, chikhalidwe chathu kapena maphunziro amene tinachita.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Zithunzi zitatu zosonyeza zimene zikuchitika misonkhano isanayambe, ikuchitika komanso itatha. 1: Mkulu akupereka moni mwansangala kwa mlendo, m’bale wachinyamata wanyamula maikofoni komanso mlongo wachitsikana akucheza ndi mlongo wachikulire. 2: Ana komanso achikulire akweza manja kuti ayankhe paphunziro la Nsanja ya Olonda. 3: Banja likugwira nawo ntchito yoyeretsa m’Nyumba ya Ufumu. Mayi akuthandiza mwana wake kuti aponye ndalama m’bokosi. M’bale wachinyamata akusamalira mabuku komanso m’bale wina akulimbikitsa mlongo wachikulire.