Achinyamata, Mlengi Wanu Amafuna Kuti Muzikhala Osangalala
“Amene akukukhutiritsa pa nthawi ya moyo wako ndi zinthu zabwino.”—SAL. 103:5.
NYIMBO: 135, 39
1, 2. N’chifukwa chiyani ndi nzeru kumvera Mlengi wathu posankha zoti tichite pa moyo wathu? (Onani zithunzi zoyambirira.)
NGATI ndinu wachinyamata, muyenera kuti mwapatsidwapo malangizo ambiri okhudza tsogolo lanu. Aphunzitsi, alangizi komanso anthu ena angakulimbikitseni kuti muphunzire kwambiri n’cholinga choti mudzapeze ntchito yapamwamba. Koma izi si zimene Yehova amakuuzani kuti muchite. N’zoona kuti amafuna kuti muzilimbikira sukulu n’cholinga choti muzidzapeza zofunika pa moyo. (Akol. 3:23) Koma amafuna kuti muzitsatira mfundo zake posankha zinthu zofunika kwambiri pa moyo wanu. Amafunanso kuti muziganizira cholinga chake komanso zimene amatipempha kuti tizichita m’masiku otsirizawa.—Mat. 24:14.
2 Musaiwale kuti Yehova amadziwa zambiri chifukwa akudziwa zonse zimene zichitike padzikoli komanso nthawi imene lidzathe. (Yes. 46:10; Mat. 24:3, 36) Iye amatidziwanso bwino ndipo amadziwa zimene zingatithandize kukhala osangalala ndi zimene zingatichititse kukhala osasangalala. Choncho ngakhale malangizo a munthu atamveka abwino chotani, ngati sakugwirizana ndi Mawu a Mulungu ndiye kuti si anzeru.—Miy. 19:21.
OTSUTSANA NDI YEHOVA AMACHITA ZINTHU ZOPANDA NZERU ZOKHAZOKHA
3, 4. Kodi kutsatira malangizo opanda nzeru kunakhudza bwanji Adamu ndi Hava komanso ana awo?
3 Malangizo opanda nzeru anayamba kalekale pamene Satana analankhula ndi Hava. Anauza Hava kuti iye ndi mwamuna wake angakhale osangalala kwambiri akamasankha okha zochita. (Gen. 3:1-6) Koma Satana anali ndi zolinga zadyera. Iye ankafuna kuti Adamu ndi Hava komanso ana awo azilambira iyeyo osati Yehova. Koma Satana anali asanawachitire chilichonse chabwino. Yehova ndi amene anali atawapatsa zinthu zonse monga banja losangalala, malo okongola, matupi angwiro komanso mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha.
4 N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu ndipo anasokoneza ubwenzi wawo ndi iye. Zotsatira zake zinali zoopsa kwambiri. Mofanana ndi duwa limene limayamba kufota likathyoledwa, iwo anayamba kufooka mwapang’onopang’ono mpaka kufa. Ana awonso anakumana ndi mavuto chifukwa cha uchimo. (Aroma 5:12) Ngakhale zili choncho, anthu ambiri amasankhabe kuti asamamvere Mulungu. Iwo amafuna kuti azingochita chilichonse chimene akufuna. (Aef. 2:1-3) Zotsatira zake zimasonyeza kuti munthu akamatsutsana ndi Yehova, zochita zake zimakhala zopanda nzeru zokhazokha.—Miy. 21:30.
5. Kodi Mulungu sankakayikira chiyani zokhudza anthu, nanga zimenezi zachitikadi?
5 Koma Yehova sankakayikira kuti anthu ena akuluakulu komanso achinyamata adzafuna kumudziwa ndiponso kumutumikira. (Sal. 103:17, 18; 110:3) Iye amakonda kwambiri anthu oterewa. Kodi inuyo mumaona kuti muli m’gulu la anthu amenewa? Ngati zili choncho, muyenera kuti mukupeza “zinthu zabwino” zambiri zimene Mulungu akukupatsani zomwe zimakuthandizani kuti mukhale osangalala. (Werengani Salimo 103:5; Miy. 10:22) Tsopano tiyeni tikambirane “zinthu zabwino” zimenezi. Zinthu zake ndi chakudya chauzimu, anzathu abwino, zolinga zabwino komanso ufulu weniweni.
YEHOVA AMAKUSAMALIRANI MWAUZIMU
6. N’chifukwa chiyani muyenera kuyesetsa kuti mupeze zosowa zanu zauzimu, nanga Yehova amakusamalirani bwanji pa nkhaniyi?
6 Mosiyana ndi zinyama, anthufe timakhala ndi zosowa zauzimu ndipo amene angatisamalire pa nkhaniyi ndi Mlengi wathu yekha. (Mat. 4:4) Mukamamumvera ndi mtima wonse mumayamba kukhala ozindikira, anzeru komanso osangalala. Paja Yesu ananena kuti: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mat. 5:3) Mulungu amakusamalirani mwauzimu pogwiritsa ntchito Mawu ake ndiponso chakudya chambiri chauzimu chimene chimachokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Chakudyachi chimakhala chosiyanasiyana komanso chabwino kwambiri.—Yes. 65:13, 14.
7. Kodi chakudya chauzimu chingakuthandizeni bwanji?
7 Chakudya chauzimu chimene Mulungu amapereka chingakuthandizeni kukhala anzeru komanso oganiza bwino. Zimenezi zingakutetezeni m’njira zosiyanasiyana. (Werengani Miyambo 2:10-14.) Mwachitsanzo, kuganiza bwino komanso nzeru zingakuthandizeni kuzindikira mfundo zabodza monga yakuti kulibe Mulungu. Zingakutetezeni ku bodza lakuti ndalama ndi chuma n’zimene zingakuthandizeni kukhala osangalala. Zimakuthandizaninso kuzindikira ndiponso kupewa kulakalaka zinthu zimene zingakupwetekeni. Choncho muziyesetsa kukhala anzeru komanso oganiza bwino. Mukatero mudzaona nokha kuti Yehova amakukondani ndiponso amakufunirani zabwino.—Sal. 34:8; Yes. 48:17, 18.
8. N’chifukwa chiyani muyenera kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova panopa, nanga zimenezi zidzakuthandizani bwanji m’tsogolo?
8 Posachedwapa, mbali iliyonse ya dziko la Satana idzawonongedwa. Yehova yekha ndi amene adzatiteteze ndipo tidzayenera kumudalira pa chilichonse, mwina ngakhalenso kuti tipeze chakudya. (Hab. 3:2, 12-19) Choncho panopa ndi nthawi yoti muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova komanso kumudalira kwambiri. (2 Pet. 2:9) Mukamachita zimenezi, mudzadalira Yehova zivute zitani ngati mmene Davide ankachitira. Paja iye analemba kuti: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.”—Sal. 16:8.
YEHOVA AMAKUPEZERANI ANZANU ABWINO KWAMBIRI
9. (a) Malinga ndi Yohane 6:44, kodi Yehova amachita chiyani? (b) Kodi kukumana koyamba ndi wa Mboni kumasiyana bwanji ndi kukumana ndi munthu wina?
9 Yehova amakoka anthu amtima wabwino mwapang’onopang’ono kuti ayambe kumulambira n’kukhala m’banja lake lauzimu. (Werengani Yohane 6:44.) Mukakumana koyamba ndi munthu amene si wa Mboni, kodi mumadziwa zotani zokhudza munthuyo? Mumadziwa zochepa, mwina dzina ndi maonekedwe ake basi. Koma si mmene zimakhalira mukakumana ndi munthu amene amadziwa Yehova komanso kumukonda. Ngakhale kuti mumasiyana naye dziko, mtundu kapena chikhalidwe, mumadziwa zambiri zokhudza iyeyo ndipo iyenso amadziwa zambiri zokhudza inuyo.
10, 11. Kodi anthu a Yehova amafanana bwanji, nanga zimenezi zimawapatsa mwayi uti?
10 Mwachitsanzo, ngakhale kuti mumalankhula zilankhulo zosiyana, nonse mumadziwa “chilankhulo choyera.” (Zef. 3:9) Choncho aliyense amadziwa zimene mnzake amakhulupirira zokhudza zinthu monga Mulungu, makhalidwe abwino ndiponso zimene tikuyembekezera m’tsogolo. Ndipotu zimenezi ndi mfundo zofunika kwambiri kuzidziwa chifukwa ndi zimene zingakuthandizeni kukhulupirira munthu. Zimakuthandizaninso kuti muzigwirizana naye kwambiri.
11 Kunena zoona, popeza mumalambira Yehova muli ndi anzanu abwino kwambiri. Anzanuwo amapezeka padziko lonse kungoti simunakumane nawo. Kodi pali anthu ena, kupatulapo anthu a Yehova, amene alinso ndi mwayi umenewu?
YEHOVA AMAKUTHANDIZANI KUKHALA NDI ZOLINGA ZABWINO
12. Kodi inuyo mungakhale ndi zolinga zabwino ziti?
12 Werengani Mlaliki 11:9–12:1. Kodi muli ndi zolinga zauzimu zimene mukuyesetsa kuti mukwaniritse? N’kutheka kuti mukuyesetsa kuti muziwerenga Baibulo tsiku lililonse. Apo ayi mwina mukuchita khama kuti mukhale ndi luso lokamba nkhani kapena lophunzitsa. Mukayamba kukwaniritsa zolinga zanu kapena anthu ena akakuyamikirani pa zimene mukuchitazo, kodi mumamva bwanji? Muyenera kuti mumasangalala kwambiri. Izi ndi zomveka chifukwa mukuika zimene Mulungu amafuna pamalo oyamba ndipo mukutsatira chitsanzo cha Yesu.—Sal. 40:8; Miy. 27:11.
13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kutumikira Mulungu n’kwabwino kwambiri kuposa kufunafuna zinthu za m’dzikoli?
13 Mukamaika kutumikira Yehova pamalo oyamba, ndiye kuti mukuchita zimene zingakuthandizeni kukhala ndi cholinga chabwino pa moyo komanso kukhala osangalala. Paja mtumwi Paulo analemba kuti: “Khalani olimba, osasunthika, okhala ndi zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye, podziwa kuti zonse zimene mukuchita mu ntchito ya Ambuye sizidzapita pachabe.” (1 Akor. 15:58) Koma anthu amene amayesetsa kuti alemere kapena akhale otchuka m’dzikoli, ngakhale amene angaoneke kuti zinthu zikuwayendera bwino, sakhala osangalala. (Luka 9:25) Munthu wina amene anazindikira mfundoyi komanso anatithandiza kuidziwa ndi Mfumu Solomo.—Aroma 15:4.
14. Kodi mukuphunzira chiyani pa nkhani ya Solomo?
14 Solomo, yemwe anali wachuma kwambiri komanso mfumu, anasankha zoti ‘ayesereko kusangalala komanso kupeza zinthu zabwino.’ (Mlal. 2:1-10) Iye anamanga nyumba, kudzala mitengo ndi maluwa okongola ndiponso kuchita chilichonse chimene ankafuna. Kodi atachita zimenezi anamva bwanji? Kodi anakhala wosangalala? Solomo analemba yekha kuti: ‘Nditaganizira ntchito zonse zimene manja anga anagwira, ndinaona kuti zonse zinali zachabechabe. Panalibe chaphindu chilichonse.’ (Mlal. 2:11) Kodi inuyo mukuphunzirapo chiyani pa nkhani ya Solomoyi?
15. Mogwirizana ndi Salimo 32:8, kodi chikhulupiriro n’chofunika bwanji, nanga chingakuthandizeni bwanji?
15 Yehova safuna kuti muziphunzira nkhwangwa ili m’mutu. Koma pamafunika chikhulupiriro champhamvu kuti muzimvera Mulungu komanso kuika zofuna zake pamalo oyamba. Mukamasankha zochita chifukwa chokhulupirira Yehova simudzanong’oneza bondo ngakhale pang’ono. Ndipotu Yehova sadzaiwala ‘chikondi chimene mumachisonyeza pa dzina lake.’ (Aheb. 6:10) Choncho yesetsani kulimbitsa chikhulupiriro chanu ndipo mudzaona nokha kuti Yehova amakufunirani zabwino.—Werengani Salimo 32:8.
MULUNGU AMAKUPATSANI UFULU WENIWENI
16. N’chifukwa chiyani tiyenera kuona kuti ufulu wathu ndi wamtengo wapatali, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuugwiritsa ntchito mwanzeru?
16 Paulo analemba kuti: “Pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.” (2 Akor. 3:17) Yehova amakonda ufulu ndipo anakupatsani mtima wofuna ufuluwo. Koma amafuna kuti muzigwiritsa ntchito ufuluwo mwanzeru kuti mukhale otetezeka. Mwina mukudziwa achinyamata amene amaonera zolaula, kuchita chiwerewere, kuchita masewera oika moyo pa ngozi, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapena kuledzera. N’zoona kuti kwakanthawi angaoneke kuti akusangalala. Koma zotsatira zake zimakhala zoopsa, mwina kutenga matenda, kukhala chidakwa kapena kufa kumene. (Agal. 6:7, 8) Achinyamatawo amaona kuti ali pa ufulu koma amakhala akungodzinamiza.—Tito 3:3.
17, 18. (a) Kodi kumvera Mulungu kumatithandiza bwanji kukhala pa ufulu? (b) Kodi ufulu umene Adamu ndi Hava anali nawo poyamba ukusiyana bwanji ndi umene anthu ali nawo panopa?
17 Ndiye mudzifunse kuti, kodi ndi anthu angati amene anadwala chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo? Apa zikuonekeratu kuti kumvera Yehova n’kothandiza komanso kumatipatsa ufulu. (Sal. 19:7-11) Ndipotu mukamagwiritsa ntchito ufulu wanu motsatira mfundo za Mulungu, mumasonyeza Mulunguyo komanso makolo anu kuti mutapatsidwa ufulu wina mungaugwiritse ntchito bwino. Paja cholinga cha Yehova n’choti adzapatse atumiki ake okhulupirika ufulu weniweni womwe umafotokozedwa m’Baibulo kuti “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21.
18 Adamu ndi Hava anali ndi ufulu umenewu. Paja m’munda wa Edeni Yehova anangowapatsa lamulo loti asadye chipatso cha mtengo umodzi wokha. (Gen. 2:9, 17) Kodi munganene kuti lamulo limeneli linali lopanikiza kapena lankhanza? Ayi. Ndiye tayerekezerani ndi malamulo ambirimbiri a anthu amene timafunika kuwatsatira.
19. Kodi Yehova ndi Yesu akutiphunzitsa bwanji kuti tipeze ufulu weniweni?
19 Yehova amachita zinthu motiganizira. M’malo motipatsa malamulo ambirimbiri, iye amatiphunzitsa moleza mtima kuti tizitsatira lamulo la chikondi. Iye amafuna kuti tiziyendera mfundo zake komanso kudana ndi zoipa. (Aroma 12:9) Chitsanzo chabwino cha mmene Yehova amatiphunzitsira ndi ulaliki wapaphiri wa Yesu. Tikutero chifukwa chakuti umafotokoza zimene zimachititsa kuti munthu achite zoipa. (Mat. 5:27, 28) Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzapitiriza kutiphunzitsa tikadzalowa m’dziko latsopano kuti tizidzamutsanzira pa nkhani yokonda zabwino ndi kudana ndi zoipa. (Aheb. 1:9) Iye adzatithandizanso kuti matupi ndi maganizo athu akhale angwiro. Pa nthawi imeneyo simudzavutikanso ndi uchimo kapena zotsatira zake. Kenako mudzasangalala ndi “ufulu waulemerero” umene Yehova wakulonjezani.
20. (a) Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji ufulu wake? (b) Kodi inuyo mungatsanzire bwanji Mulungu?
20 Koma sikuti ufulu wathu m’dziko latsopano udzakhala wopanda malire. Tikutero chifukwa chakuti tizidzafunikabe kuchita zinthu mosonyeza kuti timakonda Mulungu ndi anzathu. Pochita zimenezi tidzakhala tikungotsanzira zimene Yehova amachita. Paja iye ali ndi ufulu wopanda malire koma amasankha kuti azichita zinthu mosonyeza chikondi kwa anthu ndi angelo. (1 Yoh. 4:7, 8) Apa mfundo ndi yakuti ufulu wathu umakhala weniweni ngati tikuchita zinthu motsanzira chikondi cha Mulungu.
21. (a) Kodi Davide ananena zotani zokhudza Yehova? (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?
21 Kodi inuyo mumayamikira zinthu zabwino zimene Yehova wakupatsani? Paja watipatsa chakudya chauzimu chambiri, anzathu abwino, zolinga zabwino komanso tikuyembekezera kudzakhala ndi “ufulu waulemerero.” (Sal. 103:5) Kuyamikira zimene wakuchitirani kungakuchititseni kumva ngati Davide amene anapemphera kuti: “Mudzandidziwitsa njira ya moyo. Chifukwa cha nkhope yanu, munthu adzakondwera mokwanira. Kudzanja lanu lamanja kuli chimwemwe mpaka muyaya.” (Sal. 16:11) Munkhani yotsatira tidzakambirana mfundo zina zothandiza zopezeka mu Salimo 16. Mfundo zimenezi zidzakuthandizani kudziwa zoyenera kuchita kuti mukhale ndi moyo wosangalala kwambiri.
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA